Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Khalani Okonzekera!
PAMBUYO pa kuchenjeza khamu ponena za kusirira, ndi kuchenjeza ophunzira ake ponena za kupereka chisamaliro chosayenera ku zinthu zakuthupi, Yesu akulimbikitsa kuti: “Musawopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.” Iye chotero akuvumbula kuti kokha chiŵerengero chochepera (pambuyo pake chozindikiritsidwa monga 144,000) chidzakhala mu Ufumu wakumwamba. Ochulukira a amene adzalandira moyo wosatha adzakhala nzika za pa dziko lapansi za Ufumuwo.
Ndi mphatso yodabwitsa chotani nanga, “ufumu”! Akumalongosola kuyankha koyenera kumene ophunzirawo ayenera kukhala nako pa kulandira iwo, Yesu akulimbikitsa iwo kuti: “Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo.” Inde, iwo afunikira kugwiritsira ntchito chuma chawo kupindulitsa ena mwauzimu ndipo chotero kumangirira “chuma chosatha m’mwamba.”
Yesu chotsatira akulangiza ophunzira ake kukhala okonzekera kaamba ka kubwera kwake. Iye akunena kuti: “Khalani odzimangira m’chuwuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka; ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wawo, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo. Odala akapolowo amene mbuye wawo, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndi inu, kuti Iye adzadzimangira m’chuwuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika nadzawatumikira.”
M’fanizoli, kukonzekera kwa atumiki pa kubwera kwa mbuye wawo kwasonyezedwa ndi kukokera kwawo m’mwamba zovala zawo zazitali ndi kuzimanga zimenezi m’chuwuno mwawo; ndipo akupitirizabe kusamalira kaamba ka mathayo awo kufikira usiku m’kuwala kwa nyali zoikidwa mafuta bwino. Yesu akulongosola kuti: ‘Ngati mbuyeyu akadza ulonda wachiŵiri [kuyambira chifupifupi ora lachisanu ndi chinayi madzulo kufika pakati pa usiku], kapena wachitatu [pakati pa usiku kufika ku chifupifupi ora lachitatu m’mawa], nakawapeza atero, odala amenewa!’
Mbuyeyo amapatsa mphoto akapolo ake m’njira yosakhala ya nthaŵi zonse. Iye adzawakhalitsa pansi kudya ndi kuyamba kuwatumikira iwo. Iye awachita iwo, osati monga akapolo, koma monga mabwenzi okhulupirika. Ndi mphoto yabwino chotani nanga kaamba ka kupitirizabe kugwira ntchito kwawo kaamba ka mbuye wawo kupyola usiku wonse pamene akuyembekezera kaamba ka kubwerera kwake! Yesu akutsiriza kuti: “Khalani okonzeka, inunso chifukwa nthaŵi imene simulingalira, Mwana wa muthu akudza.”
Petro tsopano akufunsa kuti: “Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife kapena kwa onse?”
M’malo moyankha mwachindunji, Yesu apereka fanizo lina. “Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika,” iye akufunsa tero, “amene mbuye wake adzamuika kapitawo wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lawo pa ntahŵi yake? Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika adzampeza alikuchita chotero! Ndinena ndi inu zowona, kuti Adzamuika iye kapitawo wa pa zonse ali nazo.”
“Mbuyeyo” mwachiwonekere ali Yesu Kristu. “Mdindoyo” amachitira chithunzi “kagulu ka nkhosa” ka ophunzira monga bungwe lonse, ndipo “a pa banja” amalozera ku gulu limodzimodzili la 144,000 omwe amalandira Ufumu wa kumwamba, koma limagogomezera ntchito yawo monga aliyense payekha. “Zonse ali nazo” zimene mdindo wokhulupirika waikidwa kusamalira kaamba ka izo ziri zikondwerero za ufumu za ambuye pa dziko lapansi, zomwe zimaphatikizapo nzika za padziko lapansi za Ufumuwo.
Akumapitiriza ndi fanizolo, Yesu akulozera ku kuthekera kwakuti siziwalo zonse za mdindoyo, kpaena gulu la kapolo, zomwe zidzakhala zokhulupirika, akumalongosola kuti: “Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, ‘Mbuye wanga azengereza kudza,’ ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi, ndi kudya ndi kumwa ndi kuledzera, mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera . . . ,adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.”
Yesu akupitirizabe kudziŵitsa kuti kudza kwake kwadzetsa nthaŵi ya moto kaamba ka Ayuda, popeza kuti ena amalandira ndipo ena amakana ziphunzitso zake. Mkati mwa zaka zitatu kumayambiriro, iye anabatizidwa m’madzi, koma tsopano ubatizo wake wa imfa ukuyandikira kwambiri kumapeto ake, ndipo monga mmene iye akunenera: “ndikanikizidwa ine kufikira ukatsirizidwa!”
Pambuyo pa kulunjikitsa mawu amenewa kwa ophuzira ake, Yesu kachiŵirinso akulankhula kwa khamu. Iye akuchitira chisoni kukana kwawo kowuma mutu kwa kulandira umboni womvekera bwino wa chizindikiritso chake ndi kukhala kwake kwapadera. “Pamene pali ponse muwona mtambo wokwera kumadzulo,” iye akuwona tero, “pomwepo munena, kuti ‘ikudza mvula,’ ndipo itero. Ndipo pamene mphepo ya kum’mwera iwomba, munena kuti, ‘Kudzakhala kotenthatu,’ ndipo kuterodi. Onyenga inu, mudziŵa kuzindikira nkhope yake lya dziko lapansi ndi ya thambo, koma simudziŵa bwanji kuzindikira nyengo ino?” Luka 12:32-59.
◆ Ndi angati omwe amapanga “kagulu ka nkhosa,” ndipo nchiyani chimene iwo akulandira?
◆ Ndimotani mmene Yesu akugogomezerera kufunika kwa atumiki ake kukhala okonzekera?
◆ M’fanizo la Yesu, ndani yemwe ali “mbuye,” “mdindo,” “a pa banja,” ndi “zonse ali nazo”?