Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 9/8 tsamba 21-24
  • Kusunga Maphunziro Pamalo Ake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusunga Maphunziro Pamalo Ake
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro Ofunika Koposa
  • Maphunziro Okhala ndi Cholinga
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Baibulo Limaletsa Maphunziro Akusukulu?
    Galamukani!—1998
  • Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani ya Maphunziro?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Maphunziro—Agwiritsireni Ntchito Kutamanda Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 9/8 tsamba 21-24

Kusunga Maphunziro Pamalo Ake

KATSWIRI wojambula zithunzi ndi manja amadziŵa kutulutsa chinthu monga momwe chilili. Zinthu zoonekera kumaso zimasamaliridwa kwambiri kuposa zapakati kapena kumbuyo pa zithunzipo. Zimenezi nzofanana kwambiri ndi zinthu zathu zofunika kwambiri m’moyo. Zina zimafuna chisamaliro chachikulu kuposa zina.

Yesu Kristu anati: “Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wawo Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:3) Motero, zinthu zauzimu ziyenera kukhala patsogolo penipeni. Mosiyana ndi zimenezo, chuma chakuthupi chiyenera kukhala chofunika pang’ono.

Kodi mpati pamene maphunziro amaloŵa munkhaniyi? Ndithudi imeneyi sili mbali yosafunika kwa Mkristu. Kaŵirikaŵiri maphunziro akutiakuti akuthupi ngofunika kukwaniritsira thayo la Malemba loperekedwa ndi mtumwi Paulo: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Ndiponso, lamulo limene Yesu anapatsa ophunzira ake, la kupanga ophunzira, “kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene [analamulira],” limafuna kuti munthu ‘adziŵe’ ndiyeno alangize ena mogwira mtima.—Mateyu 28:19, 20; Yohane 17:3; Machitidwe 17:11; 1 Timoteo 4:13.

Komabe, maphunziro ayenera kusungidwa pamalo ake. Sayenera kungochitidwa chifukwa cha kufuna kupambana m’zamaphunziro kapena kupeza madigiri apamwamba. Kusamalira maphunziro mopambanitsa kumagwiritsa mwala. Zoonadi, iwo angapereke mapindu akuthupi akanthaŵi. Koma monga momwe mfumu yanzeru Solomo inanenera: “Umagwirira ntchito kanthu kena ndi nzeru zako zonse, chidziŵitso, ndi luso, ndiyeno ufunikira kukasiyira wina amene sanakagwirire ntchito.”—Mlaliki 2:21, Today’s English Version.

Mboni za Yehova zimakonda maphunziro, osati chifukwa cha kuti zingokhala nawo, koma kuti zigwiritsire ntchito mapindu ake mu utumiki wa Mulungu ndi kudzichirikiza iwo eni. Popeza kuti utumiki wawo ngwosafuna phindu, ambiri amadalira ntchito yolembedwa kuti apeze zokhalira moyo. Zimenezi zingakhale zovuta makamaka kwa atumiki anthaŵi yonse a Mboni za Yehova, otchedwa kuti apainiya. Iwo ayenera kutsatira mndandanda waukulu mu utumiki pamene akudzipezera ndalama zokwanira za iwo eni ndi mabanja awo ngati ali okwatira.a—Miyambo 10:4.

Pambuyo pa kupenda zinthu zosiyanasiyana zoloŵetsedwamo, Mboni za Yehova zina zasankha kuchita maphunziro owonjezera. Zoonadi, izo zasamala kotero kuti zisunge maphunziro pamalo ake. Kodi nchiyani chimene chawathandiza kuchita zimenezi? “Zinthu zingapo zinandithandiza,” akutero wachichepere wina wa ku Brazil wotchedwa John. “Ngakhale kuti ndinali kuŵerenga usiku, sindinaphonye misonkhano Yachikristu. Ndinadziŵitsanso bwino lomwe anzanga a m’kalasi pachiyambi penipeni kuti ndinali mmodzi wa Mboni za Yehova.”

Eric, nayeso wa ku Brazil, anagwiritsira ntchito mwaŵi wopezeka kulankhula kwa ena ponena za zikhulupiriro zake pamene anali kuwonjezera maphunziro ake. “Ndinaona sukulu monga gawo langa lolalikiramo lapadera,” iye akutero. “Ndinali wokhoza kuchititsa maphunziro a Baibulo ndi aphunzitsi ndi ophunzira angapo, asanu a iwo tsopano ali obatizidwa, aŵiri a iwo akutumikira monga akulu.”

Richard anabwereranso kusukulu kwakanthaŵi kuti apeze digiri ya luso la mapulani. “Maphunziro anga anandithandiza kupeza ntchito yoti indichirikize ine ndi mkazi wanga,” iye akutero, “komanso inatsegula chitseko cha mwaŵi wina. Pamene ndinali kupita ku ntchito zomanga mofulumira Nyumba Yaufumu ndi kulankhula ndi amene anali kuyang’anira, ndinazindikira kuti panalibe waluso la mapulani.b Tsopano maphunziro angawo akugwiritsiridwa ntchito m’njira yopindulitsa m’ntchito zimenezi. Ndiponso, m’kupita kwa nthaŵi mkazi wanga ndi ine tikuyembekezera kukatumikira kaya kumalikulu adziko lonse kapena m’ntchito za kumanga zapadziko lonse za Mboni za Yehova.”

Panthaŵi imodzimodziyo, ambiri a Mboni za Yehova agonjetsa vuto la kudzichirikiza iwo eni ndi mabanja awo popanda maphunziro owonjezera. “Ndimadzichirikiza mwa kugwira ntchito ya m’nyumba kaŵiri pamlungu,” akufotokoza motero Mary. “Nzodabwitsa kuti ndimalandira ndalama zambiri pa ola kuposa anthu ena amene ndimawagwirira ntchito. Koma ndimaona ntchito yangayo monga njira yopezera ndalama. Imandichititsa kukhalabe mu ntchito yaupainiya, ndipo ndilibe chisoni.”

Steve akulingalira mofananamo. “Pamene ndinayamba kuchita upainiya,” iye akutero, “ena anati kwa ine: ‘Kodi udzatani ukadzakwatira ndi kukhala ndi ana? Kodi udzakhoza kupeza ndalama zokhalira moyo?’ Monga momwe zachitikira, ndachita ntchito zambiri zamitundu yosiyanasiyana kwakuti ndimadziŵa pafupifupi zonse zimene mungaganizire. Tsopano popeza kuti ndili ndi mkazi wofuna kusamaliridwa, ndimapeza kuti ndimalandira ndalama zambiri kuposa omaliza maphunziro a ku koleji amene amagwira ntchito pa kampani pathu.”

Atate osakhulupirira angafune kuti ana aang’ono achite maphunziro owonjezera, ndipo iwo ali ndi ulamuliro wa m’Malemba wochita zimenezi. Komabe, m’nkhani zotero, ndipo mogwirizana ndi Mateyu 6:33, achichepere angatenge makosi amene adzawathandiza kukhala anthu ofunika kwambiri mu utumiki wa Yehova kapena ngakhale kuwalola kuloŵa mu utumiki wa nthaŵi yonse panthaŵi imodzimodziyo pamene akuchita maphunzirowo.

Maphunziro Ofunika Koposa

Mboni zonse za Yehova, mosasamala kanthu za mkhalidwe wawo wa maphunziro, zili ndi kanthu kena kofanana. Zimazindikira kuti maphunziro ofunika koposa amene alipo lerolino ali ndi magwero ake m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Yohane 17:3 amati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Mosasamala kanthu za maphunziro akuthupi amene Mkristu amapeza, kuloŵetsa chidziŵitso cha Yehova ndi Mwana wake, Yesu, kuyenera kukhala chinthu choyamba.

Chitsanzo chimenechi chinaikidwa ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba. Manayeni, “anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira wachigawocho,” komabe analipo ndipo anali wokangalika pakati pa aneneri ndi aphunzitsi a mpingo wa Antiokeya. (Machitidwe 13:1, NW) Mofananamo, Paulo analandira maphunziro amene lerolino angayerekezeredwe ndi maphunziro a ku yunivesite. Komabe, pambuyo pa kukhala Mkristu, anasunga maphunziro akewo pamalo ake. Mmalo mwa kuwagwiritsira ntchito kuwopsezera ena, anagwiritsira ntchito chidziŵitso chake cha makhalidwe a anthu, malamulo, ndi mbiri yakale kulalikira kwa anthu a mitundu yonse.—Machitidwe 16:37-40; 22:3; 25:11, 12; 1 Akorinto 9:19-23; Afilipi 1:7.

Akristu a m’zaka za zana loyamba anali odziŵika osati makamaka chifukwa cha mkhalidwe wawo wa maphunziro. Ambiri anali “osaphunzira ndi opulukira,” osaphunzira m’sukulu zachirabi. Koma zimenezi sizimatanthauza kuti iwo anali osadziŵa kanthu. Mosiyana ndi zimenezo, amuna ndi akazi ameneŵa anali okonzekera kutetezera chikhulupiriro chawo—luso limene linapereka umboni wa maphunziro okhala ndi maziko olimba.—Machitidwe 4:13.

Chifukwa chake, Akristu onse ali okondweretsedwa kwambiri ndi maphunziro. Panthaŵi imodzimodziyo, amayesayesa “kutsimikizira zinthu zofunika koposa,” akumasunga maphunziro—ndi kuyesayesa kwina kulikonse—pamalo ake oyenera.—Afilipi 1:9, 10, NW.

[Mawu a M’munsi]

a Nkosangalatsa kudziŵa kuti mtumwi Paulo wophunzira kwambiriyo anasankha kudzichirikiza mu utumiki mwa kupanga mahema, umisiri umene mwinamwake anauphunzira kwa atate wake. Kupanga mahema sikunali ntchito yosavuta. Nsalu ya ubweya wa mbuzi imene inagwiritsiridwa ntchito, yotchedwa cilicium, inali yokhuthala ndi ya nyankhalala, yovuta kudula ndi kusoka.—Machitidwe 18:1-3; 22:3; Afilipi 3:7, 8.

b Mawu akuti “yomanga mofulumira” amanena za njira yolinganizidwa bwino koposa ya kumanga yoyambitsidwa ndi Mboni za Yehova. Antchito odzifunira amene amagwira ntchito imeneyi samalipidwa; amapereka mwaufulu nthaŵi yawo ndi nyonga. Chaka chilichonse pafupifupi Nyumba Zaufumu zatsopano 200 zimamangidwa ku United States, zinanso 200 zimakonzedwanso mwa kugwiritsira ntchito njira imeneyi.

[Bokosi patsamba 23]

Chiyamikiro Choyenerera Kwambiri

Chaka Cha Kumaliza Maphunziro Ake A Sukulu Ya Sekondale Chisanafike, Matthew Anasinkhasinkha Mwamphamvu Ponena Za Mmene Adzadzichirikizira Pamene Alondola Ntchito Yodzisankhira Monga Mtumiki Wanthaŵi Yonse Wa Mboni Za Yehova. Pambuyo Pa Kulingalira Mwapemphero Pa Nkhaniyo, Matthew Ndi Makolo Ake Analingalira Kuti Maphunziro Owonjezereka Akakhala Opindulitsa Kukwaniritsa Chonulirapo Chake. Motero, Anafunsira Thandizo La Ndalama. Phungu Wa Sukulu Wa Matthew Anawonjezerapo Kalata Ya Chiyamikiro Pa Kufunsirako, Akumanena Kuti:

“Mkati Mwa Zaka Ziŵiri Ndi Theka Zapitazo, Ndasangalala Kukhala Phungu Ndi Bwenzi La Matt. Matt Ndi Munthu Wosatekeseka . . . Ali Ndi Chikhulupiriro Chachikulu Ndi Chikhutiro Champhamvu, Chimene Chimayambukira Maunansi Ndi Machitidwe Ake.

“M’zaka Zonse Zapita, Matthew Wakhala Akuphunzira Kaamba Ka Utumiki. Mtumiki Wa Chipembedzo Chake Samalandira Ndalama Zilizonse. Utumikiwo Ulidi Ntchito Yochitidwa Chifukwa Cha Chikondi. Matt Ndi Mnyamata Wosadzikonda, Wanzeru Ndi Wolingalira Ena. Kufunsira Thandizo La Ndalama Kumeneku Kungakhale Njira Yochirikizira Mwamuna Wachikhulupiriro Ameneyu Kuti Apitirizebe Maphunziro Ake Ndi Ntchito Yodzifunira.

“Ponena Za Ntchito Yodzifunira Ndi Utumiki Wa M’chitaganya, Matt Wathera Maola Ambirimbiri Akulalikira Kukhomo Ndi Khomo Pa Kutha Kwa Milungu Ndiponso Ataŵeruka Ku Sukulu Ndi Mkati Mwa Tchuthi Cha Sukulu. Amagwira Ntchito M’chitaganya Pakati Pa Anthu Osiyanasiyana. Matt Wasonyeza Kukhoza Kwake Ndi Maluso Ake A Utsogoleri Mwa Kuchititsa Maphunziro A Baibulo Kwa Achichepere Ndi Achikulire Omwe. . . . Ali Wokhoza Kusonkhezera Anthu Ndi Kuwathandiza Kuzindikira Maluso Awo Enieni. M’kalasi, Aphunzitsi Anena Kuti Nthaŵi Zonse Ali Ndi Chiyambukiro Chabwino Pa Ena. Amatsogolera M’makambitsirano A M’kalasi Ndipo Ndi Mlankhuli Wogomeka Wamphamvu. . . .

“Matt Ali Mmodzi Wa Anyamata Abwino Kwambiri Amene Ndinachita Mwaŵi Kuwalangiza. Amakondedwa Ndi Kulemekezedwa Ndi Ausinkhu Wake Ndi Aphunzitsi. Umphumphu Wake Uli Wapamwamba Kwambiri.”

[Zithunzi patsamba 24]

Mboni za Yehova zili zokondweretsedwa ndi maphunziro makamaka kuti zikhale atumiki a Mulungu ogwira mtima kwambiri

[Bokosi patsamba 22]

Maphunziro Owonjezera

Nsanja ya Olonda ya November 1, 1992, inanena za Mboni za Yehova ndi utumiki wanthaŵi yonse kuti: “Chikhoterero chochuluka m’maiko ambiri nchakuti mlingo wa kuphunzira wofunikira kuti munthu azilandira malipiro oyenera tsopano ngwokwera kuposa mmene unaliri zaka zingapo zapitazo. . . . Nkovuta kupeza ntchito za malipiro oyenerera pambuyo pakumaliza maphunziro oyambirira ofunidwa ndi lamulo . . .

“Kodi mawuwa ‘malipiro oyenerera’ akutanthauzanji? . . . Malipiro awo anganenedwe kukhala ‘okwanira,’ kapena ‘okhutiritsa,’ ngati zimene amalandirazo zimawalola kukhala ndi moyo woyenerera ndi kuwapatsa nthaŵi yokwanira ndi mphamvu kuchita uminisitala wawo Wachikristu.”

Chotero Nsanja ya Olonda imeneyo inati: “Sipayenera kukhala malamulo ankhokera osonkhezera kapena kutsutsa maphunziro apamwamba.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena