Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 10/15 tsamba 3
  • Chizindikiro Umboni Wakuti Dziko Latsopano Liri Pafupi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chizindikiro Umboni Wakuti Dziko Latsopano Liri Pafupi?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mbiri Yabwino”
  • Kodi Baibulo Linaneneratu Zotani pa Nkhani ya Zivomerezi Zamphamvu?
    Nkhani Zina
  • Mbadwo Wa 1914—Kodi Nchifukwa Ninji Uli Wapadera?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • “Mapeto a Dziko” Ayandikira!
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Masiku Otsiriza
    Kukambitsirana za m’Malemba
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 10/15 tsamba 3

Chizindikiro Umboni Wakuti Dziko Latsopano Liri Pafupi?

“Mtundu udzatsutsana ndi mtundu wina, ndi ufumu molimbana ndi ufumu: ndipo padzakhala njala, ndi miliri, ndi zivomezi, m’malo [osiyanasiyana].”​—Mateyu 24:7, King James Version.

PAMENE Nkhondo ya Dizko ya I inkamenyedwa, Nsanja ya Olonda, April 15, 1917, (Chingelezi) inagwira mawu awa ndi kulongosola kuti: “Tikuwona tsopano kukwaniritsidwa kwa pambali kwa ndemanga ya ulosi imeneyi, m’chakuti m’chenicheni mitundu yonse ya padziko lapansi ikulowetesedwa m’kukanthana kodzetsa imfa. Kuperekedwa komwe kulipo kwa chakudya kulikonse kukutsika ndipo mtengo wa kakhalidwe ukuwonjezereka.”

Tsopano, zaka 71 pambuyo pake, magazini imeneyi ikukokerabe chisamaliro cha aŵerengi ake ku ulosi umenewu. Odziŵa mbiri yakale atatu analemba ulosi umenewu kukhala monga mbali ya “chizindikiro” chopatsidwa ndi Yesu Kristu.​—Matthew 24:3, 7; Mark 13:4, 8; Luke 21:7, 10, 11.

Chiyambire 1914, mazana a mamiliyoni a miyoyo yathetsedwa ndi nkhondo, njala, miliri, ndi matsoka ena. The New Encyclopædia Britannica (1987) imandandalitsa “Zivomezi zazikulu za m’mbiri” 63 zowulika zaka 1,700 zapitazo. Pa unyinji wonse pamodziwu, 27, kapena 43 presenti, zachitika chiyambire 1914. Bukhu lakuti Terra Non Firma, lolembedwa ndi Maprofesa Gere ndi Shah, liri ndi ndandanda yokwaniritsa nyengo yaitali. Ponena za zivomezi zonse pamodzi “zapadera” m’ndandanda imeneyo, 54 peresenti zachitika chiyambire 1914.a Ngakhale kulingalira kuti zolembera kuchokera ku mazana a kumbuyo ziri zosakhwanira, sitingakhoze kuthaŵa malekezero akuti mu nthaŵi yathu mtundu wa anthu wayambukiridwa mokulira ndi zivomezi.

Chinachake ngakhale chowopsya kwenikweni chinakantha mitima ya anthu ndi kuphulika kwa mabomba a atomu pa mizinda ya ku Japan ya Hiroshima ndi Nagasaki. Mphamvu za nyukliya tsopano ziri ndi zida zochulukira kwambiri za kuwononga kokulira kumene munthu akuwopsyezedwa ndi kuthetsedwa. Monga mmene katswiri wa mbiri yakale Luka akupitirizira kulemba mu ulosi wa Yesu kuti: “Padzakhala zowopsya ndi zizindikiro zazikulu za kumwamba . . . ndi padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru . . . anthu akukomoka ndi mantha ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi.”​—Luka 21:11, 25, 26.

Ngakhale kui mphamvu zazikulu zadziko zingavomerezane kuchepetsa ziŵerengero za zida zina m’zosungira zida mwawo, kuvomerezana koteroko sikudzachepetsa mantha a munthu a upandu wachiwawa, kugwa kwa zachuma, ndi uchigaŵenga. “Chimene chikudetsa nkhaŵa anthu mokulira lerolino,” yalongosola tero nyuzipepala ya ku Africa, “kuli kusungika kwawo kwaumwini . . . Upandu wafikira kumlingo wofuntha . . . ; pali mantha omalamulira.” Inde, ndipo Yesu ananeneratu kuti “kuwonjezeka kwa kusayeruzika” kuli tsatanetsatane wina wolongosoka wa chizindikiro.​—Mateyu 24:12.

“Mbiri Yabwino”

Inu mudzapatsidwa mpumulo kumva, ngakhale ndi tero, kuti kukula kwa tsoka komwe kwangotchulidwa kumeneko kukunenedweratu kukhala kukutsagana ndi “mbiri yabwino [i]kulalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu.” (Mateyu 24:14) “Mbiri yabwino” iri yonena za Ufumu wa Mulungu. Kalekale, boma loposa la umunthu limenelo lasonkhanitsa mamiliyoni a nzika zokhulupirika. Ilo psachedwapa lidzalowerera m’zochitika za anthu ndi kukhutiritsa chifuno cha munthu kaamba ka dziko latsopano lolungama.​—Luka 21:29-32; 2 Petro 3:13.

Ambiri amaika pambali “mbiri yabwino” m’kusakhulupirira. Ena amanena kuti amakhulupirira iyo, koma amachita zochepera ponena za iyo. Ena amagwirirapo ntchito pa iyo kwa kanthaŵi, kenaka amayamba kukaikira. Kodi chiyambukiro chosatsimikizirika chimenechi chinanenedweratu kukhala mbali ya chizindikiro? Chofunika koposa, ndimotani mmene inu mwaumwini mungapindulire kuchokera ku chizindikiro chimenechi?

[Mawu a M’munsi]

a The World Book Encyclopedia (1987) imandandalitsa “Zivomezi Zazikulu” 37, kuchokera mu 526 C.E. kupita patsogolo. Pa ndandandayi, 65 peresenti yachitika chiyambire 1914.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena