Kodi Mukuchita Chifuniro cha Mulungu?
MUUTUMIKI wawo wakunyumba ndi nyumba, Mboni za Yehova ziŵiri zinakumana ndi wansembe wa Tchalitchi cha Episcopal. Iye anaonekera kukhala munthu waubwenzi, wokhala ndi ndevu, wazaka zakubadwa pafupifupi 60, atavala sikipa yolembedwa dzina la tchalitchi chake. Iye ananena mwachidule kuti: “Ndikulakalaka kuti bwenzi ziŵalo za tchalitchi chathu zili zachangu monga mmene muliri pofalitsa Mawu, koma ndidzayenera kukupemphani kusabweranso pakhomo panga.”
Inde, pali anthu ambiri amene amasirira ntchito ya Mboni za Yehova ndi kuziyamikira chifukwa cha changu chawo ndi kukangalika. Komabe, sali okondweretsedwa mpang’ono pomwe ndi zimene Mboni zikuchita, ndipo samalingalira zochita ntchitoyo iwo eni. Komabe, kusemphana maganizo kwachionekere kumeneku sikuli kwatsopano. Yesu anakuona m’tsiku lake, ndipo anagogomezera mwamphamvu mfundoyo mwakupereka fanizo lotokosa maganizo.
“Nanga mutani? Munthu anali nawo ana aŵiri; nadza iye kwa woyamba, nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito ku munda wampesa. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapita. Ndani wa aŵiriwo anachita chifuniro cha atate wake?”—Mateyu 21:28-31.
Yankho nlodziŵikiratu. Mofanana ndi khamu limene linamva Yesu, tingayankhe kuti, “Woyambayo.” Koma kuposa pamenepo, mwa fanizo limenelo, Yesu anali kutisonyeza kuti kuchita zimene atate anafuna ndiko kunali kanthu. Ngakhale kuti mwana woyambayo ananena kuti sanafune kupita, iye anapitabe ndipo anayamikiridwa chifukwa cha zimenezo. Kuchita ntchito yamtundu woyenera nkofunikanso kwambiri. Mwana woyambayo anachitapo kanthu mwa kugwira ntchito m’munda wampesa wa atatewo; iye sanapite kukagwira ntchito m’munda wake wampesa.
Kodi zonsezi zili ndi tanthauzo lotani kwa ife? Kodi Mulungu amafuna chiyani kwa olambira lerolino? Kodi tingaphunzirenji m’moyo wa Yesu chimene chidzatithandiza kuchita chifuniro cha Atate wake? Ameneŵa ndimafunso ofunika, ndipo kupeza kwathu mayankho olondola kudzatanthauza ubwino wathu wosatha, popeza kuti “iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17; Aefeso 5:17.
Kodi “Chifuniro cha Mulungu” Nchiyani?
Nauni lakuti “will” (chifuniro) landandalikidwa nthaŵi zoposa 80 mu Comprehensive Concordance of the New World Translation of the Holy Scriptures. Pafupifupi nthaŵi 60 za zimenezi (kapena pafupifupi 75 peresenti ya nthaŵizo) liwulo limanena za chifuniro cha Mulungu. Mawu onga ngati “chifuniro cha Mulungu,” “chifuniro cha Atate wanga,” ndi “chifuniro cha Mulungu” amaoneka nthaŵi zoposa 20. Kuchokera m’zimenezi tingaone kuti chifuniro chaumulungu chiyenera kukhala chofunika koposa kwa ife. Kuchita chifuniro cha Mulungu kuyenera kukhala nkhaŵa yaikulu m’miyoyo yathu.
M’Chingelezi nauni lakuti “chifuniro” limatanthauza ‘chilakolako, chikhumbo, kutsimikiza mtima, chinthu chokhumbirika, makamaka chosankha kapena kutsimikiza mtima kwa munthu wokhala ndi ulamuliro kapena mphamvu.’ Chotero pamenepa, Yehova, Wolamulira Wamkulu, ali ndi chifuniro, chilakolako kapena kutsimikiza mtima. Kodi icho nchiyani? Malemba amatiuza, mwapang’ono, kuti “[Mulungu] afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira chowonadi.” (1 Timoteo 2:4) Yesu Kristu ndi Akristu oyambirira anagwira ntchito ndi moyo wonse kutengera chidziŵitso cholongosoka chimenechi kwa ena.—Mateyu 9:35; Machitidwe 5:42; Afilipi 2:19, 22.
Kodi ndani amene akuchita chifuniro cha Mulungu lerolino? Pakati pa anthu oposa mamiliyoni zikwi ziŵiri amene amadzitcha kukhala otsatira a Yesu Kristu, kodi ndiangati amene ali ngati mwana woyamba m’fanizo la Yesu, amene anapita ndi kukachita chifuniro cha atate wake? Yankho silovuta kupeza. Otsatira mapazi a Yesu Kristu owona akakhala akuchita ntchito imene iye ananena kuti akaichita: “Ndipo uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Mboni za Yehova, zofika pafupifupi mamiliyoni anayi ndi theka padziko lonse, zikulalikira mokangalika mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi kuphunzitsa ena, zikumasonyeza Ufumuwo monga chiyembekezo chokha cha anthu cha mtendere ndi chisungiko. Kodi mukukhala ndi phande lokwanira m’kuchita chifuniro cha Mulungu? Kodi mukulalikira mbiri yabwino ya Ufumu monga momwe Yesu anachitira?—Machitidwe 10:42; Ahebri 10:7.
Kupeza Chisangalalo m’Kuchita Chifuniro cha Mulungu
Pamene kuli kwakuti muli chisangalalo m’kuphunzira chimene chili chifuniro cha Atate, muli chisangalalo chokulirapo m’kuphunzitsa ena chifuniro cha Mulungu. Yesu anasangalala kuphunzitsa anthu ponena za Atate wake. Kunali ngati chakudya kwa iye. (Yohane 4:34) Nafenso tidzakhala ndi chimwemwe chenicheni ngati tichita monga momwe Yesu anachitira, ndiko kuti, kulalikira ndi kuphunzitsa zinthu zimene anaphunzitsa, zinthu zimene analandira kwa Atate wake. (Mateyu 28:19, 20) Monga momwe Yesu analonjezera, “ngati mudziŵa izi, odala inu ngati muzichita.”—Yohane 13:17.
Mwachitsanzo: Mayi wina amene analoŵanso posachedwapa muutumiki wa upainiya wanthaŵi yonse anati: “Kumakhala kosangalatsa kwambiri kuona nkhope ya wophunzira Baibulo ikuŵala pamene chowonadi cha Baibulo chosiyanasiyana chikhudza mtima! Nkokondweretsa kwa ine kuona wophunzira wina akulemba malemba onse phunziro lisanayambe ndi kutenga manotsi mkati mwa phunzirolo kotero kuti akhoze kuyankha mafunso alionse akapendedwe pambuyo pake.” Wophunzira Baibulo wake wina anamva chowonadi ali wa zaka za pakati pa 13 ndi 16. Pokhala wokwatiwa tsopano ndi wodera nkhaŵa ndi mavuto ena aumwini, iye analakalaka kupeza Mboni. Anali wachimwemwe chotani nanga pamene mlongo wochita upainiyayo anampeza! Mkazi wachichepereyo anasangalala kuyambanso phunziro lake la Baibulo.
Kusunga Chisangalalo cha Kuchita Chifuniro cha Mulungu
Mfumu Davide wa Israyeli wakale anali mmodzi amene anafuna kuchita chifuniro cha Mulungu moyo wake wonse. Mosasamala kanthu za zovuta zambiri ndi zitsenderezo zimene zinali pa iye, anauziridwa kunena kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali mkati mwamtima mwanga.” (Salmo 40:8) Kuchita chifuniro cha Yehova kunali m’moyo mwa Davide, mkati mwake mwenimweni. Chimenecho chinali chinsinsi cha chisangalalo chake chosazirala m’kutumikira Yehova. Kuchita chifuniro cha Mulungu sikunali cholemetsa kwa Davide. Mmalomwake, kunali kosangalatsa, kanthu kamene kanachokera mumtima mwake. M’moyo wake wonse, anayesayesa kuchita zabwino koposa kutumikira Mulungu wake, Yehova, ngakhale kuti nthaŵi zina anachimwa ndi kuphophonya.
Nthaŵi zina, chisangalalo chathu chingazirale. Tingatope kapena kulefuka. Mwinamwake zinthu zimene tinachita kale zimativutitsa maganizo, chikumbumtima chathu chimatisautsa chifukwa cha cholakwa chimene chinachitidwa kale kwambiri. Kaŵirikaŵiri, tikhoza kugonjetsa malingaliro ameneŵa mwakuphunzira mosamalitsa kwambiri Mawu a Mulungu. Tingakhale ndi chonulirapo cha kulemba chilamulo cha Mulungu “mkati mwamtima” mwathu, monga momwe Davide anachitira. Ngati tiyesa kuchita chifuniro cha Mulungu ndi moyo wonse, ndiko kuti, monga momwe tingathere, iye adzatifupa molinganamo chifukwa chakuti ngwokhulupirika.—Aefeso 6:6; Ahebri 6:10-12; 1 Petro 4:19.
Mokondweretsa, pa Ahebri 10:5-7, mtumwi Paulo anagwira mawu a Davide a pa Salmo 40:6-8 ndi kuwagwiritsira ntchito kwa Yesu Kristu. Mwakutero, Paulo anasonyeza mmene Yesu analiri woyandikana ndi Atate wake. Liwu Lachihebri lakuti “chifuniro” limatanthauza ‘chisangalalo, chikhumbo, chiyanjo, kapena chosangulutsa.’ Pamenepo, lemba la Salmo 40:8 limaŵerengedwa motere ponena za Kristu: “Kuchita chosangulutsa chanu kundikonda, Mulungu wanga.”a Yesu anafuna kuchita zimene zinakondweretsa Atate wake. Yesu anapyola pakuchita zimene anapemphedwa. Iye anachita zimene zinali pamtima pa Atate wake, ndipo anakondwera kuzichita.
Moyo wonse wa Yesu unazikidwa pa kuphunzitsa ena chimene chinali chifuniro cha Mulungu ndi zimene ayenera kuchita kuti alandire dalitso la Mulungu. Iye anali mlaliki ndi mphunzitsi wa nthaŵi yonse ndipo anapeza chisangalalo chachikulu m’kuchita ntchito imeneyo. Chotero zimachitika kuti ngati tichita ntchito ya Yehova mowonjezereka, timalandira chisangalalo chowonjezereka. Kodi nanunso mungatumikire nthaŵi yonse m’ntchito yolalikira kotero kuti chisangalalo chanu chikhale chochuluka?
Chithandizo chowonjezereka chosungira chisangalalo pochita chifuniro cha Mulungu ndicho kuyang’ana mtsogolo mwachidwi. Zimenezo nzimene Yesu anachita. “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira [mtengo wozunzirapo, NW], nanyoza manyazi.” Kwa iye, chimwemwe chake chinali cha kutsimikizira kukhala wokhulupirika kwa Mulungu kufikira mapeto ndiyeno kulandira mphotho ya ufumu kudzanja lamanja la Atate wake.—Ahebri 12:2.
Talingalirani za chisangalalo chamtsogolo chimene chidzabwera kwa awo amene akupitiriza kuchita chifuniro cha Mulungu. Iwo adzaona kuwonongedwa kwa awo amene amaumirira kuchita chifuniro chawo chadyera ngakhale ngati kutero kumavutitsa awo amene amayesayesa kuchita chifuniro cha Mulungu. (2 Atesalonika 1:7, 8) Talingalirani za chisangalalo cha okondedwa oukitsidwa mwakukhala ndi mwawi wakuphunzira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Kapena talingalirani za chifuno cha Mulungu cha kubwezeretsa dziko lapansi kukhala Paradaiso. Ndipo pomaliza, talingalirani ufulu umene udzakhalapo chifukwa cha kuwonongedwa kotheratu kwa Satana, wotsutsa chifuniro cha Yehova.
Inde, kuchita chifuniro cha Mulungu lerolino kungabweretse chisangalalo chochuluka koposa tsopano ndi chimwemwe chosatha mtsogolo. Mosasamala kanthu za chilabadiro chimene tingapeze m’ntchito yolalikira, tiyeni titsanzire chitsanzo cha Yesu m’kusangalala ndi kuchita chifuniro cha Atate wake.
[Mawu a M’munsi]
a Onani mawu amtsinde pa Salmo 40:8, NW.