-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
2. M’fanizo la Yesu la tirigu ndi namsongole, kodi mbewu yabwino ikuimira chiyani?
2 Koma fanizo lina la Yesu limafotokoza kwambiri za kusonkhanitsa anthu amene adzalamulira naye mu Ufumu wake kumwamba. Fanizoli limatchedwa fanizo la tirigu ndi namsongole ndipo lili pa Mateyo chaputala 13. M’fanizo lina Yesu ananena kuti mbewu zofesedwa, zikuimira “mawu a ufumu” koma mu fanizoli iye anati mbewu zabwino zikuimira “ana a ufumu.” (Mat. 13:19, 38) Iwo si nzika za Ufumu koma ndi “ana” kapena kuti olandira cholowa cha Ufumu.—Aroma 8:14-17, werengani Agalatiya 4:6, 7.
-
-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
4. (a) Kodi munthu wa m’fanizoli ndi ndani? (b) Ndi liti pamene Yesu anayamba kufesa mbewu, ndipo kodi anachita zimenezi motani?
4 Kodi munthu amene anafesa mbewu zabwino m’munda wake ndi ndani? Yesu anayankha funso limeneli pamene ankafotokoza tanthauzo la fanizoli kwa ophunzira ake. Iye anati: “Wofesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu.” (Mat. 13:37) Yesu yemwe ndi “Mwana wa munthu” ankalima munda pa zaka zitatu ndi theka za utumiki wake padziko lapansi. (Mat. 8:20; 25:31; 26:64) Ndiyeno kuyambira pa Pentekosite mu 33 C.E. iye anayamba kufesa mbewu zabwino zomwe ndi “ana a ufumu.” Kufesa kumeneku kunayambika pa nthawi imene Yesu, yemwe ndi woimira Yehova, anayamba kudzoza ophunzira ake ndi mzimu woyera kuti akhale ana a Mulungu.b (Mac. 2:33) Mbewu zabwinozi zinakula n’kukhala tirigu wokhwima bwino. Motero, cholinga cha kufesa mbewu zabwino, chinali chakuti asonkhanitse anthu okwanira kudzakhala olandira cholowa ndiponso mafumu limodzi ndi Khristu mu Ufumu wake.
-
-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
5. Mu fanizo la Yesu, kodi mdani akuimira ndani, nanga namsongole akuimira ndani?
5 Kodi mdani akuimira ndani, ndipo namsongole akuimira ndani? Yesu ananena kuti mdaniyo “ndi Mdyerekezi.” Ndipo anati namsongole ndi “ana a woipayo.” (Mat. 13:25, 38, 39) Namsongole amene Yesu ankanena, ndi mtundu wa udzu woipa kwambiri umene ukakhala waung’ono umafanana kwambiri ndi tirigu. Ilitu ndi fanizo labwino kwambiri pofotokoza za anthu amene amanamizira kuti ndi ana a Ufumu koma sabala zipatso zabwino. Akhristu onyenga amenewa, amanamizira kuti ndi otsatira Khristu koma zoona zake n’zakuti iwo ndi mbali ya “mbewu” ya Satana Mdyerekezi.—Gen. 3:15.
-
-
“Olungama Adzawala Ngwee Ngati Dzuwa”Nsanja ya Olonda—2010 | March 15
-
-
7. Kodi tirigu wina anasintha n’kukhala namsongole? Fotokozani.
7 Yesu sananene kuti tirigu adzasintha n’kukhala namsongole koma anati namsongole anafesedwa m’munda wa tirigu. Choncho fanizoli silikunena za Akhristu oona amene agwa m’choonadi. Koma likunena za zimene Satana wachita n’cholinga chofuna kuipitsa mpingo wachikhristu mwa kulowetsa anthu oipa mumpingomo. Panthawi imene mtumwi Yohane anali wokalamba, mpatuko umenewo n’kuti utayamba kale kuonekera.—2 Pet. 2:1-3; 1 Yoh. 2:18.
-