Ulamuliro Wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso
Gawo 10: Pomalizira Pake Papezeka Boma Langwiro!
Teokrase: lotengedwa ku mawu Achigiriki akuti “the·osʹ” (mulungu) ndi “kraʹtos” (ulamuliro); motero, ndiboma lotsogozedwa kapena kulamulidwa ndi Mulungu, nthaŵi zina kupyolera mwa oimira oikidwa.
NGATI mukadakhoza kugula unyolo wamkhosi wa ngale yeniyeni kapena mphete ya diamond yeniyeni, kodi mukadagula chinthu chongoyerekezera chopanda pake cha chinthu chenichenicho? Mwinamwake ayi, kusiyapo kokha ngati mudanyengedwa kukhulupirira kuti chomwe munkagulacho ndicho chinthu chabwino koposa chomwe mungapeze.
Ponena za boma, anthu mamiliyoni mazana ambiri anyengedwa kukhulupirira kuti iwo akupeza labwino koposa lomwe angakhoze. Kunena zowonadi iwo akukhala ndi zongoyerekezera zopanda pake. Nzosadabwitsa kuti iwo ngwogwiritsidwa mwala, osakhutira, ndi okhumudwitsidwa.
Kufunafuna Boma Labwino
William Ralph Inge, yemwe kale adali mtsogoleri wa Tchalitchi cha Angilikani cha St. Paul’s Cathedral, London, adalemba motere mu 1922: “Boma labwino ndilo dalitso lalikulu koposa la anthu, ndipo palibe dziko lomwe lasangalalapo nalo.” Nchifukwa ninji?
Kalongosoledwe kochepa kangapezeke m’mawu a John F. Kennedy, pulezidenti wa 35 wa United States. Iye anati: “Palibe boma limene liri labwinopo kuposa anthu olipangawo.” Popeza kuti ngakhale wandale zadziko waluso kwenikweni ngopanda ungwiro, boma lirilonse limene anthu alikhazikitsa linka ku kulephera.
Wolemba seŵero wa m’zaka za zana lakhumi mphambu zisanu ndi ziŵiri Wachingelezi, Philip Massinger adali wolondola pamene adalemba kuti: “Munthu amene adzalamulira ena, choyamba ayenera kukhala mbuye wa iye yekha.” Koma kodi ndimunthu wopanda ungwiro uti amene alidi mbuye wa iye yekha? Ndithudi, palibe wandale zadziko amene ali ndi chidziŵitso chokwanira ndi nzeru zakulamulira zochitika ndi mikhalidwe ndipo mwakutero kutsimikizira chimwemwe chake ndi ubwino, sangathe kutero kaamba ka chimwemwe ndi ubwino wa anthu ena mamiliyoni. Ndipo ngakhale ngati iye nthaŵi zonse anali wokhoza kupanga zosankha zolondola, iye sakanakhala ndi mphamvu yozichitira izo.
Katswiri wolemba nkhani waku Amereka, Brooks Atkinson, atazindikira vutoli, anatsimikiza motere kalelo mu 1951: “Tikufunikira anthu apamwamba kuti adzatilamulire—ntchitoyo njaikulu ndipo kufunika kwa chiweruzo chanzeru nkofulumira. Koma, kalanga ine,” iye anatero, “kulibeko anthu apamwamba.” Lerolino, zaka makumi anayi pambuyo pake, kudakalibe aliwonse.
Kwenikweni, Mulungu sanafune kuti anthu adzidzilamulira okha. Kuti asangalale ndi boma langwiro, anthu afunikira zoposa kokha boma lolamulidwa ndi anthu apamwamba. Iwo akufunikira teokrase, boma lolamulidwa ndi Mulungu.
Teokrase Yamtundu Wanji?
Teokrase ndi mtundu waboma lomwe lidalipo mu Edene, kumene Mulungu adaika anthu aŵiri oyambirira. Monga Mfumu yoyenera, Mulungu poyambirira ankalamulira zinthu ndikuchita ulamuliro.
Pamene katswiri wa mbiri yakale Wachiyuda, Flavius Josephus analemba kwanthaŵi yoyamba liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “teokrase” pafupifupi zaka mazana 19 zapitazo, iye analigwiritsira ntchito kulozera ku mtundu wakale wa Israyeli. Kumeneku kudali kuzindikiritsa kolondola, popeza kuti Israyeli panthaŵiyo unali mtundu wosankhidwa ndi Mulungu. Iwo unkalamulidwa ndi iye, ngakhale kuti ulamuliro wake unkachitidwa kupyolera mwa oimira apadziko lapansi.—Deuteronomo 7:6; 1 Mbiri 29:23.
Pamene liwu lakuti “teokrase” linaloŵa m’zinenero zina, ilo poyambirira linalekezera ku tanthauzo lomwe Josephus analifuna. Koma pambuyo pake linadzatenga matanthauzo owonjezereka. Mogwirizana ndi The Encyclopedia of Religion, ilo “lagwiritsiridwa ntchito mofala ku mikhalidwe yosiyanasiyana monga ngati Igupto wachifarao, Israyeli wakale, Chikristu Chadziko cha nyengo yapakati, Calvanism, Chisilamu, ndi Chibuddha cha ku Tibet.”
Katswiri wambiri yakale W. L. Warren akunena kuti “muufumu wa monarchy Wachingelezi mudali mbali ya ufumu wateokratiki—mfumu idali monga chiwiya chachikulu m’makonzedwe aumulungu opangitsira dongosolo m’dziko, mfumu inali woimira wa Mulungu ndi wopulumutsa ku chiweruzo.” M’nthaŵi zamakono liwulo lagwiritsiridwadi ntchito monga kalongosoledwe ka “chidani ‘chowunikiridwa’ cha zitaganya ‘zotsogozedwa ndi ansembe,” akulongosola motero Dewey Wallace, Jr., wa pa Yunivesite ya George Washington.
Tsopano tanthauzo lalikulu la liwulo limavomereza kukhalapo kwa mitundu yambiri ya teokrase. Kodi ndi mtundu uti umene tikuufunikira?
Mateokrase Achinyengo
Boma la anthu loyambirira lolembedwa m’mbiri yakale linakhazikitsidwa ndi Nimrode zaka 4,000 zapitazo. Mdzukulu wa Nowa ameneyu anadzipanga yekha kukhala mfumu ndipo anakhala, monga momwe Baibulo likumulongosolera iye, “mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.” (Genesis 10:8, 9) Mwakudzikhazikitsa yekha kukhala wolamulira motsutsana ndi Yehova, Nimrode anadzipanga yekha kukhala mulungu wandale zadziko. Motero, iye anali ndi chilikizo la wotsutsa wamkulu wa Mulungu, mulungu wonama Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4) Chotero ulamuliro wa Nimrode unali chinyengo cha teokrase yeniyeni.
Pamene nzika za ufumu wa Nimrode zinamwazidwa pambuyo pake kuzungulira padziko lonse lapansi, anthu anapitirizabe kulingalira kuti maboma awo anali ateokratiki, uku ndiko kuti, otenga ulamuliro kuchokera kwa mulungu kapena milungu yomwe ankailambira. (Genesis 11:1-9) Chotero “teokrase” inafikira pakugwiritsiridwa ntchito, ikutero The Encyclopedia of Religion, “kulongosola mbali yoyambirira ija ya kutsungula kwa kum’mawa imene inalibe kusiyana pakati pa chipembedzo ndi boma.”
M’miyambo ina, monga ngati Igupto muulamuliro wa Afarao, mfumu inakhulupiridwa kukhala mkazi wa mulungu wachikazi wamkulu kapena mwana wa mulungu. Miyambo ina sinanene zambiri ponena za mikhalidwe yaumulungu yolingaliridwa kapena chibadwa cha mfumu, kugogomezera lingaliro lakukhala kwake wosankhidwa mwaumulungu. M’Girisi wa nthaŵi ya Alexander ndi pambuyo pake, mfumu inalingaliridwa kukhala mulungu, likulongosola motero bukhu lakuti A History of Political Theory, “chifukwa chakuti anabweretsa chigwirizano mu ufumu wake monga mmene Mulungu amabweretsera chigwirizano m’dziko.” Bukhu lambiri yakale limeneli likupitiriza motere: “Iye anali ndi umulungu umene munthu wamba analibe ndiponso umene unabweretsa tsoka kwa wolanda ulamuliro wosayenerera amene anatenga malo apamwamba popanda dalitso la Kumwamba.”
Lingaliro limeneli lakuti mfumu ndiyo mulungu linadzafika ku nyengo yotchedwa Yachikristu. Pambuyo pakuti mafuko Achijeremani anatembenuzidwira ku Chikatolika, kutchuka kwa mfumu kunawonjezereka. Kuvekedwa chisoti chachifumu kochitidwa ndi tchalitchi kunasonyeza kuti Mulungu iyemwini wasankha mfumuyo kuti ilamulire. Kuchokera ku chiyambi chimenechi, chiphunzitso chodziŵika monga kuyenerera kwaumulungu kwa mafumu chinakula pang’onopang’ono.
Ngakhale pamene nyengo “Yachikristu” inali isanafike, Akaisara a Roma anapangitsa boma lawo kuwoneka la teokratiki mwakudzinenera kukhala mulungu. Kwa Aroma, ulamuliro wa anthu unali wofanana ndi ulamuliro wa mulungu, kupangitsa boma lawo, lotsanzira la Nimrode, kukhala teokrase yachinyengo. Chotero pamene atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’zaka za zana loyamba C.E. anakana Yesu monga Mfumu yoyembekezera, akumati, “Tiribe Mfumu koma Kaisara,” kwenikweni, iwo ankasonyeza chikondi kaamba ka teokrase yachinyengo mmalo mwa yeniyeni imene Yesu ankailalikira.—Yohane 19:15.
Popeza kuti ulamuliro wateokratiki wa Yehova ngwapamwamba kwenikweni ku ulamuliro wina uliwonse, nzosadabwitsa kuti Satana wayesayesa kuloŵetsamo mbali zake zina muufumu wake wachinyengo wopangidwa ndi anthu—koma sanapambane. Mateokrase odzipangira onseŵa sanafanane konse ndi yeniyeni. M’chenicheni, palibe ndi umodzi womwe umene walamulidwa ndi Mulungu kapena oimira ake. Iwo akhala zoyerekezera zopanda pake za chinthu chenicheni, zisonyezero za ulamuliro wa anthu opanda ungwiro pansi pa mulungu wachinyengo.
Moyenerera, Baibulo limatcha mulungu ameneyu kukhala “mkulu wa dziko ili lapansi” ndi “mulungu wa nthawi yino ya pansi pano.” (Yohane 12:31; 14:30; 2 Akorinto 4:4) Chimenecho ndicho chifukwa chake iye anali wokhoza kupereka ‘maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo’ kwa Yesu, chiyeso chimene Yesu anachitsutsa kotheratu. (Mateyu 4:8-10) Podziŵa kuti teokrase yeniyeni imalamulidwa ndi Mulungu mmodzi wowona, Yehova, Yesu sananyengedwe kuvomereza zoloŵa mmalo zopangidwa ndi anthu zomwe nzosakhoza kusonyeza kulinganizika kwaumulungu kwa mikhalidwe yopezeka m’chinthu chenichenicho.
Boma Langwiro Liri Pafupi
Zaka zingapo zapitazo, Hugh Brogan wa pa Yunivesite ya Essex anatsimikiza motere: “Ngati munthu, nyama yandale zadziko, ati adzipulumutse yekha ndi zitaganya zake, iye sangaleke kufunafuna mitundu ya boma yatsopano kuti akwaniritse zosoŵa zatsopano za nthaŵi yake.” Chiyambire tsiku la Nimrode, anthu akhala akuchita zimenezo, mobwerezabwereza akhala akupanga mitundu yatsopano ya boma kuti akwaniritse zosoŵa za nthaŵi. Koma kodi ndinthaŵi yochuluka motani imene ikufunikira kuti atsimikizire kuti ulamuliro wa anthu sugwira ntchito?
Mwachimwemwe, mu 1914 inafika nthaŵi yakuyesa boma la anthu kuti litokosedwe ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumu Waumesiya wa Yehova kumwamba!a Chiyambire 1914, maboma a anthu, ngakhale kuti adakalipobe, akukhala ndi moyo m’nthaŵi yobwereka. (Danieli 7:12) Tikukhala m’nyengo imene Baibulo limaitcha kukhala “masiku otsiriza.” (2 Timoteo 3:1-5) Dzanja lolemba pakhoma limene likulengeza chiwonongeko cha ulamuliro wa anthu nlowonekeratu kwakuti palibe amene mowona mtima angalinyalanyaze. Ilo linganyalanyazidwe, koma silingachotsedwepo.
Ulamuliro wateokratiki mwa Ufumu Waumesiya wa Yehova waimiridwa m’Baibulo pa Danieli mutu 2 ndi mwala ‘wosemedwa popanda manja’ umene ‘unagunda fanoli [lophiphiritsira ulamuliro wa anthu] pa mapazi ake okhala chitsulo ndi dongo, nuwaphwanya.’ Ichi chikutanthauza kuti Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu posachedwapa udzakantha ulamuliro woipa wa anthu m’mbali zake zonse, ndikuuphwanya. Kuuphwanya kotheratu motani? Baibulo likuyankha kuti: ‘Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizinasanduka ngati mungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziuluza, osapezekanso malo awo.’—Danieli 2:34, 35.
Ngati maboma oipa a anthu adzasesedweratu kwakuti malo awo sadzapezekanso, nchachidziŵikire kuti achilikizi a ulamuliro wa anthu akuyang’anizana ndi nthaŵi zovuta. Anthu mamiliyoni ambiri, pozindikira mfundo imeneyi, akuwona nzeru yakusamutsa chidaliro chawo kuchoka ku ulamuliro woipitsidwa wa anthu kunka ku winawake wabwinopo. Ulamuliro wa Yehova Mulungu wokha, Mlengi wa chilengedwe chonse, ndiwo ungathetse mavuto amene achititsidwa ndi kulamulira koipa ndi kusasamala kwa anthu kwa zaka zikwi zambiri. Teokrase yowona yokha ndiyo ingakwaniritse zosoŵa za nthaŵi zathu.
Galamukani! ikukhulupirira kuti mpambo wa magawo khumi wakuti “Ulamuliro wa Anthu Uyesedwa Pamiyeso” wagogomezera kwa inu kufunika kwa kupanga chosankha chaumwini m’nkhani imeneyi ya boma. Ndipo chofunika kuposa, tikukhulupirira kuti zidzakuthandizani kupanga chosankha chanzeru. Ulamuliro wa anthu wayesedwa pamiyeso nupezeka wopereŵera. Kodi mudzasankhanji? Kodi chidzakhala chinthu chachinyengo chopanda pake kapena chinthu chenichenicho? Kodi udzakhala ulamuliro wa anthu kapena ulamuliro wa Mulungu wowona, Yehova?—Danieli 2:44; Mateyu 6:10.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka umboni wakuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa mu 1914 ndikuti dziko lino lakhala m’masiku ake otsiriza chiyambire nthaŵiyo, onani mitu 16 ndi 18 ya bukhu lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa mu 1984 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 27]
Zimene Ulamuliro Wateokratiki wa Yehova Udzachita
◆ Udzabwezeretsa anthu ofooka okalamba ku mphamvu yaunyamata.—Yobu 33:25.
◆ Udzapangitsa nkhondo kukhala chinthu chakale.—Salmo 46:9; Yesaya 9:7.
◆ Udzapereka ku banja lirilonse nyumba yabwino koposa.—Yesaya 65:21.
◆ Udzachiritsa odwala ndi opunduka.—Yesaya 33:24; 35:5, 6.
◆ Udzaukitsa akufa.—Yesaya 25:8; Machitidwe 24:15; Chibvumbulutso 20:13.
◆ Udzachotsa padziko lapansi kupereka ziphuphu, chisembwere, ndi upandu.—Miyambo 2:21, 22.
◆ Udzapereka chakudya chochuluka kwa onse.—Salmo 72:16; Yesaya 25:6.
◆ Udzabwezeretsa unansi wamtendere pakati pa anthu ndi zinyama.—Yesaya 11:6-9; Ezekieli 34:25.
◆ Udzagaŵira aliyense ntchito yatanthauzo ndi yopindulitsa.—Yesaya 65:22, 23.
◆ Udzasintha dziko lapansi kukhala paradaiso wapadziko lonse.—Yesaya 35:1, 6, 7; Luka 23:43.
Ameneŵa simalonjezo andale zadziko opanda pake opangidwa ndi anthu; iwo ndimalonjezo opangidwa ndi Mulungu, ndipo “Mulungu sakhoza kunama.”—Ahebri 6:18.
[Chithunzi patsamba 28]
Madalitso osatha a boma langwiro angakhale anu!