Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 10/1 tsamba 10-15
  • Atumiki a Mulungu—Anthu Olinganizidwa ndi Achimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Atumiki a Mulungu—Anthu Olinganizidwa ndi Achimwemwe
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Atumiki Amakono Alinso Olinganizidwa
  • Olinganizidwa Komabe Achimwemwe
  • Chikondi Chimatulutsa Chimwemwe
  • Chimwemwe Chochepa Chimene Chilipo Tsopano
  • Chimwemwe Chowona Potumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Yehova Ndi Mulungu Wadongosolo
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 10/1 tsamba 10-15

Atumiki a Mulungu​—Anthu Olinganizidwa ndi Achimwemwe

“Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”​—SALMO 144:15.

1, 2. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova ali ndi kuyenera kwa kuikira miyezo atumiki ake? (b) Kodi ndi mikhalidwe iŵiri iti ya Yehova imene makamaka tiyenera kutsanzira?

YEHOVA ndiye Mfumu Yachilengedwe Chonse, Mulungu wamphamvuyonse, Mlengi. (Genesis 1:1; Salmo 100:3) Popeza ali wotero, iye moyenerera amaika miyezo ya khalidwe la atumiki ake, akumadziŵa zimene zili zabwino koposa kwa iwo. (Salmo 143:8) Ndipo iye ndiye Wopereka Chitsanzo wawo Wamkulu amene mikhalidwe yake afunikira kuitsanzira. “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa,” analemba motero mtumwi wina.​—Aefeso 5:1.

2 Mkhalidwe wa Mulungu umene tifunikira kutsanzira umakhudza kulinganiza zinthu. Iye “sali Mulungu wa chisokonezo.” (1 Akorinto 14:33) Pamene tipenda mosamalitsa zimene Mulungu walenga, timasonkhezeredwa kunena kuti iye ndiye Munthu wodziŵa kulinganiza zinthu koposa m’chilengedwe chonse. Komabe, mkhalidwe wina wa Mulungu umene amafuna kuti atumiki ake atsanzire ndiwo chimwemwe chake, pakuti iye ali “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Motero, kukhoza kwake kwa kulinganiza zinthu kuli kolinganizika ndi chimwemwe. Mkhalidwe umodzi sumakulitsidwa kuposa wina.

3. Kodi thambo la nyenyezi limasonyeza motani kukhoza kwa Mulungu kwa kulinganiza?

3 Zonse zimene Yehova wapanga, kuyambira pachinthu chachikulu koposa kufikira pa kanthu kochepetsetsa, zimapereka umboni wakuti iye ali Mulungu wolinganiza zinthu. Mwachitsanzo, talingalirani za chilengedwe chooneka. Chili ndi zikwi za mamiliyoni zikwi a nyenyezi. Koma zimenezi sizomwazikana paliponse mopanda dongosolo. Katswiri wa physics ya zakuthambo George Greenstein akunena kuti “m’kalinganizidwe ka nyenyezi muli dongosolo.” Izo zalinganizidwa m’magulu otchedwa milalang’amba, ena okhala ndi mazana a mamiliyoni zikwi a nyenyezi. Ndipo kukuyerekezeredwa kuti pali mamiliyoni zikwi zambiri ya milalang’amba! Milalang’ambayonso njolinganizidwa, yambiri ya iyo (kuyambira pa yoŵerengeka kufikira pa zikwi zingapo) ili m’magulu a milalang’amba. Ndipo magulu a milalang’ambawo akulingaliridwa kukhala olinganizidwa m’magulu aakuludi otchedwa magulu aakulu koposa.​—Salmo 19:1; Yesaya 40:25, 26.

4, 5. Perekani zitsanzo za kulinganizika kumene kuli pa zinthu zamoyo za padziko lapansi.

4 Kulinganizika kopambana kwa chilengedwe cha Mulungu kumaoneka kulikonse, osati kokha kuthambo looneka komanso padziko lapansi, lokhala ndi zinthu zake zamoyo miyandamiyanda. Ponena za zinthu zonsezi, Paul Davies, profesa wa physics, analemba kuti openyerera “amachita mantha” ndi “kulinganizika kwakukulu ndi kocholoŵana kwa dziko lotizingali.”​—Salmo 104:24.

5 Lingalirani zitsanzo zingapo za “kulinganizika . . . kocholoŵana” kumene kumapezeka m’zinthu zamoyo. Dokotala wa opaleshoni ya ubongo ndi mitsempha Joseph Evans ponena za ubongo wa munthu ndi minyewa ya m’fupa lamsana anati: “Mkhalidwe weniweni wa dongosolo lalikululo ngwochititsa mantha.” Ponena za selo lamoyo laling’onong’ono, katswiri wa sayansi ya tizilombo H. J. Shaughnessy anati: “Kucholoŵana ndi dongosolo labwino kwambiri la tamoyo tating’ono nzolinganizidwa bwino kwambiri kwakuti zimaonekera kukhala mbali ya dongosolo loikidwa ndi Mulungu.” Ndipo katswiri wa molecular biology Michael Denton ponena za dongosolo la majini (DNA) lokhala mkati mwa selo anati: “Limagwira ntchito bwino kwakuti chidziŵitso chonse . . . chofunikira kusiyanitsira mpangidwe wa mitundu yonse ya zamoyo zimene zakhala ndi moyo pa pulaneti . . . chingathe kuikidwa m’tisupuni ndipo mungakhalebe malo otsala a chidziŵitso chonse cha m’buku lililonse limene linalembedwapo.”​—Onani Salmo 139:16.

6, 7. Kodi ndi kulinganizika kotani kumene kukusonyezedwa pakati pa zolengedwa zauzimu, ndipo kodi ndimotani mmene zimenezi zimasonyezera chiyamikiro kwa Mpangi wawo?

6 Yehova samangolinganiza chabe chilengedwe chake chakuthupi komanso amalinganiza chilengedwe chake chauzimu kumwamba. Danieli 7:10 amatidziŵitsa kuti angelo ofikira ‘zikwizikwi anamtumikira, naima pamaso pa Yehova.’ Mamiliyoni zana a zolengedwa zauzimu zamphamvu zotumikira, aliyense wopatsidwa ntchito yake yoyenera! Kuganiza za luso limene liyenera kukhala litagwiritsiridwa ntchito kulinganizira chiŵerengero chachikulukulu chotero nkozunguzitsa mutu. Moyenerera, Baibulo limati: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; amphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse [aungelo]; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.”​—Salmo 103:20, 21; Chivumbulutso 5:11.

7 Ha, zimene Mlengiyo anapanga nzolinganizidwa modabwitsa ndipo zimagwira ntchito bwino chotani nanga! Mposadabwitsa kuti zolengedwa zauzimu zamphamvuzo kumwamba zimalengeza mwaulemu ndi mogonjera kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”​—Chivumbulutso 4:11.

8. Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti Yehova amalinganiza atumiki ake padziko lapansi?

8 Yehova amalinganizanso atumiki ake padziko lapansi. Pamene anadzetsa Chigumula cha m’tsiku la Nowa mu 2370 B.C.E., Nowa ndi anzake asanu ndi aŵiri anapulumuka Chigumulacho monga gulu lolinganizika la banja. Paulendo wotchedwa Eksodo mu 1513 B.C.E., Yehova anatulutsa mamiliyoni angapo a anthu ake mu ukapolo wa ku Igupto ndi kuwapatsa mpambo womvekera bwino wa malamulo olinganizira zochita zawo zatsiku ndi tsiku ndi kulambira. Ndipo pambuyo pake, ali m’Dziko Lolonjezedwa, zikwi makumi ambiri a iwo analinganizidwa kaamba ka utumiki wapadera pa kachisi. (1 Mbiri 23:4, 5) M’zaka za zana loyamba, mipingo Yachikristu inalinganizidwa pansi pa chitsogozo chaumulungu: “Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki.”​—Aefeso 4:11, 12.

Atumiki Amakono Alinso Olinganizidwa

9, 10. Kodi ndimotani mmene Yehova walinganizira anthu ake m’nthaŵi yathu?

9 Mofananamo, Yehova walinganiza atumiki ake amakono kotero kuti achite ntchito yake ya m’tsiku lathu bwino lomwe​—kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wake iyeyo asanadzetse mapeto a dongosolo la zinthu losapembedza limene lilipoli. (Mateyu 24:14) Lingalirani zimene zikuloŵetsedwa m’ntchito imeneyi ya padziko lonse ndi mmene kulinganiza kwabwino kulili kofunika. Mamiliyoni a amuna, akazi, ndi ana akuphunzitsidwa kuphunzitsa ena choonadi cha Baibulo. Kuthandiza pa maphunziro ameneŵa, Mabaibulo ndi zofalitsidwa zofotokoza Baibulo zochuluka koposa zikusindikizidwa. Eya, kope lililonse la Nsanja ya Olonda tsopano likusindikizidwa m’makope oposa 16 miliyoni m’zinenero 118, ndipo Galamukani! pafupifupi makope 13 miliyoni m’zinenero 73. Pafupifupi makope onse akusindikizidwa panthaŵi yofanana kotero kuti pafupifupi atumiki onse a Yehova amapeza chidziŵitso chimodzimodzicho panthaŵi yofanana.

10 Ndiponso, mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 73,000 padziko lonse yalinganizidwa kuti izisonkhana nthaŵi zonse kaamba ka malangizo a Baibulo. (Ahebri 10:24, 25) Palinso zikwi zambiri za misonkhano yaikulu​—misonkhano yadera ndi misonkhano yachigawo​—chaka chilichonse. Pali ntchito yomanga Nyumba Zaufumu zatsopano kapena kuzikonzanso, Nyumba za Misonkhano, nyumba za Beteli, ndi malo osindikizira mabuku a Baibulo, yochitidwa padziko lonse. Pali sukulu za maphunziro apamwamba za aphunzitsi a Baibulo, monga ngati Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower ya amishonale ndi Sukulu Yautumiki Waupainiya, ochititsidwa m’maiko ambiri padziko lonse.

11. Kodi ndi mapindu amtsogolo otani amene adzadza chifukwa cha kuphunzira kulinganiza kwabwino tsopano lino?

11 Yehova walinganiza bwino chotani nanga anthu ake padziko lapansi kuti ‘akwaniritse utumiki wawo,’ mothandizidwa ndi angelo ake otumikirawo! (2 Timoteo 4:5; Ahebri 1:13, 14; Chivumbulutso 14:6) Mwa kulangiza atumiki ake m’njira za kulinganiza kwabwino tsopano lino, Mulungu akukwaniritsa kanthu kena. Atumiki ake akukonzekeretsedwa bwino kotero kuti pamene apyola mapeto a dongosolo ili la zinthu, iwo adzakhala olinganizidwa kale kuyamba moyo wina m’dziko latsopano. Ndiyeno, m’njira yolinganizidwa pansi pa chitsogozo cha Yehova, iwo adzayamba kumanga Paradaiso wadziko lonse. Adzakhalanso okonzekera bwino lomwe kuphunzitsa zofuna za Mulungu zomvekera bwino kaamba ka moyo ku mamiliyoni zikwi a anthu amene adzaukitsidwa kwa akufa.​—Yesaya 11:9; 54:13; Machitidwe 24:15; Chivumbulutso 20:12, 13.

Olinganizidwa Komabe Achimwemwe

12, 13. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Yehova amafuna kuti anthu ake akhale achimwemwe?

12 Pamene kuli kwakuti Yehova ali wantchito wamkulu kopambana ndi wodziŵa kulinganiza bwino zinthu, iye sali wopanda ubwenzi, wouma khosi, kapena wochita zinthu mosalingalira. Mmalomwake, iye ndi Munthu wachikondi ndi wachimwemwe kwambiri, amene amadera nkhaŵa za chimwemwe chathu. “Iye asamalira inu,” akulengeza motero 1 Petro 5:7. Tingathe kuona chisamaliro chake pa atumiki ake ndi chikhumbo chake chakuti iwo akhale achimwemwe m’zimene iye wapangira anthu. Mwachitsanzo, pamene Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi angwiro, anawaika m’paradaiso wa chisangalalo. (Genesis 1:26-31; 2:8, 9) Iye anawapatsa zonse zimene anafunikira kuwachititsa kukhala achimwemwe kwambiri. Komano anataya zonsezo kupyolera mwa chipanduko. Monga chotulukapo cha uchimo wawo, tinalandira choloŵa cha kupanda ungwiro ndi imfa.​—Aroma 3:23; 5:12.

13 Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro tsopano lino, anthufe tingathe kupezabe chimwemwe m’zimene Mulungu wapanga. Pali zinthu zambiri zimene zimatipatsa chisangalalo​—mapiri aakulu; nyanja, mitsinje, nyanja zamchere ndi magombe okongola; maluŵa okongola onunkhira bwino ndi zomera zina zambirimbiri zosiyanasiyana; zakudya zambiri zokoma; kuloŵa kwa dzuŵa kochititsa chidwi kumene sitimatopa nako; thambo lanyenyezi zimene timasangalala kupenyerera mosinkhasinkha usiku; chilengedwe cha nyama zosiyanasiyana ndi ana ake okongola oseŵera moseketsa; nyimbo zotsitsimula mtima; ntchito yokondweretsa ndi yothandiza; mabwenzi abwino. Nkwachionekere kuti Uyo amene analinganiza zinthu zotero ndi munthu wachimwemwe amene amasangalala kuchititsa ena kukhala achimwemwe.

14. Kodi nkulinganizika kotani kumene Yehova akutipempha kumtsanzira?

14 Motero, kuyenda bwino kwa zinthu kolinganizika sindiko kokha kumene Yehova amafuna. Iye amafunanso kuti atumiki ake akhale achimwemwe, monga momwe iye alili wachimwemwe. Samafuna kuti iwo akhale olinganiza zinthu motengeka maganizo moti nkuwonongetsa chimwemwe chawo. Atumiki a Mulungu ayenera kuchititsa maluso a kulinganiza zinthu kukhala olinganizika ndi chimwemwe, monga momwe iye amachitira, pakuti pamene pali mzimu wake woyera wamphamvuwo, palinso chimwemwe. Indedi, Agalatiya 5:22 amasonyeza kuti chipatso chachiŵiri cha mzimu woyera wa Mulungu wogwira ntchito pa anthu ake ndicho “chimwemwe.”

Chikondi Chimatulutsa Chimwemwe

15. Kodi nchifukwa ninji chikondi chili chofunika kwambiri pa chimwemwe chathu?

15 Nkokondweretsa kwambiri kudziŵa kuti Baibulo limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8, 16) Ilo silimanena konse kuti: “Mulungu ndiye kulinganizika.” Chikondi ndicho mkhalidwe waukulu wa Mulungu, ndipo chiyenera kutsanziridwa ndi atumiki ake. Nchifukwa chake chipatso choyamba cha mzimu wa Mulungu chondandalikidwa pa Agalatiya 5:22 chili “chikondi,” ndipo “chimwemwe” chikumatsatira. Chikondi chimatulutsa chimwemwe. Pamene titsanzira chikondi cha Yehova m’zochita zathu ndi ena, chimwemwe chimatsatira, pakuti anthu achikondi ndiwo achimwemwe.

16. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kufunika kwa chikondi?

16 Kufunika kwa kutsanzira chikondi chaumulungu kwadziŵikitsidwa kwambiri m’kuphunzitsa kwa Yesu. Iye anati: “Monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” (Yohane 8:28) Kodi nchiyani makamaka chimene Yesu anaphunzitsidwa, chimene nayenso anaphunzitsa ena? Chinali chakuti malamulo aŵiri aakulu koposa ndiwo a kukonda Mulungu ndi kukonda mnansi. (Mateyu 22:36-39) Yesu anasonyeza chitsanzo cha chikondi chotero. Iye anati: “Ndikonda Atate,” akumasonyeza zimenezi mwa kuchita chifuniro cha Mulungu kufikira imfa. Ndipo anasonyeza kukonda kwake anthu mwa kuwafera. Mtumwi Paulo anauza Akristu mu Efeso kuti: ‘Kristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwanu.’ (Yohane 14:31; Aefeso 5:2) Motero, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.”​—Yohane 15:12, 13.

17. Kodi ndimotani mmene Paulo anasonyezera kuti kusonyeza chikondi kwa ena nkofunika?

17 Paulo anasonyeza mmene chikondi chaumulungu chimenechi chilili chofunika mwa kunena kuti: “Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziŵe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ayi. . . . Zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi.”​—1 Akorinto 13:1-3, 13.

18. Kodi nchiyani chimene tingayembekezere kwa Yehova chimene chimawonjezera chimwemwe chathu?

18 Pamene titsanzira chikondi cha Yehova, tingadalire kuti adzatikonda, ngakhale ngati tipanga zolakwa, pakuti iye ndiye “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 34:6) Ngati tilapa moonadi pamene tipanga zolakwa, Mulungu samasunga mangawa a zimenezi koma mwachikondi amatikhululukira. (Salmo 103:1-3) Inde, “Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Kudziŵa zimenezi kumawonjezera chimwemwe chathu.

Chimwemwe Chochepa Chimene Chilipo Tsopano

19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji chimwemwe chachikulu chili chosatheka tsopano lino? (b) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti ife tingakhale ndi chimwemwe chochepa panthaŵi ino?

19 Komabe, kodi nkotheka kukhala wachimwemwe lerolino, tikumakhala ndi moyo monga momwe tikukhaliramu m’masiku otsiriza a dziko ili lodzala ndi upandu, chiwawa, ndi chisembwere lolamuliridwa ndi Satana, mmene timayang’anizana ndi matenda ndi imfa? Zoonadi, sitingayembekezere kukhala ndi mlingo wachimwemwe umene udzakhala m’dziko latsopano la Mulungu, monga umene umanenedweratu ndi Mawu ake kuti: “Taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.”​—Yesaya 65:17, 18.

20 Chimene atumiki a Mulungu angakhale nacho tsopano lino ndicho chimwemwe chochepa chifukwa chakuti amadziŵa chifuniro chake ndipo ali ndi chidziŵitso cholongosoka cha madalitso abwino kwambiri amene ati adze posachedwapa m’dziko lake latsopano la paradaiso. (Yohane 17:3; Chivumbulutso 21:4) Nchifukwa chake Baibulo limati: “Yehova wa makamu, wodala munthu wakukhulupirira Inu,” “wodala yense wakuwopa Yehova, wakuyenda m’njira zake,” “odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Salmo 84:12; 128:1; Mateyu 5:5) Motero, mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta imene ilipoyi imene tiyenera kulimbana nayo, ife tingakhale ndi mlingo wokulirapo wa chimwemwe. Ngakhale pamene zinthu zoipa zitichitikira, sitimakhala achisoni monga mmene amachitira awo amene samadziŵa Yehova ndi amene alibe chiyembekezo cha moyo wosatha.​—1 Atesalonika 4:13.

21. Kodi ndimotani mmene kudzipereka kwawo kumachirikizira chimwemwe cha atumiki a Yehova?

21 Chimwemwe chimadzanso kwa atumiki a Yehova chifukwa chakuti amapereka nthaŵi, nyonga, ndi ndalama kuti aphunzitse choonadi cha Baibulo kwa ena, makamaka kwa anthu amene “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse” zochitidwa m’dziko la Satana. (Ezekieli 9:4) Baibulo limati: “Wodala iye amene asamalira wosauka: tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa: Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi.” (Salmo 41:1, 2) Monga momwe Yesu ananenera, “kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

22. (a) Ponena za chimwemwe, siyanitsani atumiki a Mulungu ndi awo amene samamtumikira. (b) Kodi ndi kaamba ka chifukwa chapadera chotani chimene ife tiyenera kuyembekezera kukhala achimwemwe?

22 Chotero pamene kuli kwakuti atumiki a Mulungu sangathe kuyembekezera chimwemwe chachikulu koposa panthaŵi inoyo, iwo angapeze chimwemwe chimene sichimapezedwa ndi awo amene samatumikira Mulungu. Yehova akulengeza kuti: “Taonani, atumiki anga adzaimba ndi mtima wosangalala, koma inu mudzalira ndi mtima wachisoni; ndipo mudzafuula chifukwa cha kusweka mzimu.” (Yesaya 65:14) Ndiponso, awo amene amatumikira Mulungu ali ndi chifukwa chapadera kwambiri chokhalira achimwemwe tsopano lino​—ali ndi mzimu wake woyera umene “Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.” (Machitidwe 5:32) Ndipo kumbukirani, pamene pali mzimu wa Mulungu, pali chimwemwe.​—Agalatiya 5:22.

23. Kodi nchiyani chimene chidzalingaliridwa m’nkhani yathu yotsatira?

23 M’gulu la atumiki a Mulungu lerolino, mbali yofunika ikuchitidwa ndi “akulu,” amene amatsogolera m’mipingo, akumachirikiza chimwemwe cha anthu a Yehova. (Tito 1:5) Kodi ndimotani mmene ameneŵa ayenera kuonera mathayo awo ndi unansi wawo kwa abale ndi alongo awo? Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza zimenezi.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi ndimotani mmene chilengedwe chimachitira umboni wakuti Yehova ali wolinganizika?

◻ Kodi ndimotani mmene Yehova walinganizira atumiki ake m’nthaŵi yakale ndiponso tsopano lino?

◻ Kodi nkulinganizika kotani kumene Yehova amafuna kwa ife?

◻ Kodi chikondi nchofunika motani pa chimwemwe chathu?

◻ Kodi ndi chimwemwe chotani chimene tingayembekezere m’nthaŵi yathu?

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Pamwamba: Mwachilolezo cha ROE/​Anglo-Australian Observatory, chojambulidwa ndi David Malin

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena