Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndinu “Wolemera kwa Mulungu”?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Munthu Amene Anaiwala Mulungu
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kodi Chofunika Kwambiri Ndi Chiyani?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Mzimu wa Munthu Sufa?
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

◼ M’fanizo la Yesu la munthu wachuma yemwe sanali wolemera kulinga kwa Mulungu, kodi ndi ndani amene anali “iwo” amene anafuna moyo wa munthuyo?

Yesu sanali kutanthauza gulu liri lonse la anthu kapena angelo. Mu Luka 12:20, (NW) iye anagwiritsira ntchito liwu lotsimikizirika “iwo” kokha monga njira ya kulongosolera chomwe chinayenera kuchitika kwa munthuyo.

Fanizo limeneli likupezeka pa Luka 12:16-21. Munthu wachuma m’fanizolo sanali wokhutiritsidwa ndi zinthu zake za kuthupi zokwanira. lye anapitirizabe kuumilira pa bizinesi yake kotero kuti awonjezere chuma chake. Yesu anamaliza: “Koma Mulungu anati kwa [munthu wachuma], ‘wopusa iwe, usiku uno [iwo kuufuna moyo wako kuchokera kwa iye, NW]. Ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?’ Anatero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.”

Matembenuzidwe ena amagwiritsira ntchito pasivi, monga ngati: “Usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako.” (New American Standard Bible) “Usiku womwe uno funika kudzapangidwa kaamba ka moyo wako.” (The Jerusalem Bible) “Usiku womwe uno moyo wako ukufunidwa.” (The Twentieth Century New Testament) “Usiku uno moyo wako udzaitanidwa.” (Byington) Komabe, Chihebri (mu chimene Yesu analankhula) ndi Chigriki (mu chimene Luka analemba) chimagwiritsira ntchito mkhalidwe wa munthu wachitatu osatsimikizirika. Lemba la Chigriki pa Luka 12:20 kugwiritsira ntchito tanthauzo lenileni la mawu ilo limati “ku ichi usiku moyo wako iwo akuufunsa kuchokera kwa iwe.” Verebu liri mu pulula ya munthu wa chitatu. Mwakutero, m’malo mwakulisintha ilo kupita ku pasivi formu (monga ngati mu chitsanzo chapamwambapo, ), New World Translation ndi ena amagwiritsira ntchito katchulidwe mongangati “iwo akufuna.”

Tidzachita bwino, angakhale kuli tero, kusalola kagwiritsidwe ka ntchito ka galamala kubisa chenjezo lowonekera la Yesu ponena za kukonda zinthu zakuthupi. lye sanali kunena mwachindunji ponena za ndi motani mmene munthu wachuma adzafera. Nsonga inali yakuti mwanjira ina yake munthuyo anayenera kutaya moyo wake, usiku umenewo. Koma kodi ndi motani mmene iye anaimira ndi Mulungu? Aliyense wa ife angakhale womwerekera mu kupititsa patsogolo mkhalidwe wathu wakuthupi ndipo mofananamo kuphonya kukhala wachuma kulinga kwa Mulungu. Dziko la malonda limapereka mzimu wa “zowonjezereka.” Angakhale anthu amene makampani awo amapanga mapindu okulira kuchokera ku zomwe amagulitsa mu mamiliyoni amadola, mapaundi, ma marks, ndi zina zotero, angayesedwe kufunafuna zowonjezereka​—ogwira ntchito ambiri, zogulitsa zambiri, mapindu ambiri, zinthu zosangalatsa zosafunika kwenikweni zowonjezeka, kukhala ndi zochuluka mu banki. Funso la Yesu liri logwira ntchito lerolino monga momwe linaliri pamene iye analifunsa poyamba: “Ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?”​—Luka 12:20.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena