Yehova Aŵerengeretu Bwino Mlandu Wanu
“Mundikumbukire . . . Mulungu wanga, . . . Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.”—NEHEMIYA 13:22, 31.
1. Kodi nchiyani chimene chimathandiza awo amene ali odzipatulira kwa Mulungu kudziŵerengera bwino mlandu wawo kwa Yehova?
ATUMIKI a Yehova ali ndi thandizo lonse limene amafuna pa kudziŵerengera bwino mlandu wawo kwa iye. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ali ndi unansi wapafupi ndi Mulungu monga mbali ya gulu lake lapadziko lapansi. Wavumbula zifuno zake kwa iwo, ndipo wawapatsa thandizo ndi chidziŵitso chauzimu mwa mzimu wake woyera. (Salmo 51:11; 119:105; 1 Akorinto 2:10-13) Polingalira mikhalidwe yapadera imeneyi, mwachikondi Yehova amafuna kuti atumiki ake apadziko lapansi adziŵerengere mlandu kwa iye wa zimene ali ndi zimenenso amakwaniritsa kuchita ndi nyonga yake ndi thandizo la mzimu wake woyera.
2. (a) Kodi Nehemiya anadziŵerengera bwino motani mlandu wa iye mwini kwa Mulungu? (b) Kodi Nehemiya anamaliza buku la m’Baibulo la dzina lake ndi pempho lotani?
2 Mwamuna wina amene anadziŵerengera bwino mlandu wake kwa Mulungu anali Nehemiya, wopereka chikho wa Mfumu yachiperisiya Aritasasta (Longimanus). (Nehemiya 2:1) Nehemiya anakhala bwanamkubwa wa Ayuda ndipo anamanga malinga a Yerusalemu akumayang’anizana ndi adani ndi ngozi. Pokhala ndi changu cha kulambira koona, anachirikiza Chilamulo cha Mulungu ndi kusonyeza nkhaŵa kaamba ka oponderezedwa. (Nehemiya 5:14-19) Nehemiya analimbikitsa Alevi kudziyeretsa nthaŵi zonse, kulonda zipata, ndi kupatula tsiku la Sabata. Motero anatha kupemphera kuti: “Mundikumbukire ichinso, Mulungu wanga, ndi kundileka monga mwa chifundo chanu chachikulu.” Moyenereranso, Nehemiya anamaliza buku lake louziridwa ndi Mulungu ndi pempho lakuti: “Mundikumbukire, Mulungu wanga, chindikomere.”—Nehemiya 13:22, 31.
3. (a) Kodi mungafotokoze motani munthu amene amachita zabwino? (b) Kodi kulingalira za njira ya Nehemiya kungatichititse kudzifunsa mafunso ati?
3 Munthu amene amachita zabwino ngwaukoma ndipo amachita zinthu zowongoka zimene zimapindulitsa ena. Nehemiya anali munthu wotero. Anali wowopa Mulungu mwaulemu ndi changu chachikulu pa kulambira koona. Ndiponso, anali woyamikira chifukwa cha mwaŵi wake mu utumiki wa Mulungu ndipo anadziŵerengera bwino kwambiri mlandu wake kwa Yehova. Kulingalira za njira yake kungatichititse kudzifunsa kuti, ‘Kodi ine ndimaona motani mwaŵi ndi mathayo amene ndapatsidwa ndi Mulungu? Kodi ndi mlandu wotani umene ndikudziŵerengera kwa Yehova Mulungu ndi kwa Yesu Kristu?’
Chidziŵitso Chimatichititsa Kudziŵerengera Mlandu
4. Kodi Yesu anatuma otsatira ake kuchita ntchito yotani, ndipo kodi aja amene anali “ofuna moyo wosatha” anachitanji?
4 Yesu anatuma otsatira ake motere: “Mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Ophunzira anafunikira kupangidwa mwa kuwaphunzitsa. Motero awo amene anaphunzitsidwa ndi amene ‘anafuna moyo wosatha’ akanatha kubatizidwa, monga momwe Yesu anachitira. (Machitidwe 13:48, NW; Marko 1:9-11) Chikhumbo chawo cha kusunga zinthu zonse zimene analamula chinali chochokera mumtima. Anali kufikira pa kudzipatulira mwa kuloŵetsa ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu.—Yohane 17:3.
5, 6. Kodi tiyenera kumvetsa motani Yakobo 4:17? Perekani chitsanzo cha kugwira kwake ntchito.
5 Pamene chidziŵitso chathu cha Malemba chizama, mpamenenso maziko a chikhulupiriro chathu amakhala abwino kwambiri. Panthaŵi imodzimodziyo, kudziŵerengera mlandu kwathu kwa Mulungu kumakhala kokulirapo. Yakobo 4:17 amati: “Kwa iye amene adziŵa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo.” Mawu ameneŵa mwachionekere ndiwo kugamula kwa zimene wophunzira Yakobo anali atangonena kumene ponena za kudzitamandira m’malo mwa kudalira Mulungu kotheratu. Ngati munthu amadziŵa kuti sangathe kuchita chilichonse chokhalitsa popanda thandizo la Yehova komano nachita mosayenera, limenelo ndi tchimo. Koma mawu a Yakobo angagwirenso ntchito pa machimo a kunyalanyaza zinthu. Mwachitsanzo, m’fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi, mbuzi zikutsutsidwa osati chifukwa cha ntchito zoipa, koma chifukwa cha kusathandiza abale ake a Kristu.—Mateyu 25:41-46.
6 Mwamuna wina amene ankachititsidwa phunziro la Baibulo ndi Mboni za Yehova ankangopita patsogolo mwauzimu pang’ono, mwachionekere chifukwa chakuti sanaleke kusuta fodya, ngakhale kuti anadziŵa kuti anayenera kuchita motero. Mkulu wina anampempha kuti aŵerenge Yakobo 4:17. Atakambitsirana za tanthauzo la lembali, mkuluyo anati: “Ngakhale kuti simunabatizidwe, ndinu woyenera kudziŵerengera mlandu ndipo muyenera kusenza thayo la chosankha chanu.” Mwamwaŵi, mwamunayo anachitapo kanthu, analeka kusuta fodya, ndipo posakhalitsa anayenerera ubatizo kuti asonyeze kudzipatulira kwake kwa Yehova Mulungu.
Odziŵerengera Mlandu Kaamba ka Utumiki Wathu
7. Kodi ndi iti imene ili njira imodzi yosonyezera chiyamikiro chathu kaamba ka “kumdziŵadi Mulungu”?
7 Chikhumbo chathu cha mumtima chiyenera kukhala cha kukondweretsa Mlengi wathu. Njira imodzi yosonyezera chiyamikiro chathu kaamba ka “kumdziŵadi Mulungu” ndiyo kuchita ntchito imene tinatumidwa ya kupanga ophunzira a Mwana wake, Yesu Kristu. Imeneyinso ndi njira yosonyezera chikondi chathu kwa Mulungu ndi kwa mnansi wathu. (Miyambo 2:1-5; Mateyu 22:35-40) Inde, kudziŵa kwathu Mulungu kumatipangitsa kukhala odziŵerengera mlandu kwa iye, ndipo tifunikira kuona anthu anzathu monga oyembekezeredwa kukhala ophunzira.
8. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Paulo anamva kukhala ndi mlandu kwa Mulungu kaamba ka utumiki wake?
8 Mtumwi Paulo anadziŵa kuti kuvomereza ndi mtima wonse ndi kumvera uthenga wabwino kumachititsa chipulumutso, pamene kuli kwakuti kuukana kungabweretse chiwonongeko. (2 Atesalonika 1:6-8) Chotero anamva kukhala wamlandu kwa Yehova kaamba ka utumiki wake. Kwenikweni, Paulo ndi mabwenzi ake anayamikira utumiki wawo kwambiri kwakuti anapeŵa mosamalitsa ngakhale kupereka lingaliro lakuti anali kupanga nawo phindu la ndalama. Ndiponso, mtima wa Paulo unamsonkhezera kunena kuti: “Ngati ndilalikira uthenga wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.”—1 Akorinto 9:16.
9. Kodi ndi ngongole yofunika yotani imene Akristu onse afunikira kuilipira?
9 Popeza kuti ndife atumiki a Yehova odzipatulira, ‘tagwidwa ndi chikakamizo cha kulalikira uthenga wabwino.’ Ndi ntchito yathu kulalikira uthenga wa Ufumu. Tinalandira thayo limenelo pamene tinadzipatulira ife eni kwa Mulungu. (Yerekezerani ndi Luka 9:23, 24.) Ndiponso, tili ndi mangaŵa oti tilipire. Paulo anati: “Ine ndili wamangawa wa Ahelene ndi wa akunja, wa anzeru ndi wa opusa. Chotero, momwe ndingakhoze ine, ndilikufuna kulalikira uthenga wabwino kwa inunso a ku Roma.” (Aroma 1:14, 15) Paulo anali wamangaŵa chifukwa chakuti anadziŵa kuti linali thayo lake kuti alalikire kotero kuti anthu amve uthenga wabwino ndi kupulumutsidwa. (1 Timoteo 1:12-16; 2:3, 4) Motero iye anagwiritsa ntchito kuti akwaniritse utumiki wake ndi kulipira mangaŵa ake kwa anthu anzake. Monga Akristu, nafenso tili ndi mangaŵa otero oti tilipire. Kulalikira Ufumu kulinso njira yaikulu yosonyezera kukonda kwathu Mulungu, Mwana wake, ndi anansi athu.—Luka 10:25-28.
10. Kodi ena afutukula utumiki wawo mwa kuchita chiyani?
10 Njira imodzi yodziŵerengerera mlandu wovomerezeka kwa Mulungu ndiyo kugwiritsira ntchito maluso athu kufutukula utumiki wathu. Mwachitsanzo: Pakhala anthu ochuluka amitundu yambiri amene aloŵa m’Britain m’zaka zaposachedwapa. Kuti afikire anthu amenewo ndi uthenga wabwino, apainiya (alaliki anthaŵi zonse a Ufumu) oposa 800 ndi mazana a Mboni zina akuphunzira zinenero zosiyanasiyana. Zimenezi zachititsa chisonkhezero chabwino kwambiri pa utumiki. Mpainiya wina amene amaphunzitsa kalasi lachitchayina anati: “Sindinaganizepo kuti ndidzaphunzitsa Mboni zina chinenero changa, kuti nawonso auze ena choonadi mwa njira imeneyi. Nzokhutiritsa kwambiri!” Kodi mungafutukule utumiki wanu m’njira yofananayo?
11. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Mkristu wina anachitira umboni mwamwaŵi?
11 Mwachionekere, aliyense angachite zimene angathe kuti apulumutse munthu amene akumira m’madzi. Mofananamo atumiki a Yehova ali ofunitsitsa kugwiritsira ntchito maluso awo kuti achitire umboni pa mpata uliwonse. Posachedwapa Mboni ina inakhala pafupi ndi mkazi wina m’basi ndipo inalankhula naye za m’Malemba. Mkaziyo pokondwa ndi zimene anamva, anafunsa mafunso ambiri. Pamene Mboniyo inali pafupi kutsika m’basimo, mkaziyo anaichonderera kuti idzafike kwawo m’malo mwake, popeza kuti anali adakali ndi mafunso ambiri. Mboniyo inavomera. Chotulukapo chake? Phunziro la Baibulo linayambidwa, ndipo pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi mkaziyo anakhala wofalitsa wa Ufumu wosabatizidwa. Posapita nthaŵi iyeyo anali kuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba asanu ndi limodzi akeake. Ha, ndi mphotho yokondweretsa kwambiri chotani nanga imeneyi chifukwa cha kugwiritsira ntchito maluso athu mu utumiki wa Ufumu!
12. Kodi tingagwiritsire ntchito bwino motani maluso athu monga atumiki mu utumiki wakumunda?
12 Maluso athu monga atumiki angagwiritsiridwe ntchito mogwira mtima m’munda mwa kugwiritsira ntchito zofalitsa zonga buku la masamba 192 lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Podzafika April wa 1996, Writing Committee [Komiti Yolemba] ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova inali itavomereza kufalitsidwa kwa buku la Chidziŵitso m’zinenero 140, ndipo panthaŵiyo makope ake 30,500,000 anali atasindikizidwa kale m’zinenero 111. Buku limeneli linalembedwa ndi cholinga cha kuthandiza ophunzira Baibulo kuphunzira zokwanira ponena za Mawu a Mulungu ndi zifuno kuti adzipatulire kwa Yehova ndi kubatizidwa. Popeza kuti ofalitsa Ufumu sadzachititsa phunziro la Baibulo lapanyumba kwa wophunzira mmodzimodziyo kwazaka zambiri, iwo adzatha kuchititsa maphunziro kwa anthu ambiri kapena kuwonjezera kukhala ndi phande kwawo m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba ndi mitundu ina ya utumiki. (Machitidwe 5:42; 20:20, 21) Pozindikira za kudziŵerengera mlandu kwawo kwa Mulungu, amasamalira machenjezo a Mulungu. (Ezekieli 33:7-9) Koma chifuno chawo chachikulu ndicho kulemekeza Yehova ndi kuthandiza anthu ambiri monga momwe angathere kuti adziŵe za uthenga wabwino m’nthaŵi yaifupi imene yatsalira dongosolo la zinthu loipa lino.
Kudziŵerengera Mlandu Wathu Bwino Monga Mabanja
13. Kodi nchifukwa ninji mabanja aumulungu ayenera kukhala ndi phunziro la Baibulo la banja lokhazikika?
13 Munthu aliyense ndi banja lililonse lokhala m’Chikristu choona nlofunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu ndipo motero liyenera “kutsata ukulu msinkhu” ndi kukhala “okhazikika m’chikhulupiriro.” (Ahebri 6:1-3; 1 Petro 5:8, 9) Mwachitsanzo, awo amene aphunzira buku la Chidziŵitso ndi kubatizidwa afunikira kuwonjezera mokwanira chidziŵitso cha m’Malemba mwa kufika pa misonkhano nthaŵi zonse ndiponso mwa kuŵerenga Baibulo ndi zofalitsa zina zachikristu. Mabanja aumulungu ayeneranso kukhala ndi phunziro la banja lokhazikika, pakuti imeneyo ndiyo njira yofunika ya ‘kudikira, kuchirimika m’chikhulupiriro, kudzikhalitsa amuna, kulimbika.’ (1 Akorinto 16:13) Ngati ndinu mutu wa banja, mudzadziŵerengera mlandu wanu kwa Mulungu mwapadera wa kutsimikizira kuti banja lanu likudyetsedwa bwino mwauzimu. Monga momwe chakudya chakuthupi chomanga thupi chimachirikizira thanzi lakuthupi, ndimo mmene chakudya chauzimu chambiri ndi chanthaŵi zonse chimafunikira kwa inu ndi banja lanu kuti likhalebe “lathanzi m’chikhulupiriro.”—Tito 1:13, NW.
14. Kodi nchiyani chimene chinachitika pa umboni woperekedwa ndi buthu lachiisrayeli lophunzitsidwa bwino?
14 Ngati m’banja mwanu muli ana, Mulungu adzakuchitirani zabwino pa mlandu wanu chifukwa cha kuwapatsa malangizo auzimu anzeru. Chiphunzitso chimenecho chidzawapindulitsa, monga momwe chinachitira kwa buthu lachiisrayeli logwidwa undende ndi Aaramu m’masiku a Elisa mneneri wa Mulungu. Ilo linakhala mdzakazi wa mkazi wa kazembe wa khamu lankhondo wachiaramu wakhateyo, Namani. Ngakhale kuti msungwanayo anali wamng’ono, anauza mbuyake wamkaziyo kuti: “Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m’Samariya, akadamchiritsa khate lake.” Chifukwa cha umboni wake, Namani anapita ku Israyeli, potsirizira pake anachita mogwirizana ndi malangizo a Elisa a kukasamba kasanu ndi kaŵiri mu mtsinje wa Yordano, ndipo anakonzeka pa khatelo. Ndiponso, Namani anakhala wolambira Yehova. Zimenezo ziyenera kukhala zitakondweretsa buthulo chotani nanga!—2 Mafumu 5:1-3, 13-19.
15. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti makolo apereke maphunziro auzimu abwino kwambiri kwa ana awo? Perekani chitsanzo.
15 Kulera ana owopa Mulungu sikokhweka m’dziko lino lopanda makhalidwe limene lagona mu mphamvu ya Satana. (1 Yohane 5:19) Komabe, kuyambira paukhanda wa Timoteo, agogo ake a Loisi ndi amake, a Yunike, anamphunzitsa Malemba mwachipambano. (2 Timoteo 1:5; 3:14, 15) Kuphunzira Baibulo ndi ana anu, kumka nawo ku misonkhano yachikristu mokhazikika, ndipo potsirizira pake kuwachititsa kutsagana nanu ku utumiki zonsezo ndi mbali za njira ya chiphunzitso chimene muyenera kudzadziŵerengera mlandu kwa Mulungu. Mkristu wina ku Wales, amene tsopano ali m’zaka zake zakubadwa za m’ma 80, akukumbukira kuti kuchiyambi kwa ma 1920, atate wake anali kumtenga pamene anali kuyenda mtunda wa makilomita 10 kudzera paphiri (mtunda wa makilomita 20 kupita ndi kubwera) kukagaŵira matrakiti ofotokoza Baibulo kwa anthu akumidzi ya kuchigwa chapafupi. “Munali mkati mwa kuyenda kumeneko pamene atate analoŵetsa choonadi mumtima mwanga,” akutero mkaziyo moyamikira.
Akulu Amadziŵerengera Mlandu—Motani?
16, 17. (a) Kodi ndi mwaŵi wotani umene akulu okula msinkhu mwauzimu anali nawo mu Israyeli wakale? (b) Poyerekezera ndi mkhalidwe wa mu Israyeli wakale, kodi nchifukwa ninji zambiri zimafunidwa kwa akulu achikristu lerolino?
16 “Imvi ndiyo korona wa ulemu, [pamene ipezedwa, NW] m’njira ya chilungamo,” anatero munthu wanzeruyo Solomo. (Miyambo 16:31) Komatu si usinkhu wakuthupi chabe umene umakonzekeretsa munthu kusenza thayo mumpingo wa anthu a Mulungu. Amuna achikulire okula msinkhu mwauzimu mu Israyeli wakale anatumikira monga oweruza ndi akapitawo kaamba ka kupereka chiweruzo cholungama ndi kusungitsa mtendere, bata, ndi thanzi lauzimu. (Deuteronomo 16:18-20) Ngakhale kuti zili chimodzimodzinso ndi mpingo wachikristu, zambiri zikufunidwa kwa akulu pamene mapeto a dongosolo ili la zinthu akuyandikira. Chifukwa ninji?
17 Aisrayeli anali ‘mtundu wosankhika’ umene Mulungu anaulanditsa ku Igupto wakale. Popeza kuti analandira Chilamulo kupyolera mwa nkhoswe yawo, Mose, ana awo anabadwira mu mtundu wodzipatulira ndipo anali kudziŵa malamulo a Yehova. (Deuteronomo 7:6, 11) Komabe, lerolino palibe amene amabadwira mumtundu wodzipatulira wotero, ndipo tikayerekezera pali oŵerengeka okha amene amakulira m’mabanja aumulungu odziŵa bwino choonadi cha m’Malemba. Makamakatu aja amene angoyamba posachedwa “kuyenda m’choonadi” afunikira malangizo onena za mmene angakhalire ndi moyo mogwirizana ndi mapulinsipulo a m’Malemba. (3 Yohane 4) Motero, akulu okhulupirika ali ndi thayo lalikulu chotani nanga pamene ‘akugwira chitsanzo cha mawu a moyo’ ndi kuthandiza anthu a Yehova!—2 Timoteo 1:13, 14.
18. Kodi akulu a mumpingo ayenera kukonzekera kupereka thandizo lotani, ndipo chifukwa ninji?
18 Mwana wamng’ono amene akuphunzira kuyenda angapunthwe ndi kugwa. Samamva kukhala wosungika ndipo amafuna thandizo ndi chitsimikiziro cha kholo. Munthu wodzipatulira kwa Yehova mofananamo angapunthwe kapena kugwa mwauzimu. Ngakhale mtumwi Paulo anaona kukhala kofunika kumenya nkhondo ya kuchita cholondola kapena chabwino pamaso pa Mulungu. (Aroma 7:21-25) Abusa a gulu la nkhosa la Mulungu afunikira kupereka thandizo lachikondi kwa Akristu amene achimwa komano amene ali olapadi. Pamene akulu ena anafikira mkazi wina wodzipatulira amene anachita chophophonya chachikulu, iyeyo pamaso pa mwamuna wake wodzipatulira anati: “Ndikudziŵa kuti mundichotsa mumpingo!” Komano anayamba kulira pamene anauzidwa kuti akuluwo anafuna kudziŵa thandizo limene linali lofunika kuti abwezeretse mkhalidwe wauzimu wa banjalo. Pozindikira kuti iwo anayenera kudziŵerengera mlandu, akuluwo anali achimwemwe kuthandiza wokhulupirira mnzawo wolapa.—Ahebri 13:17.
Pitirizani Kudziŵerengera Bwino Mlandu Wanu
19. Kodi tingapitirize motani kudziŵerengera bwino mlandu wa ife eni kwa Mulungu?
19 Akulu a mumpingo ndi atumiki ena onse a Mulungu afunikira kupitirizabe kudziŵerengera bwino mlandu wa iwo eni kwa Yehova. Zimenezi nzotheka ngati timamatira ku Mawu a Mulungu ndi kuchita chifuniro chake. (Miyambo 3:5, 6; Aroma 12:1, 2, 9) Ife makamaka tikufuna kuchita zabwino kwa awo amene ali a m’banja lathu la chikhulupiriro. (Agalatiya 6:10) Komabe, kututa kudakali kwakukulu, ndipo antchito akali ochepa. (Mateyu 9:37, 38) Chotero tiyeni tichitire ena zabwino mwa kulengeza mosamalitsa uthenga wa Ufumu. Yehova adzatichitira zabwino pa mlandu wathu ngati tikwaniritsa kudzipatulira kwathu, kuchita chifuniro chake, ndi kulengeza uthenga wabwino mokhulupirika.
20. Kodi timaphunziranji pa kukambitsirana za njira ya Nehemiya?
20 Chotero tiyenitu tipitirize kuchita zochuluka mu ntchito ya Ambuye. (1 Akorinto 15:58) Ndipo tingachite bwino kulingalira za Nehemiya, amene anamanganso malinga a Yerusalemu, nachirikiza Chilamulo cha Mulungu, ndi kupititsa patsogolo mwachangu kulambira koona. Anapemphera kuti Yehova Mulungu amkumbukire chifukwa cha ubwino umene iyeyo anachita. Musonyezetu kukhala odzipereka kwa Yehova, ndipo iye akuchitirenitu zabwino pa kudziŵerengera kwanu mlandu.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi Nehemiya anapereka chitsanzo chotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso chimatipangitsa kukhala ofunikira kudziŵerengera mlandu kwa Mulungu?
◻ Kodi tingadziŵerengere mlandu wovomerezeka motani kwa Yehova mu utumiki wathu?
◻ Kodi mabanja angachitenji kuti adziŵerengere bwino mlandu wawo kwa Mulungu?
◻ Kodi akulu achikristu amadziŵerengera mlandu motani?
[Zithunzi patsamba 18]
Monga Paulo, tingadziŵerengere bwino mlandu wathu kwa Mulungu monga olengeza Ufumu
[Chithunzi patsamba 19]
Kodi ana anu ngolimba m’chikhulupiriro monga buthu lachiisrayeli m’nyumba ya Namani?