Kodi Mumafunikiranji Kuti Mukhale Wachimwemwe?
ATSOGOLERI andale zadziko osankhidwa ndi anthu amayesayesa mwamphamvu kukondweretsa anthuwo. Ndiiko komwe, ntchito zawo zimadalira pamenepo. Koma magazini ankhani amalankhula za “ochita masankho onyengedwa ndi okwiitsidwa” ku Poland. Mtola nkhani wina analongosola kuti United States ndidziko “lodzazidwa ndi kusakhulupirira ndale zadziko zanthaŵi zonse.” Wolemba nkhani wina akutiuza za “mphwayi zomakulakula m’zandale zadziko ku Falansa.” Kufalikira kwa mphwayi ndi kusakhutira kumeneko—komwe mosakaikira konse sikuli kumaiko atatu okhawa—kukusonyeza kuti atsogoleri andale zadziko akulephera m’zoyesayesa zawo zakukondweretsa anthu.
Atsogoleri achipembedzo nawonso amalonjeza chimwemwe, ngati sim’moyo uno, mwina wamtsogolo. Iwo amazika zimenezi palingaliro lakuti anthu ali ndi moyo wosakhoza kufa kapena umene umasamuka, lingaliro limene anthu ambiri amakana pazifukwa zambiri ndipo Baibulo limalikana kotheratu. Matchalitchi opanda anthu ndi kutsika kwa ziŵerengero za ziŵalo zake kumasonyeza kuti mamiliyoni ambiri samawonanso chipembedzo kukhala chofunika kubweretsa chimwemwe.—Yerekezerani ndi Genesis 2:7, 17; Ezekieli 18:4, 20.
Okonda Siliva Osakhutira
Ngati chimwemwe sichipezeka m’ndale zadziko kapena chipembedzo, kodi chingapezeke kuti? Mwinamwake m’zamalonda kodi? Nazonso zimanena kuti zikhoza kupereka chimwemwe. Zimapereka zigomeko zake mwakusatsa malonda, zikumanena momvekera kuti: Chimwemwe chimakhalapo ngati uli ndi zinthu zonse zakuthupi ndi zinthu zimene ndalama zingagule.
Unyinji wa anthu ofunafuna chimwemwe mwanjira imeneyi ukuwoneka kukhala ukuwonjezereka. Kunasimbidwa zaka zingapo zapitazo kuti banja lachiŵiri lililonse m’Jeremani linali m’ngongole zowopsa. Pamenepo, mposadabwitsa kuti nyuzipepala yotchuka ya ku Jeremani Die Zeit inalosera kuti “ambiri [a ameneŵa] sadzakhoza konse kutuluka m’ngongole zimenezo.” Inafotokoza kuti: “Nkwapafupi kwambiri kukongola ndalama zowonjezereka zimene banki imakupatsani—ndipo nkovuta kwambiri kutuluka m’ngongolezo.”
Mkhalidwewu ngwofanana m’maiko ena otukuka kwambiri. Zaka zingapo zapitazo, David Caplovitz, katswiri wa kakhalidwe ka anthu pa City University ya ku New York, anayerekezera kuti mu United States, pakati pa mabanja 20 miliyoni ndi 25 miliyoni anali ndi ngongole zazikulu. “Anthu amizidwa m’ngongole,” iye anatero, “ndipo zikuwononga miyoyo yawo.”
Zimenezo sizikumveka monga chimwemwe konse! Koma kodi tiyenera kuyembekezera dongosolo lamalonda kukhala lokhoza kukwaniritsa zimene ziŵiri zinazo (ndale zadziko ndi chipembedzo) sizingathe kuchita? Mfumu yolemera Solomo panthaŵi ina inalemba kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.”—Mlaliki 5:10.
Kufunafuna chimwemwe m’chuma chakuthupi ndiko maloto. Angakhale osangalatsa kuwalota, koma mudzakhala m’mavuto ngati muyesa kuwadalira.
Chimwemwe Chikhoza Kupezeka Koma Motani?
Mtumwi Paulo anatcha Yehova “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Mwakulenga anthu m’chifaniziro chake, Mulungu wachimwemweyo anawapatsanso kuthekera kwakukhala achimwemwe. (Genesis 1:26) Koma chimwemwe chawo chinayenera kudalira pa kutumikira kwawo Mulungu, monga momwe wamasalmo anasonyezera: “[Achimwemwe, NW] anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Salmo 144:15b) Zimene utumiki wathu kwa Mulungu umaphatikizapo ndi mmene kumtumikira iye kungatsogolere ku chimwemwe chenicheni zingamvedwe bwino ngati tilingalira malo oŵerengeka mwa malo 110 mu New World Translation kumene mawu akuti “achimwemwe” ndi “chimwemwe” amapezeka.
Kuzindikira Zosoŵa Zauzimu
Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, ananena mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri kuti: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Dongosolo lamalonda limayesayesa kutisocheretsa kulingalira kuti kugula zinthu zosangulutsa nkokwanira kubweretsa chimwemwe. Limatiuza kuti chimwemwe ndicho kukhala ndi kompyuta panyumba, kamera ya vidiyo, telefoni, galimoto, ziwiya zamakono kwambiri za maseŵera, zovala zamakono. Zomwe silimatiuza nzakuti anthu mamiliyoni makumi ambiri m’dziko alibe zinthu zimenezi ndipo sali opandiratu chimwemwe. Pamene kuli kwakuti mwinamwake zimachititsa moyo kukhala wabwino ndi wosangalatsa, zinthu zimenezi sizili zofunika pa chimwemwe.
Monga momwe anachitira Paulo, awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu amati: “Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.” (1 Timoteo 6:8) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti kukwaniritsa zosoŵa zauzimu ndiko kumatsogolera ku moyo wamuyaya.—Yohane 17:3.
Kodi pali cholakwa chilichonse ndi kusangalala ndi zinthu zabwino ngati tili ndi ndalama zozigulira? Mwinamwake ayi. Komabe, kuphunzira kusadziloŵetsa m’zinthu zonse kapena kusagula kanthu kena kokha chifukwa chakuti tikhoza kukagula kumalimbitsa uzimu wathu. Motero timaphunzira kukhutira ndi kusunga chimwemwe, monga momwe Yesu anachitira, ngakhale kuti mkhalidwe wake wachuma sunali wabwino koposa malinga ndi miyezo yakudziko. (Mateyu 8:20) Ndipo Paulo sanasonyeze kupanda chimwemwe pamene analemba kuti: “Sikuti ndinena monga mwa chipereŵero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndadziŵa ngakhale kupeputsidwa, ndadziŵanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa.”—Afilipi 4:11, 12.
Kukhulupirira Yehova
Kuzindikira kusoŵa kwauzimu kwa munthuwe kumasonyeza kufunitsitsa kukhulupirira Mulungu. Zimenezi zimapangitsa chimwemwe, monga momwe Mfumu Solomo anafotokozera kuti: “Wachimwemwe ali iye amene akukhulupirira Yehova.”—Miyambo 16:20, NW.
Komabe, kodi sizowona kuti anthu ambiri amaika chikhulupiriro chachikulu m’ndalama ndi chuma kuposa mwa Mulungu? Polingalira za mfundo imeneyi, kuli kosayenera konse kusonyeza mawu akuti “In God We Trust” (Timakhulupirira Mulungu) pa ndalama, ngakhale kuti mawu amenewo amawoneka pa ndalama za ku United States.
Mfumu Solomo, amene sanasoŵe kanthu kabwino kalikonse kamene ndalama zingagule, anazindikira kuti kukhulupirira chuma chakuthupi sikumatsogolera ku chimwemwe. (Mlaliki 5:12-15) Ndalama zosungidwa kubanki zingatayike mwakugwa kwa banki kapena kukwera mitengo kwa zinthu. Malo ndi nyumba zingawonongedwe ndi mkuntho. Mainshuwalansi, ngakhale kuti amabwezeretsa pang’ono zotayika zakuthupi, samalipira konse kutayika kwachimwemwe. Zikole zamalonda ndi zikalata za ngongole zingathe ntchito patsiku limodzi pamene malonda agwa pamsika wa zikole zamalonda. Ngakhale ntchito yamalipiro abwino—pa zifukwa zambiri—ingakhale yosakhalitsa.
Pazifukwa zimenezi munthu amene amakhulupirira Yehova amawona nzeru yakumvera chenjezo la Yesu lakuti: “Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.”—Mateyu 6:19, 20.
Kodi pali chisungiko ndi chimwemwe chilichonse chachikulu kuposa kudziŵa kuti munthu waika chikhulupiriro chake mwa Mulungu Wamphamvuyonse, amene nthaŵi zonse amapereka zofunika?—Salmo 94:14; Ahebri 13:5, 6.
Kulandira Chidzudzulo Chaumulungu
Uphungu, ngakhale chidzudzulo, zimalandiridwa pamene ziperekedwa ndi mzimu wachikondi ndi bwenzi lowona. Yemwe anadzinenera kukhala bwenzi la Yobu mtumiki wa Mulungu, modzilungamitsa anamuuza kuti: “[Wachimwemwe, NW] munthu amene Mulungu amdzudzula.” Ngakhale kuti mawuwa ngowona, zimene Elifazi anatanthauza ndi mawu ameneŵa—kuti Yobu anali ndiliŵongo la cholakwa chachikulu—sizinali zowona. Iye anali ‘wotonthoza mtima molemetsa’ wotani nanga! Komabe, pamene Yehova anadzudzula Yobu pambuyo pake mwachikondi, Yobu analandira chidzudzulocho modzichepetsa ndipo anapeza chimwemwe chachikulu.—Yobu 5:17; 16:2; 42:6, 10-17.
Lerolino, Mulungu samalankhula ndi atumiki ake mwachindunji monga momwe anachitira ndi Yobu. M’malomwake, iye amawadzudzula kudzera m’Mawu ake ndi gulu lake lotsogozedwa ndi mzimu. Komabe, Akristu amene amalondola zinthu zakuthupi, kaŵirikaŵiri amakhala opanda nthaŵi, nyonga, kapena chikhumbo chakuphunzira Baibulo mokhazikika ndi kufika pamisonkhano yonse imene gulu la Yehova limakonza.
Munthu amene Mulungu amamdzudzula, mogwirizana ndi Miyambo 3:11-18, amazindikira nzeru yakulandira chidzudzulo chimenecho: “[Wachimwemwe, NW] ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira [adzatchedwa wachimwemwe, NW].”
Kukhala Oyera ndi Okonda Mtendere
Yesu analongosola anthu achimwemwe kukhala “oyera mtima” ndi “amtendere.” (Mateyu 5:8, 9) Koma m’dziko limene limalimbikitsa njira yamoyo yokondetsa zakuthupi, kumakhala kosavuta chotani nanga kuti dyera, kapena ngakhale zikhumbo zoipa, zizike mizu m’mitima mwathu! Ngati sititsogozedwa ndi nzeru yaumulungu, kungakhale kosavuta chotani nanga kwa ife kusocheretsedwa ndi kufunafuna mkhalidwe wabwino wazachuma mwanjira zokaikitsa zimene zingawononge unansi wathu wamtendere ndi ena! Pali chifukwa chabwino chimene Baibulo limachenjezera kuti: “Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.”—1 Timoteo 6:10.
Chikondi cha pandalama chimasonkhezera lingaliro lodzikonda limene limachititsa kusakhutira, kusayamikira, ndi umbombo. Kuti apeŵe kukulitsa mzimu wolakwa umenewo, Akristu ena amadzifunsa mafunso otsatirawa asanapange zosankha zazikulu zachuma: Kodi ndikufunikiradi zimenezi? Kodi ndifunikiradi chinthu chodulachi kapena ntchito yamalipiro abwino koma yodya nthaŵi kuposa anthu ena mamiliyoni ambiri amene alibe zimenezi? Kodi ndingagwiritsire ntchito bwino ndalama zanga kapena nthaŵi yanga kufutukula phande langa m’kulambira kowona, m’kuchilikiza ntchito yolalikira yapadziko lonse, kapena kuthandiza anthu ena osaukirapo kuposa ine?
Kusonyeza Chipiriro
Chimodzi cha ziyeso zimene Yobu anakakamizika kupirira chinali kulandidwa chuma. (Yobu 1:14-17) Monga momwe chitsanzo chake chikusonyezera, chipiriro chimafunikira m’mbali zonse za moyo. Akristu ena ayenera kupirira chizunzo; ena chiyeso; enanso mikhalidwe yachuma yosayenerera. Koma chipiriro cha mtundu uliwonse chidzafupidwa ndi Yehova, monga momwe wophunzira Wachikristu Yakobo analembera ponena za Yobu kuti: “Tawonani tiwayesera [achimwemwe, NW] opirirawo.”—Yakobo 5:11.
Kunyalanyaza zinthu zauzimu kuti tiwongolere mkhalidwe wathu wachuma kungakhale ndi mpumulo wazachuma wakanthaŵi, koma kodi zikatithandiza kusunga chiyembekezo cholimba cha mpumulo wokhalitsa wa zachuma pansi pa Ufumu wa Mulungu? Kodi upandu wotero ngwoyenera?—2 Akorinto 4:18.
Kupeza Chimwemwe Tsopano ndi Kosatha
Mosakaikira anthu ena amatsutsa lingaliro limene Yehova ali nalo la zimene zimachititsa anthu kukhala achimwemwe. Mwakunyalanyaza mapindu okhalitsa ofunika kwambiri, iwo amawona kuti palibe phindu lililonse laumwini limene angapeze tsopanoli mwakuchita zimene Mulungu amalangiza. Iwo amalephera kuzindikira kuti kudalira zinthu zakuthupi ndikwachabe ndipo kumagwiritsa mwala. Wolemba Baibulo ananena zowona pamene anafunsa kuti: “Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso awo?” (Mlaliki 5:11; onaninso Mlaliki 2:4-11; 7:12.) Chikondwerero chimatha msanga motani nanga ndipo zinthu zimene tinalingalira kuti tinazifunikira zimangokhala osagwiritsiridwa ntchito!
Mkristu wowona sadzalola konse kukakamizidwa ‘kukhala wamakono’ m’njira yakuthupi. Iye amadziŵa kuti kuyenera kwenikweni kumapimidwa, osati ndi zimene munthu ali nazo, koma amene iye ali. Iye samakaikira konse m’maganizo mwake ponena za zimene zingachititse munthu kukhala wachimwemwe—wachimwemwe mowonadi: kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova ndi kukhala wotanganitsidwa muutumiki Wake.
[Chithunzi patsamba 20]
Zinthu zakuthupi zokha sizingabweretse chimwemwe chosatha
[Chithunzi patsamba 22]
Baibulo limati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu”