CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 11-12
Anaponya Zochuluka Kuposa Onse
Kodi mavesiwa akutithandiza bwanji kumvetsa mfundo zotsatirazi?
Yehova amayamikira zimene timachita
Tizitumikira Yehova ndi mtima wonse
Tisamayerekezere zomwe tikuchita ndi zimene anthu ena akuchita kapenanso ndi zimene tinkachita m’mbuyomu
Nawonso osauka akhoza kupereka ngakhale tindalama tochepa tomwe angakhale nato
Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene mwaphunzira m’nkhaniyi?