Chaputala 3
Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere” Pakati pa Adani Ake
1, 2. (a) Kodi ndimawu otsazika otani amene Yesu ananena ku kagulu ka ophunzira ake? (b) Kodi mawu ameneŵa anafunikiritsa kutembenuka kwa dziko lonse iye asanayambe kulamulira monga “Kalonga wa Mtendere”?
MWAMSANGA asanakwere kumwamba zaka zoposa mazana 19 zapitazo, amene panthaŵiyo anali “Kalonga wa Mtendere,” wamtsogolo Yesu Kristu, ananena mawu otsazikana ndi kagulu ka ophunzira ake okhulupirika aŵa: “Mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera . . . wonani, ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.”—Mateyu 28:19, 20.
2 Kodi mawu a Yesu ameneŵa anafunsira kutembenuzidwa kwa dziko lonse “mapeto a dongosolo la zinthu” amene anayamba 1914 asanafike? Ayi. Lerolino, pafupi ndi mapeto a zaka za zana la 20 limeneli, dziko la mtundu wa anthu likali kutali ndi kutembenuzidwira kwa Yesu Kristu kukhala Mpulumutsi wake ndi Mfumu yoyenerera. Komabe, zimenezi sizinachedwetse kuchitidwa kwa zimene Yehova adaneneratu m’maulosi a Baibulo. Sichinali chifuno cha Mulungu konse kuti dziko lonse la anthu litembenuke Yesu Kristu asanayambe kulamulira monga “Kalonga wa Mtendere.” Mosiyana kotheratu, iye adanenedweratu kuyamba kulamulira pakati pa adani ake.
3. Kodi ndimotani mmene kugwira mawu Salmo 110 kwa Yesu kumasonyezera kuti iye akalamulira pakati pa adani?
3 Ngakhale pamene iye anali pansi pano padziko lapansi, Yesu Kristu anadziŵa chenicheni chimenechi. Mwamsanga imfa yake yophedwera chikhulupiriro isanachitike, iye anakangana ndi adani ake achipembedzo ndipo anagwira mawu Salmo 110. Timaŵerenga za zimenezi pa Luka 20:41-44 kuti: “Iye anati kwa iwo, Amanena bwanji kuti Kristuyo ndiye Mwana wa Davide? Pakuti Davide yekha ananena m’bukhu la Masalmo, Ambuye ananena kwa Ambuye wanga, Ukhale padzanja langa lamanja, kufikira ine ndikaika adani ako pansi pa mapazi ako. Chotero Davide anamtchula iye Ambuye, ndipo nanga ali mwana wake bwanji?”
4-6. (a) Kodi ndimotani mmene Salmo 2 mofananamo limasonyezera kuti Yesu sanafunikire kuyembekezera kutembenuzidwa kwa dziko asanayambe kulamulira kwake monga “Kalonga wa Mtendere”? (b) Kodi ndipanthaŵi iti pamene Salmo 2:7 linakwaniritsidwa?
4 Pamenepa, mwachiwonekere, Yesu Kristu, monga Mwana wa Davide, sanali kudzayamba kulamulira pambuyo pa kutembenuka kwadziko. Mmalo mwake, iye anali kudzayamba kulamulira pakati pa adani amene Yehova Mulungu potsirizira pake mwa nkhondo akawapangitsa kukhala chopondapo mapazi cha Mwana wake woikidwa pampando wachifumu. Mofananamo Salmo 2, m’mawu otsatira, likusonyeza chiyambi cha ulamuliro wake monga “Kalonga wa Mtendere” pakati pa adani:
5 “Aphokoseranji amitundu, nalingiliranji anthu zopanda pake? Adzikhazikitsa mafumu adziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, [Kristu Wake], ndi kuti, Tidule zomangira zawo, titaye nsinga zawo. Wokhala m’mwambayo adzaseka; Ambuye adzawanyoza. Pomwepo adzalankhula nawo mu mkwiyo wake, nadzawawopsa mu ukali wake: Koma Ine ndadzoza mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.
6 “Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi ine [Kristu], Iwe ndiwe Mwana wanga; ine lero ndakubala. [Salmo 2:7 linakwaniritsidwa pamene Yehova anaukitsa Mwana wake kwa akufa, motero anakhala Atate wosatha kwa Yesu. (Aroma 1:4)] Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako. Udzaŵathyola ndi ndodo yachitsulo; udzawaphwanya monga mbiya ya woumba. Tsono, mafumu inu, chitani mwanzeru: Langikani, oweruza inu a dziko lapansi. Tumikirani Yehova ndi mantha, ndipo kondwerani ndi chinthenthe. Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m’njira, ukayaka pang’ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira iye.”
7. Kodi ndikugwira mawu kwa Salmo 2 kotani kumene atumwi a Yesu Kristu anapanga pambuyo pa tsiku la Pentekoste?
7 Mogwirizana ndi kunena kwa Machitidwe 4:24-27, atumwi a Yesu Kristu anagwira mawu salmo lachiŵiri limeneli pambuyo pa tsiku la Pentekoste, 33 C.E. kuti: “Anakweza mawu kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, ndinu wolenga thambo lakumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri mmenemo; amene mwa mzimu woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu asokosera chifukwa chiyani? Nalingilira zopanda pake anthu? Anadzindandalitsa mafumu a dziko, ndipo oweruza anasonkhanitsidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye ndi Kristu wake. Pakuti zowonadi anasonkhanidwa m’mudzi muno Herode, ndi Pontiyo Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza.”
Kukawaniritsidwa Kwakukulu kwa Salmo 2
8. (a) Kodi ndiliti pamene kukwaniritsidwa koyamba kwa Salmo 2:1, 2 kunachitika? (b) Kodi nkuyambira liti pamene kukwaniritsidwa kwakukulu kwa Salmo 2 kwakhala kukuchitika?
8 Kukwaniritsidwa koyamba kwa mawu olosera amenewo a Salmo 2:1, 2 kunachitika m’chaka cha 33 cha zaka za zana loyamba. Kumeneku kunaphatikizapo munthuyo Yesu Kristu padziko lapansi. Iye anali atadzozedwa ndi mzimu woyera wa Yehova panthaŵi ya ubatizo wake ndi Yohane Mbatizi. Koma kukwaniritsidwa kwakukulu kwa Salmo 2 kwachitika chiyambire mapeto a Nthaŵi za Akunja m’chaka cha 1914. (Luka 21:24) Kwatsimikiziridwa mokwanira kuti “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu,” zimene zinayamba pa chiwonongeko choyamba cha mzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E., zinatha m’chaka cha 1914.a Pamenepo mitundu ya dziko lino, kuphatikizapo ya Dziko Lachikristu inachenjezedwa za imfa.
9. Kodi nchiyani chimene chinachitika pa chiwonongeko choyamba cha Yerusalemu ponena za Ufumu wa Mulungu monga momwe unaimiridwira ndi mzera wachifumu wa Mfumu Davide?
9 Pa chiwonongeko choyamba cha Yerusalemu, chochitidwa ndi Ababulo, Ufumu wa Yehova Mulungu pamtundu wa Israyeli, monga momwe unaimiridwira ndi mzera wachifumu wa Davide, unatha. Kuyambira pamenepo, Ayuda akuthupi sanakhale ndi mfumu ya mzera wa nyumba yachifumu ya Davide. Koma Ufumu wa Mulungu Wam’mwambamwamba m’manja mwa mbadwa ya Davide, amene Yehova anachita naye pangano la Ufumu wosatha m’mzera wake, sunali kudzakhala wosagwira ntchito kosatha padziko lapansi.
10, 11. (a) Kodi nchiyani chimene Mulungu kudzera mwa mneneri wake Ezekieli adanena ponena za mpando wachifumu wa Davide? (b) Kodi ndani amene anafika ndi “kuyenera” kwa kukhala pampando wachifumu wa Davide? (c) Kodi nchiyani chimene khamu la Ayuda lidanena pamene iye anadzipereka kukhala woloŵa nyumba walamulo?
10 Mwamsanga chiwonongeko chake choyamba chisanachitike, Yehova anachititsa mneneri wake Ezekieli kulunjikitsa mawu aŵa kwa mfumu ya Yerusalemu wakale: “Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israyeli, amene lafikira tsiku lako, nthaŵi ya mphulupulu yotsiriza; atero Ambuye Yehova, Chotsa zilemba, vula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza chopepuka, tchepsa chokwezeka. Ndidzagubuduza gubuduza gubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa iye.”—Ezekieli 21:25-27.
11 Iye amene ali “mwini chiweruzo” anadza monga munthu Yesu Kristu, ndipo mzera wake wobadwiramo wa Davide walembedwa pa Mateyu 1:1-16 ndi pa Luka 3:23-31. Kaŵirikaŵiri iye anadziŵika kukhala “Mwana wa Davide.” Patsiku la kukwera kwake kwa chilakiko kuloŵa m’Yerusalemu, atakwera pabulu mokwaniritsa ulosi, khamu lochita chidwi la Ayuda limene linamperekeza ndi atumwi ake linafuula mokondwera kuti: “Hosana kwa Mwana wa Davide! Wolemekezeka ndiye wakudza m’dzina la Ambuye, Hosana m’Kumwambamwamba!”—Mateyu 21:9.
“Mwana wa Davide” Ayikidwa pa Mpando Wachifumu Kumwamba
12. Pamene nthaŵi za Akunja zinatha mu 1914, kodi nkuti kumene Kristu, monga woloŵa nyumba wachikhalire wa Davide anaikidwa pa mpando wachifumu?
12 Zaka 2 520 zakuti Akunja aponderezere pansi Ufumu wa Mulungu umene unali mu mzera wa nyumba ya Davide zinatha mu 1914. Pamenepo nthaŵi inafika yakuti Yesu Kristu, “Mwana wa Davide,” aikidwe pampando wachifumu, osati pampando wachifumu wa pansi pano, koma m’miyamba yokwezeka kudzanja lamanja la Yehova Mulungu!—Danieli 7:9, 10, 13, 14.
13. (a) Kodi nkuyambira chaka chiti pamene chaka cha 1914 chinatchulidwa pasadakhale kukhala mapeto a Nthaŵi za Akunja, ndipo ndi ayani? (b) Kodi nchiyani chimene chinali mkhalidwe wa mitundu padziko lapansi kulinga kwa “Mwana wa Davide” woikidwa pampando wachifumu chatsopanoyo?
13 Kuyambira 1876 ndi awo amene anagwirizanitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society anasonya mtsogolo ku chaka chosaiŵalika chimenecho. Koma mitundu ya dziko lapansi, ngakhale ya Dziko Lachikristu, inakana kuchivomereza kukhala nthaŵi yakuti iwo atembenuzire maufumu awo a padziko lapansi kwa “Mwana wa Davide” woikidwa pampando wachifumu chatsopanoyo. Iwo sanavomereze kuti iye anali ndi kuyenera kopatsidwa ndi Mulungu kukhala ndi ulamuliro padziko lonse lapansi, limene liri chopondapo mapazi cha Mulungu. (Mateyu 5:35) Iwo anasonyeza kukana kwawo kotheratu Mfumu yoyenererayo mwa kuchita nkhondo ya dziko yoyamba.
14. (a) Ndi kuulika kwa Nkhondo Yadziko I, kodi ndimkhalidwe wotani umene mitundu inasonyeza kulinga kwa Akristuwo ogwirizana ndi Watch Tower Society? (b) Chifukwa cha zimenezi, kodi mkhalidwe wa dziko lonse umatanthauzanji?
14 M’mitundu yonse yochita nkhondo, Akristu odzipatulira amene anali ogwirizana ndi Watch Tower Society anatsenderezedwa kwambiri kuti asiye chitsimikizo chawo cha kukhala aufulu ku liwongo la mwazi. Panthaŵiyo iwo sankamvetsetsa mokwanira chofunika cha uchete Wachikristu. Ulosi wa “Mwana wa Davide,” Yesu Kristu, kwa ophunzira ake wonena za ‘mapeto a dongosolo la zinthu’ unakwaniritsidwa momvetsa chisoni: “Amitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Udani umenewu sunathe chiyambire mapeto a Nkhondo Yadziko I. Chifukwa cha maumboni otsimikizirika a mbiri yamakono ameneŵa, kodi mkhalidwe wa dziko lonse ukutanthauzanji? Ichi: “Kalonga wa Mtendere” akulamulira pakati pa adani amene ali pompano padziko lapansi!
15. Kodi nchiyani chimene chinachitika kwa Satana Mdyerekezi ndi magulu ake a ziŵanda pamene nkhondo inaulika kumwamba, ndipo kodi ndi m’chaka chiti pamene zotulukapo ziyenera kukhala zitamalizidwa?
15 Mulungu Wamphamvuyonse anachititsa kubadwa kwa Ufumu Waumesiya panthaŵi yake yoikidwiratu mosasamala kanthu za adani onse amene anali kumwamba ndi padziko lapansi. Chivumbulutso 12:1-9 chimasonyeza kuti pambuyo pa kubadwa kwa ‘mwana wamwamuna’ Ufumuwo m’miyamba kuchokera m’mimba mwa gulu la Yehova longa mkazi, kunena kwake titero, nkhondo inaulika mwamsanga kumwamba kwenikweniko. Miyamba yoyera siinalinso malo a chinjoka chophiphiritsira, Satana Mdyerekezi, ndi angelo ake auchiŵanda. M’nkhondo imeneyi, mosawoneka kumaso aumunthu, “Mwana wa Davide” Waufumu wopatsidwa ulamuliroyo anamenya nkhondo molakika natulutsa Satana Mdyerekezi ndi magulu ake a ziŵanda kuchokera kumiyamba ndi kuwabindikiritsira kuchigawo cha mbulumbwa yathu yadziko lapansi. Mwachiwonekere kutsitsidwira pansi kumeneku kwa magulu aziŵanda kunakwaniritsidwa mokwanira podzafika 1918, chaka chimene Nkhondo Yadziko I inatha.
Mdyerekezi Wotsitsidwayo, Achita Nkhondo
16, 17. (a) Kodi Satana Mdyerekezi wotsitsidwayo akuchita nkhondo ndi ayani? (b) Kodi amagwiritsira ntchito ndani kuchita nkhondo imeneyi?
16 Satana Mdyerekezi wotsitsidwayo, chinjoka chophiphiritsira, tsopano ngwaukali mwapadera kulinga kugulu la Yehova Mulungu longa mkazi. (Chivumbulutso 12:17) Motero iye mwankhalwe akuchita nkhondo motsutsana ndi otsalira obadwa ndi mzimu a Akristu odzipatulira amene ali ndi umboni wakuti iro ndiro amayi wawo wauzimu.—Agalatiya 4:26.
17 Satana amathiranso nkhondo pa “nkhosa zina,” zimene momvera zimagwira ntchito ndi otsalira odzozedwa m’kuchitira umboni kubadwa kwa Ufumu. (Yohane 10:16) Sikokha kuti iye amagwiritsira ntchito magulu ake a ziŵanda zotsitsidwazo, zimene tsopano ziri m’gawo la padziko lapansi, komanso amagwiritsira ntchito mbali yowoneka ya gulu lake kuchita nkhondo imeneyi pa otsalira ndi “nkhosa zina.”
18. (a) Ngakhale kuli kwakuti Mdyerekezi mwankhalwe amachita nkhondo ndi otsalira odzozedwa ndi atsamwali awo, kodi ndinyonga yotetezera yotani imene ali nayo? (b) Kodi ndimbali iti ya ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere” imene iri pafupi kutha?
18 Kulamulira kwa “Kalonga wa Mtendere” pakati pa adani ake tsopano padziko lapansi kuli pafupi kutha. Iye walamulira bwino kwambiri. Angelo ake opatulika okhulupirikawo amaimirira mwachidwi usana ndi usiku, ali okonzekera kulandira malangizo a mfumu kuchokera kwa iye ndi kuchitapo kanthu mofulumira. Iwo amatumikira monga mphamvu yoteteza kwa otsalira odzozedwa ndi atsamwali awo, a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” pamene ameneŵa apitirizabe kutumikira zinthu za ufumu mkati mwa nthaŵi yofulumira kutha imeneyi pamene “Kalonga wa Mtendere” alamulira pakati pa adani ake.—Chivumbulutso 7:9.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka maumboni, wonani bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, tsamba 138-41, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.