Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 12/15 tsamba 14-18
  • Yandikirani kwa Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yandikirani kwa Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyankhidwa Mogwirizana ndi Chifuniro cha Mulungu
  • Zitsanzo za Kumyandikira Yehova
  • Yesu, Chitsanzo Chathu
  • Kumsenzetsa Yehova Nkhaŵa Zathu
  • Pemphero ndi Chiyembekezo Zidzapitirizabe
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupemphera Kosaleka?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mmene Mungapemphelere ndi Kumvedwa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kwezani Manja Okhulupirika m’Pemphero
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 12/15 tsamba 14-18

Yandikirani kwa Yehova

‘Limbikani chilimbikire m’kupemphera.’​—AROMA 12:12.

1. Kodi chifuniro cha Yehova nchotani ponena za pemphero, ndipo kodi mtumwi Paulo anapereka chilimbikitso chotani papemphero?

YEHOVA ndi “Mulungu amene amapereka chiyembekezo” kwa anthu ake okhulupirika onse. Monga “Wakumva pemphero,” iye amamvetsera kuchonderera kwawo chithandizo chakupeza chiyembekezo chokondweretsa chimene wawaikira patsogolo pawo. (Aroma 15:13, NW; Salmo 65:2) Ndipo kupyolera m’Mawu ake, Baibulo, iye amalimbikitsa atumiki ake onse kudza kwa iye panthaŵi iriyonse imene akhumba. Iye alipo nthaŵi zonse, wokonzeka kulandira nkhaŵa zenizeni za mumtima mwawo. Kwenikweni, amawalimbikitsa ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera’ ndi ‘kupemphera kosaleka.’a (Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Yehova amafuna kuti Akristu onse aitanire pa iye m’pemphero mosalekeza, akumuuza zakukhosi kwawo ndikutero m’dzina la Mwana wake wokondedwa, Yesu Kristu.​—Yohane 14:6, 13, 14.

2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji Mulungu anatifulumiza ‘kulimbika chilimbikire m’kupemphera’? (b) Kodi tiri ndi chitsimikiziro chotani chakuti Mulungu amafuna kuti tipemphere?

2 Kodi Mulungu akutifulumiziranji kuchita zimenezi? Chifukwa chakuti zitsenderezo za moyo ndi mathayo zikhoza kutididikiza ndi kutiiŵalitsa kupemphera. Kapena mavuto akhoza kutikulira ndi kutipangitsa kuleka kukondwera m’chiyembekezo ndi kuleka kupemphera. Chifukwa cha zimenezi, tifunikira zokumbutsa zotilimbikitsa kupemphera ndi kuyandikira pafupi ndi magwero a chithandizo ndi chitonthozo, Yehova Mulungu wathu.

3 Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Inde, Mulungu sali kutali kwakuti angalephere kumva zonena zathu kwa iye, mosasamala kanthu za mkhalidwe wathu wopanda ungwiro. (Machitidwe 17:27) Ndiponso, iye sali wosasamala ndi wosaikako nzeru. Wamasalmo anati: ‘Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwawo.’​—Salmo 34:15; 1 Petro 3:12.

4. Kodi kumvetsera mapemphero kwa Yehova kungachitiridwe fanizo motani?

4 Yehova akuitanira pemphero. Tikhoza kuyerekezera chimenechi ndi gulu la anthu amene akulankhula pamodzi. Inu mulipo pamenepo, mukumvetsera kwa ena akulankhula. Mbali yanu ndi ija ya wopenyerera. Komano winawake atembenukira kwa inu, akutchulani dzina, ndi kukulankhuzani. Izi zikukopa chidwi chanu mwanjira yapadera. Mofananamo, Mulungu nthaŵi zonse amamvetsera kwa anthu ake, kulikonse kumene angakhale. (2 Mbiri 16:9; Miyambo 15:3) Chotero iye amamva mawu athu, natiyang’anira mwakutitetezera ndi kukondwera nafe. Komabe, pamene tiitanira padzina la Mulungu m’pemphero, timakopa chidwi chake, ndipo iye amatitchera khutu mosamalitsa. Mwamphamvu zake, Yehova akhoza kuzindikira ndi kumvetsetsa pempho losanenedwa loperekedwa mkati mwa mtima wathu ndi m’maganizo. Mulungu amatitsimikizira kuti adzayandikira kwa onse oitanira padzina lake mowona mtima ndi ofuna kuyandikira kwa iye.​—Salmo 145:18.

Kuyankhidwa Mogwirizana ndi Chifuniro cha Mulungu

5. (a) Kodi uphungu wakuti ‘limbikani chilimbikire m’kupemphera’ umasonyeza chiyani ponena za mapemphero athu? (b) Kodi ndimotani mmene Mulungu amayankhira mapemphero?

5 Uphungu wa kulimbika chilimbikire m’kupemphera umasonyeza kuti nthaŵi zina Yehova angatilole kupempherera chinthu kwa nthaŵi yakutiyakuti asanatiyankhe. Nthaŵi zina tikhoza kutopa ndi kuchonderera kwa Mulungu kuti tipeze chiyanjo chake kapena kukoma mtima kwachikondi kumene kungawonekere kukhala kofunikira kotheratu koma kukuchedwa. Chifukwa chake, Yehova Mulungu amatipempha kusagonja ku chikhoterero chirichonse choterocho koma kupitirizabe kupemphera. Tiyenera kupitiriza kumchonderera ponena za nkhaŵa zathu, tiri ndi chidaliro chakuti iye amasamala mapemphero athu ndipo adzakwaniritsa zosoŵa zathu zenizenizo, osati kokha zimene tinalingalira. Mosakaikira Yehova Mulungu amalinganiza zopempha zathu ndi chifuniro chake. Mwachitsanzo, ena angayambukiridwe ndi pempho lathu. Tikhoza kuyerekezera nkhaniyi ndi tate amene mwana wake ampempha kumgulira njinga. Tateyo akudziŵa kuti ngati agulira mwanayo njinga, mwana wake wina adzafunanso. Koma popeza kuti mwana winayo angakhale wamng’ono kukhala ndi njinga, tateyo angasankhe kusagula iriyonse panthaŵiyo. Mofananamo, polingalira chifuniro chake ndi nthaŵi yoikidwa ya zinthu, Atate wathu wakumwamba amasankha chimene chiridi chabwino koposa kwa ife ndi ena.​—Salmo 84:8, 11; yerekezerani ndi Habakuku 2:3.

6. Kodi Yesu anapereka fanizo lotani ponena za pemphero, ndipo kodi kulimbika m’pemphero kumasonyezanji?

6 Lapadera ndifanizo limene Yesu anapereka ponena za kufunika kwa ophunzira ake “kupemphera nthawi zonse, [osaleka, NW].” Mkazi wamasiye wina, polephera kupeza chiweruzo cholungama, analimbikira m’kupempha kwake kwa woweruza waumunthu kufikira analandira chiweruzo cholungama pomalizira pake. Yesu anawonjezera kuti: ‘Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake?’ (Luka 18:1-7) Kulimbikira m’kupemphera kumasonyeza chikhulupiriro chathu, chidaliro chathu pa Yehova, kufunitsitsa kwathu kuyandikira ndi kupempha kwa iye, tikusiya zotulukapo zake m’manja mwake.​—Ahebri 11:6.

Zitsanzo za Kumyandikira Yehova

7. Kodi tingachitsanzire motani chikhulupiriro cha Abele cha kumyandikira Yehova?

7 Baibulo liri ndi nkhani zambiri za mapemphero operekedwa ndi atumiki a Mulungu. Izi ‘zinalembedwa kutilangiza, kuti mwachipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.’ (Aroma 15:4) Chiyembekezo chathu chimalimbitsidwa mwakupenda kwathu zitsanzo za amene anamyandikira Yehova. Abele anapereka nsembe yolandirika kwa Mulungu, ndipo ngakhale kuti pemphero silikutchulidwa, mosakaikira anapempha m’pemphero kwa Yehova kuti nsembe yake ilandiridwe. Ahebri 11:4 amanena kuti: ‘Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, amene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama.’ Abele anadziŵa za lonjezo la Mulungu la pa Genesis 3:15, koma kuyerekezera ndi zimene timadziŵa tsopano, iye anadziŵa zochepa kwambiri. Komabe, Abele anachita mogwirizana ndi chidziŵitso chimene anali nacho. Choteronso lerolino, ena a okodwerera chatsopano m’chowonadi cha Mulungu sanapezebe chidziŵitso chochuluka, koma iwo amapemphera ndikugwiritsira ntchito bwino koposa chidziŵitso chimene alinacho, monga momwe anachitira Abele. Inde, iwo amachita mwachikhulupiriro.

8. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti Abrahamu anayandikira kwa Yehova, ndipo ndifunso lotani limene tiyenera kudzifunsa?

8 Mtumiki wina wokhulupirika wa Mulungu anali Abrahamu, “kholo la onse akukhulupira.” (Aroma 4:11) Lerolino, kuposa ndi kalelonse, timafunikira chikhulupiriro cholimba, ndipo tifunikira kupemphera mwachikhulupiriro, monga momwe anachitira Abrahamu. Genesis 12:8 amanena kuti iye ‘anammangira Yehova guwa la nsembe, naitanira dzina la Yehova.’ Abrahamu analidziŵa dzina la Mulungu ndipo analigwiritsira ntchito m’pemphero. Iye analimbika m’pemphero mobwerezabwereza, akuitana pa ‘dzina la Yehova, Mulungu wa nthaŵi zonse.’ (Genesis 13:4; 21:33) Abrahamu anaitanira pa Mulungu m’chikhulupiriro chimene chinamtchukitsa. (Ahebri 11:17-19) Pemphero linathandiza Abrahamu kupitiriza kukondwera mokulira m’chiyembekezo cha Ufumu. Kodi tikutsatira chitsanzo cha Abrahamu cha kulimbika m’kupemphera?

9. (a) Kodi nchifukwa ninji mapemphero a Davide ali aphindu kwambiri kwa anthu a Mulungu lerolino? (b) Kodi nchiyani chingatulukepo ngati tipempherera kumyandikira Yehova monga mmene Davide anachitira?

9 Davide anali wapadera ponena za kulimbika m’kupemphera, ndipo masalmo ake amasonyeza mmene mapemphero ayenera kukhalira. Mwachitsanzo, atumiki a Mulungu akhoza kupempherera zinthu zonga chipulumutso kapena kulanditsidwa (3:7, 8; 60:5), chitsogozo (25:4, 5), chitetezo (17:8), kukhululukidwa machimo (25:7, 11, 18), ndi mtima woyera (51:10). Pamene Davide anapsinjika mtima, anapemphera kuti: ‘Kondwetsani moyo wa mtumiki wanu.’ (86:4) Mofanafamo tikhoza kupempherera chimwemwe cha mtima, tikudziŵa kuti Yehova amafuna kuti tikondwere m’chiyembekezo. Davide anamyandikira Yehova ndipo anapemphera kuti: ‘Moyo wanga uumirira inu: dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.’ (63:8) Kodi tidzamyandikira Yehova, monga momwe Davide anachitira? Tikatero, adzatigwiriziza.

10. Kodi ndimalingaliro olakwika otani amene wamasalmo Asafu anali nawo panthaŵi ina, koma kodi anazindikira chiyani?

10 Ngati titi timyandikire Yehova, tifunikira kupeŵa kukhumbira oipa chifukwa cha miyoyo yawo yosasamala ndi yokondetsa zinthu zakuthupi. Wamasalmo Asafu panthaŵi ina analingalira kuti kunali kopanda phindu kutumikira Yehova, popeza kuti oipa ‘akhazikika chikhazikikire.’ Chikhalirechobe, iye anazindikira kuti kulingalira kwake kunali kolakwa ndikuti oipa ali “poterera.” Iye anawona kuti palibe chimene chinaposa kumyandikira Yehova, ndipo ponena za mwini yekha anati kwa Mulungu: ‘Ndikhala ndi inu chikhalire: mwandigwira dzanja langa la manja. Pakuti, tawonani, iwo okhala patali adzawonongeka; . . . Koma ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu. Ndimuyesa [Mfumu, NW] Ambuye Yehova pothaŵirapo ine, kuti ndifotokoze ntchito zanu zonse.’ (Salmo 73:12, 13, 18, 23, 27, 28) Mmalo mokhumbira moyo wosasamala wa anthu oipa, anthu opanda chiyembekezo, tiyeni titsatire Asafu m’kumyandikira Yehova.

11. Kodi nchifukwa ninji Danieli ali chitsanzo chabwino chakumyandikira Yehova, ndipo kodi tingamtsanzire motani?

11 Danieli analimbika m’kupemphera motsimikiza mtima, ngakhale poyang’anizana ndi upandu wakukhala m’dzenje la mikango chifukwa cha kunyalanyaza lamulo laboma loletsa pemphero. Koma Yehova ‘anatuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango,’ namlanditsa Danieli. (Danieli 6:7-10, 22, 27) Danieli anadalitsidwa kwenikweni chifukwa cha kulimbika m’kupemphera. Kodi nafenso timalimbika m’kupemphera, makamaka pamene tiyang’anizana ndi chitsutso cha kulalikira kwathu Ufumu?

Yesu, Chitsanzo Chathu

12. (a) Kuchiyambi kwa uminisitala wake, kodi nchitsanzo chotani chimene Yesu anapereka ponena za pemphero, ndipo kodi chimenechi chingawapindulire motani Akristu? (b) Kodi chitsanzo cha Yesu cha pemphero chimavumbulanji ponena za pemphero?

12 Kuyambira kuchiyambi kwa uminisitala wake wapadziko lapansi, zolembedwa zimasonyeza kuti Yesu anapemphera. Mkhalidwe wake wa kupemphera pamene ankabatizidwa unapereka chitsanzo chabwino kwa oloŵa muubatizo wam’madzi m’nthaŵi zamakono. (Luka 3:21, 22) Munthu akhoza kupempherera chithandizo cha Mulungu kuti achite chimene chimaphiphiritsidwa ndi ubatizo wam’madzi. Yesu anathandizanso ena kumfikira Yehova m’pemphero. Panthaŵi ina pamene Yesu ankapemphera m’malo ena, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa iye pambuyo pake: ‘Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera.’ Pamenepo Yesu anafotokoza limene limadziŵika mofala monga pemphero lachitsanzo, m’limene kundandalikidwa kwa nkhani kumasonyeza kuti dzina la Mulungu ndi chifuno chake ziyenera kupatsidwa malo oyamba. (Luka 11:1-4) Chifukwa chake, m’mapemphero athu tiyenera kukhala ndi malingaliro abwino ndi kukhala achikatikati, osanyalanyaza “zinthu zofunika kopambana.” (Afilipi 1:9, 10, NW) Ndithudi, pamakhala nthaŵi za zosoŵa zapadera kapena pamene vuto lakutilakuti liyenera kusamaliridwa. Mofanana ndi Yesu, Akristu akhoza kumfikira Mulungu m’pemphero ndi kupempha nyonga yakuti akwaniritse gawo lakutilakuti kapena kuti apirire mayesero kapena maupandu. (Mateyu 26:36-44) Kwenikweni, mapemphero aumwini angakhudze mbali iriyonse ya moyo.

13. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kufunika kwa kupempherera ena?

13 Mwachitsanzo chake chabwino, Yesu anasonyeza kufunika kwa kupempherera ena. Iye anadziŵa kuti ophunzira ake akadedwa ndi kuzunzidwa, monga momwe zinachitikira kwa iye. (Yohane 15:18-20; 1 Petro 5:9) Chotero, iye anapempha Mulungu ‘kuti awasunge iwo kuletsa woipayo.’ (Yohane 17:9, 11, 15, 20) Ndipo podziŵa chiyeso chapadera chomwe chinali patsogolo pa Petro, iye anamuuza kuti: ‘Ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime.’ (Luka 22:32) Nkopindulitsa chotani nanga ngati nafenso tilimbika m’kupempherera abale athu, kumaganizira za ena osati mavuto athu okha ndi zikondwerero!​—Afilipi 2:4; Akolose 1:9, 10.

14. Kodi timadziŵa motani kuti Yesu anamyandikira kwambiri Yehova m’nthaŵi yonse ya uminisitala wake padziko lapansi, ndipo kodi tingamtsanzire motani?

14 Muuminisitala wake wonse, Yesu analimbika m’kupemphera, akumayandikira mwathithithi kwa Yehova. (Ahebri 5:7-10) Mtumwi Petro, pa Machitidwe 2:25-28, anagwira mawu Salmo 16:8 ndi kuligwiritsira ntchito kwa Ambuye Yesu Kristu kuti: ‘Davide ananena za iye, Ndinawona [Yehova, NW] pamaso panga nthaŵi zonse; chifukwa ali pa dzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike.’ Nafenso tingatero. Tikhoza kupemphera kwa Mulungu kuti atiyandikire, ndipo tingasonyeze chidaliro chathu mwa Yehova mwakukhala naye m’maganizo nthaŵi zonse. (Yerekezerani ndi Salmo 110:5; Yesaya 41:10, 13.) Pamenepo tidzapeŵa mavuto amtundu uliwonse, chifukwa chakuti Yehova adzatigwiriziza, ndipo sitidzagwedezeka konse.

15. (a) Kodi sitiyenera konse kuleka kupemphera ponena za chiyani? (b) Kodi ndichenjezo lotani limene likuperekedwa ponena za kuyamikira kwathu?

15 Tisalephere konse kusonyeza chiyamikiro kwa Yehova kaamba ka ubwino wake wonse kwa ife, inde, ‘chisomo cha Mulungu’ chimene chimaphatikizapo mphatso ya Mwana wake monga nsembe ya dipo kaamba ka machimo athu. (2 Akorinto 9:14, 15; Marko 10:45; Yohane 3:16; Aroma 8:32; 1 Yohane 4:9, 10) Ndithudi, m’dzina la Yesu, ‘tiyamikire Mulungu Atate masiku onse.’ (Aefeso 5:19, 20; Akolose 4:2; 1 Atesalonika 5:18) Tiyenera kusamala kusalola chiyamikiro cha zimene tirinazo kululuzidwa chifukwa cha kutanganitsidwa kwambiri ndi zimene tiribe kapena mavuto athu.

Kumsenzetsa Yehova Nkhaŵa Zathu

16. Pamene vuto lina litivutitsa, kodi tiyenera kuchitanji?

16 Kulimbika m’kupemphera kumasonyeza kuzama kwa kudzipereka kwathu. Pamene tiitanira pa Mulungu, timayamba kumva bwino ngakhale pamene iye sanatiyankhebe. Ngati vuto lakutilakuti likutivutitsa maganizo, tikhoza kumyandikira Yehova mwakutsatira uphungu uwu: ‘Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo iye adzakugwiriziza.’ (Salmo 55:22) Mwakumsenzetsa Mulungu mavuto athu onse​—nkhaŵa, kugwiritsidwa mwala, mantha, ndi zina zotero​—ndi chikhulupiriro chokwanira mwa iye, timalandira chitonthozo cha mtima, ‘mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.’​—Afilipi 4:4, 7; Salmo 68:19; Marko 11:24; 1 Petro 5:7.

17. Kodi ndimotani mmene tingapezere mtendere wa Mulungu?

17 Kodi mtendere wa Mulungu umenewu umabwera panthaŵi imodzi? Ngakhale kuti tingapeze chitonthozo mwamsanga, zimene Yesu ananena ponena za kupempherera mzimu woyera zimagwiranso ntchito pano: “Pitirizani kupempha, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza; pitirizani kugogoda, ndipo adzakutsegulirani.” (Luka 11:9-13, NW) Popeza kuti mzimu woyera ndiwo umatithandiza kutaya nkhaŵa, tiyenera kulimbika m’kupempha mtendere wa Mulungu ndi chithandizo chake pa mavuto athu. Tingakhale otsimikiza kuti mwakulimbika m’kupemphera, tidzapeza mpumulo ndi chitonthozo cha mtima zokhumbidwazo.

18. Kodi Yehova amatichitiranji ngati sitidziŵa kwenikweni chimene tiyenera kupempherera m’mkhalidwe winawake?

18 Koma bwanji ngati sitidziŵa kwenikweni chimene tiyenera kupempherera? Madandaulo athu amkati kaŵirikaŵiri amatsala osatchulidwa chifukwa chakuti sitimamvetsetsa mokwanira mkhalidwe wathu, kapena timasoŵa chomuuza Yehova. Apa mpamene mzimu woyera ungatichonderere. Paulo analemba kuti: ‘Chimene tichipempha monga chiyenera, sitidziŵa; koma mzimu [weniweniwo, NW] utipemphera ndi zobuula zosatheka kuneneka.’ (Aroma 8:26) Umatero motani? Mawu a Mulungu ali ndi maulosi ouziridwa ndi mapemphero amene amachita ndi mkhalidwe wathu. Iye amalola zimenezi kutichonderera, titero kunena kwake. Amazilandira kukhala zimene tikanapempherera ngati tidziŵa chimene zikutanthauza m’chochitika chathu, ndipo amazikwaniritsa moyenerera.

Pemphero ndi Chiyembekezo Zidzapitirizabe

19. Kodi nchifukwa ninji pemphero ndi chiyembekezo zidzapitirizabe kosatha?

19 Kupemphera kwa Atate wathu wakumwamba kudzapitiriza kosatha, makamaka ponena za kuyamikira dziko latsopano ndi madalitso ake onse. (Yesaya 65:24; Chibvumbulutso 21:5) Tidzapitirizanso kukondwera m’chiyembekezo, chifukwa chakuti chiyembekezo cha mtundu winawake chidzakhalapobe kosatha. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:13.) Ponena za zinthu zatsopano zimene Yehova adzabweretsa atamaliza tsiku lake lakupuma la Sabata lodziikira yekha kulinga ku dziko lapansi, sititha ngakhale kuzilingalira. (Genesis 2:2, 3) Ku umuyaya wonse, iye adzasungira anthu ake zodabwitsa zachikondi, ndipo mtsogolo muli zinthu zazikulu pamene chifuniro chake chidzakwaniritsidwa.

20. Kodi tiyenera kufuna kuchitanji motsimikiza mtima, ndipo chifukwa ninji?

20 Pokhala ndi chiyembekezo chochititsa nthumanzi choterocho, tiyeni tonsefe timyandikiretu Yehova mwakulimbika m’kupemphera. Tisaleke konse kumyamikira Atate wathu wakumwamba kaamba ka madalitso athu onse. Panthaŵi yake zimene tikuyembekezera zidzakwaniritsidwa mwachimwemwe, ngakhale kuposa zimene tingakhale tinaganizirapo kapena kuyembekezera, chifukwa chakuti Yehova ‘angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza.’ (Aefeso 3:20) Tsono polingalira zimenezi, tiyeni tipereke chitamando chonse ndi ulemerero ndi ziyamiko ku umuyaya wonse kwa Yehova Mulungu wathu, “Wakumva pemphero”!

[Mawu a M’munsi]

a Malinga ndi Webster’s New Dictionary of Synonyms, “Kulimbika kaŵirikaŵiri kumatanthauza mkhalidwe wabwino; kumapereka lingaliro la kukana kulefulidwa ndi kulephera, zikaikiro, kapena zovuta, ndipo kuchirimika kapena kuumirira pakulondola chonulirapo kapena ntchito.”

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Kodi nchifukwa ninji tifunikira kulimbika m’kupemphera?

◻ Kodi timaphunziranji m’zitsanzo za pemphero zokhalako Chikristu chisanadze?

◻ Kodi chitsanzo cha Yesu chimatiphunzitsanji ponena za pemphero?

◻ Kodi tingamsenzetse motani nkhaŵa zathu Yehova ndipo ndi chotulukapo chotani?

[Chithunzi patsamba 17]

Danieli analimbika m’kupemphera mosasamala kanthu za chiwopsezo chakuponyedwa m’dzenje la mikango

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena