Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ndani Amaumba Maganizo Anu?
    Nsanja ya Olonda—1999 | April 1
    • Choncho, Paulo anachonderera Akristu anzake kuti ‘asafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.’ (Aroma 12:2) Wotembenuza Baibulo wina analemba mawu a Paulo m’njira ina kuti: “Musalole dziko lokuzingani kukukanikizirani m’chikombole chake.” (Aroma 12:2, Phillips) Satana adzayesetsa kukukanikizirani m’chikombole chake, monga momwe woumba miphika wakale ankakanikizira dothi m’chikombole kuti litengere zizindikiro ndi zinthu zina zimene anafuna kuti likhale nazo. Satana ali wokonzeka kugwiritsa ntchito ndale, chipembedzo, ndi zosangulutsa za dzikoli pochita zimenezo. Kodi chisonkhezero chake n’chofala motani? N’chofala monga momwe chinalili m’tsiku la mtumwi Yohane. “Dziko lonse lapansi,” anatero Yohane, “ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19; onaninso 2 Akorinto 4:4.) Ngati mukukayikira kuti Satana ali ndi mphamvu yonyengera anthu ndi kuipitsa maganizo awo, kumbukirani mmene anachitira zimenezi ku mtundu wonse wa anthu, Aisrayeli, amene anali opatuliridwa kwa Mulungu. (1 Akorinto 10:6-12) Kodi zimenezo zingachitikenso kwa inu? Zingatheke ngati mulola chisonkhezero chachinyengo cha Satana kuloŵa m’maganizo mwanu.

  • Kodi Ndani Amaumba Maganizo Anu?
    Nsanja ya Olonda—1999 | April 1
    • Chosankha ndi chanu. Mungasankhe ‘kufanizidwa ndi makhalidwe a pansi pano’ mwa kulola mafilosofi ndi zokonda za dziko lino kusonkhezera maganizo anu. (Aroma 12:2) Koma dzikoli silikukufunirani zabwino. Chotero “penyani,” akuchenjeza motero mtumwi Paulo, “kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu.” (Akolose 2:8) Kukanikizidwa motero m’chikombole cha Satana, kapena kuti ‘akulandeni ngati chuma,’ si kovuta. Kuli ngati utsi wa fodya wosuta munthu wina. Mungakhudzidwe mwa kungopuma mpweya woipitsidwawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena