Kusonyeza Chiyamikiro Kaamba ka Zisonyezero Ziŵiri Zazikulu Kwambiri za Chikondi
“Tikonda ife, chifukwa anayamba iye kutikonda.”—1 YOHANE 4:19.
1. Kodi ndi chitsanzo chotani chimene Yesu anakhazikitsa kaamba ka ife?
NDIMOTANI mmene tingasonyezere chiyamikiro choposa kaamba ka chikondi chachikulu chomwe Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anasonyeza kulinga kwa ife? Njira yoyambirira iri mwa kutsanzira Yesu, amene mosatopa anachitira umboni ku dzina la Atate wake ndi Ufumu. (1 Petro 2:21) Iye anachita tero m’nyumba, mmasunagoge, m’kachisi, mphepete mwa mapiri, ndi mphepete mwa nyanja. Tiyeni tilingalire njira zisanu ndi zinai zomwe zingakhale zotseguka kwa ife zomwe ziri zowonekera.
Ntchito ya ku Nyumba ndi Nyumba
2. Kodi ndimotani mmene mungapiririre mu ntchito ya ku nyumba ndi nyumba
2 Njira yoyamba, ndipo mwina mwake yodziwika kwambiri, mu imene tingasonyezere chikondi chathu ndi chiyamikiro iri mwa kupita ku nyumba ndi nyumba ndi mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Kuchita choncho kumafunikira kukhala womasuka mkalankhulidwe chifukwa iyo mopitiriza imakhudza kuyang’anizana kwa chindunji ndi ena, ambiri a iwo amene amationa ife monga chokhumudwitsa. Chimatenga chikondi chenicheni kaamba ka Mulungu ndi kaamba ka mnzathu kupitiriza kupita kukhomo ndi khomo, ngakhale kuti timakumana ndi kusiyana, kuipidwa, kuukira, kapena chitsutso cha chindunji.—Yerekezani ndi Ezekieli 3:7-9.
3. Kodi ndi maziko a Malemba ati amene muli nawo kaamba ka ntchito ya ku nyumba ndi nyumba?
3 Mbiri ya Uthenga Wabwino wa malangizo wa Yesu kwa ophunzira ake 12, ndipo pambuyo pake alaliki 70, mwachiwonekere imasonyeza kuti iwo anali kupita ku nyumba ndi nyumba kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 10:5-14; Luka 10:1-7) Pa Machitidwe 20:20 Paulo akunena ponena za kupita kwake ku nyumba ndi nyumba. Mawu amenewo agwiritsidwa ntchito mkupanga kwake maulendo a ubusa, koma versi 21 silikusiya chikaikiro chiri chonse ponena za chimene ntchitoyo inatanthauza, popeza Paulo akuwonjezera: “Ndinachitira umboni Ayuda ndi Ahelene [ Agiriki]”—osati kwa abale ndi alongo a Chikristu“kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu ndi Ambuye wathu Yesu Kristu.” Pamene akupanga maulendo a ubusa, mkulu kawirikawiri safulumiza ‘kutembenuka mtima kulinga kwa Mulungu ndi chikhulupiriro mwa Yesu.’ Mmalo mwake, iye amalimbikitsa Akristu anzake kukhala ndi chiyamikiro chowonjezereka cha misonkhano kapena utumiki, kapena iye amawathandiza iwo ndi mavuto aumwini.
4. Ndi chiyani chomwe chimatilimbikitsa ife kugawana mu kulalikira ku nyumba ndi nyumba?
4 Sikuti kokha pali maziko abwino a Malemba kaamba ka kupita kwathu ku nyumba ndi nyumba koma zipatso za ntchito imeneyo zimasonyeza kuti madalitso a Yehova ali pa iwo. Inde, “nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Kawirikawiri, awo amene amapita ku nyumba ndi nyumba awona chitsimikiziro cha chitsogozo cha angelo chomwe chimawatsogoza iwo kwa awo omwe ali a njala ndi ludzu la chilungamo. Mwini nyumba anena kuti iye anakhala ali kumapemphera kaamba ka thandizo ndipo Mboni inamufikira mkuyankha ku pemphero limenelo.
5. Kodi ndi chothandizira chabwino chotani chimene tiri nacho kaamba ka utumiki wathu wa ku nyumba ndi nyumba, ndipo ndi mu njira zosiyanasiyana ziti mmene icho chingatithandizire ife?
5 Liri thandizo labwino kwambiri chotani kaamba ka utumiki wa m’munda limene tiripeza mubukhu la Reasoning From the Scriptures! Ilo liri ndi mayambidwe abwino kaamba ka kukambitsirana kwa Baibulo limodzinso ndi chidziŵitso chothandiza pa Malemba ochuluka kapena mitu ya zipembedzo. Chotero, tisangolitenga kokha koma tiyenera kupitirizabe kuloza ku ilo. Makamaka apainiya alongosola chiyamikiro chawo chachikulu kaamba ka thandizo la mtengo wapatali limeneli la utumiki wa mmunda. Kodi mungasonyeze chiyamikiro chanu kaamba ka chikondi cha Mulungu mwakugwiritsira ntchito bukhuli mowonjezereka ndipo mokhutiritsa koposerapo?
6 Kodi ndi phindu laumwini liti limene tingapeze mwakupita ku nyumba ndi nyumba ndi uthenga wa Ufumu?
6 Sitiyenera kuchepsa chenicheni chakuti ife mwaumwini tidzapeza phindu lalikulu mwa kugawana mu utumiki wa ku nyumba ndi nyumba. Pamene ife Akristu tigwirira ntchito pa chikhulupiriro chathu, chimakhala cholimba kwambiri; pamene tikulankhula ndi chitsimikizo, icho chimalimbikitsidwa. Sitingathe kuuza ena ponena za chiyembekezo chathu popanda kuwalitsa chiyembekezo chathu. Palibe china chiri chonse chofanana ndi kutenga mbali mokhazikika mu utumiki wa ku nyumba ndi nyumba kaamba ka kukulitsa zipatso za mzimu zotchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23. Icho chiyenera kokha kukhala mu njira imeneyo, popeza Baibulo limatitsimikizira ife: “Munthu wa mtima wa mataya adzalemera; iye amene atsitsimula ena iye mwini adzatsitsimulitsidwa.”—Miyambo 11:25, New International Version.
Kupanga Maulendo Obwereza
7, 8. Ndi pa zifukwa ziti za nzeru ndi zenizeni zomwe tiyenera kupangila maulendo obwereza?
7 Njira yachiwiri kaamba ka ife ya kuvomerera ku chikondi chomwe Mulungu ndi Kristu anasonyeza kwa ife iri mwa kupanga maulendo obwereza pa anthu omwe poyambirira anasonyeza chikondwerero mu uthenga wa Ufumu. Paulo ndi Barnaba anali odera nkhawa ponena za awo amene iwo analalikirako. (Machitidwe 15:36) Mchenicheni, kukhazikika kumafunikira kuti tipange maulendo obwereza. Pamene tichitira umboni ku khomo ndi khomo, mwa mwawi, kapena mu makwalala, tikuyang’ana kaamba ka awo “odera nkhawa kaamba ka zosowa zawo zauzimu, NW”(Mateyu 5:3) Mwachiwonekere, kuwapatsa iwo, monga mmene kunaliri, chikho chimodzi cha madzi auzimu kapena mtanda umodzi wa mkate mosakaikira iri yosakwanira. Kaamba ka iwo kuti apite ku njira ya moyo, amafunikira thandizo lowonjezereka.
8 Kuyesayesa kwathu koyambirira kungafanizidwe ku kuwokedwa kwa mbewu ya chowonadi. Monga momwe mtumwi Paulo anasonyezera pa 1 Akorinto 3:6, 7, zowonjezeka ziri zofunikira. Sichinali chokwanira kuti iye anawoka. Mbewuzo zinafunikira madzi, monga ngati amene Apolo anapereka. Kenaka chikayembekezeredwa kuti Mulungu adzazipanga izo kukula. Mawonekedwe antchito amenewa akunyalanyazidwa ndi ena, koma ochuluka amailingalira iyo kukhala mawonekedwe aafupi kwambiri a uminisitala wa Chikristu. Chifukwa ninji? Chifukwa anthu amene tinaitanira pa iwo anasonyeza kale chikondwerero china chake.
Kutsogoza Maphunziro a Baibulo Apanyumba
9 Kodi nchifukwa ninji chiyenera kukhala chonulirapo chanu kutsogoza phunziro la Baibulo la panyumba?
9 Pamene maulendo obwereza apangidwa mokhazikika pa anthu omwe anasonyeza chikondwerero mu uthenga wa Ufumu, zotulukapo zake kawirikawiri zimakhala phunziro la Baibulo la panyumba—njira yachitatu mu imene tingasonyezere chiyamikiro chathu. Iyo kwenikwenidi ingakhale yosangalatsa kwambiri ndipo mkhalidwe wopatsa mphoto wa mu utumiki wathu. Chifukwa ninji? Chabwino, chiri chimwemwe chotani kuwona anthu akukula mu chidziwitso ndi chiyamikiro cha chowonadi cha Baibulo, kuwona iwo akupanga kusintha mu miyoyo yawo, ndi kuwathandiza iwo kufikira atadzipereka iwo eni kuchita chifuniro cha Mulungu ndi kubatizidwa! Anthu oterowo mowonadi amawonedwa monga ana athu auzimu ndipo ife monga makolo auzimu.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 4:14, 15; 1 Petro 5:13.
10. Kodi ndi chitsanzo chenicheni chiti chomwe chimasonyeza kufunika kwa kutsogoza maphunziro a Baibulo a panyumba?
10 Talingalirani chitsanzo chabwino ichi. Mmishonale popita ku nyumba ndi nyumba mu chisumbu cha Caribbean anakumana ndi anthu osasangalala awiri omwe nyumba yawo sinali ya ukhondo ndi yolongosoka. Koma iwo anasonyeza chikondwerero. Chothandiza kuphunzira Baibulo chinaperekedwa, ndipo phunziro la Baibulo la panyumba linayambidwa ndi anthu awiriwo, omwe anali asanakwatirane angakhale kuti anali ndi ana ambiri. Pamene phunziro linapita patsogolo, nyumba yawo inayamba kuwoneka bwino ndiponso iwo eni ndi ana awo. Pasanapite nthaŵi yaikulu anthu awiriwo anafunsa amishonalewo kuwakwatitsa iwo, kutsegula njira kaamba ka kubatizidwa kwawo. Kenaka tsiku lina mbale wachatsopanoyo mwachimwemwe anasonyeza msonkho wake woyendetsera galimoto, chinthu choyamba chomwe anachipeza. Inde, asanakhale m’modzi wa Mboni za Yehova, iye sanawone chifukwa chakukhalira ndi mtchato wa ukwati kapena msonkho woyendetsera galimoto, koma tsopano iye anali kumvera ponse pawiri malamulo a Mulungu ndi a kaisara.
Umboni wa Mkhwalala
11, 12. (a) Tiri ndi chilimbikitso chiti cha Malemba cha kugawana mu umboni wa mkhwalala? (b) Kodi ndi zifukwa ziti zomwe ziripo kaamba ka kuchita tero?
11 Njira yachinayi mu imene tingasonyezere chiyamikiro chathu kaamba ka zimene Mulungu ndi Kristu anachita kwa ife iri mwakuchitira umboni mu makwalala. Pamene titengamo mbali, tikuthandiza kukwaniritsa Miyambo 1:20, 21 mu njira yeniyeni: “ Nzeru ipfuula panja; imveketsa mawu ache pabwalo; iitana posonkhana anthu polowera pachipata; m’mudzi inena mawu ake.”
12 Pali zifukwa zabwino kwambiri kaamba ka ife kugawana mokhazikika mu mbali imeneyi ya kulalikira Ufumu. Mu madera ambiri, kuli kovuta mowonjezerekawonjezereka kupeza anthu ali kunyumba. Iwo mwina mwake akugawana mu- mkhalidwe wina wake wa zosangalatsa, kugula, kapena ntchito. Ndiponso, anthu ambiri amakhala mu nyumba zomangidwa bwino koposa kapena nyumba za chifumu, osaiwala awo amene amakhala mu mahotela. Kawirikawiri pali anthu omwe amawoneka mkhwalala.
