Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 3
  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Baibulo Ndi Buku Lochokera Kwa Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 3
Phunziro 3. Mipukutu yakale ya Baibulo ili patebulo.

PHUNZIRO 03

Kodi Muyenera Kukhulupirira Baibulo?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Baibulo limapereka malonjezo komanso malangizo ambirimbiri. N’kutheka kuti mumafuna kudziwa zimene limaphunzitsa, koma mwinanso mumachita mantha. Kodi ndi bwino kukhulupirira zimene buku lakale chonchi limalonjeza komanso malangizo amene limapereka? Nanga ndi nzeru kukhulupirira zimene Baibulo limanena zoti n’zotheka kukhala wosangalala panopa komanso m’tsogolo? Anthu ambiri amakhulupirira zimenezi. Tiyeni tione ngati inunso mungazikhulupirire.

1. Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona kapena n’zongopeka?

Baibulo limanena kuti uthenga wake ndi “mawu olondola a choonadi.” (Mlaliki 12:10) Limafotokoza nkhani zenizeni zokhudza anthu enieni. (Werengani Luka 1:3; 3:​1, 2.) Anthu ofufuza mbiri yakale komanso asayansi apeza umboni wakuti madeti, mayina a anthu, malo ndiponso nkhani za m’Baibulo ndi zolondola.

2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo silinathe ntchito?

Olemba Baibulo analemba mfundo zimene pa nthawiyo ambiri sankazidziwa. Mwachitsanzo, limatha kufotokoza molondola zinthu zokhudza sayansi. Pa nthawi imene ankalemba zimenezi anthu anali asanadziwe zoona zake pa nkhanizo. Koma asayansi apanopa atsimikizira kuti zimene Baibulo limanena ndi zolondola. Mawu a m’Baibulo “ndi odalirika . . . mpaka kalekale.”​​​—Salimo 111:​7, 8.

3. N’chifukwa chiyani tingakhulupirire zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo?

M’Baibulo muli maulosia a “zinthu zimene sizinachitike.” (Yesaya 46:10) Linaneneratu nkhani zina kutatsala zaka zambirimbiri kuti zichitike. Linaneneratunso ndendende mmene moyo ulili padzikoli masiku ano. M’mutuwu tikambirana maulosi ena a m’Baibulo. Mudabwa kwambiri kuona kukwaniritsidwa kwake.

FUFUZANI MOZAMA

Onani kugwirizana pakati pa sayansi yamakono ndi Baibulo, ndipo fufuzani maulosi ena a m’Baibulo ochititsa chidwi.

4. Baibulo ndi lolondola pa nkhani za sayansi

Kale anthu ankakhulupirira kuti dzikoli lakhazikika pachinthu chinachake. Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Dziko Silikhala Pachilichonse (1:13)

Ndiyeno onani zimene zinalembedwa m’buku la Yobu zaka 3,500 zapitazo. Werengani Yobu 26:​7, kenako mukambirane funso ili:

  • N’chifukwa chiyani mfundo yakuti dzikoli lili “m’malere” ndi yodabwitsa?

Cha m’ma 1800 m’pamene anthu anazindikira za kayendedwe ka madzi. Koma taonani zimene Baibulo linanena zaka pafupifupi 3,500 zapitazo. Werengani Yobu 36:27, 28, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani kufotokoza za kayendedwe ka madzi m’njira yosavuta chonchi n’kochititsa chidwi?

  • Kodi malemba amene mwawerengawa akuthandizani kukhulupirira Baibulo?

Baibulo limafotokoza za kayendedwe ka madzi. Miviyo ikusonyeza mmene madzi amayendera kuchoka padziko kupita kumwamba kenako n’kubwerera.

5. Baibulo linaneneratu nkhani zofunika kwambiri

Werengani Yesaya 44:27–45:2, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Baibulo linaneneratu za chiyani kutatsala zaka 200 kuti ufumu wa Babulo ugonjetsedwe?

Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Baibulo Linaneneratu Kuti Mzinda wa Babulo Udzagonjetsedwa (0:​58)

Olemba mbiri anatsimikizira kuti Mfumu Koresi ya Perisiya, inagonjetsa mzinda wa Babulo mu 539 B.C.E.b Iye ndi asilikali ake anapatutsa madzi a mumtsinje umene unkateteza mzindawo. Kenako anapeza mageti osatseka n’kulanda mzindawo popanda kumenya nkhondo. Panopa, padutsa zaka 2,500 chigonjetsereni Babulo, koma pamalo pamene panali mzindawu sipanamangidwe chilichonse mpaka pano. Taonani zimene Baibulo linaneneratu.

Werengani Yesaya 13:​19, 20, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi zimene zinachitika ku Babulo zimasonyeza bwanji kuti ulosiwu unakwaniritsidwa?

Malo amene panali mzinda wa Babulo ku Iraq

Zithunzi: Zithunzi zosonyeza zinthu zosiyanasiyana zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika ‘masiku otsiriza.’ 1. Nyumba zikuyaka. 2. Msilikali wanyamula mfuti ndipo akuombera. 3. Anthu ochita zionetsero akulimbana ndi apolisi okhazikitsa bata. 4. Anthu awiri akubera munthu musitolo. 5. Kasinja akuphwasula mzinda winawake. 6. Anthu osowa chakudya avala masiki ndipo aima pamzere wolandiritsa chakudya. 7. Nthaka yagumuka m’dera lalikulu. 8. Nyumba yagwa ndi chivomezi.

6. Baibulo linaneneratu zimene zikuchitika masiku ano

Baibulo limasonyeza kuti masiku ano, ndi “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Taonani zimene Baibulo linaneneratu zokhudza masiku ano.

Werengani Mateyu 24:6, 7, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi Baibulo linaneneratu kuti masiku otsiriza kudzachitika zotani?

Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:

  • Kodi Baibulo linaneneratu kuti anthu ambiri adzakhala otani?

  • Kodi ndi makhalidwe ati amene inuyo mwaonapo?

ZIMENE ENA AMANENA: “Baibulo ndi buku la nkhani zongopeka basi.”

  • Kodi inuyo muli ndi umboni wotani wotsimikizira kuti Baibulo ndi lodalirika?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Mbiri yakale, sayansi komanso maulosi zimasonyeza kuti Baibulo ndi lodalirika.

Kubwereza

  • Kodi zimene Baibulo limanena ndi zoona kapena n’zongopeka?

  • Kodi Baibulo ndi lolondola pa nkhani ziti zokhudza sayansi?

  • Kodi inuyo mumaona kuti Baibulo limalosera zam’tsogolo? N’chifukwa chiyani mukutero?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi Baibulo limatsutsana ndi zimene asayansi amanena?

“Kodi Sayansi Imagwirizana ndi Baibulo?” (Nkhani yapawebusaiti)

Kodi ndi zinthu ziti zomwe tiyenera kudziwa pa nkhani ya “masiku otsiriza”?

Maulosi 6 a M’Baibulo Amene Akukwaniritsidwa Masiku Ano” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2011)

Kodi ulosi wa m’Baibulo wonena za Ufumu wa Girisi unakwaniritsidwa bwanji?

’Mawu a Ulosi’ Amatilimbikitsa (5:22)

Kodi maulosi a m’Baibulo anathandiza bwanji munthu wina kusintha mmene ankaonera Baibulo?

“Ndinkaona Kuti Kulibe Mulungu” (Nsanja ya Olonda Na. 5 2017)

a Maulosi ena ndi okhudza uthenga wochokera kwa Mulungu wonena zimene zichitike m’tsogolo.

b B.C.E. imaimira “Before the Common Era,” kutanthauza nthawi yathu isanafike, ndipo C.E. imaimira “Common Era,” kutanthauza nthawi yathu ino.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena