Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Muyenda ndi Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2005 | November 1
    • 5. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ananena za kuwonjezera mkono pa moyo wa munthu?

      5 Baibulo nthawi zambiri limayerekezera moyo ndi ulendo. M’mavesi ena kuyerekezera kumeneku kumakhala kochita kuonekeratu, koma m’mavesi ena sizikhala choncho. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Ndani wa inu ndi kudera nkhawa angathe kuwonjezera pa msinkhu [kapena kuti pa moyo] wake mkono umodzi?” (Mateyu 6:27) M’vesili muli mawu ena omwe angazunguze munthu. N’chifukwa chiyani Yesu ananena za kuwonjezera “mkono umodzi,” womwe ndi muyeso wa mtunda, pa moyo wa munthu, womwe umayesedwa ndi nthawi?a N’zoonekeratu kuti Yesu apa anali kuyerekezera moyo ndi ulendo. Ndi fanizoli, Yesu anaphunzitsa kuti kuda nkhawa sikungakuthandizeni kuwonjezera ngakhale phazi limodzi pa ulendo wanu pa moyo. Ndiyeno, kodi tinene kuti palibe chimene tingachite kuti titalikitse mtunda wa ulendowu? Ayi, sichoncho. Zimenezi zikutifikitsa pa funso lathu lachiwiri loti, N’chifukwa chiyani tifunika kuyenda ndi Mulungu?

  • Kodi Muyenda ndi Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—2005 | November 1
    • a Mabaibulo ena amachotsa mawu oti “mkono” m’vesili n’kuikapo muyeso wa nthawi, monga “kamphindi” (The Emphatic Diaglott) kapena “mphindi imodzi” (A Translation in the Language of the People, la Charles B. Williams). Koma mawu amene anagwiritsidwa ntchito m’malemba oyambirira amatanthauza muyeso wa masentimita pafupifupi 45.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena