Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 2/8 tsamba 13-15
  • Kodi Umodzi Wachikristu Umalola Maumunthu Osiyanasiyana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Umodzi Wachikristu Umalola Maumunthu Osiyanasiyana?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mulungu Amakopa Aliyense Payekha
  • Zimene Mulungu Ankafuna Poyamba
  • Kulingalira za Ena
  • Umodzi ndi Kusiyana Maumunthu—Zinthu Zovuta Kuyendera Limodzi
  • Kodi Umodzi wa Akristu Umalira Kuchita Chilichonse Mofanana?
    Galamukani!—2003
  • Lemekezani Mulungu Ndi ‘Pakamwa Pamodzi’
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Mgwirizano wa Akhristu Umalemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Sungani Umodzi m’Masiku Ano Otsiriza
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 2/8 tsamba 13-15

Lingaliro la Baibulo

Kodi Umodzi Wachikristu Umalola Maumunthu Osiyanasiyana?

UMODZI mumpingo wachikristu ndi wofunika kwambiri. Kusiyana pa zikhulupiriro kukhoza kuyambitsa mikangano yoopsa, magaŵano, ndipo mwina ngakhale chidani. (Machitidwe 23:6-10) Baibulo limanena kuti “Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere” (1 Akorinto 14:33) Motero Akristu amalangizidwa kulankhula chimodzimodzi ndi kukhala ndi mtima umodzi ndiponso malingaliro amodzi.—1 Akorinto 1:10.

Kodi mawu ameneŵa ndiponso ena ofanana nawo m’Baibulo akulimbikitsa kuti Akristu onse ayenera kukhala chimodzimodzi pa chilichonse? (Yohane 17:20-23; Agalatiya 3:28) Kodi Chikristu choona monga momwe Baibulo limachilongosolera si chimalimbikitsa kusiyana maumunthu? Kodi Akristu onse amayembekezeredwa kukhala ofanana maumunthu osasiyana mpang’ono pomwe?

Mulungu Amakopa Aliyense Payekha

Anthu ena amakhulupirira kwambiri kuti Baibulo ndi chida cholamulirira anthu ambiri mwankhanza. Ndithudi, kaŵirikaŵiri zipembedzo zina zakhala zikuligwiritsira ntchito motero. Komabe, Yesu anasonyeza kuti Malemba ndi Mlembi wake Waumulungu si wotero. Iye analongosola Mulungu monga wokhala ndi chidwi mwa zolengedwa zake chilichonse pachokha.

Yesu anati pa Yohane 6:44: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa Ine koma ngati Atate wondituma Ine amkoka iye.” Verebu logwiritsiridwa ntchito pano silisonyeza kuti Mulungu amaguza anthu pamene iwo sakufuna ayi. M’malo mwake, Mulungu amawakopa bwinobwino, kuwakopa mtima, kukhala wolakalaka mumtima. Monga mmene katswiri wa Baibulo wina akunenera, ‘pakhala mphamvu yosonkhezera malingaliro yochokera kwa Mulungu imene imapangitsa kukhulupirira.’ Mlengi saona anthu monga gulu lopanda aliyense umunthu wakewake. Amaonetsetsa aliyense payekha ndipo pang’onopang’ono amakokera kwa iyemwini onse omwe ali ndi mitima yabwino.—Salmo 11:5; Miyambo 21:2; Machitidwe 13:48.

Onani mmene mtumwi Paulo ankasinthira malinga ndi malo amene anali. Iye ankazindikira zosowa za munthu aliyense payekha ndipo ankazindikira kuti kalingaliridwe kena kanali kofala kwa anthu a maiko ena kapena okhala ndi makulidwe akutiakuti ndiye ankawafikira mosiyanasiyana. Iye analemba kuti: “Kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda . . . Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.”—1 Akorinto 9:20-22.

Nzachionekere kuti Paulo sanalimbikitse kuti anthu akhale chimodzimodzi kapena kuwachitira onse chimodzimodzi. Iye anawalimbikitsa motere: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.” (Akolose 4:6) Inde, Paulo ndi Akristu ena anayenera kuzindikira ndi kulemekeza umunthu wa aliyense payekha ncholinga choti amthandize.

Zimene Mulungu Ankafuna Poyamba

Ulemu umenewu kwa munthu aliyense payekha umapitirira munthuyo ataloŵa mumpingo wachikristu. Anthu a Mulungu sasintha kakhalidwe ka munthu payekha kuti afanane ndi wina ndendende ncholinga chokondweretsa omwe ali ndi maudindo. M’malo mwake, amasangalala pokhala aliyense ndi umunthu wakewake ndipo ali ndi maluso, zizoloŵezi, malingaliro osiyanasiyana. Umunthu wa aliyense payekha sumaonedwa monga chokhumudwitsa kapena wovutitsa. Nzimene Mulungu anafuna poyamba.

Choncho, m’dziko lapansi latsopano la olungama lolonjezedwa m’Baibulo, ungwiro umene anthu adzakhala nawo udzalolabe kuti anthu akhale osiyanasiyana maumunthu. (2 Petro 3:13) Pansi pa mutu wakuti “Perfection (ungwiro),” insaikulopediya ya Baibulo, Insight on the Scripturesa moyenerera imapereka ndemanga zotsatirazi: “Ungwiro sutanthauza kutha kwa mitundumitundu ya zinthu monga mmene anthu kaŵirikaŵiri amaganizira. Zinyama, zimene zili zina mwa ‘ntchito zangwiro’ za Yehova (Ge[nesis] 1:20-24; De[uteronomy] 32:4), nzosiyanasiyana.”

Insight imawonjezera kuti: “Mofananamo ungwiro wa Dziko Lapansi sutanthauza kuti silosiyana m’malo ena, silisintha, kapena kuti lilibe zinthu zamitundumitundu; ilo lili ndi mwina mosadabwitsa, mwina modabwitsa, mwina mosakongola, mwina mokongola, zowawasa ndi zotsekemera, mwina mwa miyalamiyala mwina mosalala, madambo ndi nkhalango, mapiri ndi zigwa. Umaphatikizapo kukongola kotsitsimula kuchiyambi kwa nyengo ya ngululu, kufundira kwa m’chilimwe limodzi ndi maonekedwe a bluu a thambo, maonekedwe okongola a nyengo ya phukuto kukongola kwa chipale chofeŵa chongogwa kumene. (Ge[nesis] 8:22) Motero anthu angwiro sadzakhala ofanana umunthu, maluso, ndi zochita.”

Kulingalira za Ena

Komabe, Chikristu choona sichiloleza kudzitukumula ndi kunyalanyaza omwe timakhala nawo. Mtumwi Paulo ankaonetsetsa kalikonse komwe ankachita m’moyo wake kuti asakhumudwitse ena. Iye anati m’kalata yake ku mpingo wa ku Korinto: “Osapatsa chokhumudwitsa konse m’chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe.” (2 Akorinto 6:3) Nthaŵi zina, tiyenera kulamulira zikhumbo zathu ndi kuona zokonda za ena kukhala zoposa zathu. Mwachitsanzo, Paulo analembera Akristu ku Roma kuti: “Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.”—Aroma 14:21.

Mofananamo lerolino, munthu angasankhe kusamwa zoledzeretsa pali wina yemwe amavutika kuwongolera kamwedwe kake. (1 Akorinto 10:23, 24) Amachita zimenezi si chifukwa chakuti atsatire zokonda za wina, koma chifukwa cha kukoma mtima ndi chikondi. “Kristunso sanadzikondweretsa yekha.” Yesu anali munthu payekha, koma sanaike zokonda zake patsogolo nkunyalanyaza za ena.—Aroma 15:3.

Komabe, chimodzi cha zinthu zosangalatsa m’Chikristu choona ndicho kulemekeza ufulu wa munthu ndi zokonda zake malinga zisadutse malamulo a m’Baibulo. Chimatiphunzitsa kuti Mulungu anatipanga kuti tikhale osiyana ndi a umunthu wathuwathu. Pa 1 Akorinto 2:11, timaŵerenga kuti: “Ndani wa anthu adziŵa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye?” Timayesetsa kumvetsetsa anthu ena momwe tingathere. Koma vesi limeneli likusonyeza kuti aliyense wa ife ali ndi umunthu wakewake womwe amauzindikira iye yekha ndi Mlengi wathu. Tili ndi “munthu wobisika wamtima,” umene timasonyeza tikamasankha kutero.—1 Petro 3:4.

Umodzi ndi Kusiyana Maumunthu—Zinthu Zovuta Kuyendera Limodzi

Mtumwi Paulo anasonyeza chitsanzo chabwino cha kusamala monga Mkristu. Ngakhale kuti anali ndi udindo ngati mtumwi wa Kristu, anali wosamala kuti asaumirize malingaliro ake pa ena.

Mwachitsanzo, Paulo analimbikira pa lingaliro lakuti kuli bwino kwambiri kukhala wosakwatira m’dziko lopanda ungwiro lino. Iyemwini anali wosakwatira pamene ankalemba kuti: “Koma otere [okwatira] adzakhala nacho chisautso m’thupi,” ndi kuti “[mkazi wamasiye] akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga.” Pokhala kuti mawu akewa anakhala mbali ya Mawu a Mulungu ouziridwa zimasonyeza kuti palibe cholakwika ndi kuganiza kwakeko. Koma ananenanso kuti: “Ungakhale ukwatira, sunachimwa.”—1 Akorinto 7:28, 40.

Nzoonekeratu kuti atumwi ambiri anali anthu okwatira, monga mmene Paulo anasonyezera ponena mawu akuti: “Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?” (1 Akorinto 9:5) Akristu ankazindikira kuti pa nkhani imeneyi akanasankha kuchita zosiyana ndi za Paulo ndipo iye akanawalemekezabe.

Olambira Mulungu nthaŵi zonse akhala ololedwa kusonyeza chikhulupiriro chawo mogwirizana ndi umunthu wawo. Ndipo, Mulungu anafika ngakhale polola kuti alembi a Baibulo agwiritsire ntchito kalembedwe kakekake aliyense. Mwachitsanzo, ndi kudzichepetsa mtima konse Nehemiah analemba nkhani yake modzisonya. (Nehemiya 5:6, 19) Kumbali ina, ndi mtima wodzichepetsa mtumwi Yohane sanatchulepo dzina lake nkamodzi komwe polemba Uthenga Wabwino ndipo ndi mwakamodzikamodzi pamene anatchulapo za iyemwini. Mulungu anavomereza kalembedwe konseko ndipo anakasunga m’Baibulo.

Zitsanzo zofanana ndi zimenezi zosamala ndi zololera zimapezeka m’Malemba monse. Nzoonekeratu kuti umodzi wachikristu umalolera maumunthu osiyana. Ndithudi, kusiyana makulidwe ndi kalingaliridwe zikhoza kubweretsa kusagwirizana ngati mikhalidwe yauzimu palibe. (Aroma 16:17, 18) Koma ‘tikakhala nacho chikondano, chomangira cha mtima wamphumphu,’ timaphunzira kulolera ndi kusangalala ndi umunthu wapadera wa ena.—Akolose 3:14.

“Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Kristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero,” limatero Baibulo. (Aroma 15:7) Ndi chithandizo cha mzimu wa Mulungu, Akristu akhoza kukwanitsa kusunga umodzi wosakhalira kuwonongekawo pamene akusangalala ndi maumunthu osiyanasiyana mumpingo.

[Mawu a M’munsi]

a Yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Mlengi saona mtundu wa anthu monga gulu lopanda umunthu wakewake aliyense

[Mawu Otsindika patsamba 15]

Aliyense wa ife ali ndi umunthu wakewake womwe amauzindikira iye yekha ndi Mlengi wathu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena