Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 7/1 tsamba 14-19
  • Akulu, Weruzani Mwachilungamo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akulu, Weruzani Mwachilungamo
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kristu​—Woweruza Wachitsanzo Chabwino
  • Oweruza Apadziko Lapansi
  • Oweruza Amene ‘Amakhala Amantha’
  • Abusa Anthaŵi Yonse
  • Kutumikira Monga Abusa ndi Oweruza Achifundo
  • Mkhalidwe Woyenera Pamilandu
  • Chifuno cha Milandu Yachiweruzo
  • Akulu—Samalirani Gulu la Mulungu Mokoma Mtima!
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Yehova, “Woweruza Wa Dziko Lonse” Wopanda Tsankhu
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kuyesetsa Kuti Anthu Mumpingo Apitirize Kukhala Amtendere Komanso Oyera
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Mmene Tingasonyezere Chikondi ndi Chifundo Wina Akachita Tchimo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 7/1 tsamba 14-19

Akulu, Weruzani Mwachilungamo

“Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake.”​—DEUTERONOMO 1:16.

1. Pankhani ya chiweruzo, kodi ndikuperekedwa kwaulamuliro kotani kumene kwachitika, ndipo kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa oweruza aumunthu?

MONGA Woweruza Wamkulu Woposa Onse, Yehova wapereka ulamuliro wa kuweruza kwa Mwana wake. (Yohane 5:27) Nayenso, monga Mutu wa mpingo Wachikristu, Kristu amagwiritsira ntchito kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi Bungwe lake Lolamulira kuika akulu, amene panthaŵi zina ayenera kuchita monga oweruza. (Mateyu 24:45-47; 1 Akorinto 5:12, 13; Tito 1:5, 9) Monga oweruza aang’ono, amenewa ali ndi thayo la kutsatira mosamalitsa chitsanzo cha Oweruza akumwamba, Yehova ndi Kristu Yesu.

Kristu​—Woweruza Wachitsanzo Chabwino

2, 3. (a) Kodi ndiulosi Waumesiya uti umene umavumbula makhalidwe a Kristu monga Woweruza? (b) Kodi ndimfundo ziti zofunikira kulingaliridwa mwapadera?

2 Ponena za Kristu monga Woweruza, kunalembedwa molosera kuti: “Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wa nzeru ndi wa kuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wa kudziwa ndi wa kuwopa Yehova; Ndipo adzakondwera nako kumuwopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera: Koma ndi chilungamo adzaweruza aumphaŵi, nadzadzudzulira ofatsa a m’dziko mowongoka.”​—Yesaya 11:2-4.

3 Wonani muulosiwo mikhalidwe imene imakhozetsa Kristu ‘kuweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo.’ (Machitidwe 17:31) Iye amaweruza mogwirizana ndi mzimu wa Yehova, nzeru yaumulungu, kuzindikira, uphungu, ndi chidziwitso. Wonaninso, kuti akuweruza mowopa Yehova. Chotero, “mpando wa kuweruza wa Kristu” umaimira “mpando wakuweruza wa Mulungu.” (2 Akorinto 5:10; Aroma 14:10) Iye amasamala kuti akuweruza nkhani monga momwe Yehova amaweruzira. (Yohane 8:16) Iye samaweruza kokha mwamawonekedwe kapena mwamphekesera chabe. Iye amaweruza ofatsa ndi aumphaŵi mowongoka. Ali Woweruza wabwino kwambiri chotani nanga! Ndipo ali chitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga kaamba ka anthu opanda ungwiro amene amaikiziridwa thayo lachiweruzo lerolino!

Oweruza Apadziko Lapansi

4. (a) Kodi imodzi ya ntchito za a 144,000 idzakhala yotani mkati mwa Kulamulira Kwazaka Chikwi kwa Kristu? (b) Kodi ndiulosi uti umene umasonyeza kuti Akristu ena odzozedwa akaikidwa monga oweruza adakali padziko lapansi?

4 Malemba amasonyeza kuti chiwerengero chaching’ono chabe cha Akristu odzozedwa, oyambira ndi atumwi 12, adzakhala oweruza anzake a Kristu Yesu mkati mwa Zaka Chikwi. (Luka 22:28-30; 1 Akorinto 6:2; Chivumbulutso 20:4) Otsalira a ziwalo zodzozedwa za Israyeli wauzimu padziko lapansi iwo eniwo anaweruzidwa ndi kubwezeretsedwa mu 1918-19. (Malaki 3:2-4) Ponena za kubwezeretsedwa kwa Israyeli wauzimu kumeneku, kunaloseredwa kuti: “Ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi.” (Yesaya 1:26) Chotero, monga momwe anachitira “pachiyambi” pa Israyeli wakuthupi, Yehova wapatsa otsalira obwezeretsedwawo oweruza olungama ndi aphungu.

5. (a) Kodi ndani amene ‘anaikidwa kukhala oweruza’ pambuyo pa kubwezeretsedwa kwa Israyeli wauzimu, ndipo kodi ndimotani mmene iwo achitidwira chithunzi m’bukhu la Chivumbulutso? (b) Kodi oyang’anira odzozedwa tsopano akuthandizidwa ndi ayani m’ntchito yachiweruzo, ndipo kodi ndimotani mmene amenewa akuphunzitsidwira kuti akhale oweruza abwinopo?

5 Choyamba, ‘amuna anzeru’ amene ‘anaikidwa kuweruza’ onsewo anali akulu odzozedwa, kapena madoda. (1 Akorinto 6:4, 5) Oyang’anira odzozedwa, okhulupirika olemekezedwawo akuchitiridwa chithunzi m’bukhu la Chivumbulutso kukhala ali m’dzanja lamanja la Yesu, ndiko kuti, pansi pa ulamuliro wake ndi chitsogozo. (Chivumbulutso 1:16, 20; 2:1) Kuyambira mu 1935 odzozedwawo alandira chichirikizo chokhulupirika cha “khamu lalikulu” lomakulakula, limene chiyembekezo chawo chiri kudzapulumuka “chisautso chachikulu” ndi kudzakhala ndi moyo kosatha padziko lapansi laparadaiso. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14-17) Pamene “ukwati wa Mwanawankhosa” uyandikira, owonjezerekawonjezereka a ameneŵa akuikidwa ndi Bungwe Lolamulira lodzozedwa kuti atumikire monga akulu ndi oweruza m’mipingo yoposa 66,000 ya Mboni za Yehova kuzungulira padziko lonse lapansi.a (Chivumbulutso 19:7-9) Mwanjira ya sukulu zapadera, iwo akuphunzitsidwa kusamalira thayo m’chimangidwe cha “dziko latsopano.” (2 Petro 3:13) Sukulu Yautumiki Waufumu, yochitidwa chakumapeto kwa 1991 m’maiko ambiri, inagogomezera pa kusamaliridwa koyenera kwa nkhani zachiweruzo. Akulu amene amatumikira monga oweruza ali ndi thayo la kutsanzira Yehova ndi Kristu Yesu, amene ziweruzo zawo ziri zowona ndi zolungama.​—Yohane 5:30; 8:16; Chivumbulutso 19:1, 2.

Oweruza Amene ‘Amakhala Amantha’

6. Kodi nchifukwa ninji akulu otumikira pamakomiti achiweruzo ayenera ‘kukhala amantha’?

6 Ngati Kristu iyemwiniyo amaweruza mowopa Yehova ndi mothandizidwa ndi mzimu Wake, akulu opanda ungwiro ayenera kutero kwambiri chotani nanga! Pamene agaŵiridwa kutumikira pakomiti yachiweruzo, iwo afunikira ‘kukhala ndi mantha,’ ‘akumaitanira pa Atate amene aweruza mopanda tsankhu’ kuwathandiza kuweruza mwachilungamo. (1 Petro 1:17) Iwo ayenera kukumbukira kuti akuchita ndi miyoyo ya anthu, “miyoyo” yawo, monga awo amene ‘adzaŵerengeredwa mlandu.’ (Ahebri 13:17) Polingalira zimenezi, ndithudi iwo adzaŵerengeredwanso mlandu pamaso pa Yehova kaamba ka zophophonya zachiweruzo zirizonse zokhoza kupewedwa zimene iwo apanga. M’ndemanga zake pa Ahebri 13:17, J. H. A. Ebrard analemba kuti: “Ndithayo la mbusa kuyang’anira miyoyo yoikiziridwa m’chisamaliro chake, ndipo . . . ayenera kuŵerengeredwa mlandu wa yonseyo, imenenso yataika chifukwa cha kulakwa kwake. Ameneŵa ndimawu otsimikizirika. Minisitala aliyense wa mawu ayenera kulingalira, kuti iye modzifunira wadzitengera udindo wa thayo lowopsa [lalikulu] limeneli.”​—Yerekezerani ndi Yohane 17:12; Yakobo 3:1.

7. (a) Kodi oweruza amakono ayenera kukumbukiranji, ndipo kodi cholinga chawo chiyenera kukhala chotani? (b) Kodi ndimaphunziro otani amene akulu ayenera kupeza pa Mateyu 18:18-20?

7 Akulu amene akusamalira thayo lachiweruzo ayenera kukumbukira kuti Oweruza enieni a mlandu uliwonse ndiwo Yehova ndi Kristu Yesu. Kumbukirani zimene oweruza m’Israyeli anauzidwa: “Simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu iyeyu pakuweruza mlandu. Ndipo tsono, kuwopa Yehova kukhale pa inu, . . . Mudzitero, ndipo simudzapalamula.” (2 Mbiri 19:6-10) Limodzi ndi mantha olemekeza, akulu oweruza nkhani ayenera kuchita zonse zimene angathe kutsimikizira kuti ndithudi Yehova ‘ali nawo pankhani yachiweruzo.’ Chosankha chawo chiyenera kusonyeza molondola mmene Yehova ndi Kristu amalingalilira nkhaniyo. Zimene iwo mophiphiritsira ‘amanga’ (kupeza liwongo) kapena ‘kumasula’ (kusakhala ndi liwongo) padziko lapansi ziyenera kukhala zimene zamangidwa kapena kumasulidwa kale kumwamba​—monga momwe zasonyezedwera ndi zimene zalembedwa m’Mawu ouziridwa a Mulungu. Ngati iwo apemphera kwa Yehova m’dzina la Yesu, Yesu adzakhala “pakati pawo” kuti awathandize. (Mateyu 18:18-20, mawu amtsinde; Nsanja ya Olonda, February 15, 1988, tsamba 9) Mkhalidwe pamlandu wachiweruzo uyenera kusonyeza kuti Kristu alidi pakati pawo.

Abusa Anthaŵi Yonse

8. Kodi thayo loyambirira la akulu ndi liti, monga momwe lachitidwira chitsanzo ndi Yehova ndi Kristu? (Yesaya 40:10, 11; Yohane 10:11, 27-29)

8 Akulu saali oweruza anthaŵi yonse. Iwo ali abusa anthaŵi yonse. Iwo ali ochiritsa, osati olanga. (Yakobo 5:13-16) Lingaliro lalikulu la liwu Lachigiriki la woyang’anira (e·piʹsko·pos) ndilo lija la chisamaliro chotetezera. Theological Dictionary of the New Testament limafotokoza kuti: “Likumawonjezera pa mbusa [pa 1 Petro 2:25], liwulo [e·piʹsko·pos] limapereka lingaliro la ntchito yaubusa ya kuyang’anira kapena kutetezera.” Inde, thayo lawo loyamba ndilo kuyang’anira nkhosa ndi kuzitetezera, kuzisungabe ziri mkati mwa gulu.

9, 10. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anagogomezera thayo loyamba la akulu, chotero kodi ndifunso lotani limene lingafunsidwe bwino lomwe? (b) Kodi mawu a Paulo pa Machitidwe 20:29 amapereka lingaliro lotani, chotero kodi ndimotani mmene akulu angayesere kuchepetsa chiŵerengero cha nkhani zachiweruzo?

9 Polankhula kwa akulu a mpingo wa ku Efeso, mtumwi Paulo anaika chigogomezero pamene chifunikira: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo mzimu woyera anakuikani oyang’anira, kuti muwete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi [wa Mwana, NW] wake.” (Machitidwe 20:28) Paulo akugogomezera kuweta, osati kulanga. Akulu ena angachite bwino kulingalira funso lotsatirapoli: ‘Kodi tingawombole nthaŵi yochuluka yofunikira kufufuza ndi kusamalira nkhani zachiweruzo ngati tingathere nthaŵi yowonjezereka ndi kuyesayesa m’kuweta?’

10 Nzowona, Paulo anachenjeza motsutsana ndi “mimbulu yosautsa.” Koma kodi iye sanaitsutse imeneyi kaamba ka ‘kusachita ndi gulu lankhosa mokoma mtima’? (Machitidwe 20:29, NW) Ndipo pamene kuli kwakuti iye anapereka lingaliro lakuti oyang’anira okhulupirika ayenera kuchotsa “mimbulu” imeneyi, kodi mawu ake samasonyeza kuti akulu ayenera kuchita ndi ziwalo zina za gululo ‘mokoma mtima’? Pamene nkhosa ifikira kukhala yofoka mwauzimu niileka kutumikira Mulungu, kodi iyo ifunikira chiyani​—kumenyedwa kodi kapena kuchiritsidwa, kulanga kapena kuweta kodi? (Yakobo 5:14, 15) Chotero, akulu ayenera mokhazikika kumandandalitsa nthaŵi yantchito yaubusa. Kutero kungakhale ndi zotulukapo zabwino zakuchepetsako nthaŵi yowonongedwera m’khani zachiweruzo zambiri zowononga nthaŵi zophatikizapo Akristu amene anagonjetsedwa ndi uchimo. Ndithudi, nkhaŵa yoyamba ya akulu iyenera kukhala kupereka chitonthozo ndi chitsitsimulo, mwakutero akumapititsa patsogolo mtendere, chisangalalo, ndi chitetezo pakati pa anthu a Yehova.​—Yesaya 32:1, 2.

Kutumikira Monga Abusa ndi Oweruza Achifundo

11. Kodi nchifukwa ninji akulu otumikira pamakomiti achiweruzo afunikira mkhalidwe wa kupanda tsankhu ndi wa “nzeru yochokera kumwamba”?

11 Kubusa kowonjezereka Mkristu asanatenge njira yolakwa angachepetse kwambiri chiŵerengero cha nkhani zachiweruzo pakati pa anthu a Yehova. (Yerekezerani ndi Agalatiya 6:1.) Mosasamala kanthu za zimenezo, chifukwa cha uchimo waumunthu ndi kupanda ungwiro, oyang’anira Achikristu panthaŵi ndi nthaŵi angafunikire kusamalira nkhani za cholakwa. Kodi ndimalamulo amakhalidwe abwino ati amene ayenera kuwatsogoza? Amenewa sanasinthe chiyambire m’nthaŵi ya Mose kapena ija ya Akristu oyambirira. Mawu a Mose olunjikitsidwa kwa oweruza m’Israyeli adakagwirabe ntchito akuti: “Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama . . . Musamasamalira munthu poweruza mlandu.” (Deuteronomo 1:16, 17) Kupanda tsankhu ndiwo mkhalidwe wa “nzeru yochokera kumwamba,” nzeru imene iri yofunika kwambiri kwa akulu otumikira pamakomiti achiweruzo. (Yakobo 3:17; Miyambo 24:23) Nzeru yoteroyo idzawathandiza kuzindikira kusiyana kwa pakati pa kufooka ndi kuipa.

12. Kodi ndimlingaliro lotani limene oweruza samafunikira kokha kukhala amuna olungama komanso amuna abwino?

12 Akulu ‘ayenera kuweruza m’chilungamo,’ mogwirizana ndi miyezo ya Yehova ya chabwino ndi choipa. (Salmo 19:9) Komabe, pamene akuyesayesa kukhala amuna olungama, iwo ayenera kuyesayesanso kukhala amuna abwino, mogwirizana ndi lingaliro la kusiyanitsa limene Paulo akupereka pa Aroma 5:7, 8. Likumathirira ndemanga mavesi amenewa m’nkhani yake yonena za “Righteousness” (Chilungamo), bukhu lakuti Insight on the Scriptures limafotokoza kuti: “Kugwiritsiridwa ntchito kwa liwu Lachigiriki kumasonyeza kuti munthu wodziŵidwa ndi, kapena wosiyanitsidwa ndi, ubwino ndiye munthu wopindulitsa (wokhala ndi chikhoterero cha kuchitira ena zabwino kapena kubweretsa phindu kwa ena) ndi wopindulitsa (akumasonyeza mwachangu ubwino woterowo). Iye samangodera nkhaŵa chabe ndi kuchitira ena chiweruzo cholungama koma amachita zambiri koposa zimenezi, akumasonkhezeredwa ndi kuchitira chifundo ena ndi chikhumbo cha kuwapindulitsa ndi kuwathandiza.” (Voliyumu 2, tsamba 809) Akulu amene sangokhala olungama komanso abwino adzachita ndi ochimwawo mwaubwenzi ndi mokoma mtima. (Aroma 2:4) Iwo ayenera kukhala ofuna kusonyeza chifundo ndi kukoma mtima. Ayenera kuchita zonse zimene angathe kuthandiza wochimwa kuwona kufunika kwa kulapa, chinkhana kuti poyamba angawonekere kukhala wosalabadira ku zoyesayesa zawo.

Mkhalidwe Woyenera Pamilandu

13. (a) Pamene mkulu achita monga woweruza, kodi iye samaleka kukhala chiyani? (b) Kodi ndiuphungu wotani woperekedwa ndi Paulo umene umagwiranso ntchito pamilandu yachiweruzo?

13 Pamene mkhalidwe ufunikiritsa mlandu wachiweruzo, oyang’anira sayenera kuiwala kuti adakali abusa, akumachita ndi nkhosa za Yehova, zimene ziri pansi pa “mbusa wabwino.” (Yohane 10:11) Uphungu umene Paulo anapereka wophatikizapo chithandizo chanthaŵi zonse choperekedwa ku nkhosa zimene ziri pamavuto umagwira ntchito ndi mphamvu yofanana pamilandu yachiweruzo. Iye analemba kuti: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mumzimu wachifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.”​—Agalatiya 6:1, 2.b

14. Kodi ndimotani mmene oyang’anira ayenera kuwona kachitidwe kakuzenga mlandu, ndipo kodi malingaliro awo ayenera kukhala otani kulinga kwa wochita choipayo?

14 Mmalo mwa kudzilingalira kukhala oweruza apamwamba osonkhana kuti apereke chilango, akulu otumikira pakomiti yachiweruzo ayenera kulingalira mlanduwo monga mbali ina ya ntchito yawo yoweta. Imodzi ya nkhosa za Yehova iri m’vuto. Kodi iwo angachitenji kuipulumutsa? Kodi kukakhala kuchedwa kwambiri kuthandiza nkhosayi imene yasokera kuchoka pagulu? Tikhulupirira kuti sikuli kuchedwa. Akulu ayenera kukhala ndi malingaliro abwino akusonyeza chifundo pamene chingakhale choyenera. Sikuli kwakuti iwo ayenera kuchepetsa miyezo ya Yehova ngati tchimo lowopsa lachitidwa. Koma kuzindikira kwawo mikhalidwe iriyonse yochititsa kudzawathandiza kusonyeza chifundo pamene kuli kotheka. (Salmo 103:8-10; 130:3) Nzachisoni kunena kuti, ochita zoipa ena amakhala ouma khosi kwambiri mumkhalidwe wawo wamaganizo kotero kuti akulu amakakamizika kusonyeza mphamvu, komabe osati ukali.​—1 Akorinto 5:13.

Chifuno cha Milandu Yachiweruzo

15. Pamene vuto lalikulu libuka pakati pa anthu, kodi nchiyani chimene chiyenera kupendedwa choyamba?

15 Pamene vuto lowopsa libuka pakati pa anthu, akulu anzeru amayamba kupenda kuti kaya ophatikizidwawo ayesa kuthetsa nkhaniyo mwamtseri, mogwirizana ndi Mateyu 5:23, 24 kapena Mateyu 18:15. Ngati zimenezi zalephera, mwinamwake uphungu wa mkulu mmodzi kapena aŵiri udzakwanira. Kachitidwe kachiweruzo nkoyenerera kokha ngati pachitidwa tchimo lalikulu limene lingatsogolere kukuchotsedwa. (Mateyu 18:17; 1 Akorinto 5:11) Payenera kukhala chifukwa chabwino Chamalemba chopangira komiti yachiweruzo. (Wonani Nsanja ya Olonda, ya September 15, 1989, tsamba 18.) Pamene komiti yapangidwa, akulu oyeneretsedwa koposa ayenera kusankhidwa kaamba ka mlandu uliwonse.

16. Kodi akulu amayesa kukhoza kuchitanji mwanjira ya milandu yachiweruzo?

16 Kodi akulu amayesa kupezanji mwakutsatira kachitidwe kachiweruzo kakuzenga mlandu? Choyamba, nkosatheka kuweruza mwachilungamo kusiyapo ngati chowonadi chadziwidwa. Monga m’Israyeli, nkhani zazikulu ziyenera ‘kufufuzidwa.’ (Deuteronomo 13:14; 17:4) Chotero cholinga chimodzi cha kuzenga mlandu ndicho kupeza zenizeni za nkhaniyo. Komabe zimenezi zingakhoze ndipo ziyenera kuchitidwa mwachikondi. (1 Akorinto 13:4, 6, 7) Zenizeni zitadziwidwa, akuluwo adzachita zonse zimene ziri zoyenera kutetezera mpingo ndi kusunga miyezo yapamwamba ya Yehova mkati mwake ndi kulola mzimu wake kuyenda mwatawatawa. (1 Akorinto 5:7, 8) Komabe, chimodzi cha zifuno zakuzenga mlandu ndicho kupulumutsa wochimwa yemwe ali paupanduyo, ngati kuli kotheka.​—Yerekezerani ndi Luka 15:8-10.

17. (a) Kodi munthu wonenezedwayo ayenera kuchitiridwa motani mkati mwa kuzenga mlandu, ndipo ndi chifuno chotani? (b) Kodi zimenezi zidzafunikiritsa chiyani kuziwalo zakomiti yachiweruzo?

17 Munthu wonenezedwayo sayenera kuchitiridwa mwanjira ina koposa yakuti iye ndinkhosa ya Mulungu. Iye ayenera kuchitiridwa mokoma mtima. Ngati tchimo (kapena machimo) lachitidwa, chifuno cha oweruza olungama chidzakhala cha kuthandiza wochimwayo kusintha, kuzindikira kulakwa kwa njira yake, kulapa, ndipo motero kumkwatula pa “msampha wa Mdyerekezi.” Zidzafunikiritsa ‘luso la kuphunzitsa,’ ‘kulangiza mwachifatso.’ (2 Timoteo 2:24-26; 4:2, NW) Nanga bwanji ngati wochimwayo wafikira pakuzindikira kuti anachimwa, walaswa mtima mowonadi, ndipo akupempha Yehova chikhululukiro? (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:37.) Ngati komiti yakhutira kuti iye mowona mtima akufuna chithandizo, kaŵirikaŵiri sipamakhala chifuno chomchotsera.​—Wonani Nsanja ya Olonda Yachingelezi, ya January 1, 1983, tsamba 31, ndime 1.

18. (a) Kodi ndiliti pamene komiti yachiweruzo iyenera kusonyeza kuima nji kuchotsa wochita choipa? (b) Kodi ndipolingalira za mkhalidwe wodetsa nkhaŵa wotani kuti akulu ayenera kugwira ntchito zolimba kaamba ka nkhosa zomasochera?

18 Kumbali ina, pamene ziwalo za komiti yachiweruzo zapeza mpatuko wosalapa konse, wopandukira dala malamulo a Yehova, kapena kuipa kwenikweniko, thayo lawo ndilo kutetezera ziwalo zinazo za mpingo mwa kuchotsa wolakwa wosalapayo. Komiti yachiweruzo siyenera kumakumana mobwerezabwereza ndi wochimwayo kapena kumdyetsa mawu, kuyesa kumkakamiza kulapa, ngati nkowonekeratu kuti alibe chisomo cha Mulungu.c M’zaka zaposachedwapa kuchotsa padziko lonse kwakhala pafupifupi 1 peresenti ya ofalitsa. Zimenezo zimatanthauza kuti mwa nkhosa pafupifupi zana limodzi zimene zimakhalabe m’khola, imodzi imataika​—pafupifupi kwakanthaŵi. Tikumalingalira za nthaŵi ndi kuyesayesa zimene kumatenga kubweretsa munthu m’khola, kodi sikodetsa nkhaŵa kudziwa kuti zikwi makumi ambiri ‘zimabwezeretsedwa kwa Satana’ chaka chirichonse?​—1 Akorinto 5:5.

19. Kodi nchiyani chimene akulu otumikira pakomiti yachiweruzo sayenera kuiwala, chotero kodi chiyani chimene chidzakhala cholinga chawo?

19 Akulu amene akuyamba nkhani yachiweruzo ayenera kukumbukira kuti nkhani zambiri za zolakwa mumpingo zimaphatikizapo kufoka, osati kuipa. Iwo sayenera kuiwala fanizo la Yesu la nkhosa yotaika, limene anatsiriza mwamawu akuti: “Ndinena kwa inu, kotero kudzakhala chimwemwe kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi wotembenuka mtima, koposa anthu olungama makumi asanu ndi anayi mphambu asanu ndi anayi, amene alibe kusowa kutembenuka mtima.” (Luka 15:7) Ndithudi, “Ambuye [Yehova, NW] . . . safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Mwachithandizo cha Yehova, makomiti achiweruzo kuzungulira padziko lonse achitetu zonse zimene angakhoze kupangitsa chimwemwe kuwamba mwa kuthandiza ochita zolakwa kuwona kufunika kwakulapa ndi kuyamba kubwerera panjira yopapatiza yomka ku moyo wamuyaya.​—Mateyu 7:13, 14.

[Mawu a M’munsi]

a Ponena za unansi wa akulu ochokera pakati pa a nkhosa zina ndi dzanja lamanja la Kristu, wonani bukhu lakuti Revelation​—Its Grand Climax At Hand!, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., tsamba 136, mawu amtsinde.

b Wonani Nsanja ya Olonda, ya September 15, 1989, tsamba 19.

c Wonani Nsanja ya Olonda Yachingelezi, ya September 1, 1981, tsamba 26, ndime 24.

Mafunso Akupenda

◻ Motsatira chitsanzo cha Mbusa Wamkulu ndi Mbusa Wabwino, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chikondwerero chachikulu cha akulu?

◻ Kodi ndimnjira yotani imene akulu angayeseyesere kuchepetsa chiŵerengero cha nkhani zachiweruzo?

◻ Kodi ndimlingaliro lotani mlimene oweruza afunikira osati kokha kukhala olungama komanso abwino?

◻ Kodi wochita zoipa ayenera kuchitiridwa motani mkati mwa mlanduwo, ndipo limodzi ndi chifuno chotani?

◻ Kodi nchifukwa ninji kuchotsa kuli mchitidwe wotsiriza?

[Chithunzi patsamba 16]

Pamene kuweta kwapasadakhale kuchitidwa nkhani zachiweruzo zambiri zingapewedwe

[Chithunzi patsamba 18]

Ngakhale mkati mwa kuzenga mlandu, akulu ayenera kuyesa kubweza choipa mumzimu wachifatso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena