Ufumu wa Mulungu—Kodi Mukumvetsa Lingaliro Lake?
“Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mawu [namvetsa lingaliro lake, NW].”—MATEYU 13:23.
1. Kodi nzikhulupiriro zotani zimene ambiri ali nazo ponena za ‘ufumu wakumwamba’?
KODI ‘mwamvetsa lingaliro la’ chimene Ufumu wa Mulungu uli? Zikhulupiriro ponena za ‘ufumu wakumwamba’ zakhala zosiyanasiyana kwambiri m’kupita kwa zaka mazana ambiri. Chikhulupiriro chofala pakati pa anthu ena atchalitchi lerolino nchakuti Ufumuwo ndiwo kanthu kena kamene Mulungu amaika mumtima mwa munthu pakutembenuka kwake. Ena amalingalira kuti ndiwo malo kumene anthu abwino amapita atamwalira kukapeza chimwemwe chosatha. Enanso amanena kuti Mulungu anasiyira nkhaniyo kwa anthu kuti abweretse Ufumuwo padziko lapansi mwa zochita zawo za kusonkhezera ziphunzitso zachikristu ndi ntchito zake pakati pa nkhani za anthu ndi nkhani za boma zomwe.
2. Kodi Baibulo limalongosola motani Ufumu wa Mulungu, ndipo udzachita chiyani?
2 Komabe, Baibulo limasonyeza bwino kuti Ufumu wa Mulungu suli gulu lapadziko lapansi. Ndiponso suli mkhalidwe wa mtima kapena kutembenuza anthu onse kukhala Akristu. Zoona, kumvetsa molondola chimene Ufumu umenewu uli kumachititsa awo amene amaukhulupirira kusintha moyo wawo kwambiri. Koma Ufumu weniweniwo uli boma lakumwamba lokhazikitsidwa ndi Mulungu limene lidzachita chifuniro chake, likumachotsa ziyambukiro za uchimo ndi imfa ndi kubwezeretsa mikhalidwe yolungama padziko lapansi. Ufumu umenewu unayamba kale kulamulira kumwamba, ndipo posachedwapa “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [a anthu]. Nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44; Chivumbulutso 11:15; 12:10.
3. Pamene Yesu anayamba utumiki wake, kodi nchiyani chimene chinatsegulidwa kwa anthu?
3 Wolemba mbiri H. G. Wells analemba kuti: “Chiphunzitso chimenechi cha Ufumu wa Kumwamba, chimene chinali chiphunzitso chachikulu cha Yesu, chomwenso chili ndi mbali yaing’ono m’zikhulupiriro zachikristu, chilidi chimodzi cha ziphunzitso zosintha zinthu kwambiri zomwe zinadzutsa ndi kusintha malingaliro a anthu.” Kuyambira pachiyambi pomwe, mutu wa nkhani wa utumiki wa Yesu unali wakuti: “Tembenukani mitima, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Iye anali padziko lapansi monga Mfumu yodzozedwa, ndipo chinthu chosangalatsa kwambiri chinali chakuti, tsopano njira inali kutsegulidwa kaamba ka anthu osati kungogaŵana nawo madalitso a Ufumuwo komanso kukhala olamulira ndi ansembe pamodzi ndi Yesu mu Ufumuwo!—Luka 22:28-30; Chivumbulutso 1:6; 5:10.
4. Kodi ndi motani mmene makamu anachitira ndi “uthenga wabwino wa ufumu” m’zaka za zana loyamba, zikumabweretsa chiweruzo chotani?
4 Pamene kuli kwakuti makamu anamva “uthenga wabwino waufumu” wokondweretsawo, oŵerengeka okha ndiwo amene anakhulupirira. Zimenezi mwapang’ono zinali chifukwa chakuti atsogoleri achipembedzo anali “[ata]tsekera anthu ufumu wakumwamba.” ‘Anachotsa chifungulo cha nzeru’ ndi ziphunzitso zawo zonyenga. Chifukwa chakuti anthu ochuluka anakana Yesu kukhala Mesiya ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu yodzozedwa, Yesu anati kwa iwo: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.”—Mateyu 4:23; 21:43; 23:13; Luka 11:52.
5. Kodi ochuluka a awo amene anamva mafanizo a Yesu anasonyeza motani kuti sanamvetse?
5 Panthaŵi ina pamene anali kuphunzitsa khamu lalikulu, Yesu, monga mwa chizoloŵezi chake, anagwiritsira ntchito mpambo wa mafanizo kuti ayese khamulo ndi kuchotsa awo amene anali ndi chidwi chachiphamaso pa Ufumuwo. Fanizo loyamba linali la wofesa mbewu amene anafesa mbewu panthaka ya mitundu inayi. Itatu yoyamba inali yosayenera kumerapo mbewu, koma yomalizira inali “nthaka yabwino” imene inabala zipatso zabwino. Anamaliza fanizo lalifupilo ndi chilimbikitso chakuti: “Amene ali ndi makutu, amve.” (Mateyu 13:1-9) Ambiri amene analipo anamumva, koma ‘sanamvetse.’ Analibe chikhumbo chenicheni chakuti adziŵe za mmene mbewu zofesedwa m’mikhalidwe yosiyanasiyana zinalili ngati Ufumu wakumwamba. Anapita kwawo kukakhala monga mwa masiku onse, mwachionekere akumaganiza kuti mafanizo a Yesu anangokhala nkhani zina zabwino pamakhalidwe abwino. Ha, ndi chuma chanzeru chofunika chotani nanga ndipo ndi mwaŵi waukulu chotani nanga umene iwo anataya chifukwa chakuti mitima yawo inali yosalabadira!
6. Kodi nchifukwa ninji kumvetsa “zinsinsi za ufumu” kunaperekedwa kwa ophunzira a Yesu okha?
6 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Kwapatsidwa kwa inu kudziŵa zinsinsi za ufumu wakumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.” Pogwira mawu a Yesaya, iye anawonjezera kuti: “Chifukwa unalemera mtima wa anthu aŵa, ndipo m’makutu awo anamva mogontha, ndipo maso awo anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, [ndi kumvetsa lingaliro lake ndi mitima yawo, NW], asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo. Koma maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.”—Mateyu 13:10-16; Marko 4:11-13.
“Kumvetsa Lingaliro la” Ufumuwo
7. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika ‘kumvetsa lingaliro la’ Ufumuwo?
7 Yesu anasonyeza vuto lake. Linali lokhudza “kumvetsa lingaliro la” uthenga wa Ufumu. Iye ananena kwa ophunzira ake mwamseri kuti: “Ndipo tsono mverani inu fanizolo la wofesa mbewu uja. Munthu aliyense wakumva mawu a ufumu, [koma osamvetsa lingaliro lake], woipayo angodza, nakwatula chofesedwacho mumtima mwake.” Anapitiriza kulongosola kuti mitundu inayi ya nthaka inaimira mikhalidwe yosiyanasiyana ya mtima mmene “mawu a ufumu” amafesedwamo.—Mateyu 13:18-23; Luka 8:9-15.
8. Kodi nchiyani chimene chinaletsa “mbewu” zofesedwa pa nthaka zitatu zoyamba kubala zipatso?
8 “Mbewu” imeneyo inali yabwino m’mikhalidwe yonseyo, koma zipatso zake zinadalira pa mkhalidwe wa nthakayo. Ngati nthaka ya mtima inali ngati njira yoyendamo anthu ambiri, yogangatiridwa, yolimba chifukwa cha zochitika zambiri zosakhala zauzimu, kukanakhala kosavuta kwa munthu wakumva uthenga wa Ufumu kudzipatsa chodzikhululukira, akumanena kuti analibe nthaŵi ya Ufumuwo. Mbewu yonyalanyazidwayo ikanakwatulidwa mosavuta isanazike mizu. Komano bwanji ngati mbewuyo ikanafesedwa mumtima wonga nthaka ya pamiyala? Mbewuyo ikanamera, koma sikanatha kuloŵetsa mizu yake pansi kuti ipeze chakudya ndi kulimba. Lingaliro la kukhala mtumiki wa Mulungu womvera, makamaka pa chizunzo chachikulu, likanapereka vuto lalikulu, ndipo munthuyo akanakhumudwa. Ndiyenonso, ngati nthaka ya mtima inali ndi nkhaŵa zonga minga kapena kukhumbitsa chuma, mbewu yonyozololoka ya Ufumuyo ikanatsamwitsidwa. Mbewuzo sizikanabala zipatso za Ufumu m’mikhalidwe itatu imeneyi ya moyo.
9. Kodi nchifukwa ninji mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino zinabala zipatso zabwino?
9 Komabe, bwanji nanga za mbewu ya Ufumu imene inabzalidwa pa nthaka yabwino? Yesu akuyankha kuti: “Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mawu [namvetsa lingaliro lake]; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.” (Mateyu 13:23) ‘Atamvetsa lingaliro la’ Ufumuwo, iwo akabala zipatso zabwino mogwirizana ndi mikhalidwe yawo.
Thayo Limadza Pamodzi ndi Kumvetsa
10. (a) Kodi ndi motani mmene Yesu anasonyezera kuti ‘kumvetsa lingaliro la’ Ufumu kumabweretsa madalitso ndi mathayo? (b) Kodi lamulo la Yesu la kupita kukapanga ophunzira linagwira ntchito kwa ophunzira a m’zaka za zana loyamba okha?
10 Atapereka mafanizo ena asanu ndi limodzi polongosola mbali zosiyanasiyana za Ufumu, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Mwamvetsa zonsezi kodi?” Pamene anayankha kuti “inde,” anati: “Chifukwa chake, mlembi aliyense, [pamene waphunzitsidwa za, NW]ufumu wakumwamba, ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m’chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.” Ziphunzitso ndi malangizo operekedwa ndi Yesu zidzachititsa ophunzira ake kukhala Akristu okula misinkhu amene adzatulutsa chakudya chauzimu chosatha chopatsa thanzi mu “chuma” chawo. Chakudya chake chambiri nchogwirizana ndi Ufumu wa Mulungu. Yesu anasonyeza bwino kuti ‘kumvetsa lingaliro la’ Ufumuwo sikudzangobweretsa madalitso okha komanso thayo. Iye analamula kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 13:51, 52; 28:19, 20.
11. Pamene 1914 anafika, kodi nzochitika zotani zimene zinachitika zokhudza Ufumuwo?
11 Monga momwe analonjezera, Yesu wapitiriza kukhala pamodzi ndi ophunzira ake oona m’zaka mazana ambiri kufikira lero. M’masiku otsiriza ano, iye wawachititsa kumvetsa zinthu mopita patsogolo, ndipo wawapatsa thayo la kupereka kuunika kowonjezereka kwa choonadi. (Luka 19:11-15, 26) Mu 1914, zochitika za Ufumu zinayamba kuvumbulika mofulumira ndi mwamphamvu. M’chaka chimenecho, si ‘kubadwa’ kwa Ufumu woyembekezeredwa kokha kumene kunachitika komanso “chimaliziro cha nthawi ya pansi pano” chinayamba. (Chivumbulutso 11:15; 12:5, 10; Danieli 7:13, 14, 27) Akristu oona, pozindikira tanthauzo la zochitika zamakono, achita mkupiti waukulu koposa wa kulalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu m’mbiri. Yesu ananeneratu zimenezi, akumati: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”—Mateyu 24:14.
12. (a) Kodi nchiyani chimene chachitika chifukwa cha umboni waukulu wamakono wonena za Ufumu? (b) Kodi ndi ngozi yotani imene ilipo kwa Akristu m’dziko lokayika lino?
12 Umboni waukulu wa Ufumu umenewu wafika m’maiko oposa 230. Anthu oposa mamiliyoni asanu [akusonyeza kukhala] ophunzira oona amene ayamba kale kuchita nawo ntchito imeneyi, ndipo enanso akusonkhanitsidwa. Koma ngati tiyerekezera chiŵerengero cha ophunzirawo ndi 5.6 biliyoni ya anthu apadziko lapansi, kuli kwachionekere kuti monga momwe zinalili m’tsiku la Yesu, unyinji wa anthu ‘sumamvetsa lingaliro la’ Ufumu. Ambiri, monga kunanenedweratu, amaseka ndi kunena kuti: “Lili kuti lonjezano la [kukhalapo, NW] kwake?” (2 Petro 3:3, 4) Ngozi imene ilipo kwa ife monga Akristu njakuti kusalabadira kwawo, kukayikira, kukondetsa kwawo zinthu zakuthupi kungayambukire pang’onopang’ono mmene timaonera mathayo athu a Ufumu. Pokhala ozingidwa ndi anthu a dzikoli, tingayambe mosavuta kutengera mikhalidwe ndi machitachita awo ena. Nkofunika chotani nanga kuti ife ‘timvetse lingaliro la’ Ufumu wa Mulungu ndi kuugwiritsitsa!
Kudzipenda Ife Eni Mogwirizana ndi Ufumu
13. Ponena za lamulo la kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu, kodi tingadziyese motani kuti tione ngati tikupitiriza ‘kumva’ ndi kuzindikira?
13 Yesu anafotokoza za nyengo ya kututa imene tikukhalamo kuti: “Mwana wa munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusayeruzika . . . Pomwepo olungamawo adzaŵalitsa monga dzuŵa, mu ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu amve.” (Mateyu 13:41, 43) Kodi mukupitiriza ‘kumva’ ndi kulabadira momvera lamulo la kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira? Kumbukirani kuti “amene anafesedwa pa nthaka yabwino” ‘anamva mawuwo ndi kumvetsa lingaliro lake’ nabala zipatso zabwino.—Mateyu 13:23.
14. Pamene malangizo aperekedwa, kodi timasonyeza motani kuti ‘tikumvetsa lingaliro la’ uphungu woperekedwa?
14 Pamene tichita phunziro laumwini ndi kufika pamisonkhano yachikristu, tiyenera ‘kulozetsa mtima wathu kukuzindikira.’ (Miyambo 2:1-4) Pamene uphungu uperekedwa ponena za khalidwe, kavalidwe, nyimbo, ndi kusanguluka, tiyenera kuulola kuloŵa m’mitima mwathu ndi kutisonkhezera kupanga masinthidwe onse ofunika. Sitiyenera kuchepetsa, kupereka zodzikhululukira, kapena mwina kulephera kuchitapo kanthu. Ngati Ufumuwo ulidi weniweni m’moyo wathu, tidzatsatira miyezo yake ndi kuulengeza kwa ena mwachangu. Yesu anati: “Si yense wakunena kwa ine, Ambuye, Ambuye, adzaloŵa mu ufumu wakumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.”—Mateyu 7:21-23.
15. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika ‘kuthanga tafuna ufumu ndi chilungamo chake’?
15 Chibadwa cha munthu nchakudera nkhaŵa za chakudya chofunika, zovala, ndi nyumba, koma Yesu anati: “Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33, 34) Poika zinthu zoyamba m’moyo, ikani Ufumu pamalo oyamba m’moyo wanu. Khalani ndi moyo wosacholoŵana, mukumakhutira ndi zofunika zomwe muli nazo. Kungakhale kupusa ngati tidzaza moyo wathu ndi machitachita ndi zosafunika, mwinamwake tikumapeputsa zinthu mwa kuganiza kuti palibe cholakwika pa kuchita zimenezo, popeza kuti zinthu zimenezi si zoipa nkomwe. Pamene kuli kwakuti zimenezo zingakhale zoona, kodi kupeza ndi kugwiritsira ntchito zinthu zosafunikira zimenezo kungayambukire motani phunziro lathu laumwini, kufika kwathu pamisonkhano yachikristu, ndi kukhala ndi phande mu ntchito yolalikira? Yesu anati Ufumu uli ngati munthu wamalonda amene anapeza “ngale imodzi ya mtengo wapatali, [ndipo] anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” (Mateyu 13:45, 46) Umu ndimo mmene tiyenera kulingalirira ponena za Ufumu wa Mulungu. Tiyenera kutsanzira Paulo osati Dema, amene analeka utumiki ‘chifukwa chakuti anakonda dziko lino lapansi.’—2 Timoteo 4:10, 18; Mateyu 19:23, 24; Afilipi 3:7, 8, 13, 14; 1 Timoteo 6:9, 10, 17-19.
“Osalungama Sadzalandira Ufumu wa Mulungu”
16. Kodi ‘kumvetsa lingaliro la’ Ufumu wa Mulungu kudzatithandiza motani kupeŵa khalidwe loipa?
16 Pamene mpingo wa Akorinto unali kulekerera mkhalidwe woipa, Paulo mosabisa anati: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Ngati ‘timvetsa lingaliro la’ Ufumu wa Mulungu, sitidzadzinyenga mwa kuganiza kuti Yehova adzalekerera mkhalidwe wina woipa malinga ngati ationa tili otanganitsidwa mu utumiki wachikristu. Chidetso sichiyenera kutchulidwa konse pakati pathu. (Aefeso 5:3-5) Kodi mukupeza kuti kaganizidwe kena koipa ka dzikoli kapena machitachita ake akuyamba kuloŵa pang’onopang’ono m’moyo wanu? Achotseni msanga m’moyo wanu! Ufumuwo ngwamtengo wapatali kwambiri wosayenera kuutaya chifukwa cha zinthu zimenezo.—Marko 9:47.
17. Kodi ndi motani mmene kuzindikira Ufumu wa Mulungu kudzachirikizira kudzichepetsa ndi kuchotsa zinthu zokhumudwitsa?
17 Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Ndani kodi ali wopambana mu ufumu wakumwamba?” Yesu anayankha mwa kuimika kamwana pakati pawo nati: “Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzaloŵa konse mu ufumu wakumwamba. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu ufumu wakumwamba.” (Mateyu 18:1-6) Anthu onyada, adyera, osasamala za ena, ndi osaweruzika sadzakhala mu Ufumu wa Mulungu, ndipo sadzakhalanso nzika za Ufumuwo. Kodi kukonda kwanu abale, kudzichepetsa kwanu, mantha anu aumulungu, zimakusonkhezerani kupeŵa kukhumudwitsa ena mwa khalidwe lanu? Kapena kodi mumaumirira pa “zoyenera” zanu mosasamala kanthu za mmene maganizowo ndi khalidwe zingayambukirire ena?—Aroma 14:13, 17.
18. Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa anthu omvera pamene Ufumu wa Mulungu udzapangitsa chifuno Chake kuchitika “monga kumwamba chomwecho pansi pano”?
18 Atate wathu wakumwamba, Yehova, posachedwa adzayankha mokwanira pemphero laphamphulo lakuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” Posachedwapa Mfumu yolamulirayo, Yesu Kristu, adzadza m’lingaliro la kudzakhala pa mpando wake wachifumu kaamba ka chiweruzo, kudzalekanitsa “nkhosa” ndi “mbuzi.” Panthaŵi yoikika imeneyo, “mfumuyo idzanena kwa iwo akudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Mbuzi “[zi]dzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse; koma olungama ku moyo wa nthaŵi zonse.” (Mateyu 6:10; 25:31-34, 46) “Chisautso chachikulu” chidzachotsa dongosolo lakale ndi onse amene amakana ‘kumvetsa lingaliro la’ Ufumu. Koma mamiliyoni a opulumuka “chisautso chachikulu” ndi miyandamiyanda ya amene adzaukitsidwa adzalandira madalitso osatha a Ufumuwo m’Paradaiso wapadziko lapansi wobwezeretsedwa. (Chivumbulutso 7:14) Ufumuwo ndiwo boma latsopano la dziko lapansi, lolamulira kuchokera kumwamba. Udzakwaniritsa chifuno cha Yehova kaamba ka dziko lapansi ndi anthu, kuyeretsa dzina lake lopatulika koposalo. Kodi chimenecho si choloŵa choyenera kuchimenyera nkhondo, chodzimanira, ndi kuyembekezera? ‘Kumvetsa lingaliro la’ Ufumuwo kuyenera kutanthauza zimenezi kwa ife!
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji omvetsera ambiri a Yesu ‘sanamvetse lingaliro la’ Ufumu?
◻ Kodi ‘kumvetsa lingaliro la’ Ufumu kumabweretsa motani madalitso ndi thayo?
◻ Ponena za kulalikira, kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti kaya ‘tamvetsa lingaliro la’ Ufumu kapena ayi?
◻ Kodi timasonyeza motani ndi khalidwe lathu kuti ‘tamvetsa lingaliro la’ uphungu woperekedwa?
[Zithunzi patsamba 17]
Ophunzira a Yesu ‘anamvetsa lingaliro la’ Ufumu nabala zipatso zabwino