Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 3/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi ‘Angelo Ankhope 4 Aliyense’ Akuimira Chiyani?
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Chimene Muyenera Kudziŵa Ponena za Angelo
    Galamukani!—1990
  • Kodi Angelo Ndi Otani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mmene Angelo Amatikhudzira
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 3/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Angelo ndimizimu, alibe matupi anyama, nangano bwanji mumawasonyeza m’zithunzithunzi ali ndi mapiko? Kodi kumeneku kuli chabe mwambo wachipembedzo?

Kaŵirikaŵiri timasonyeza angelo ali ndi mapiko chifukwa cha malongosoledwe ophiphiritsira opezedwa m’Baibulo.

Ndinu wolondola ponena kuti zolengedwa zauzimu ziribe matupi anyama ndi mapiko enieni​—ziribenso nkhope, manja, mapazi, kapena ziŵalo zina zathupi. Komabe, pamene angelo anawonekera kwa atumiki a Mulungu, ayenera kukhala anawoneka mofanana ndi anthu enieni, popeza kuti anawonedwa molakwa kukhala anthu.​—Genesis 18:2, 22; 19:1; Oweruza 6:11-22.

Komabe, nthaŵi zina anthu analandira masomphenya a angelo ndi kuwalongosola. Mneneri Ezekieli anawona ‘zamoyo zinayi,’ ndipo m’masomphenya apambuyo pake, anazizindikira zimenezi kukhala angelo audindo otchedwa akerubi. (Ezekieli 1:5; 9:3; 10:3) Aliyense wa angelo ameneŵa anali ndi mapiko anayi, amene anasonyeza kukhoza kwawo kupita mofulumira kumbali iriyonse pomvera malamulo a Mulungu. ‘Sizinatembenuka poyenda; chirichonse chinayenda ndikulunjika kutsogolo . . . Uko mzimu unafuna kumukako zinamuka, sizinatembenuka poyenda.’​—Ezekieli 1:6, 9, 12.

Koma angelo owonedwa m’masomphenya sanawoneke ofanana nthaŵi zonse. Zolengedwa zaungelo zotchedwa aserafi zimene Yesaya anaziwona zinali ndi mapiko asanu ndi limodzi. (Yesaya 6:1, 2) Panali kusiyana ngakhale pakati pa masomphenya a Ezekieli. Mu oyamba, angelo anali ndi mapazi, manja pansi pa lirilonse la mapiko anayi, ndi nkhope zinayi (yonga nkhope ya munthu, ya mkango, ya ng’ombe, ndi ya chiombankhanga). M’masomphenya ake otsatira, imodzi ya nkhope inafanana ndi ya kerubi mmalo mwa ng’ombe, mwinamwake kusonyeza mphamvu ya akerubi. M’masomphenya enanso a zokometseredwa za kachisi wophiphiritsira, Ezekieli anawona akerubi okhala ndi nkhope ziŵiri, imodzi ya munthu ndi ina ya mkango. (Ezekieli 1:5-11; 10:7-17; 41:18, 19) M’malo Opatulikitsa a chihema, limodzinso ndi m’kachisi womangidwa ndi Solomo m’Yerusalemu, munali akerubi okhala ndi mapiko aŵiri. Awa anali pa chivundikiro chagolidi cha bokosi lotchedwa likasa lachipangano. Akerubi agolidi aŵiriwo anayang’anizana, ndipo onse aŵiri anali ndi mapiko aŵiri otambasulidwa pamwamba pa Likasalo. (Eksodo 25:10-22; 37:6-9) Pamwamba pa Likasalo (ndi chivundikiro chake) m’kachisi wa Solomo panaimirira akerubi aakulupo aŵiri agolidi, aliyense ali ndi mapiko aŵiri otambasulidwa.​—1 Mafumu 8:6-8; 1 Mbiri 28:18; 2 Mbiri 5:7, 8.

Josephus analemba kuti: “Ponena za akerubi [amenewo], palibe amene anganene kapena kuyerekezera mmene amawonekera.” Chotero, akatswiri ena amaphunziro ndi amisiri amazika zithunzithunzi zawo za angelo (makamaka akerubi) pa zotchedwa zitsanzo zamakedzana za ku Near East za milungu yamtundu wa zirombo zokhala ndi mapiko. Koma chitsogozo chodalirika kwambiri ndicho ndemanga ya Ezekieli yakuti zimene anawona ‘maonekedwe awo ndiwo anafanana ndi munthu.’ (Ezekieli 1:5) Chotero pamene angelo akumwamba amasonyezedwa pazithunzithunzi m’mabuku athu, timawasonyeza mwachisawawa mumpangidwe wa anthu. Timawasonyeza ndi mapiko chifukwa cha malongosoledwe ambiri a m’Baibulo a angelo osiyanasiyana onenedwa kukhala ndi mapiko ndi chifukwa cha ndemanga zonena za “kuuluka” kwa angelo.​—Chibvumbulutso 14:6; Salmo 18:10.

Potsirizira, tsamba 288 la Revelation​—Its Grand Climax At Hand! limasonyeza cholengedwa chakumwamba chokhala ndi mapiko, ndi korona pamutu pake ndi mfungulo m’dzanja lake. Ili ndi fanizo lapachithunzi la Chibvumbulutso 20:1: ‘Ndipo ndinawona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake.’ Timamvetsetsa kuti mngelo ameneyu wokhala ndi chifungulo ndiye Yesu Kristu wolemekezedwa. Chithunzithunzicho chimamsonyeza ali ndi mapiko kugwirizana ndi mfundo yakuti angelo owonedwa m’masophenya kaŵirikaŵiri anali ndi mapiko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena