Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 2/1 tsamba 8-13
  • Mphatso ya Yehova ya Mzimu Woyera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mphatso ya Yehova ya Mzimu Woyera
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphamvu ya Mzimu Woyera
  • Ntchito Zozizwitsa
  • Zolembedwa Zowuziridwa
  • Kudalira pa Mzimu Woyera
  • Mzimu wa Mulungu m’Zaka za Zana Loyamba
  • Pindulani ndi Mzimu Woyera wa Mulungu
  • ‘M’Dzina la Mzimu Woyera’
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Akhristu Oyambirira Ndipo Ukutsogoleranso Akhristu Masiku Ano
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kuuzindikira Mzimu Woyera
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Muziyenda mwa Mzimu Kuti Mukwaniritse Kudzipereka Kwanu
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 2/1 tsamba 8-13

Mphatso ya Yehova ya Mzimu Woyera

‘Koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye?’​—LUKA 11:13.

1, 2. (a) Kodi Yesu anapanga lonjezo lotani ponena za mzimu woyera, ndipo nchifukwa ninji liri lotonthoza kwenikweni? (b) Kodi mzimu woyera nchiyani?

PAMENE Yesu anali kulalikira mbiri yabwino m’Yudeya m’mphakasa ya chaka cha 32 C.E., anauza ophunzira ake ponena za kuwolowa manja kwa Yehova. Anagwiritsira ntchito mafanizo ogwira mtima ndiyeno nkupanga lonjezo labwino kwabasi, kumati: ‘Ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wakumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akumpempha iye?’​—Luka 11:13.

2 Ha, ngotonthoza chotani nanga mawuwo! Pamene tipirira chipolowe cha masiku otsiriza a dzikoli, kuyang’anizana ndi udani wa Satana ndi ziŵanda zake, ndi kulimbana ndi zikhoterero zathu zauchimo, kulidi kotonthoza kudziŵa kuti Mulungu adzatilimbitsa ndi mzimu wake. Ndithudi, kupirira mokhulupirika nkosatheka popanda chichirikizo chimenecho. Kodi munachirikizidwapo ndi mphamvu ya mzimu umenewu, umene uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu? Kodi mumadziŵa bwino mmene ingakuthandizireni kwambiri? Kodi mumaigwiritsira ntchito mokwanira?

Mphamvu ya Mzimu Woyera

3, 4. Ifotokozeni mwafanizo mphamvu ya mzimu woyera.

3 Choyamba tangoilingalirani mphamvu ya mzimu woyera. Tabwererani kumbuyo m’chaka cha 1954. Munali m’chaka chimenecho pamene bomba la hydrogen linaphulitsidwa pachilumba cha Bikini Atoll ku South Pacific. Posapita nthaŵi pambuyo pa kuphulitsidwa kwa bombalo, chilumba chokongola chonsecho chinakutidwa ndi chimoto chachikulu ndipo panakhala kuphulika kwa mphamvu yolingana ndi kuphulika kwa matani mamiliyoni 15 a msanganizo wa makemikolo wotchedwa TNT. Kodi mphamvu yosakaza yonseyo inachokera kuti? Inachititsidwa ndi kusanduka nyonga kwa kanusu kakang’ono ka uranium ndi hydrogen zimene zinapanga chithima cha bombalo. Komabe, bwanji ngati asayansi akanakhoza kutembenuzanso zimene anachita ku Bikini? Tayerekezerani kuti iwo anakhoza kutenga nyonga yamoto yonseyo ndi kuisandutsa kukhala miyeso yochepa ya uranium ndi hydrogen. Ha, chimenecho chikakhala chipambano chotani nanga! Komabe, Yehova anachita kanthu kena kofanana ndi zimenezo koma pamlingo waukulu kwambiri pamene ‘pachiyambi [iye] adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.’​—Genesis 1:1.

4 Yehova ali ndi mphamvu zopanda polekezera. (Yesaya 40:26) Polenga, iye ayenera kuti anagwiritsira ntchito ina ya nyongayo pamene anapanga zinthu zonse zimene zimapanga chilengedwe chonse. Kodi anagwiritsira ntchito chiyani m’ntchito imeneyi yakulenga? Mzimu woyera. Timaŵerenga kuti: ‘Zakumwamba zinalengedwa ndi mawu a Yehova; ndipo ndi [mzimu, NW] wa m’kamwa mwake khamu lawo lonse.’ (Salmo 33:6) Ndipo nkhani yakulenga ya m’Genesis imati: ‘Ndipo mzimu [woyera] wa Mulungu unalinkufungatira pamwamba pa madzi.’ (Genesis 1:2) Ha, ndimphamvu yaikulu chotani nanga imene mzimu woyera uli!

Ntchito Zozizwitsa

5. Kodi mzimu woyera umagwira ntchito m’njira zazikulu zotani?

5 Mzimu woyera ukugwirabe ntchito m’njira zazikulu kopambana. Umatsogoza ndi kuyendetsa gulu lakumwamba la Yehova. (Ezekieli 1:20, 21) Mofanana ndi nyonga yotulutsidwa ndi bomba la hydrogen, ukhoza kugwiritsiridwa ntchito m’njira yowononga kupereka chiweruzo pa adani a Yehova, koma wagwiranso ntchito m’njira zina zimene zimatisangalatsa ndi kuzizwa.​—Yesaya 11:15; 30:27, 28; 40:7, 8; 2 Atesalonika 2:8.

6. Kodi ndimotani mmene mzimu woyera unachirikizira Mose ndi ana a Israyeli m’zochita zawo ndi Igupto?

6 Mwachitsanzo, pafupifupi 1513 B.C.E., Yehova anatumiza Mose kukawonekera pamaso pa Farao wa Igupto kukapempha kumasulidwa kwa ana a Israyeli. Kwazaka 40 kumbuyoko, Mose anali mbusa ku Midyani, choncho chifukwa ninji Farao anayenera kumvera mbusa? Chifukwa chakuti Mose anadza m’dzina la Mulungu wowona yekha, Yehova. Kuti atsimikizire zimenezo, Yehova anampatsa mphamvu yakuchita zozizwitsa. Zimenezo zinali zochititsa chidwi kwambiri moti ngakhale ansembe a Igupto anakakamizika kuvomereza kuti: ‘Chala cha Mulungu ichi’!a (Eksodo 8:19) Yehova anadzetsa miliri khumi pa Igupto, womalizira umene unakakamiza Farao kulola anthu a Mulungu kuchoka m’Igupto. Pamene Farao ndi gulu lake lankhondo anawalondola mouma khosi, Aisrayeli anathaŵa pamene njira inatseguka mozizwitsa pa Nyanja Yofiira. Gulu lankhondo la Igupto linawalondola nilimira m’nyanjayo.​—Yesaya 63:11-14; Hagai 2:4, 5.

7. (a) Kodi ndizifukwa zotani zimene mzimu woyera unachitira zozizwitsa? (b) Ngakhale kuti zozizwitsa zochitidwa ndi mzimu woyera sizikuchitikanso, nchifukwa ninji cholembedwa chake m’Baibulo chiri chotonthoza?

7 Inde, Yehova anachita zozizwitsa zazikulu kupyolera mwa mzimu wake mmalo mwa Aisrayeli m’nthaŵi ya Mose, ndi panthaŵi zinanso. Kodi cholinga cha zozizwitsazo chinali chotani? Zinapititsa patsogolo zifuniro za Yehova, kudziŵikitsa dzina lake, ndi kusonyeza mphamvu yake. Ndipo nthaŵi zina, monga momwe zinaliri kwa Mose, zinatsimikiziritsa kuti munthuyo anali ndi chichirikizo cha Yehova. (Eksodo 4:1-9; 9:14-16) Komabe, zozizwitsa zochitidwa ndi mzimu woyera zakhala zakamodzikamodzi m’mbiri.b Mwachiwonekere, anthu ochuluka amene anakhala ndi moyo m’nthaŵi ya Baibulo sanawonepo chozizwitsa chirichonse, ndipo lerolino sizimachitikanso. Chikhalirechobe, pamene ifeyo lerolino tilimbana ndi mavuto amene angawonekere kukhala osalakika, kodi sikotonthoza kudziŵa kuti ngati timpempha Yehova ndi chikhulupiriro, adzatipatsa mzimu umodzimodziwo umene unachirikiza Mose pamaso pa Farao ndi kuwatsegulira Aisrayeli njira kuwoloka Nyanja Yofiira?​—Mateyu 17:20.

Zolembedwa Zowuziridwa

8. Kodi mzimu woyera unachita mbali yotani m’kuperekedwa kwa Malamulo Khumi?

8 Atalanditsidwa ku Igupto, Mose anatsogolera Aisrayeli ku phiri la Sinayi, kumene Yehova anapangana nawo pangano nawapatsa Chilamulo chake. Mbali yaikulu ya Chilamulocho choperekedwa kupyolera mwa Mose inali Malamulo Khumi, ndipo makope ake oyambirira anazokotedwa pamagome amiyala. Motani? Mwa mzimu woyera. Baibulo limati: ‘Ndipo atatha [Yehova] kulankhula ndi Mose, pa Phiri la Sinayi, anampatsa magome aŵiri a Mboni, magome amiyala, olembedwa ndi chala cha Mulungu.’​—Eksodo 31:18; 34:1.

9, 10. Kodi mzimu woyera unagwira ntchito motani m’kulembedwa kwa Malemba Achihebri, ndipo kodi zimenezi zikuwonekera motani m’mawu ogwiritsiridwa ntchito ndi ophunira a Yesu?

9 Kuwonjezera pa Malamulo Khumiwo, Yehova, kupyolera mwa mzimu wake woyera, anapatsa Israyeli mazana a malamulo ndi malangizo otsogoza miyoyo ya amuna ndi akazi okhulupirika. Ndipo zolembedwa zina zowuziridwa zinali kubwera mtsogolo. Zaka mazana ambiri nthaŵi ya Mose itapita, Alevi anapereka umboni m’pemphero lapoyera kwa Yehova kuti: ‘Munawalekerera [Aisrayeli] zaka zambiri, ndi kuwachitira umboni ndi mzimu wanu, mwa aneneri anu.’ (Nehemiya 9:5, 30) Maulosi ambiri onenedwa ndi aneneriwo analembedwa. Ndiponso, mzimu woyera unasonkhezera amuna okhulupirika kulemba mbiri zopatulika ndi nyimbo zachitamando zochokera mumtima.

10 Paulo anali kunena za zolembedwa zonsezi pamene anati: ‘Lemba lirilonse adaliwuzira Mulungu.’ (2 Timoteo 3:16; 2 Samueli 23:2; 2 Petro 1:20, 21) Ndithudi, pogwira mawu malemba ameneŵa, ophunzira a Yesu a m’zaka za zana loyamba anagwiritsira ntchito mwakaŵirikaŵiri mawu onga ‘mzimu woyera unayamba kunena mwa m’kamwa mwa Davide,’ ‘mzimu woyera unalankhula kokoma mwa Yesaya,’ kapena kungoti ‘monga unena mzimu woyera.’ (Machitidwe 1:16; 4:25; 28:25, 26; Ahebri 3:7) Ha, ndidalitso lotani nanga kuti mzimu woyera umodzimodziwo umene unasonkhezera kulembedwa kwa Malemba Opatulika wawasungitsa Malembawo kotero kuti atitsogoze ndi kutitonthoza lerolino!​—1 Petro 1:25.

Kudalira pa Mzimu Woyera

11. Kodi ndintchito iti ya mzimu woyera imene inawoneka pomanga chihema cholambirira?

11 Pamene Aisrayeli anamanga msasa munsi mwa phiri la Sinayi, Yehova anawalamula kumanga chihema cholambirira monga malo apakati a kulambira kowona. Kodi ndimotani mmene iwo akachitira zimenezi? ‘Mose anati kwa ana a Israyeli, Tawonani, Yehova anaitana, ndi kumtchula dzina lake, Bezaleli, mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda; ndipo anamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziŵitso, za m’ntchito zirizonse.’ (Eksodo 35:30, 31) Mzimu woyera unachirikiza luso lachibadwa lirilonse limene Bezaleli anali nalo, ndipo anakhoza kuyang’anira mwachipambano kumangidwa kwa chihema chozizwitsacho.

12. Kodi ndimotani mmene mzimu unalimbitsira anthu m’njira zodabwitsa pambuyo pa Mose?

12 Panthaŵi ina mtsogolo mwake, mzimu wa Yehova unagwira ntchito pa Samsoni, kumpatsa mphamvu zoposa zaumunthu zimene zinamkhozetsa kulanditsa Aisrayeli kwa Afilisiti. (Oweruza 14:5-7, 9; 15:14-16; 16:28-30) Panthaŵi inanso pambuyo pake, Solomo anapatsidwa nzeru yapadera monga mfumu ya anthu osankhidwa a Mulungu. (2 Mbiri 1:12, 13) Pansi pa ulamuliro wake, Israyeli anakhupuka kuposa ndi kalelonse, ndipo mkhalidwe wake wachimwemwe unakhala chitsanzo cha madalitso amene anthu a Mulungu adzakhala nawo pansi pa Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Kristu Yesu, Solomo Wamkulu.​—1 Mafumu 4:20, 25, 29-34; Yesaya 2:3, 4; 11:1, 2; Mateyu 12:42.

13. Kodi cholembedwa cha mmene mzimu unalimbitsira Bezaleli, Samsoni, ndi Solomo chimatilimbikitsa motani lerolino?

13 Ha, ndidalitso lotani nanga kuti Yehova amapereka mzimu umodzimodziwo kwa ife! Pamene tidzimva kukhala wosakhoza kukwaniritsa gawo lathu kapena kuchita ntchito yolalikira, tingampemphe Yehova kuti atipatse mzimu umodzimodziwo umene anapatsa Bezaleli. Pamene tidwala kapena kupirira chizunzo, mzimu umodzimodziwo umene unapatsa Samsoni mphamvu yodabwitsa udzatilimbitsa nafenso​—ngakhale kuti simozizwitsa. Ndipo pamene tiyang’anizana ndi mavuto aakulu kapena pamene tifunikira kupanga zosankha zazikulu, tikhoza kumpempha Yehova, amene anapatsa Solomo nzeru yodabwitsa, kuti atithandize kuchita mwanzeru. Ndiyeno, mofanana ndi Paulo, tidzanena kuti: ‘Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.’ (Afilipi 4:13) Ndipo lonjezo lotsatira la Yakobo lidzagwira ntchito kwa ife: ‘Wina wa inu ikamsoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.’​—Yakobo 1:5.

14. Kodi ndani amene, m’nthaŵi yamakedzana ndi lerolino, achirikizidwa ndi mzimu woyera?

14 Mzimu wa Yehova unalinso pa Mose m’ntchito yake yoweruza mtunduwo. Pamene ena anaikidwa kuthandiza Mose, Yehova anati: ‘Ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu aŵa, kuti usasenze wekha.’ (Numeri 11:17) Chotero, amuna amenewo sanachite zinthu ndi nyonga yawoyawo. Mzimu woyera unawachirikiza. Timaŵerenga kuti m’zochitika za pambuyo pake, mzimu wa Yehova unali pa anthu ena. (Oweruza 3:10, 11; 11:29) Pamene Samueli anadzoza Davide monga mfumu yamtsogolo ya Israyeli, cholembedwacho chimati: ‘Samueli anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli.’ (1 Samueli 16:13) Awo amene ali ndi mathayo olemera lerolino​—abanja, ampingo, kapena agulu lonse​—angatonthozedwe kudziŵa kuti mzimu wa Mulungu umachirikizabe atumiki ake pamene akusamalira mathayo awo.

15. Kodi ndim’njira zotani zimene mzimu woyera walimbitsira gulu la Yehova (a) m’nthaŵi ya Hagai ndi Zekariya? ndi (b) lerolino?

15 Pafupifupi zaka chikwi pambuyo pa nthaŵi ya Mose, okhulupirika a ana a Israyeli anabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo ndi ntchito yokamanganso kachisi. (Ezara 1:1-4; Yeremiya 25:12; 29:14) Komabe, panabuka zopinga zazikulu ndipo iwo analefulidwa kwazaka zambiri. Pomalizira pake, Yehova anautsa aneneriwo Hagai ndi Zekariya kuti alimbikitse Ayuda kusadalira pa mphamvu yawoyawo. Koma kodi ntchitoyo ikachitidwa motani? ‘Ndi khamu lankhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.’ (Zekariya 4:6) Ndipo mochirikizidwa ndi mzimu wa Mulungu, kachisiyo anamangidwa. Anthu a Mulungu lerolino achita zambiri m’njira yofananayo. Kulalikidwa kwa mbiri yabwino kwafutukukira padziko lonse lapansi. Anthu mamiliyoni akuphunzitsidwa chowonadi ndi chilungamo. Misonkhano ikulinganizidwa. Nyumba Zaufumu ndi maofesi anthambi zikumangidwa. Zochuluka za zimenezi zachitidwa moyang’anizana ndi chitsutso chowopsa. Koma Mboni za Yehova sizinalefulidwe, podziŵa kuti kalikonse kamene zakwaniritsa kachitika, osati ndi khamu lankhondo, kapena ngakhale ndi mphamvu yaumunthu, koma ndi mzimu wa Mulungu.

Mzimu wa Mulungu m’Zaka za Zana Loyamba

16. Kodi atumiki a Mulungu a m’nyengo ya Chikristu chisanakhale anadziŵanji ponena za kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu?

16 Monga momwe tawonera, atumiki a Mulungu a m’nyengo ya Chikristu chisanakhale anali kuizindikira bwino lomwe mphamvu ya mzimu wa Mulungu. Anaidalira kuti iwathandize kukwaniritsa mathayo olemera ndi kuchita chifuniro cha Mulungu. Anadziŵanso kuti Chilamulo ndi zolembedwa zopatulika zinali zowuziridwa, zolembedwa pansi pa chisonkhezero cha mzimu wa Yehova, ndipo motero zinali ‘Mawu a Mulungu.’ (Salmo 119:105) Komano, bwanji ponena za nyengo ya Chikristu?

17, 18. Kodi ndizisonyezero zozizwitsa zotani za mzimu zimene zinachitika m’nyengo ya Chikristu, ndipo kodi zinali ndi cholinga chotani?

17 Zaka za zana loyamba la Nyengo Yathu ino nazonso zinali ndi ntchito zodabwitsa za mzimu wa Mulungu. Panali kulosera kowuziridwa ndi mzimu. (1 Akorinto 14:1, 3) Kukwaniritsa lonjezo la Yesu lakuti mzimu woyera ukakumbutsa ophunzira ake zinthu zonse zimene iye ananena ndi kuwaphunzitsa mbali zowonjezereka za chowonadi, mabuku angapo analembedwa mosonkhezeredwa ndi mzimu woyera. (Yohane 14:26; 15:26, 27; 16:12, 13) Ndipo panali zozizwitsa, zomwe zidzafotokozedwa mokwanira m’nkhani yathu yotsatira. Ndithudi, zaka za zana loyamba zinafika ndi chozizwitsa chachikulu. Pafupifupi chaka cha 2 B.C.E., mwana wapadera akabadwa, ndipo monga chizindikiro, amayi ŵake wachichepere anayenera kukhala namwali. Kodi zimenezo zikatheka motani? Mwa mzimu woyera. Cholembedwacho chimati: ‘Kubadwa kwake kwa Yesu Kristu kunali kotere: Amayi ŵake Mariya anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanakomane iwowo, anapezedwa iwo ali ndi pakati mwa mzimu woyera.’​—Mateyu 1:18; Luka 1:35, 36.

18 Pamene Yesu anakula, anatulutsa ziŵanda, kuchiritsa odwala, ngakhale kuukitsa akufa ndi mphamvu ya mzimu woyera. Ena a otsatira ake nawonso anachita zozizwitsa ndi ntchito zazikulu. Maluso apadera ameneŵa anali mphatso za mzimu. Kodi cholinga chawo chinali chotani? Monga momwe zozizwitsa zoyambirira zinachitira, zinapititsa patsogolo chifuno cha Mulungu ndi kuwonetsa mphamvu yake. Ndiponso, zinatsimikiziritsa kuwona kwa mawu a Yesu akuti anatumidwa ndi Mulungu; ndipo pambuyo pake, zinatsimikiziritsa kuti mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba unali mtundu wosankhika wa Mulungu.​—Mateyu 11:2-6; Yohane 16:8; Machitidwe 2:22; 1 Akorinto 12:4-11; Ahebri 2:4; 1 Petro 2:9.

19. Kodi chikhulupiriro chathu chimalimbitsidwa motani ndi cholembedwa cha Baibulo chofotokoza zozizwitsa za Yesu ndi atumwi ake?

19 Komabe, mtumwi Paulo ananena kuti zisonyezero zotero za mzimu zinali za nthaŵi ya ubwana wa mpingo ndipo zikapita, chotero ifeyo lerolino sitimawona zozizwitsa zotero zochitidwa ndi mzimu woyera. (1 Akorinto 13:8-11) Chikhalirechobe, zozizwitsa zochitidwa ndi Yesu ndi atumwi ake nzofunika koposa pakukhala mbiri basi. Zimalimbitsa chikhulupiriro chathu m’lonjezo la Mulungu lakuti utenda ndi imfa sizidzakhalako muulamuliro wa Yesu m’dziko latsopano.​—Yesaya 25:6-8; 33:24; 65:20-24.

Pindulani ndi Mzimu Woyera wa Mulungu

20, 21. Kodi tingapindule motani ndi kukhalapo kwa mzimu woyera?

20 Ha, mzimu umenewu uli nyonga yamphamvu chotani nanga! Koma kodi Akristu lerolino angapindule nawo motani? Choyamba, Yesu anati tiyenera kuupempherera, chotero bwanji osangochita zimenezo? Pempherani kwa Yehova kuti akupatseni mphatso yodabwitsa imeneyi osati kokha m’nthaŵi ya kupsinjika koma nthaŵi iriyonse. Ndiponso, ŵerengani Baibulo kotero kuti mzimu woyera ukhoze kulankhula nanu. (Yerekezerani ndi Ahebri 3:7.) Sinkhasinkhani pazimene muŵerenga ndipo zigwiritsireni ntchito kotero kuti mzimu woyera ukhale chisonkhezero m’moyo wanu. (Salmo 1:1-3) Ndiponso, yanjanani​—mwachindunji, mumpingo, ndi pamisonkhano​—ndi ena amene amadalira pa mzimu wa Mulungu. Ndimolemeretsa chotani nanga mmene mzimu woyera umachirikizira amene amadalitsa Mulungu wawo “m’masonkhano”!​—Salmo 68:26.

21 Kodi Yehova saali Mulungu wowoloŵa manja? Iye amati tingofunikira kumpempha mzimu woyera ndipo adzaupatsa kwa ife. Nkupusa chotani nanga kudalira pa nzeru ndi mphamvu zathu pamene chithandizo chachikulu motero chiripo! Komabe, pali zinthu zina zochita ndi mzimu wa Mulungu zimene zimatikhudza monga Akristu, ndipo zimenezi zidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Kaŵirikaŵiri mawuwo akuti ‘chala cha Mulungu’ amaloza ku mzimu woyera.​—Yerekezerani ndi Luka 11:20 ndi Mateyu 12:28.

b Zozizwitsa zambiri zolembedwa m’Baibulo zinachitika m’nthaŵi ya Mose ndi Yoswa, Eliya ndi Elisa, ndi Yesu ndi atumwi ake.

Kodi Mungayankhe Mafunso Otsatiraŵa?

◻ Kodi ndimotani mmene Yehova analengera zinthu zonse m’chilengedwe chonse?

◻ Kodi ndinjira zina zotani zimene mzimu woyera unagwirira ntchito m’nthaŵi za Chikristu chisanakhale?

◻ Kodi kumatitonthoza motani lerolino kudziŵa zimene mzimu woyera unachita m’nthaŵi yamakedzana?

◻ Kodi tingapindule motani ndi kukhalapo kwa mzimu woyera?

[Chithunzi patsamba 10]

Mzimu umene unapatsa Samsoni mphamvu zoposa zaumunthu ungatipatse mphamvu ya zinthu zonse

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena