Adrián anayamba kuphunzira Baibulo ali ndi zaka 16. Iye ananena kuti: “Ndinapitiriza kuphunzira Baibulo ndipo ndinayamba kuona kuti ndikufunika kusintha khalidwe langa.” Iye ankafunikira kuthetsa chidani mumtima mwake komanso kusiya kuchita zachiwawa. Lemba limene linamuthandiza kwambiri ndi la Aroma 12:17-19 lomwe limatilimbikitsa kuti tisamabwezere. Adrián akufotokoza kuti: “Zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti Yehova adzathetsa zinthu zopanda chilungamo pa nthawi yake ndiponso m’njira yabwino. Patapita nthawi ndinasiya kukonda ndewu.”
Tsiku lina madzulo gulu la achinyamata lomwe linkakonda kumenyana ndi gulu la Adrián linayamba kumumenya. Mtsogoleri wawo ananena kuti: “Bwanji sukubwezera?” Adrián akunena kuti: “Ndinkafunitsitsa kubwezera.” Koma m’malo mobwezera iye anapemphera kwa Yehova mwachidule n’kuchokapo.
Adrián akufotokozanso kuti: “Tsiku lotsatira ndinakumana ndi mtsogoleri wawo uja ali yekha. Nditamuona ndinkafuna kuti ndibwezere zimene anandichita koma ndinapempheranso chamumtima kuti Yehova andithandize kuugwira mtima. Koma ndinadabwa kuona kuti anabwera pafupi n’kundiuza kuti: ‘Undikhululukire chifukwa cha zimene zinachitika dzulo zija. Inenso ndikufuna nditakhala ngati iweyo. Ndikufuna kuphunzira Baibulo.’ Ndinasangalala kwambiri kuti ndinakwanitsa kuugwira mtima chifukwa zinathandiza kuti nayenso ayambe kuphunzira Baibulo.”