13. Kuchita umboni mkhwalala kungakhale ndi zoturukapo zotani? Chitirani chitsanzo.
13 Mkulu mu United States akutsogoza maphunziro a Baibulo a panyumba anayi ndi anthu omwe poyamba anakumana nawo mu ntchito ya umboni wa mu makwalala. Komabe, iye samangoima chabe chiriri (angakhale kuti mu maiko ena chimenecho ndicho chimene lamulo limalola). Mmalo mwake, ndi kumwetulira kwa ubwenzi ndi liwu losangalatsa, iye amafikira anthu omwe angoima, kudikira basi, kapena kungoyenda opanda chifukwa chenicheni. ‘Mawu ake ali m’chisomo, okoleretsa,’ ndipo amagwiritsira ntchito kuzindikira kudziwa kuti ndi motani mmene angafikire aliyense. (Akolose 4:5, 6; 1 Petro 3:15) Iye sanapeze kokha maphunziro a Baibulo a panyumba mwa umboni wa mkhwalala wotero iye alinso wachipambano koposa m’kugawira zofalitsidwa kwa ambiri. Inde, mwa kukhala wopesa bwino ndi kukhala ndi kumwetulira kwaubwenzi limodzi ndi ufulu wa kulankhula, ungakhale wokhutiritsa mu umboni wa mkhwalala. Mchenicheni, Mboni zisanu posachedwapa zinagawira makope oposa 30 a buku la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? mu mabwalo a malonda. Ambiri a mabukhu anatengedwa ndi anthu ongokhala mu magalimoto awo.
Umboni wa Mwamwawi
14. Kodi ndimotani mmene ubwino wa umboni wa mwamwawi ukuwonekera?
14 Njira yachisanu ya ife yosonyezera chiyamikiro kaamba ka chikondi chachikulu chomwe Mulungu ndi Yesu anasonyeza kwa ife iri mwa kuchitira umboni mwamwawi. Ndi mokhutiritsa chotani mmene kawirikawiri ichi chakhalira, ponse pawiri mkupeza anthu anjala ndi ludzu kaamba ka chilungamo ndi mkugawira zofalitsidwa! Iyo kwenikwenidi iri njira imodzi mu imene tingalabadire chenjezo lopezeka pa Aefeso 5:15, 16, ‘mukumadzipezera nthawi yabwino.’ (NW) M’mishonale anayambitsa kukambitsirana ndi mnzake woyenda naye yemwe anali mu galimoto. Mwamunayo anasonyeza chikondwerero. Maulendo obwereza anapangidwa ndipo phunziro la Baibulo linayambidwa. Lerolino munthu ameneyo ali mkulu wa Chikristu. Kwina kwake mkulu anayambitsa kukambitsirana ndi mayi yemwe, monga mmene zinachitikira, anali kusintha chipembedzo chake kuti akwatire m’Yuda. Iye anafuna kudziwa ndani amene anabwera poyamba, Mose, Nowa, Davide, ndi ena otero. Iye anamuuza iye kuti zomwe amafuna zimapezeka mu bukhu la Nkhani za Baibulo, lomwe limapereka zochitika za Baibulo mu mkhalidwe wolongosoka. Angakhale kuti iye anali mlendo kwenikweni kwa iye, iye mwamsanga anampatsa dzina lake ndi keyala yake ndi chopereka choyenerera kotero kuti akalitumize bukhulo kwa iye.
15. Kodi ndi chiyani chomwe chidzatithandiza ife kukhala amaso ku mwawi wa kuchitira umboni mwa mwawi?
15 Nthawi zina kaamba ka mantha kuti mwina tingakanidwe, timakaikira kuyambitsa kukambitsirana ndi wina yemwe tikuyenda naye yemwe wakhala pafupi ndi ife. Ndi kawirikawiri chotani, angakhale kuli tero, kuti timafupidwa molemerera ngati tisonkhanitsa kulimba mtima mu kuchita choncho! Chiyamikiro kaamba ka ubwino wa Mulungu ndi zofuna za anthu kudzatithandiza ife kukhala ndi kulimba mtima kofunikira. Inde, kumbukirani kuti “Mulungu sanatipatsa mzimu wamantha, komatu wamphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.”—2 Timoteo 1:7, NIV.
Kulandira Alendo
16 Ndi chifukwa ninji tiyenera kukhala amaso ku kuzindikira alendo ochezera ku Nyumba yathu ya Ufumu?
16 Njira yachisanu ndi chimodzi mu imene tingasonyezere chiyamikiro chathu kwa Mulungu ndi Kristu iri mwa kulandira alendo omwe amabwera ku Nyumba ya Ufumu yathu. Chikondi kaamba ka mbale chiyenera kutipangitsa ife kukhala a maso kuzindikira mlendo aliyense yemwe amachezera ku malo athu olambirira. Tiyeni tonse tikalamire kumupanga iye kudzimva kukhala waufulu, kudzimva kuti ali pakati pa mabwenzi omwe ali ndi chikondwerero mu ubwino wake wauzimu. Mwachidziwikire, choposa kufunitsitsa kopanda phindu kunabweretsa iye kumeneko. Iye mowonadi angakhale ali wanjala ndi waludzu kaamba ka chilungamo. Kudera nkhawa kwathu kowona mtima kaamba ka iye kungatulukemo mu kuyambitsa phunziro la Baibulo la panyumba, kumuthandiza iye kupita ku njira ya moyo. (Mateyu 5:3, 6; 7:13, 14) Mchenicheni, chinthu chimenechi chakhala chiri kuchitika kawirikawiri. Mmishonale wochokera ku kilasi yoyamba ya Watchtower Bible School of Gilead anazindikira kuti maphunziro ake awiri a Baibulo opita patsogolo anali awo omwe anakumana nawo poyamba pa Nyumba ya Ufumu.
Kumachitira Umboni mwa Kulemba Makalata
17. Kuchitira umboni mwa kulemba makalata kungabweretse zoturukapo zotani?
17 Njira yachisanu ndi chiwiri ya ife ya kuchitira umboni, mkuvomereza ku chikondi chimene Mulungu ndi Kristu anasonyeza kwa ife, iri mwa kulemba makalata. Kawirikawiri, awo amene amagwiritsira ntchito njira iyi yochitira umboni amalandira makalata achiyamikiro. Iyi iri njira imene imagwiritsidwa ntchito ndi atumiki ena a nthawi zonse omwe mwakanthawi ali osakhoza kupita ku nyumba ndi nyumba chifukwa cha kupunduka kwa kuthupi. Mwachitsanzo: Panali banja la ana 12. Tsiku lina atate anafika kunyumba nkupeza kuti asanu a iwo anawombeledwa ndi bwenzi la mmodzi wa ana ake aakazi. Mosaphula kanthu anafunafuna chitonthonzo kuchokera kwa ansembe a Chipembedzo chadziko. Kenaka tsiku lina iye analandira kalata yochokera kwa munthu wachilendo, Mboni yomwe inawerenga mu nyuzipepala ponena za tsoka lake ndipo anafuna kumutonthoza iye, akutsekeramo bukhu la Chowonadi. Ichi chinali chimene munthuyu anali kufunafuna. Lerolino iye, nayenso, ali Mboni ya changu.a
Kutumiza Lamya
18, 19. Ndi mbali ina iti ya kulalikira mbiri yabwino yomwe ena aipeza kukhala yokhutiritsa, ndipo chifukwa ninji?
18 Kutchula mbali ya chisanu ndi chitatu ya kuchitira umboni, pali mwawi wa kugwiritsira ntchito lamya mu kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. Ici mowonjezereka chikutsimikizira kukhala chabwino ndi njira yokhutiritsa yochitira umboni. Mboni zowonjezerekawonjezereka zikukhala za luso mu mbali iyi ya utumiki, yomwe iri ndi zambiri za kuiyamikira. Ndi iyo timafikira anthu ena amene sitikhoza kuwapeza pa njira ya ku nyumba ndi nyumba. Kumene umboni wa pa lamya uchitidwa mwanzeru, ndi kuleza mtima, mochenjera, ndi mwaluso, ena apeza chivomerezo chabwinopo kuposa pamene aitanira kwa anthu pa nyumba zawo.
19 Mpingo wa Chijapani mu dziko lolankhula Chingelezi umagwiritsira ntchito bukhu la lamya monga mbali ya gawo lake. Ofalitsa amatumiza lamya ku maina Achijapani ndi kupanga makonzedwe a kufikapo kwa umwini komwe apeza chikondwerero. Iwo ayamba kweni kweni maphunziro makumi awiri ochuluka mwanjira imeneyi.
Kuchitirani Umboni ndi Khalidwe Labwino
20, 21. Khalidwe lathu lingakhale ndi zoturukapo zabwino zotani? Chitirani chitsanzo
20 Njira ya chisanu ndi chinayi mmene timabweretsera chitamando kwa Mulungu iri mwa khalidwe lathu labwino. Wolemba nkhani wa Chirussia kamodzi ananena kuti khalidwe lathu labwino liri ulaliki wathu wabwino koposa. Mu chenicheni mobwerezabwereza olemba nyuzipepala amapereka ndemanga pa khalidwe lapamwamba la Mboni za Yehova. Mmodzi anasimba kuti: “Mboni za Yehova zimadziwika koposa monga anthu owona mtima mu Federal Republic ya Germany.” Kumayambiriro kwa teremu ya sukulu, Mboni ya chitsikana inabweretsa kabukhu ka School kwa mphunzitsi wake. Mogontha analikana ilo, akumanena kuti iye sanafune kuchita ndi chiri chonse chokhudzana ndi Mboni. Komabe, mkupita kwa nthawi khalidwe lake labwino linamupezera iye chitamando chapamwamba cha mphunzitsi wake ndipo linapangitsa kusintha kotheratu kwa mkhalidwe wake kulinga kwa Mboni. Yokhala ndi chinthu chofananacho inali kalata yomwe makolo a Mboni analandira kuchokera kwa m’modzi wa aphunzitsi a mwana wawo: “Muyezo wosakanidwa wa kupambana kwa zikhulupiriro zanu ali ana anu.”
21 Okhala m’dziko sanganene chabwino ponena za Mboni za Yehova popanda kubweretsa ulemu kwa Mulungu ndi Kristu. Imeneyo iri njira imene iyenera kukhalira. Kodi Yesu sananene kuti tiyenera kuwalitsa kuunika kwathu kotero kuti anthu awone ntchito zathu zabwino ndi kulemekeza Atate wathu wa kumwamba? (Mateyu 5:16) Zowonadi, ndi khalidwe lathu labwino, tidzakometsera chiphunzitso cha chowonadi. (Tito 2:10) Ndithudi, chenicheni chakuti khalidwe lathu labwino limabweretsa ulemu kwa Mulungu ndi Kristu ndi kuthandiza ena kufika ku njira ya moyo chiri chifukwa champhamvu cha kukhala kwathu mozama odera nkhawa kuti khalidwe lathu nthawi zonse liyenera kukhala losabweretsa chitonzo.
22. Ndi iti ya njira zosonyezera chiyamikiro imene mudzakalamira, ndipo chifukwa ninji?
22 Monga mmene tawonera, pali njira zambiri mu zimene tingasonyezere chiyamikiro chathu kaamba ka zonse zimene Yehova ndi Yesu Kristu anachita kwa ife, ndipo makamaka zisonyezero zawo za chikondi chokulira. Mkachitidweko, tingatsimikizire chikondi chathu cha mnansi.—Marko 12:30, 31.
23. Ndi mu njira yomalizira iti mmene mudzasonyezera chiyamikiro kwa Mulungu ndi Yesu?
23 Pomalizira, tiyeni tiwone kuti tingasonyeze chiyamikiro chathu kaamba ka zisonyezero ziwiri zazikulu kwambiri za chikondi mwa kukumbukira Mgonero wa Ambuye. Pa usiku wake womaliza pa dziko lapansi monga munthu, Yesu anakhazikitsa chakudya chokumbukira cha chaka ndi chaka cha mkate ndi vinyo, kuimira thupi lake ndi mwazi wake. Iye analamula kuti chikondwerero chimenechi chiyenera kuchitidwa mchikumbukiro chake. (1 Akorinto 11:23-26) Chaka chino Mgonero wa Ambuye udzakhala pa Sande, April 12, pambuyo pa kulowa kwa dzuwa. Kuzungulira dziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zidzakhala zikubwera pamodzi mkumvera ku lamulo la Yesu. Musaphonye icho!
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka tsatanetsatane, onani Galamukani! ya October 22, 1986 (Chingelezi) masamba 12-16.
Mafunso a Kapendedwe
◻ Ndi motani ndipo ndi kuti kumene Yesu anachitira umboni?
◻ Ndi mu njira ziti mmene ife tingatsanzirire Yesu mu kusonyeza chiyamikiro kaamba ka chikondi chachikulu cha Mulungu?