-
Anaphunzira pa Zolakwa ZakeNsanja ya Olonda—2009 | January 1
-
-
Pothedwa nzeru, Yona anapita m’chipinda cha pansi pasitimayo kuti akagone. Ndiyetu anagona tulo tofa nato.b Mkulu wa oyendetsa sitimayo atam’peza, anamudzutsa n’kumulimbikitsa kuti apemphere kwa mulungu wake, monga aliyense anali kuchitira. Poona kuti chimphepochi chinali chodabwitsa, anthuwo anachita maere kuti adziwe munthu amene wawabweretsera tsoka limeneli. N’zachidziwikire kuti mtima wa Yona unagunda kwambiri ataona kuti maerewo sakugwera aliyense mwa anthuwo. Posakhalitsa iye anadziwa kuti Yehova ndi amene anali kuchititsa chimphepocho ndi kutsogolera maerewo n’cholinga choti aliyense adziwe kuti wolakwa sanali wina ayi koma Yonayo.—Yona 1:5-7.
-
-
Anaphunzira pa Zolakwa ZakeNsanja ya Olonda—2009 | January 1
-
-
b Baibulo la Septuagint limanena kuti Yona anagona tulo mpaka kufika poliza nkonono. Komabe tisaganize kuti Yona anagona chifukwa choti analibe nazo ntchito zimene zimachitikazo. Tisaiwale kuti anthu amatha kukhala ndi tulo kwambiri chifukwa cha nkhawa. Mwachitsanzo, panthawi imene Yesu anali pachipsinjo chachikulu kwambiri m’munda wa Getsemane, Petulo, Yakobe, ndi Yohane “anagona chifukwa cha chisoni.”—Luka 22:45.
-