Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kodi Chiukiriro Chidzadzetsa Mapindu Yani?
    Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

◼ Kodi chiri chanzeru kwa Mkristu amene mnzake wa mu ukwati wafa kukhala wosakwatira mchiyembekezo cha kudzagwirizananso mtsogolo?

Chiri chabwino chotani nanga kuti Mkristu ayenera kukhala ndi chikondi choterocho kaamba ka mnzake wa mu ukwati ngakhale pambuyo pa kufa kwake! Ena mu mkhalidwe umenewu akhala osakwatira, osati chifukwa cha kukhala okhutiritsidwa ndi kukhala osakwatira, koma mchiyembekezo chakupitirizanso ndi ukwati wawo pambuyo pakuukitsidwa. Pamene ife sitikukhala osalingalira malingaliro a munthu ponena za ziyembekezo zoterozo, tikulimbikitsa oterowo kulingalira nsonga zina za Baibulo.

Mwachitsanzo, kuyang’ana pa nkhaniyo ali mawu a mtumwi Paulo: “Mkazi amangika pokhala mwamuna wake akali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Koma akakhala wokondwera koposa ngati akhala monga mmene ali.” (1 Akorinto 7:39, 40) Ichi chikusonyeza kuti kumangira kwa ukwati kumatha pamene wina afa. Chinali chikondi cha Mulungu kudziwitsa Akristu ponena za ichi, popeza chotero akazi amasiye ndi amuna amasiye angayese malingaliro awo ndi zosowa zawo zina mkulingalira kuti kaya akafunikira kukwatira iwo sali omangika kwa wakufayo.​—1 Akorinto 7:8, 9.

Kodi Baibulo, ngakhale kuli tero, limasonyeza kuti kaya owukitsidwa adzakhala okhoza kukwatira kapena kupitirizanso ndi ukwati wapapitapo umene unatha pa imfa? Mbiri ina ikuwonekera kukhala ikuyang’ana pa funsoli. lyo inaphatikizapo Asaduki amene, ngakhale kuti sanali okhulupirira mu chiwukiriro, anafika kwa Yesu kuyesa kumutchera msampha iye. Iwo anapereka vuto iri lophatikiza mulamu muukwati; “Panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anatenga mkazi nafa wopanda mwana. Chomwechonso wachiwiri, ndi wachitatu anatenga iye a Mofananamo ngakhale wachisanu ndi chiŵiriyo: sanasiye ana, koma anafa. Pomalizira mkaziyo anamwalira. Tsopano, mu chiukiriro, kodi iye adzakhala mkazi wa yani?“​—Luka 20:27-33; Mateyu 22:23-28.

Akristu sali pansi pa lamulo limenelo, koma vuto lofananalo lingabuke ponena za iwo. Mwachitsanzo: Mbale ndi mlongo C​—​anakwatirana ndipo anali ndi ana awiri. Kenaka mbaleyo anafa. Mlongo C​—​anakonda ndipo anamusowa iye mozama, koma anadzimva kusoweka kwa kukhala ndi woyanjana naye, chirikizo la ndalama, chisonyezo cha kugonana, ndi kuthandizira ana. Chotero iye anakwatiwa ndi Mbale M​—kugwirizana kumene kunali kwa mmalemba monga koyambako. Pambuyo pake iye anadwala ndi kufa. Ngati anzake a muukwati awiri amenewo anaukitsidwa ndipo ukwati unali woyenerera, kodi ndi kwandani kumene iye akakwatiwa?

Lingalirani yankho la Yesu kwa Asaduki: “Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa: koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwdtiwa. Pakuti sangathe kufanso nthawi zonse; pakuti afanana ndi angelo; ndipo ali ana a Mulungu, popeza akhala ana a kuuka kwa akufa. Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, . . . Pamene iye amchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo iye sakhala Mulungu wa akufa: komawa amoyo, pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.”​—Luka 20:34-38; Mateyu 22:29-32.

Ena anadzimva kuti Yesu pano anali kusonya ku chiukiriro cha kumwamba, komabe pali zifukwa zakukhulupirira kuti yankho lake linali kunena za chiukiriro cha pa dziko lapansi mu “dongosolo la kachitidwe kazinthu katsopano“ likudzalo. Ndi zifukwa ziti zimene zikutsimikiza kawonedwe kameneka? Awo amene anali kufunsa Yesu sanakhulupirire mwa iye kapena kudziwa ponena za chiukiriro cha kumwamba. Iwo anafunsa ponena za banja la Chiyuda pansi pa lamulo. Mkuyankha Yesu analoza kwa Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, amuna amene anayembekezera kukhala ndi moyo kachiwirinso pa dziko lapansi. (Genesis 42:38; Yobu 14:13-15; yerekezani ndi Ahebri 11:19. ) Makolo amenewo ndi mamiliyoni ena, omwe akaukitsidwa padziko lapansi ndi amene adzitsimikizira kukhala okhulupirika adzakhala “monga angelo.”Ngakhale kuti akakhoza kufa, iwo sadzafanso mwamsanga Mulungu atawalalikira iwo kaamba ka moyo wosatha.

Malingaliro a munthu lerolino angachipangitse ichi kukhala mathedwe ovuta kuwalandira. Koma chiyenera kuzindikiridwa kuti palibe paliponse pamene Baibulo limanena kuti kuukitsa kwa Mulungu kwa anthu okhulupirika kumatanthauza kubweretsa kayimidwe kawo ka chikwati. Chotero, palibe wina aliyense amene amakhulupirira kuti ngati Akula ndi Priskila alandira moyo kumwamba, iwo adzapitirizanso ndi ukwati wawo. (Machitidwe 18:2) Ndipo Yosefe ndi Mariya mwachionekere adzakhala ku mbali zosiyana​—Yosefe pa dziko lapansi ndipo Mariya kumwamba. (Yohane 19:26; Machitidwe1:13, 14) Popeza palibe aliyense wa ife amene anakhalapo kumwamba, sitinganene ndi malingaliro otani amene Akula, Priskila, ndipo Mariya angakhale nawo kumeneko. Koma tingakhale otsimikizira kuti akupeza chikwaniritso chokwanira mu utumiki wawo wa kumwamba.

Mofananamo, sitinakhalepo monga anthu angwiro. Chotero sitingakhale otsimikizira ndimotani mmene tidzamverera ponena za maunansi athu akale ngati ndiponso pamene tipeza moyo wa umunthu wangwiro mu paradaiso. Chiri chabwino kwa ife kukumbukira kuti pamene Yesu ananena chimenecho iye anali munthu wangwiro ndipo chotero anali mu mkhalidwe wabwino kuposa ife kuyamikira malingaliro a awo amene “awerengeredwa kukhala oyenera kupeza dongosolo limenelo la zinthu.” Tingakhulupirirenso kuti Yesu ali wokhoza ‘kumvera chifundo ndi zofooka zathu za lerolino.’(Ahebri 4:15)Chotero ngati Mkristu achipeza kukhala chovuta kuvomereza mapeto akuti oukitsidwa sadzakwatiranso, iye angakhale wotsimikizira kuti Mulungu ndi Kristu amamvetsetsa. Ndipo iye angangoyembekezera mopepuka kuwona chomwe chidzachitika.

Palibe chifukwa tsopano cha kugogomezera mopambanitsa nkhaniyi. Wamasalimo analemba kuti: “Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu iyeyo anatilenga ndipo ife ndife ake. Ndife anthu ake ndi nkhosa za pa busa pake. . . lemekezani dzina lake. Pakuti Yehova ndiye wabwino.”(Masalmo 100:3-5) Mulungu wathu wabwino motsimikizirika adzapereka mokwanira zosowa zathu zenizeni zoyenerera ngati tiri “kuwerengedwa oyenera kupeza dongosolo la kachitidwe ka zinthu limenelo“​—Yobu 34:10-12; Masalmo 104:28; 107:9.

Ubwino wa Mulungu umawonedwanso mkutidziwitsa kwake kuti imfa ya mzathu wa muukwati imathetsa ukwati. (Aroma 7:2) Chotero aliyense amene anataya mnzake wa muukwati angadziwe kuti iye wamkazi kapena wamwamuna ali womasuka kukwatiranso tsopano ngati chikuwoneka kukhala chofunika kwenikweni kapena chabwino koposa. Ena akwatiranso, mwakutero kuthandiza kukwaniritsa zosowa zawo za panthawi ino ndi zija za banja lawo. (1 Akorinto 7:36-38; Aefeso 6:1-4) Mofananamo, Mkristu amene mnzake wa muukwati wafa sayenera kudzimva kukhala ndi thayo la kukhala wopanda mnzake wamuukwati tsopano mchiyembekezo chakuti mnzawo wa muukwati wakale adzagwirizanitsidwanso nawo pa kuukitsidwa ku moyo pano pa dziko lapansi mu dongosolo likudzalo.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati m’lsrayeli anafa pamene mkazi wake asanabale mwana yemwe akalandira cholowa, mbale wake wamwamunayu anayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo mchiyang’aniro cha kubala mwana kaamba ka iye.​—Deuteronomo 25:5-10.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena