Kodi Kupatsa Kwanu kuli Nsembe?
Kawonedwe Kolinganizika ka Zopereka
PAMBUYO pophunzitsa anthu zinthu zambiri m’kachisi, Yesu “anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo.” (Marko 12:41) Chomwe chinatsatira chinali mbiri yodziŵika bwino ya chopereka cha mkazi wamasiye. Koma nchifukwa ninji Yesu anakhala pamenepo ndi kuwona anthu akupereka zopereka zawo? Kodi iye sanauze ophunzira ake kuti iwo sayenera kulola dzanja lawo lamanja kudziŵa chimene dzanja lawo lamanzere likuchita pamene anapereka mphatso zawo za chifundo?—Mateyu 6:3.
Kumayambiriro, Yesu anali atatsutsa mwamphamvu atsogoleri a chipembedzo kaamba ka kugwiritsira ntchito njira zosayenera kulusira “nyumba za akazi amasiye.” Iye ananena kuti anthu achipembedzo amenewa “adzalandira kulanga koposa.” (Marko 12:40) Ndi cholinga chofuna kupereka phunziro, iye kenaka anatembenuzira chisamaliro chake ku zimene anthu anali kuchita pa mosungiramo zopereka. Lerolino pamene timamva zambiri ponena za ndalama zambiri zophatikizidwa mu magulu a tchalitchi, kugwiritsira ntchito kolakwa koteroko kwa ndalama, ndi njira ya moyo yosakaza ya awo oyang’anira, tingachite bwino kumvetsera mosamalitsa ku zimene Yesu akufuna kunena.—Chonde ŵerengani Marko 12:41-44.
Mosungira Zopereka
Nkhaniyo ikunena kuti Yesu “anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka.” Umu mwachiwonekere munali m’Bwalo la Akazi, kumene unyinji wa zosungiramo kapena mabokosi, anaikidwa m’mphepete mwa khoma kaamba ka anthu kugwetseramo zopereka zawo. Mwambo wa Chiyuda umatiuza ife kuti onse pamodzi anali mabokosi 13. Mu Chihebri anatchedwa malipenga, chifukwa anali ndi khomo laling’ono pamwamba pake mu mtundu wa belu la lipenga. Chanenedwa kuti ‘palibe wina aliyense analoŵa m’kachisi popanda kuikamo chinachake.’
Profesala wa chiFrench Edmond Stapfer, mu bukhu lake lakuti Palestine in the Time of Christ (1885), anapereka kulongosola kwatsatanetsatane kwa zosungiramo zopereka zimenezi. Mbiri yake ikutipatsa ife chidziŵitso china m’moyo wa chipembedzo wa anthu pa nthaŵiyo, makamaka ponena za zopereka zawo kulinga ku utumiki wa pa kachisi.
“Chosungiramo chirichonse chinali kaamba ka chinthu chosiyana, chosonyezedwa mwa mawu ozokotedwa m’chinenero cha Chihebri. Choyamba chinali ndi mawu ozokotedwa: Mashekeli Atsopano; kunena kuti, mashekeli oikidwa pambali kaamba ka zowonongedwa za chaka chimenecho. Lachiŵiri: Mashekeli Akale; kunena kuti, mashekeli operekedwa ku zowonongedwa za chaka chapita. Lachitatu: Maunda a nkhunda ndi njiŵa zazing’ono; ndalama zoikidwa mu chosungiramo chimenechi zinali mtengo woyenera kulipiridwa ndi awo amene anabwera kudzapereka maunda a nkhunda aŵiri kapena njiŵa zazing’ono ziŵiri, imodzi monga nsembe yopsereza, ndi ina monga nsembe yauchimo. Pamwamba pa chosungiramo chachinayi panalembedwa kuti: Nsembe zopsereza; ndalama izi zinakwaniritsa zowonongedwa za nsembe zopsereza zina. Lachisanu linali ndi malemba awa: Mtengo, ndipo zinasunga mphatso za okhulupirika kaamba ka kugula mtengo kaamba ka guwa la nsembe. Lachisanu ndi chimodzi: Chofukiza (ndalama zogulira chofukiza). Lachisanu ndi chiŵiri: Kaamba ka malo opatulika (ndalama za kumpando wachifumu wa Mulungu). Zosungiramo zisanu ndi chimodzi zotsala zinali ndi malemba awa: Zopereka zaufulu.”
Zisonyezero za zosungiramo ziŵiri zoyambirira zinali ndi chilozero ku shekeli la theka (madrachmas aŵiri mu ndalama za chiGrecian) msonkho wa munthu wamwamuna wachikulire aliyense unali kufunikira kulipiridwa mwa lamulo kaamba ka kukonza kachisi, mautumiki opangidwa kumeneko, ndi zopereka za tsiku ndi tsiku zoperekedwa m’malo mwa mtundu wonse. Msonkho umenewo unasonkhanitsidwa kaŵirikaŵiri m’malo a kwawoko ndipo kenaka kubweretsedwa ku kachisi.—Mateyu 17:24.
Anthuwo anafunidwanso ndi Lamulo kudzipangira nsembe zosiyanasiyana kaamba ka iwo eni. Zina zinali kaamba ka machimo opangidwa, zina kaamba ka zifukwa za mwambo, ndipo zinanso kokha kaamba ka kudzipereka kwawo ndi chiyamikiro. Mabokosi oikidwa chizindikiro cha “Maunda a nkhunda ndi njiŵa zazing’ono” ndi “Nsembe zopsereza” akakhala kaamba ka zifuno zoterozo. “Mu Lipenga III,” likutero bukhu la The Temple, Its Ministry and Services, “akazi amenewo omwe anafunikira kubweretsa maunda a nkhunda kaamba ka nsembe yopsereza ndi yochimwa anagwetsa zolingana nazo mu mkhalidwe wa ndalama, zimene zinatengedwa tsiku lirilonse ndipo chiŵerengero chofananacho cha maunda a nkhunda anaperekedwa.” Mwachiwonekere ichi ndi chimene makolo akhanda Yesu anachita.—Onani Luka 2:22-24; Levitiko 12:6-8.
Kenaka panali nsembe za mtengo ndi chonunkhiza zogwiritsiridwa ntchito pa guwa la nsembe ndi nsembe zopereka mwaufulu. Kachiŵirinso, molingana ndi Profesala Stapfer, “ngati wina aliyense anapereka ndalama kaamba ka mtengo kapena chonunkhiza, panali unyinji wochepera wokhazikitsidwa, ndiponso zochepera pa izi sizinali kuperekedwa. Chinali choyenera kupereka chifupifupi mtengo wa dzanja lodzala ndi chonunkhiza, kapena zipika ziŵiri za nkhuni za utali wa phazi limodzi mu litali ndipo chachikulu.”
Nchiyani chimene tikuphunzira kuchokera ku zonsezi? Chiri chowonekeratu kuti Aisrayeli anali ndi mathayo ambiri kulinga ku kusungilira chihema ndipo kenaka kachisi m’Yerusalemu, malo apakati a kulambira kowona. Nsembe ndi zopereka zinali mbali yaikulu ya kulambira kwawo. M’chenicheni, Lamulo linawalamulira kuti “asawoneke pamaso pa Yehova wopanda kanthu.” (Deuteronomo 16:16) Koma nchiyani chimene chinali kawonedwe kawo ka mathayo amenewo?
Kawonedwe Kosiyana
Mbiri ya Baibulo imasonyeza kuti anthu anali aufulu ndi oolowa manja mu nthaŵi za Mose ndi Davide ndipo pambuyo pake mkati mwa ulamuliro wa Yoasi ndi Yosiya. (Eksodo 36:3-7; 1 Mbiri 29:1-9; 2 Mbiri 24:4-14; 34:9, 10) Iwo anali achimwemwe kukhala ndi mbali m’kumanga nyumba ya Yehova ndi kuisunga iyo limodzinso ndi kupititsa patsogolo kulambira kowona. Lingaliro lawo linalongosoledwa bwino ndi mawu a Davide pamene iye ananena kuti: “ndinakondwera pamene ananena nane: ‘Tiyeni ku nyumba ya Yehova.’”—Masalmo 122:1.
Mzimu woolowa manja umenewu, ngakhale kuli tero, sunali kugawanidwa ndi onse. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti m’masiku a Malaki, ansembe anali kupereka kwa Yehova “zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala.” M’malo mwa kusangalala ndi mwaŵi wawo wa utumiki, iwo ananena kuti: “Tawonani! Ncholemetsa ichi!”—Malaki 1:13.
Mofananamo, mu nthaŵi ya Yesu ena anatenga mwaŵi wa mkhalidwewo kupititsa patsogolo zikondwerero za iwo eni. Osintha ndalama oipa pa kachisi, mwachitsanzo, sanali pamenepo kokha kuti asinthe ndalama. M’malomwake, iwo anakulitsa nsonga yakuti kokha mashekeli a Chihebri anali olandiridwa monga nsembe, ndipo awo onse amene anali ndi ndalama za Chiroma kapena Chigriki anayenera kuzisintha izo. Molingana ndi Alfred Edersheim, wolamulira pa mbiri yakale ya Chiyuda, “osunga ndalama anali kuloledwa kusintha meah ya siliva, kapena chifupifupi gawo limodzi mu zinayi la denar [kapena denarius, malipiro a tsiku limodzi a wantchito] pa shekeli ya theka iriyonse.” Ngati ichi chiri cholondola, sichiri chovuta kuwona kuti panali bizinesi laphindu chotani nanga ndiponso chifukwa chimene atsogoleri a chipembedzo anakhumudwitsidwa pamene Yesu anathamangitsa osintha ndalamawo.
“Mwa Kusowa Kwake”
Zonse za izi zimangogogomezera kokha fanizo la Yesu lonena za chopereka chochepa cha mkazi wamasiye, chimene mosakaikira anagwetsera pa limodzi la mabokosi oikidwa chizindikiro chakuti “Zopereka zaufulu.” Monga mkazi wamasiye, iye sanafunikire kupereka msonkho wa munthu, ndipo pokhala ndi ndalama zochepera, iye mwinamwake sanali wokhoza kufikira chifuno chochepera kaamba ka nsembe yopsereza kapena mtengo kapena nsembe ya chonunkhiza. Komabe, iye anafuna kuchita chinachake kusonyeza chikondi chake kaamba ka Yehova. Iye sanafune kusaŵerengedwa kapena kungochisiya kokha kwa awo amene ‘angakhoze.’ Yesu ananena kuti: “Koma iye anaponya mwa kusowa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.”—Marko 12:44.
Pali maphunziro ambiri opindulitsa amene tingaphunzire kuchokera ku mbiri imeneyi. Lowoneka kwambiri, mwinamwake, liri lakuti pamene kuli kwakuti tonsefe tiri ndi mwaŵi wa kupereka chirikizo ku kulambira kowona mwa zinthu zathu zakuthupi, chimenechi chiridi chapadera m’maso mwa Mulungu, sichiri kupereka kwathu kumene tingathe kuchita popanda icho, koma kupereka kwathu chomwe chiri chamtengo wapatali kwa ife. M’mawu ena, kodi timapereka chinachake chimene sitingachisowe kwenikweni? Kapena kodi kupereka kwathu kuli nsembe yeniyeni?
Kupititsa Patsogolo Kulambira Kowona Lerolino
Lerolino, Mboni za Yehova zimapititsa patsogolo kulambira kowona mwa kulalikira mwachangu “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu . . , m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu.” (Mateyu 24:14, NW) Kuti akwaniritse ntchito yadziko lonse imeneyi kumaphatikizapo osati kokha kuyesayesa kodzipereka, nthaŵi, ndi mphamvu komanso ndalama zochulukira. 1987 Yearbook of Jehovah’s Witnesses imasimba kuti “mkati mwa 1986, chiwonkhetso cha $23,545,801.70 chinawonongedwa m’kuchirikiza mwa ndalama . . . amishonale 2,762, apainiya apadera 13,351, ndi oyang’anira ndi akazi awo kaamba ka madera ndi zigawo za dziko 3,353.” Ichi chinali chiwonjezero ku “ndalama zochulukira zowonongedwa m’kugula, kumanga, ndi kukonzanso malo; m’kugulira zinthu mafakitare ndi maofesi pa malikulu ndi nthambi za Sosaite 93; ndi m’kupereka zosowa zakuthupi za antchito aufulu 8,920 omwe amatumikira mu mabanja a Beteli.”
‘Ndikuti kumene ndalama zimenezo zimachokera?’ liri funso limene limafunsidwa kaŵirikaŵiri. Mosiyana ndi matchalitchi a Dziko la Chipembedzo, Mboni za Yehova sizimasonkhanitsa kapena kutumiza maenivulupu opemphera zopereka. M’malomwake, mabokosi a zopereka—mofanana ndi zosungiramo zopereka za m’nthaŵi ya Baibulo—amaikidwa pa Nyumba zawo za Ufumu. Nthaŵi zina, mabokosi ena angaikidwe pambali kaamba ka zifuno zapadera, monga ngati kumangidwa kwa Nyumba za Ufumu kapena Malo Osonkhaniramo kapena kuthandiza amishonale kupezeka pa misonkhano ku maiko a kwawo. Zopereka zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Society pa 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201, kapena ku ofesi ya nthambi ya Sosaite m’dziko lanu, kaamba ka kupititsa patsogolo ntchito yolalikira ya dziko lonse.
Ndimotani mmene mumawonera njira zambiri ndi zosiyana zimene zopereka zimapangidwira? Kodi inu, mofanana ndi ena m’tsiku la Malaki, mumaziwona izo monga cholemetsa, mwinamwake kunena mu mtima mwanu: “Tawonani! Ncholemetsa ichi!”? Kapena inu, mofanana ndi “mkazi wamasiye wosauka,” mumaziwona izo monga mwaŵi wa kusonyezera changu chanu ndi kudera nkhaŵa kaamba ka kulambira kowona ndi chikhumbo chanu cha kulemekeza Yehova ndi zinthu zanu za mtengo wapatali? Musaiwale funso loyenerera: Kodi kupereka kwanu kuli nsembe?
“‘Mundiyese nako tsono,’ ati Yehova wa makamu, ‘ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.’” (Malaki 3:10) Kupita patsogolo kwauzimu ndi kufutukuka kwa dziko lonse pakati pa anthu a Yehova kumatsimikizira kuti Yehova akuchita kale chimenecho. Lolani kuti tipitirize kupereka kwa Yehova nsembe yomwe iridi nsembe yeniyeni.
[Bokosi patsamba 30]
MMENE ENA AMAPEREKERA KU NTCHITO YA UFUMU
◻ MPHATSO: Zopereka zaufulu za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York, 11201, kapena ku ofesi ya nthambi ya Sosaite ya kumaloko. Zinthu zonga ngati munda, limodzinso ndi zokometsera kapena zinthu zina za mtengo wapatali, zingaperekedwenso. Kalata yachidule yolongosola kuti zimenezo ziri zopereka zaufulu iyenera kutsagana ndi zopereka zimenezi.
◻ MAKONZEDWE A CHOPEREKA CHOKHALA NDI MALIRE: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti zisungidwe mwachikhulupiriro, ndi makonzedwe akuti ngati pali chifuno chaumwini, zidzabwezeredwa kwa mwini wake.
◻ INSUWARANSI: Watch Tower Society ingatchulidwe monga mwini wa lamulo wa insuwaransi ya moyo kapena makonzedwe a kuleka ntchito/ndi kupuma ntchito. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse oterowo.
◻ KUIKIZIDWA: Ndalama zosungidwa ku banki zingaikidwe mu kuikizidwa kaamba ka Sosaite. Ngati ichi chachitidwa, chonde dziŵitsani Sosaite. Ndalama, mapangano, ndi katundu zingaperekedwenso pansi pa makonzedwe a kupindulira mwiniwake mkati mwa moyo wake wonse. Njira imeneyi imathetsa ndalama zowonongedwa ndi kusatsimikizirika kwa pangano losatsimikiziridwa ndi maulamuliro, pamene mukutsimikizira kuti Sosaite idzalandira katunduyo m’chochitika cha imfa.
◻ PANGANO LA KUGAWA CHUMA: Katundu kapena ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kupyolera mwa pangano la kugawa katundu loikidwa mwalamulo. Kope liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ndi malangizo onena za nkhani zoterezi, lemberani ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201, kapena ku ofesi ya nthambi ya Sosaite ya kumaloko.