Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 3/8 tsamba 26-28
  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro m’Zaka za Zana Loyamba
  • Kuonetsetsa Bwino Zinthu
  • Chosankha cha Munthu Mwini
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Maphunziro—Agwiritsireni Ntchito Kutamanda Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Maphunziro Okhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kusunga Maphunziro Pamalo Ake
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 3/8 tsamba 26-28

Lingaliro la Baibulo

Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?

“Ndi anthu osazindikira okha amene amanyalanyaza maphunziro.”—Anatero Publilius Syrus, m’buku lotchedwa Moral Sayings, la m’zaka za zana loyamba B.C.E.

BAIBULO limatilimbikitsa ‘kusunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira.’ (Miyambo 3:21) Yehova, Mulungu wachidziŵitso, amafuna kuti olambira ake akhale anthu ophunzira. (1 Samueli 2:3; Miyambo 1:5, 22) Komabe, pali mfundo zina m’Baibulo zimene zingatipangitse kukhala ndi mafunso. Mwachitsanzo, pamene mtumwi Paulo ankanena za zomwe ankachita m’mbuyo, kuphatikizapo maphunziro ake apamwamba, analemba kuti: “Ndiziyesa zapadzala,” (Afilipi 3:3-8) M’kalata ina yomwenso analemba mouziridwa, iye analemba kuti: “Nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu.”—1 Akorinto 3:19.

Popeza zili choncho, kodi ndiye kuti Baibulo limaletsa maphunziro? Kodi Mkristu angaphunzire kufika mpaka pati? Kodi ayenera kungophunzira ndi kumaliza maphunziro ololedwa ndi lamulo la kumaloko, kapena ayenera kuwonjezerapo?

Maphunziro m’Zaka za Zana Loyamba

Akristu oyambirira anali ophunzira mosiyanasiyana. Anthu ena apamwamba anaona atumwi a ku Galileya Petro ndi Yohane kukhala “anthu osaphunzira ndi opulukira.” (Machitidwe 4:5, 6, 13) Kodi izi zikutanthauza kuti anthu aŵiri ameneŵa anali osadziŵa kulemba ndi kuŵerenga kapena osaphunzira? Ayi. Zinkangotanthauza kuti maphunziro awo sanali akusukulu zapamwamba za Ayuda za ku Yerusalemu. Pambuyo pake zolemba za anthu aŵiri olimba mtima achikristu ameneŵa zinasonyeza kuti anali ophunzira bwino, anzeru, opangitsa Malemba kumveka bwino. Maphunziro awo anali othandizanso kuti azitha kupeza zosoŵa za pamoyo wa mabanja awo. Ankayendetsera pamodzi bizinesi yopha nsomba yomwe imaonekeratu kuti inkayenda bwino.—Marko 1:16-21; Luka 5:7, 10.

Koma kuti tiyerekeze, Luka, wophunzira yemwe analemba limodzi la mabuku a Uthenga Wabwino kuphatikizapo buku la Machitidwe, anali wophunzira kwambiri. Anali dokotala. (Akolose 4:14) Kukhala kwake wodziŵa za mankhwala kumamveketsa bwino mawu ouziridwa amene analemba.—Onani Luka 4:38; 5:12; Machitidwe 28:8.

Asanakhale Mkristu, mtumwi Paulo anaphunzitsidwa chilamulo cha Ayuda ndi mphunzitsi wanzeru kwambiri panthaŵiyo, wotchedwa Gamaliyeli. (Machitidwe 22:3) Masiku ano tikhoza kuyerekezera maphunziro a Paulo ndi maphunziro a ku yunivesite. Kuwonjezera apo, kwa Ayuda zinalinso za ulemu kuti mwana aphunzire ntchito yamanja, ngakhale ngati mtsogolo adzaphunzira maphunziro apamwamba. Nzoonekeratu kuti Paulo anaphunzira kusoka matenti pamene anali mwana. Maphunziro ameneŵa anamthandiza kudzipezera zosoŵa zake mu utumiki wake wa nthaŵi zonse.

Komabe, Paulo anazindikira kuti poyerekezera ndi chidziŵitso cha Mulungu chomwe chimaposeratu zina, maphunziro akusukulu—ngakhale kuti ndi ofunika—kufunika kwake nkwakanthaŵi. Motero Baibulo limanena kuti chofunika kwambiri ndi kudziŵa Mulungu ndi Kristu. Lerolino Akristu angachite bwino atatsanzira kaonedwe koyenera kameneka kamaphunziro.—Miyambo 2:1-5; Yohane 17:3; Akolose 2:3.

Kuonetsetsa Bwino Zinthu

Akristu ena apeza kuti kuchita maphunziro owonjezera, kaya akusukulu chabe kapena kuphunzira ntchito, kwawathandiza kusamalira zosoŵa zakuthupi za mabanja awo. Kusamalira banja lako nkoyenera, chifukwa ‘kudzisungira mbumba yako’ ndi udindo wopatulika. (1 Timoteo 5:8) Kuphunzira maluso kuti muzitha kuchita zimenezi ndi nzeru yabwino.

Komabe amene akuona kuti nkoyenera kupitiriza maphunziro ncholinga chimenechi ayenera kupenyetsetsa ubwino ndi kuipa kwake. Phindu lake lenileni liyenera kukhala kumatha kupeza ntchito imene ingathe kumpangitsa munthu kudzisamalira yekha pamodzi ndi banja lake mokwanira kwinaku akuchita utumiki wachikristu mwachangu. Kuwonjezera apo, azitha kuthandizako ena osoŵa, ‘kuchereza osoŵa.’—Aefeso 4:28.

Kodi zina za zinthu zoipa nziti? Zikhoza kuphatikizapo kuphunzira zinthu zimene zimawononga chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Baibulo. Paulo analangiza Akristu kukhala ochenjera ndi ‘chotchedwa chizindikiritso [ch]onama’ ndi “chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu.” (1 Timoteo 6:20, 21; Akolose 2:8) Nzosatsutsika kuti maphunziro ena akhoza kuwononga chikhulupiriro cha Mkristu. Amene akufuna maphunziro owonjezera ayenera kuzindikira kuwopsa kwa zinthu zowononga zimenezi.

Mose, amene “anaphunzira nzeru zonse za Aaigupto,” anasungabe chikhulupiriro cholimba ngakhale kuti anaphunzira maphunziro omwe mosakayika anaphatikizapo zakuti kuli milungu yambiri, chiphunzitso chosalemekeza Mulungu. (Machitidwe 7:22) Momwemonso lerolino Akristu amakhala ochenjera kuti asatengeke ndi zinthu zosayenera paliponse pamene akhala.

Vuto linanso pa kuphunzira maphunziro owonjezera nlakuti kukhala wozindikira zinthu kwambiri kukhoza kukupangitsani kuyamba kudzitukumula. (1 Akorinto 8:1) Ambiri amafuna kuzindikira zinthu mwa kuphunzira ndi zolinga za dyera, koma ngakhale uli ndi zifukwa zabwino zofunira kukhala wozindikira zinthu, ukhoza kumadzimva wapamwamba ndi wofunika kwambiri. Machitidwe ameneŵa sakondweretsa Mulungu.—Miyambo 8:13.

Lingalirani za Afarisi. Mamembala a gulu lachipembedzo lotchuka limeneli ankadzinyadira chifukwa chokhala ozindikira ndi kudzinenerera kukhala achilungamo. Anali odziŵa bwino miyambo ya arabi, ndipo ankanyalanyaza anthu wamba amene anali osaphunzira kwenikweni, akumawaona monga mbuli, onyozeka, ngakhale otembereredwa. (Yohane 7:49) Kuwonjezera apo, anali okonda ndalama. (Luka 16:14) Chitsanzo chawo chimasonyeza kuti ngati muphunzira ndi zolinga zoipa, maphunziro akhoza kukupangitsani kukhala wonyada kapena wokonda ndalama. Choncho, polingalira za mtundu ndi kuchuluka kwa maphunziro oyenera kupeza, Mkristu angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi cholinga changa nchiyani?’

Chosankha cha Munthu Mwini

Akristu lerolino ndi ophunzira mosiyanasiyana, monganso mmene zinalili m’zaka za zana loyamba. Motsogozedwa ndi makolo awo, achinyamata omwe amaliza maphunziro ololedwa ndi lamulo la kumaloko angasankhe maphunziro owonjezereka. Momwemonso, akuluakulu omwe ali pamavuto a zachuma angapeze kuti kuwonjezera maphunziro kukhoza kuwathandiza kuti azipeza ndalama zokwanira.a Ena a maphunziro akusukulu a kumaloko akhoza kumagogomezera zongowonjezera nzeru zanu osati othandiza pantchito. Choncho munthu akhoza kupeza kuti atatayira nthaŵi yake yochuluka kuphunzira maphunziro ena ake, sangathe kupeza ntchito. Chifukwa cha chimenechi ena amayamba maphunziro a ntchito za muofesi kapena ntchito za manja, ncholinga choti akhale ndi maluso omwe olemba ntchito amawafuna.

Mwanjira iliyonse, kupanga zosankha pa zimenezi ndi nkhani yaumwini. Akristu sayenera kudzudzulana pa nkhani imeneyi. Yakobo analemba kuti: “Koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?” (Yakobo 4:12) Ngati Mkristu alingalira zowonjezera maphunziro ake, angachite bwino kuona kaye zolinga zake kuti atsimikizire kuti si chifukwa chadyera kapena kukonda chuma.

Nzoonekeratu kuti Baibulo limalimbikitsa kuti tikhale ndi malingaliro achikatikati a maphunziro. Makolo achikristu amazindikira ubwino wamaphunziro a zauzimu ochokera m’Mawu ouziridwa a Mulungu ndipo amapereka uphungu woyenera kwa ana awo wokhudza maphunziro owonjezera. (2 Timoteo 3:16) Pokhala amaona mmene zinthu zililidi pamoyo, amazindikira ubwino wamaphunziro pakuphunzira maluso ofunika kuti ana awo omakulawo azidzatha kudzisamalira okha pamodzi ndi mabanja awo a mtsogolo. Motero, polingalira kuti kaya muyenera kuchita maphunziro owonjezereka ndi kuti mufike mpaka pati, Mkristu aliyense akhoza kupanga zosankha zolongosoka modalira pa kudzipereka kwake kwa Yehova Mulungu, kumene ‘kumapindula zonse, popeza kumakhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mumve zambiri pa nkhani imeneyi, onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1992, masamba 10-21, ndi brosha ya Mboni za Yehova ndi Maphunziro, zofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

“Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira.”—Miyambo 3:21

[Mawu Otsindika patsamba 28]

Polingalira zakuti kaya awonjezere maphunziro, Mkristu ayenera kudzifunsa yekha kuti, ‘Kodi zolinga zanga nzotani?’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena