Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova Amayamikira Utumiki Wanu wa Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—1997 | October 15
    • 16. (a) Kodi Yesu anachidziŵa bwanji chopereka cha mkazi wamasiye waumphaŵi? (b) Kodi timakobiri ta mkazi wamasiyeyo tinali ndalama zingati?

      16 Masiku angapo zitatha izi, pa Nisani 11, Yesu anakhala tsiku lonse lathunthu m’kachisi, kumene anatsutsa ulamuliro wake ndi kuyankha mosapita mbali mafunso ovuta onena za misonkho, chiukiriro, ndi nkhani zina. Iye anadzudzula alembi ndi Afarisi chifukwa chakuti, mwa zina, ‘analusira nyumba za akazi amasiye.’ (Marko 12:40) Kenaka Yesu anakhala pansi, mwachionekere m’Bwalo la Akazi, kumene, monga mwa mwambo wachiyuda, kunali mabokosi a zopereka okwanira 13. Anakhala pamenepo kanthaŵi ndithu, kupenyerera anthu pamene anali kupereka zopereka zawo. Panabwera anthu olemera ambiri, mwinamwake ena okhala ndi maonekedwe odzilungamitsa, ngakhalenso mwina odzitukumula. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:2.) Yesu anasumika maso pa mkazi wina. Maso wamba mwinamwake sakanaona chilichonse chachilendo kwa mkaziyo kapena mphatso yake. Koma Yesu, amene anatha kudziŵa mitima ya ena, anadziŵa kuti iye anali “mkazi wamasiye waumphaŵi.” Anadziŵanso bwino lomwe kuchuluka kwa mphatso imene anapereka​—“tindalama tiŵiri tating’ono, tofa kakobiri kamodzi.”b​—Marko 12:41, 42.

  • Yehova Amayamikira Utumiki Wanu wa Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—1997 | October 15
    • b Kalikonse ka tindalama timeneti kanali ka lepton, ndalama yaing’ono koposa yachiyuda imene inali kugwiritsiridwa ntchito nthaŵi imeneyo. Ma lepton aŵiri anali ofanana ndi gawo limodzi mwa magawo 64 a malipiro a tsiku limodzi. Malinga nkunena kwa Mateyu 10:29, ndi kobiri la assarion (lofanana ndi ma lepton asanu ndi atatu), munthu anali kugula mpheta ziŵiri, zimene zinali zina mwa mbalame zotsika mtengo kwambiri zimene osauka anali kudya. Choncho, mkazi wamasiye ameneyu analidi wosauka, chifukwa chakuti anali ndi theka la ndalama yogulira mpheta imodzi, yosakwanira nkomwe kudyera chakudya.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena