Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 3/1 tsamba 23
  • ‘Kulandira Chidziŵitso cha Mulungu ndi Yesu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kulandira Chidziŵitso cha Mulungu ndi Yesu’
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • “New World Translation”—Yaukatswiri ndi Yowona
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chochitika Chosaiŵalika kwa Okonda Mawu a Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Muyenera Kuphunzira Chiheberi ndi Chigiriki?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Chipangano Chakale Chiri Chachikale?
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 3/1 tsamba 23

‘Kulandira Chidziŵitso cha Mulungu ndi Yesu’

“IZI zitanthauza moyo wosatha, kulandira kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu wowona yekha, ndi cha iye amene munamtuma, Yesu Kristu.” (Yohane 17:3, NW) Anatero Yesu m’pemphero kwa Atate wake wakumwamba, ndipo mwanjirayi anasonyeza chiyeneretso chapasadakhale chopezera moyo wamuyaya. Komabe, nchifukwa ninji New World Translation imamasulira vesili kuti “kulandira chidziŵitso cha . . . Mulungu” mmalo mwa “kudziŵa . . . Mulungu,” mmene matembenuzidwe a Mabaibulo ambiri amanenera?​—Onaninso mawu amtsinde a Yohane 17:3, New World Translation​—With References.

Liwu Lachigiriki panopa lotembenuzidwa ‘kulandira chidziŵitso’ kapena “kudziŵa” ndimtundu wa mneni gi·noʹsko. Ndipo kumasulira kwa New World Translation kuli ncholinga chomveketsa monga momwe kungathekere tanthauzo lenileni la liwulo. Tanthauzo lalikulu la gi·noʹsko ndilo “kudziŵa,” koma liwu Lachigiriki liri ndi matanthauzo osiyanasiyana. Onani malongosoledwe otsatiraŵa:

“GINŌSKŌ (γινώσκω) limatanthauza kulandira chidziŵitso, kudziŵa, kuzindikira, kumvetsetsa, kapena kumva kotheratu.” (Expository Dictionary of New Testament Words, la W. E. Vine) Chotero, kumasulira gi·noʹsko kukhala ‘kulandira chidziŵitso’ sikuli ‘kusintha Baibulo,’ monga momwe anenera osuliza New World Translation. Pokambitsirana matanthauzo osiyanasiyana amene liwulo lingapereke, wolemba dikishonale James Hope Moulton akunena kuti: “Liwu losonyeza kachitidwe katsopanoli, γινώσκειν, nlotenga nthaŵi, ‘kukhala ukulandira chidziŵitso.’”​—A Grammar of New Testament Greek.

A Grammatical Analysis of the Greek New Testament imalongosola liwu la gi·noʹsko mmene limawonekera pa Yohane 17:3 monga “lotanthauza kachitidwe kopitiriza.” Ndemanga yowonjezereka pa liwu Lachigiriki limeneli ipezeka mu Word Studies in the New Testament, yolembedwa ndi Marvin R. Vincent. Iyo imati: “Moyo wamuyaya umapezeka m’chidziŵitso, kapena kulondola chidziŵitso, popeza kuti liwu lonena kachitidwe katsopanoli limasonyeza kupitiriza, lingaliro la kupita patsogolo.” (Kanyenye ngwake.) A. T. Robertson’s Word Pictures in the New Testament ikupereka lingaliro lakumasulira liwulo kukhala “ayenera kupitirizabe kudziŵa.”

Chifukwa chake, m’Chigiriki choyambirira, mawu a Yesu pa Yohane 17:3 amapereka lingaliro la kuyesayesa kopitirizabe kwakudziŵa Mulungu wowona ndi Mwana wake, Yesu Kristu, ndipo zimenezi zikuwonekera bwino m’kumasulira kwa New World Translation. Timachipeza chidziŵitso chimenechi mwakuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi mwakumvera miyezo yake m’moyo wathu. (Yerekezerani ndi Hoseya 4:1, 2; 8:2; 2 Timoteo 3:16, 17.) Kodi ndimphotho yabwino yotani imene ikuyembekezera awo amene amaphunzira umunthu wa Mulungu ndi wa Mwana wake ndiyeno nkukalimira kuwatsanzira? Moyo wosatha!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena