Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 12/8 tsamba 20-23
  • Gawo 8: Nsanganizo Wandale Zadziko wa Chitsulo ndi Dongo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gawo 8: Nsanganizo Wandale Zadziko wa Chitsulo ndi Dongo
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusokonezedwa ndi Loto
  • ‘Zala Khumi Zakumapazi’
  • Chitsulo ndi Dongo
  • Mphamvu ya Anthu
  • Zokamba Mbwe, Zochita Pang’ono
  • Mpata wa Chiyembekezo?
  • Kuimirira ndi Kugwa kwa Fano lalikulu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Masinthidwe a Dziko Onenedweratu Kufikira ku Ufumu wa Mulungu
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • M’mene Ufumu wa Mulungu Ukukhalira Boma la Dziko
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 12/8 tsamba 20-23

Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso

Gawo 8: Nsanganizo Wandale Zadziko wa Chitsulo ndi Dongo

Utundu: lingaliro la kuzindikira mtundu lomakweza mtundu umodzi pamwamba pa ina ndikumathokoza mwambo ndi zabwino zake patsogolo pa za inayo; lingaliro limene linayamba kuwonekera kumapeto kwa zaka za zana la 18 koma limene lafika pachimake m’zaka za zana la 20.

PODZANDIRA mosoŵa chochita kuchokera ku vuto ili kunka kulinzake, maboma a anthu akulephera kudzetsa kukhazikika pa chitaganya cha anthu. Mogwirizana ndi kunena kwa Zbigniew Brzezinski, phungu wa chisungiko chadziko wa yemwe kale anali pulezidenti wa U.S. Jimmy Carter, mkhalidwewo sudzasintha mwamsanga.

Brzezinski, limodzi ndi atsogoleri ena adziko, anafunsidwa ndi mtola nkhani wamkazi Georgie Anne Geyer pamene ankakonzekera nkhani yodzafalitsidwa mu 1985 yamutu wakuti “Dziko Lathu Lomanyonyotsoka.” Mkati mwake iye anagwira mawu Brzezinski kukhala anati: “Nakatande wochititsa kusakhazikika kwa mitundu yonse akukhala wamphamvu m’mbiri yonse kupambana magulu amene akugwirira ntchito pakudzetsa chigwirizano cholinganizika bwinopo. Chigamulo chosapeŵeka chofikiridwa ndi kupenda kulikonse kochitidwa pa zikhoterero za padziko lonse nchakuti chipwirikiti cha zakakhalidwe, m’gwedegwede wandale zadziko, mavuto a zachuma, ndi kukangana kwa mitundu yonse mwachiwonekere zidzafalikira mowonjezereka mkati mwa nthaŵi yotsala ya zaka za zana lino.”

Kumeneku ndikulosera kodetsa nkhaŵa ndithu koma kosadabwitsa ophunzira Baibulo. Mkhalidwe weniweniwu unanenedweratu kalekale. Liti? Kuti?

Kusokonezedwa ndi Loto

Nebukadinezara, mfumu ya Babulo kuchokera mu 624 mpaka 582 B.C.E., anavutitsidwa maganizo ndi loto. M’kulotako iye adawona fano lalikulu lokhala ndi mutu wagolidi, chifuŵa ndi manja zasiliva, mimba ndi chuuno zamkuwa, miyendo yachitsulo, mapazi ndi zala zachitsulo chosanganizidwa ndi dongo. Mneneri wa Mulungu Danieli analongosola kwa Nebukadinezara kumasulira kwa fanolo, namuuza kuti: ‘Inu mfumu, . . . inu ndinu mutuwo wagolidi. Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi.’ Chotero, mwachiwonekere, fanolo linali kusonya ku ulamuliro wa anthu.—Danieli 2:37-39.

Nthaŵi ya Danieli isanafike, onse aŵiri Igupto ndi Asuri adapondereza Aisrayeli, anthu osankhidwa a Mkonzi wa Baibulo. (Eksodo 19:5) M’mawu apambuyo ndi patsogolo a Baibulo, ichi chinawapangitsa iwo kukhala maulamuliro adziko lonse, kwenikweni, oyambirira a mpambo wa asanu ndi aŵiri amene Baibulo limawasimba. (Chibvumbulutso 17:10) Ndiyeno, m’tsiku la Danieli, Babulo anagwetsa Yerusalemu, nakakamiza Aisrayeli kupita muukapolo. Chotero Babulo anakhala wachitatu wa maulamuliro adziko lonse ameneŵa, wosonyedwako moyenerera m’nkhani ino monga “mutu wa golidi.” Baibulo ndi mbiri yakudziko zimatchula maulamuliro adziko lonse omwe ankabwerabe kukhala Medi ndi Perisiya, Girisi, Roma, ndipo, womalizira, Anglo-Amereka.a

Mitundu imeneyi ikutchedwa m’Baibulo kukhala maulamuliro adziko lonse chifukwa chakuti inali ndi zochita ndi anthu a Mulungu ndipo inatsutsa ulamuliro waumulungu umene atumiki a Mulungu ameneŵa anauchirikiza. Chotero, fano lowonedwa ndi Nebukadinezara linachitira chithunzi bwino lomwe mmene ulamuliro wa anthu ukapitirizira kuyendetsedwa motsutsana ndi uchifumu wa Mulungu ngakhale pambuyo pa kutha kwa ufumu wake. Kuloŵana m’malo kwa maulamuliro adziko lonse kochitiridwa chithunzi ndi mbali zosiyanasiyana za fanolo kunayambira ku mutu ndikumatsikira pansi. Pamenepa, nkwanzeru kuti, mapazi ndi zala zikachitira chithunzi kuwonekera kwa ulamuliro womalizira wa anthu umene ukakhalako mkati mwa ‘nthaŵi ya chimaliziro,’ monga momwe Danieli anatchulira. Pamenepa, kodi tiyenera kuyembekezeranji?—Danieli 2:41, 42; 12:4.

‘Zala Khumi Zakumapazi’

Atumiki a Mulungu salinso mumtundu umodzi wokha kapena malo amodzi, kwakuti angaponderezedwe ndi ulamuliro umodzi wadziko. (Machitidwe 1:8; 10:34, 35) Monga ziŵalo za mitundu yonse, nzika za mtundu uliwonse wa boma la anthu, iwo amalengeza mwachangu kuti nthaŵi yachimaliziro inayamba kale ndikuti nthaŵi ya kulamulira kwa anthu yatha—posachedwapa uyenera kuloŵedwa m’malo ndi ulamuliro waumulungu.b Chotero, uthenga womwe akuulengeza molimba mtima umakhudza maulamuliro onse andale zadziko omwe alipo. Moyenerera, chiŵerengerocho “khumi” monga momwe chimagwiritsiridwa ntchito m’Baibulo chimatanthauza kukwanira kwa zinthu zapadziko lapansi. Chotero kulamulira kwa ndale zadziko konseko kwa anthu, ogwirizana m’kutsutsa ulamuliro wa Mulungu mkati mwa nthaŵi yamapeto, ndikumene moyenerera ‘zala khumi zakumapazi’ za fanolo zikuimira.

Kodi mkhalidwe wandale zadziko unali wotani kuchiyambi kwa nyengo yanthaŵi yonenedweratu imeneyi? M’chaka cha 1800, maiko a ku Yuropu analamulira 35 peresenti ya dziko lapansi, koma podzafika mu 1914 chiŵerengerocho chidakwera kupyola 84 peresenti! The Collins Atlas of World History imati “pa madzulo, nkhondo ya 1914 isanakanthe tsiku lotsatira, kunawonekera ngati kuti kugaŵidwa kwa dziko pakati pa chiŵerengero cha maulamuliro aakulu kunali kunatsala nenene kutha.” Kwenikweni, Hugh Brogan, mphunzitsi wa mbiri yakale pa Yunivesiti ya Essex, Mangalande, akuti zinawoneka kuti “posapita nthaŵi yaitali dziko lonse likalamuliridwa ndi theka la maulamuliro khumi ndi aŵiri.”

Komabe, kugwiritsira ntchito ‘zala khumi zakumapazi’ kuphiphiritsira maboma onse adziko omwe m’lingaliro lenileni sakaposa pa kokha “theka la maulamuliro khumi ndi aŵiri,” sikungawoneke kukhala kwanzeru konse. Chotero ngati, m’kukwaniritsidwa kwaulosiwo, ‘zala khumi zakumapazi’ zikakhala ndi tanthauzo lenileni, mkhalidwe wandale zadziko wokhalako mu 1914 unayenera kusintha.

Pamene zaka za m’ma 1900 zinafika, Ufumu wa Briteni, waukulu koposa umene dziko silinawonepo, unalamulira pa munthu wachinayi aliyense padziko lapansi. Maufumu ena a ku Yuropu analamulira anthu ena mamiliyoni ambiri. Koma Nkhondo Yadziko ya I inatulukapo kupambana kwa utundu. Paul Kennedy, profesa wa mbiri yakale pa Yunivesiti ya Yale, akufotokoza kuti: “Kusintha kochititsa chidwi koposa m’Yuropu, kozindikiridwa m’malamulo am’madera, kunali kubuka kwa gulu la mizinda yamaiko—Poland, Chekosolovakiya, Austria, Hungary, Yugoslavia, Finland, Estonia, Latvia, ndi Lithuania—m’malo amene kale anali mbali ya maufumu a Habsburg, Romanov, ndi Hohenzollern.”

Pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya II, kachitidweka kanawonjezereka. Utundu unabukiratu mwamphamvu. Makamaka pambuyo pa chapakati pa ma 1950, mpamene kachitidweka kanali kosabwezeka. Zaka mazana asanu a kufutukuka kwa Yuropu zinkathera m’mabwinja a kugwa kwa maufumu achitsamunda. Mitundu yambiri mu Afirika, Asia, ndi Middle East inakula mofulumira.

The New Encyclopædia Britannica imati “kuchitika kwa zinthuku kunapitirizabe mosemphana ndi ziphunzitso zofala zokhala ndi andale zadziko kwa zaka 2,000 zapitazo.” Pamene kuli kwakuti “mpaka panthaŵiyi anthu adagogomezera mkhalidwe wachisawawa ndi wakonsekonse ndipo adawona chigwirizano kukhala chonulirapo chokhumbiridwa,” utundu tsopano unagogomezera kusiyana kwamitundu. Mmalo mogwirizanitsa, unakhoterera kulekanitsa.

Chitsulo ndi Dongo

Onani kuti Baibulo limalongosola mapazi ndi zala za fanolo kukhala ‘mwina chitsulo mwina dongo la woumba,’ ndikuwonjezera kuti: ‘Ufumuwo udzakhala wogawanika, . . . mwina wolimba mwina wogamphuka . . . , koma sadzaphatikizana.’ (Danieli 2:33, 41-43) Kulephera kuphatikizana pamodzi mogwirizana kumeneku kunakhala kowonekera pamene kuthetsa ulamuliro wachitsamunda kunayambika, utundu nufalikira, ndipamene maiko otukuka kumene anakhazikika bwinopo. Dziko lapansi likagamphuka mofulumira kukhala zidutswa za ndale zadziko.

Mofanana ndi nsanganizo wosagwirana wa chitsulo ndi dongo m’mapazi ndi zala zake za fanolo, maboma ena akhala ngati chitsulo—opondereza kapena otsendereza—ndipo ena akhala ngati dongo—omvetsera anthu kwambiri kapena ademokrase. Momvekera, iwo akhala osakhoza kuphatikizana pamodzi kukhala dziko logwirizana. Potchula zimenezi m’tsiku lathu, bukhu Lachijeremani lotchedwa Unsere Welt—Gestern, Heute, Morgen; 1800-2000 (Dziko Lathu—Dzulo, Lero, ndi Mawa; 1800-2000), limati: “Podzafika zaka za zana la 19, ufulu wa demokrase unafalikira pafupifupi m’maiko onse otsungula, ndipo pofika kumapeto kwa Nkhondo Yadziko ya I, cholinga cha ufulu chinawonekera kukhala chitafikira chilakiko chake chomalizira. . . . Pokhala ndi kusintha kwa zinthu kwa m’Russia mu 1917, ulamuliro wotsendereza ufulu unabukanso. Chiyambire pamenepo zaka za zana la 20 zakhala ndi kukhalapo kwa zonse ziŵiri kutsendereza ufulu ndi demokrase ndi kukangana pakati pawo.”—Kanyenye ngwathu.

Mphamvu ya Anthu

Onaninso kuti mkati mwa kulamulira kwa ‘zala khumi zakumapazi,’ anthu wamba, “mbadwa za anthu,” zikaphatikizidwamo mowonjezereka m’boma. Kodi zenizeni zam’mbiri yakale zimachirikiza kulosera kumeneku?—Danieli 2:43, NW.

Demokrase, boma lopangidwa ndi anthu, inakhala yotchuka kwambiri kuyambira pamapeto pa Nkhondo Yadziko ya I penipeni, ngakhale kuti mkati mwa ma 1920 ndi ma 1930, maboma osiyanasiyana a demokrase m’mbali zosiyanasiyana zadziko analoŵedwa m’malo ndi otsendereza ufulu. Pamapeto pa Nkhondo Yadziko ya II, kuchotsa ulamuliro wachitsamunda kunabalanso mademokrase atsopano ambiri. Komabe, pambuyo pake, m’ma 1960 ndi m’ma 1970, maiko ambiri olamuliridwa ndi maiko achitsamunda anasankha mitundu ya boma lopondereza.

Ngakhale kuli choncho, m’zaka za zana la 20, chikhoterero chakhala kuuloŵa mmalo ufumu wa monarchy ndi autocracy ndi mademokrase kapena maboma a anthu. “Nchaka cha Anthu” ndimmene magazini a Time analongosolera m’gwedegwede wa ndale zadziko Kummawa kwa Yuropu. Ndipo pamene linga la Berlin linagwa potsirizira pake, magazini Achijeremani Der Spiegel inakometsera chikuto chake chakutsogolo ndi mawu akuti “Das Volk siegt”—anthu alakika!

Zokamba Mbwe, Zochita Pang’ono

M’maiko onse a Kummawa kwa Yuropu kumene mphamvu za anthu zakakamiza kusintha kwandale zadziko, anthu akhala akufuna masankho odzifunira ndi kupikisana kwa zipani zandale zadziko zambiri. Zipani zandale zadziko zampangidwe omwe ulipo tsopano lino, zinayambira m’Yuropu ndi Kumpoto kwa Amereka mkati mwa zaka za zana la 19. Kuyambira chapakati pa zaka za zana la 20, izo zafalikira padziko lonse. Lerolino, nzokulirapo, zolimbirapo, ndi zolinganizidwa bwinopo kuposa ndikale lonse. Mwa izo, limodzinso ndi mwa mayunioni antchito, mabungwe oimira anthu, magulu oyang’anira malo ndi mikhalidwe ya anthu, ndi magulu ena ambiri osamalira maubwino apadera a nzika, mphamvu za anthu tsopano zikulankhula kaŵirikaŵiri kwambiri ndimomveka kuposa ndikale lonse.

Komabe, pamene chiŵerengero cha anthu oloŵetsedwamo m’kayendetsedwe ka ndale zadziko chikuwonjezereka, ndimmenenso kumakhalira kovuta kuchifikira chimvano chandale zadziko. Pakati pa malingaliro ochuluka opikisana ndi maubwino, kaŵirikaŵiri pamatuluka maboma olamuliridwa ndi gulu lochepa la anthu, maboma ammawondo zii okhala ndi zokamba mbwe koma zochita zochepa.

Mofanana ndi chitsulo ndi dongo, nsanganizo wapadziko lonse wandale zadziko wakhala wosalimba chiyambire 1914. Mwachitsanzo, masiku anatha pamene anthu anafunsira chitsogozo cha Mulungu m’nkhani zaboma. “Chotero, anthu m’kutsungula Kwakumadzulo akhala akudalira kotheratu pa iwo okha, ndipo amadzipeza kukhala opereŵera,” ikumaliza motero The Columbia History of the World.

Mpata wa Chiyembekezo?

“Kodi nchifukwa ninji kuli kwakuti zochitika zosiyana koma zogwirizana zimenezi zachitikira pamodzi m’theka lomalizira la zaka za zana la 20? Kodi nchifukwa ninji ziopsezo za kunyonyotsoka kwa dzikozi zabuka m’nyengo yeniyeni imene munthu wafikira kutumba kwachipambano m’zasayansi ndi chidziŵitso kuposa m’mbiri yake yakale yonse?” Mafunsoŵa ofunsidwa ndi mtola nkhani Geyer amadzutsa malingaliro. Koma kodi pali amene ali ndi mayankho?

Pafupifupi zaka khumi zapitazo, The World Book Encyclopedia mwakukhala nacho chiyembekezo inati: “Mwinamwake tiri ndi mpata wokulirapo wakuthetsa mavuto a m’nthaŵi zathu kuposa mbadwo uliwonse wapita.” Koma tsopano, zaka khumi zapitapo, kuchiyambi kwa ma 1990, kodi pakadali mpata wokhalira nacho chiyembekezo? ‘Inde,’ inu mungatero, mukumaloza ku mapeto a Nkhondo Yamawu, ku kugwirizana kokulirapo pakati pa Kummawa ndi Kumadzulo, ndikupita patsogolo kowonekera komwe kukupangidwa kuchepetsa zida zankhondo zadziko.

Baibulo linaneneretu kuti iwo akatero. Limasonyeza kuti mkati mwa kulamulira kwa ulamuliro wadziko lonse wachisanu ndi chiŵiri wa m’mbiri ya Baibulo, ulamuliro wam’nthaŵi yake wachisanu ndi chitatu ukakhazikitsidwa mwapadera kaamba ka chifuno chogwirizanitsa mitundu. (Chibvumbulutso 17:11) Koma kodi ukapambana? Gawo 9 la “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso” lidzayankha.

[Mawu a M’munsi]

a Nsanja ya Olonda inafotokoza zochuluka pa uliwonse pawokha wa maulamuliro adziko lonse ameneŵa a mbiri ya m’Baibulo m’makope ake a February 1 mpaka June 1, 1988.

b Kaamba ka umboni wa Baibulo, onani mitu 16 ndi 18 ya bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa mu 1984 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 21]

‘Ufumu uliwonse wogaŵanika pa wokha sukhalira kupasuka.’—Mateyu 12:25

[Mawu Otsindika patsamba 21]

“Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka.”—Salmo 46:6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena