Kuthetseratu Nkhani ya Chilengedwe Chonse
‘Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake.’—SALMO 110:5.
1, 2. M’chaka cha 70 C.E., kodi nchochitika chiti chimene chingakhale chinabweretsa chikaikiro pa kulamulira kwa chilengedwe chonse kwa Yehova Mulungu, koma kodi panthaŵiyo, nkwandani kumene chiyanjo chake chinasinthidwira?
ULAMULIRO wa chilengedwe chonse wa Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi ndiwo nkhani yaikulu pamaso pa anthu ndi angelo. Posachedwapa, nkhaniyo idzathetsedweratu, koma kwa zaka mazana ambiri adani a Yehova atokosa ulamuliro wake. Ndithudi, chiwonongeko cha mu 70 C.E. cha mzinda wa Yerusalemu limodzi ndi kachisi wake woperekedwa kwa Yehova chingakhale chinabweretsa chikaikiro pa ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Mlengiyo. Komabe, panali chifukwa chodalirika chimene Yehova sanasankhire kukhala Mulungu wankhondo wa Israyeli wakuthupi panthaŵiyo.
2 Kodi chifukwacho chinali chiti? Panthaŵiyo Yehova Mulungu anali atasinthira chiyanjo chake ku mtundu watsopano, Israyeli wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” monga mmene mtumwi Paulo amautchera mpingo wa Yesu Kristu. (Agalatiya 6:16) Komabe, kufikira lero, mkati mwa Nyengo yotchedwa Yachikristu, Yehova sanamenyerepo nkhondo Israyeli wauzimu monga Mulungu wankhondo m’njira imene anamenyera Israyeli wakuthupi wokhala pansi pa pangano la Chilamulo cha Mose. Iye panthaŵi ina analoladi asilikali Achiroma, osonkhezeredwa ndi Ayuda, kuphera Yesu Kristu pamtengo wozunzira pa Kalivali. Ichi chinachitika zaka 37 chiwonongeko chachiŵiri cha Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma chisanachitike, mu 70 C.E.
3, 4. Kuyambira m’masiku a Mose mpaka kukafika kwa Mfumu Hezekiya, kodi Mulungu anadzisonyeza yekha motani kukhala munthu wankhondo, koma ponena za Aisrayeli auzimu, kodi nchiyani chomwe chakhala chowona ponena za kumenya kwake nkhondo ndi kwawo?
3 Kuchokera m’masiku a mneneri Mose mpaka kudzafika pa kulamulira kwa Mfumu Hezekiya wa ku Yerusalemu, Yehova Mulungu anachitira nkhondo mtundu wa Israyeli mozizwitsa, ndipo Aisrayeli anachita nkhondo pansi pake ndi zida zakupha. (Deuteronomo 1:30; 3:22; 20:3, 4; Yoswa 10:42) Koma sizinachitikepo tero ndi Israyeli wauzimu! Kuchokera pa imfa ya Yesu Kristu kunja kwa Yerusalemu mpaka kudzafika m’Nyengo yathu Yachisawawa, Mulungu wankhondo ameneyu sanasankhe kuchita nkhondo yakuthupi kaamba ka Israyeli wa Mulungu. Mofananamo, iye sanalamulirepo Aisrayeli auzimu opanga mpingo Wachikristu kumenya nkhondo ndi zida zankhondo zakuthupi. Akristu ali ndi mtundu wina wa nkhondo yolimbana nayo.
4 Mogwirizana ndi ichi, mmodzi wa ankhondo otchuka a chikhulupiriro Chachikristu analembera Akristu anzake pa Korinto, Grisi kuti: ‘Pakuti zida zankhondo yathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga; ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziŵitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse ku kumvera kwa Kristu; ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.’ (2 Akorinto 10:4-6) Kuchiyambiyambi m’kalata imodzimodziyo, Paulo analankhula za “zida zachilungamo ku dzanja lamanja ndi lamanzere.”—2 Akorinto 6:7, NW; onaninso Aefeso 6:11-18.
Yehova Ndiye Adzamenya Nkhondo pa Armagedo
5. M’munda wa Getsemane, kodi ndi malo otani amene Yesu anatenga ponena za kugwiritsira ntchito zida zakuthupi m’kudzichinjiriza, ndipo kodi ndi njira ya kachitidwe yotani imene ophunzira ake anatenga?
5 Yesu Kristu, pamene anali padziko lapansi, sanatembenukirepo ku zida zakupha kuti adzichinjirize. Pausiku wa kuperekedwa kwake m’munda wa Getsemane, wophunzira wake wodzipereka Simoni Petro anasolola lupanga ndi kudula khutu la kapolo wa wansembe wamkulu Wachiyuda. Koma Yesu anabwezeretsa khutulo mozizwitsa ndikuti: ‘Pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi lupanga. Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri? Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?’ (Mateyu 26:52-54) Polingalira zonsezi, atsanziri owona a Mwana wa Mulungu wodzipereka nsembe amasunga uchete wawo, ponse paŵiri mwachindunji ndi mosakhala mwachindunji, m’nkhani ya nkhondo yadziko.—Yohane 17:16; 18:36.
6. Pankhondo yatsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse pa Armagedo, kodi ndi malo otani amene Mboni za Yehova zidzatenga?
6 Chotero, pamenepa, ilekeni mitundu idziŵitsidwe kuti mkati mwa “nkhondo ya tsiku lalikuru la Mulungu, Wamphamvuyonse” pa ‘malo otchedwa m’Chihebri Harmagedo,’ Mboni za Yehova sizidzakhalamo ndi phande m’kumenyanako. Izo zidzaisiira m’manja mwa Mulungu wankhondo, “Yehova wa makamu,” limodzi ndi mabungwe a angelo pansi pa ulamuliro wa Yesu Kristu.—Chibvumbulutso 16:14-16; 19:11-21; Salmo 84:12.
Yehova ali Pafupi Kupitiriza ndi Ntchito Yake Yankhondo
7. Monga Mulungu wankhondo, kodi Yehova anadzadziŵika ndi dzina laulemu lotani, ndipo kodi iye adakadziŵikabe motero?
7 Mulungu wa Israyeli wakale anadzadziŵika ndi kutchedwa Yehova tseva·ʼohthʹ, kapena Yehova wa makamu. (1 Samueli 1:3, 11) Pa Aroma 9:29 (King James Version) mtumwi Paulo Wachikristu akulozera ku Yesaya 1:9 ndikulemba kuti: “Ngati Ambuye wa Sabaoti [Makamu] sanatisiyira ife mbewu, tikadakhala monga Sodoma, ndipo tikadafanana ndi Gomora.” Ndiponso, wophunzira Wachikristu Yakobo analemba kuti: “Mafuulo a osengawo adalowa m’makutu a Ambuye wa sabaoti.” (Yakobo 5:4, KJ; American Standard Version) Chotero Paulo ndi Yakobo anatcha Mulungu kukhala Yehova wa makamu m’zaka za zana loyamba la Nyengo yathu Yachisawawa. M’zaka mazana 18 otsatira, Mulungu sanalowepo m’nkhondo yakuthupi yomenyera Israyeli wauzimu, Israyeli wa Mulungu, m’njira imene anachitira ndi Israyeli wakale, komabe iye adakali Yehova wa makamu.
8-10 (a) Kodi ndani analamulira nkhondo m’mwamba, ndipo kodi nchifukwa ninji Mikayeli anali woyeneretsedwa koposa kuchita nkhondoyo? (b) Kodi nkhondoyo inali ndi chotulukapo chotani kumwamba, ndipo kodi patsala nthaŵi yotani nkhondo yatsiku lalikulu la Yehova isanadze?
8 Pakubadwa kwa Ufumu Waumesiya mu 1914 pamapeto pa “nthaŵi za Akunja,” nkhondo inaulika mmalo akumwamba a Yehova Mulungu. (Luka 21:24, KJ) Kodi ndani amene analamulira nkhondoyo? Yehova Mulungu iyemwini. Iye anatumiza Mwana wake wovekedwa ufumu kunkhondo m’dzina lakuti Mikayeli chifukwa chakuti Ameneyu ngoyenerera kwenikweni kuyankha funso lophatikizidwa m’dzinalo, lakuti, “Afanana ndi Mulungu Ndani?” Mikayeli anatulukira mofulumira monga woimira nkhondo wa Yehova wa makamu.
9 Mwatsatanetsatane, timaŵerenga pa Chibvumbulutso 12:7-10 kuti: ‘Ndipo munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi. Ndipo ndinamva mawu aakulu m’Mwamba, nanena, Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu.’
10 Panthaŵi ino, zaka zoposa 70 pambuyo pankhondoyo m’mwamba, ‘kanthaŵi’ kokha nkomwe katsala nkhondo ya tsiku lalikulu la Yehova isanaulike ndi pamene Mulungu adzadzisonyeza yekha mochitisa chidwi kukhala Yehova wa makamu kumbadwo wamakonowu wa anthu.—Chibvumbulutso 12:12; Zekariya 14:3.
Wankhondo wa Kuyeretsedwa kwa Yehova
11. Kodi ndi nthaŵi yoikika iti imene otsalira a kagulu kankhosa ndi khamu lalikulu akuyembekezera, ndipo kodi iwo panthaŵiyo adzafuula mokondwera ndi chiyani?
11 Pansi pa kuuziridwa, Mfumu yanzeru Solomo wa Israyeli wakale analemba kuti: ‘Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chirichonse cha pansi pathambo . . . mphindi yankhondo ndi mphindi ya mtendere.’ (Mlaliki 3:1-8) Padziko lapansi pano ophunzira a Mfumu yolamulirayo yomwe iri “wakuposa Solomo” akuyembekezera nthaŵi ndi nyengo pamene Iye adzatsogolera angelo olakika akumwamba kukachita nkhondo pa Harmagedo. (Mateyu 12:42; Chibvumbulutso 19:11-16) Pamenepo iye ‘adzawalamulira [amitundu] ndi ndodo yachitsulo,’ nadzaŵathyola ‘ndi ndodo yachitsulo.’ (Chibvumbulutso 19:15; Salmo 2:9) Ophunzira ake osunga mtendere, otetezeredwa adzakondwa chotani nanga ndi kuwapulumutsa kwake kochititsa manthaku! Uku kudzaphatikizapo onse aŵiri otsalira a “kagulu kankhosa” a olowa naye Ufumu ndi ‘khamu lalikulu’ la “nkhosa [zake] zina” amene ali ndi chiyembekezo cha kuloŵa Paradaiso wa dziko lapansi pansi pa ulamuliro wake wamtendere wa zaka chikwi. (Luka 12:32; Chibvumbulutso 7:9-17; Yohane 10:16) Mokondwera, “mu mthunzi wa Wamphamvuyonse,” iwo adzakondwera mofuula ndi chilakiko cha Mfumu ndi Mbusa, Yesu Kristu, m’kuyeretsedwa kwa ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Yehova Mulungu.—Salmo 91:1.
12. Kodi nkhondo ya mitundu ikuyandikira kuchokera kuti, ndipo ndi chotulukapo chotani mogwirizana ndi Salmo 68:1, 2?
12 Popanda kukuza mawu ndi mkamwa, tsopano kunganenedwe kuti nkhondo yochokera ku dziko lina losakhala la anthu ndi yophatikizapo kugwiritsiridwa ntchito kwa zida zosaphonya nkomwe kuposa mabomba ake a nyukliya iri pafupi kugwera mitundu yonse ya padziko lapansi, kaya ikhale mkati kapena kunja kwa gulu la Mitundu Yogwirizana. Mvetserani: ‘Auke Mulungu, abalalike adani ake; awonso akumuda athawe pamaso pake. Muwachotse monga utsi uchotseka; monga phula lisungunuka pamoto, aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.’—Salmo 68:1, 2.
13. Pamene kukonzekera nkhondo kupitiriza, kodi nkwandani kumene mawu a Salmo 45:1-6 tsopano akugwira ntchito panthaŵi yake kwenikweni?
13 Kukonzekera nkhondo ya nkhondo zonseyo tsopano kukuchitidwa. Monga Wankhondo wamkulu wa Mulungu, Womenyera kuyeretsedwa kwa Yehova ameneyu akutchulidwa motere m’mawu otsatirawa olembedwa mouziridwa ndi chiŵalo cha mtundu wa Israyeli: ‘Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu; Anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu: Chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha. Dzimangireni lupanga lanu m’chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. Ndipo pindulani, m’ukulu wanu yendani, kaamba ka chowonadi ndi chifatso ndi chilungamo: Ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa. Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu. Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthaŵi zonse zomka muyaya: Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.’—Salmo 45:1-6.
Amitundu Achita Upo Pamodzi Motsutsana Naye Yehova
14, 15. Pambuyo pa kumasulidwa m’kubindikiritsidwa, kodi ndi mawu ati ochokera pa Salmo 2 amene atumwi anawagwira mawu kukhala akukwaniritsidwa, ndipo kodi anam’pempha chiyani Mulungu?
14 Mwamsanga pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa mpingo Wachikristu patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., Akristu odzozedwa anazindikira kugwiritsiridwa ntchito kwa Salmo 2:1, 2. Lemba iri limaŵerengedwa motere: ‘Aphokoseranji amitundu, nalingiriranji anthu zopanda pake? Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, kutsutsana naye Yehova, ndi wodzozedwa wake.’ Pambuyo pakuvutika koyamba ndi kusautsidwa kwa atumwi a Wodzozedwa wa Yehova kochitidwa ndi adani Achiyuda, iwo anaphatikananso ndi Akristu anzawo ndipo kenaka anagwira mawu awa a Salmo 2 olembedwa ndi Mfumu Davide. Machitidwe 4:23-30 akusimba nkhaniyo, akuti:
15 ‘Ndipo m’mene anamasulidwa, anadza kwa anzawo a iwo okha, nawauza zirizonse oweruza ndi akulu adanena nawo. Ndipo m’mene adamva, anakweza mawu kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse ziri m’menemo; amene mwa mzimu woyera, pakamwa pa kholo lathu Davide mtumiki wanu, mudati, Amitundu anasokosera chifukwa chiyani? Nalingirira zopanda pake anthu? Anadzindandalitsa mafumu a dziko, ndipo oweruza anasonkhanidwa pamodzi, kutsutsana ndi Ambuye, ndi Kristu wake. Pakuti zowonadi anasonkhanidwa m’mudzi muno Herode, ndi Pontiyo Pilato yemwe pamodzi ndi amitundu ndi anthu a Israyeli kumchitira choipa Mwana wanu wopatulika Yesu amene munamdzoza; kuti achite zirizonse dzanja lanu ndi uphungu wanu zidaweruziratu zichitike. Ndipo tsopano Ambuye, penyani mawu awo akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse, m’mene mutambasula dzanja lanu kukachiritsa; ndi kuti zizindikilo ndi zozizwa zichitidwe mwa dzina la Mwana wanu wopatulika Yesu.’
16, 17. (a) M’mbiri yonse ya anthu, kodi pali chirichonse chimene chachitika cholingana ndi chimene chinayamba kuchitika mu 1914? Longosolani. (b) Kodi ndi njira ya kachitidwe yotani imene mitundu ikupitirizabe kutenga, akumafulumiza Yehova Mulungu kulembanji, ponena za ‘buku la nkhondo zake’?
16 Komabe, ponena za kusokosera kwa amitundu, kugwirizana kwa mafumu, kupanga upo kwa atsogoleri a ndale zadziko motsutsana ndi Yehova ndi Wodzozedwa wake, Yesu Kristu, kodi nchiyani m’mbiri yonse ya anthu chimene chingalingane ndi chomwe chinayamba zaka 76 zapitazo mu 1914? Chimenecho sichinali chaka chokha pamene nkhondo yoyamba yadziko yosachitikapo m’kukhalapo kwa munthu inaulika koma chinali makamaka chaka chimene nthaŵi za Akunja, “nthaŵi zoikidwiratu za mitundu,” zinatha! (Luka 21:24, NW) Salmo 2 linakwaniritsidwadi kwakukulu kuyambira m’chaka chimenecho.
17 Pamapeto panthaŵi za Akunja mu 1914, palibe mtundu—osati ngakhale mitundu yotchedwa ya Chikristu Chadziko, amene nzika zawo zambiri zimadzilingalira kukhala Aisrayeli auzimu—umene unafuna kulandira Wodzozedwa wa Yehova, Yesu Kristu, pampando wachifumu wa kulamulira dziko lapansi. Ndipo tsopano, zaka 71 pambuyo pakuti “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” inayamba ‘kulalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse,’ kuyambira mu 1919 kunka mtsogolo, mitundu yokhala mkati ndi kunja kwa Chikristu Chadziko kunena mwa gogogo sidzatamanda Mfumu ya Yehova yolengezedwa kwanthaŵi yaitaliyi ndi kulumbira kugwirizana nayo mwakukana ulamuliro wawo padziko lapansi. (Mateyu 24:14, NW) Mmalo mwake, pomalizira pake afika panthaŵi ndi mkhalidwe pamene iwo akumfulumiza Yehova, kunena kwake titero, kulemba mapeto aakulu “m’buku la Nkhondo za Yehova.”—Numeri 21:14.
Kulakika Kwaulemerero kwa Wankhondo wa Mulungu
18. Kodi tayanjidwa ndi kachitidwe kotani kumbali ya Yehova, ndipo kodi ndani amene adzakhala kumbali yake, kunena kwake titero, kukwaniritsa Salmo 110?
18 Pamenepo, chitani nkhondo, Yehova inu wa makamu, ndi Mwana wanu wachifumu, Yesu Kristu, kumbali kwanu! Nkwa iye kumene mawu aulosi awa analembedwera: ‘Chitani ufumu pakati pa adani anu. Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. Adzaweruza mwa amitundu, adzadzaza dziko ndi mitembo; adzaphwanya mitu m’maiko ambiri.’—Salmo 110:2, 5, 6.
19. Ponena za nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse yomwe iri patsogolopa, kodi ndi pemphero liti limene tikupereka kwa iye mmalo mwa khamu lalikulu la nkhosa zina?
19 O Yehova wa makamu, lolani atumiki anu okhulupirika a padziko lapansi akhale mboni zokondwera ndi kulakika kwanu kosayerekezeka kupyolera mwa Mfumu yanu yankhondo, Yesu Kristu, panthaŵi yankhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse pamalo otchedwa m’Chihebri Harmagedo! (Chibvumbulutso 16:14) Pambali pa otsalira a Aisrayeli auzimu oona, lolani khamu lalikulu la onga nkhosa omwe ‘anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa atuluke m’chisautso chachikulu’ mokwezeka kuti akhale mboni zanu za padziko lapansi kosatha! (Chibvumbulutso 7:14) Pansi pa chisamaliro chanu chachikondi, aloleni apulumuke popanda kufa kuloŵa m’dziko lopanda nkhondo la Mwana wanu wolakika, amene adzalamulira padziko lapansi loyeretsedwa lomwe lidzasandulizidwa kukhala paradaiso wokongola, mogwirizana ndi chifuno chanu choyambirira. Aloleni akhale umboni wooneka ndi maso kwa oukitsidwa onse kulemekeza ulamuliro wanu wolungama wa chilengedwe chonse! Tikuthokozani kuti panthaŵiyo mudzakhala mutathetseratu nkhani ya chilengedwe chonse, inde, kosatha!
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi pali nkhani yaikulu iti pamaso pa anthu ndi angelo?
◻ Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kumenyera nkhondo Israyeli wakale kwa Yehova ndi Israyeli wauzimu?
◻ Pa Armagedo, kodi ndi malo otani amene Mboni za Yehova zidzatenga, ndipo chifukwa ninji?
◻ Kodi ndiliti pamene Salmo 2:1, 2 linakwaniritsidwa mowonekera?
◻ Kodi nkhani ya chilengedwe chonse idzathetsedweratu motani?
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
‘Khamu lalikulu’ lidzakondwerera Mfumu ndi Mbusa wolakika wa Mulungu