Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/15 tsamba 8-12
  • Kudzakhala Kuuka kwa Olungama

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzakhala Kuuka kwa Olungama
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusonkhanitsidwa kwa  Onga Nkhosa
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro
  • Okhulupirira ‘Ayesedwa Olungama’
  • Chiukiriro cha pa Dziko Lapansi
  • Chiyembekezo Chimene Chimapatsa Chitonthozo
  • Chiphunzitso cha Kuuka kwa Akufa Chimakukhudzani
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Mphamvu ya Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Chiyembekezo cha Kuuka kwa Akufa Mumachiona Motani?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/15 tsamba 8-12

Kudzakhala Kuuka kwa Olungama

“Ndikukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”​—MACHITIDWE 24:15.

1. Kodi ndi mkhalidwe wotani umene anthu onse ayang’anizana nawo kuyambira pamene Adamu ndi Hava anagwera muuchimo?

“CHILICHONSE dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlaliki 9:10) Ndi mawu osankhidwa bwino ochepa ameneŵa, Mfumu yanzeru Solomo imafotokoza mkhalidwe umene mbadwo uliwonse wa anthu wayang’anizana nawo kuyambira pamene makolo athu oyamba, Adamu ndi Hava, anagwera muuchimo. Popanda kupatulapo wina, imfa potsirizira pake yameza aliyense​—wolemera ndi wosauka, mfumu ndi munthu wamba, wachikhulupiriro ndi wopanda chikhulupiriro. Ndithudi, imfa ‘yachita ufumu.’​—Aroma 5:17.

2. Kodi nchifukwa ninji okhulupirika ena angakhale atagwiritsidwa mwala m’nthaŵi ino ya mapeto?

2 Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwamakono kwa sayansi ya zamankhwala, imfa ikuchitabe ufumu ngakhale lerolino. Pamene kuli kwakuti zimenezi nzosadabwitsa, mwina mwake ena angakhale atagwiritsidwa mwala pamene anayang’anizana ndi mdani wakalekale ameneyu. Chifukwa ninji? Chabwino, kalelo m’ma 1920, Watch Tower Society inalengeza uthenga wakuti “Mamiliyoni okhala ndi moyo tsopano sadzafa konse.” Kodi mamiliyoni ameneŵa akakhala yani? “Nkhosa” za m’mawu a Yesu onena za nkhosa ndi mbuzi. (Mateyu 25:1-46) Onga nkhosa ameneŵa ananenedweratu kuti akakhalako m’nthaŵi ya mapeto, ndipo chiyembekezo chawo chikakhala moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. M’kupita kwa nthaŵi, anthu a Mulungu anayamba kuzindikira bwino za malo a “nkhosa” zimenezi m’zifuno za Yehova. Anazindikira kuti anthu omvera ameneŵa akayenera kulekanitsidwa ndi “mbuzi” zouma khosi, ndipo pambuyo pa chiwonongeko cha mbuzizo, nkhosa zikalandira gawo la pa dziko lapansi la Ufumu umene unakonzedwera iwo.

Kusonkhanitsidwa kwa  Onga Nkhosa

3. Kodi anthu a Mulungu asumika maganizo awo pa ntchito yotani kuyambira 1935?

3 Kuyambira mu 1935, “kapolo wokhulupirika” wasumika maganizo pa kupeza onga nkhosa amenewo ndi kuwabweretsa m’gulu la Yehova. (Mateyu 24:45; Yohane 10:16) Akristu ophunzitsika ameneŵa azindikira kuti Yesu akulamulira tsopano mu Ufumu wakumwamba wa Yehova ndi kuti nthaŵi ya mapeto a dongosolo ili loipa la zinthu ndi ya kukhazikitsidwa kwa dziko latsopano mmene mudzakhalitsa chilungamo ikuyandikira mofulumira kwambiri. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 12:10) M’dziko latsopano limenelo, mawu othutsa mtima a Yesaya adzakwaniritsidwa: “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse.”​—Yesaya 25:8.

4. Ngakhale kuti akhala akuyembekezera mofunitsitsa kuona ulamuliro wa Yehova ukulemekezedwa pa Armagedo, kodi nchiyani chimene chachitika kwa a nkhosa zina ambiri?

4 Popeza kuti mapeto a dziko la Satana ali pafupi kwambiri, Akristu onga nkhosa angakonde kwambiri kukhala ndi moyo kufikira ulamuliro wa Yehova utalemekezedwa mkati mwa chisautso chilinkudzacho pa Babulo Wamkulu ndi dziko lonse la Satana. (Chivumbulutso 19:1-3, 19-21) Kwa ambiri, zinthu sizinayende mwanjira imeneyo. Ambiri amene anayembekezera kudzakhala pakati pa “mamiliyoni” amene sakafa konse afadi. Ena anaphedwera chikhulupiriro cha choonadi m’ndende ndi m’misasa yachibalo kapena pamanja a anthu achipembedzo otengeka maganizo. Ena afera m’ngozi kapena ndi zotchedwa kuti zochititsa imfa zachibadwa​—matenda ndi ukalamba. (Salmo 90:9, 10; Mlaliki 9:11) Mwachionekere, ambiri adzafabe mapeto asanafike. Kodi ndimotani mmene oterowo adzaonera kukwaniritsidwa kwa lonjezo la dziko latsopano mmene mudzakhalitsa chilungamo?

Chiyembekezo cha Chiukiriro

5, 6. Kodi awo okhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi amene akufa Armagedo isanadze ali ndi mtsogolo motani?

5 Mtumwi Paulo anapereka yankho pamene anali kulankhula pamaso pa kazembe Wachiroma Felike. Monga momwe kwalembedwera pa Machitidwe 24:15, Paulo analengeza molimba mtima kuti: “Ndikukhala nacho chiyembekezo cha kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Chiyembekezo cha chiukiriro chimatilimbitsa mtima poyang’anizana ndi nsautso zoipitsitsa. Chifukwa cha chiyembekezo chimenecho, mabwenzi athu okondedwa amene amadwala ndi kuzindikira kuti adzafa samataya mtima. Chilichonse chimene chingachitike, iwo amadziŵa kuti adzalandirabe mfupo ya kukhulupirika kwawo. Chifukwa cha chiyembekezo cha chiukiriro, abale ndi alongo athu olimba mtima amene amayang’anizana ndi imfa pamanja a ozunza amadziŵa kuti ozunza awo sangapambane konse. (Mateyu 10:28) Pamene wina afa mumpingo, timakhala achisoni potayikidwa munthuyo. Panthaŵi imodzimodziyo, ngati iyeyo ali mmodzi wa nkhosa zina, timasangalala kuti wokhulupirira mnzathuyo wakhaladi wokhulupirika kufikira mapeto ndipo tsopano akupuma, ali ndi mtsogolo motsimikizirika m’dziko latsopano la Mulungu.​—1 Atesalonika 4:13.

6 Inde, chiyembekezo cha chiukiriro chili mbali yaikulu ya chikhulupiriro chathu. Komabe, kodi nchifukwa ninji chikhulupiriro chathu m’chiukiriro chili cholimba kwambiri, ndipo ndaninso ali ndi chiyembekezo chimenecho?

7. Kodi chiukiriro nchiyani, ndipo ndi malemba ena ati amene amasonyeza kutsimikizirika kwake?

7 Liwu Lachigiriki la “chiukiriro” ndilo a·naʹsta·sis, limene kwenikweni limatanthauza “kuimirira.” Ilo makamaka limanena za kunyamuka kwa akufa. Ndi iko komwe, liwu lenilenilo lakuti “chiukiriro” silimapezeka m’Malemba Achihebri, koma chiyembekezo cha chiukiriro chimafotokozedwa bwino lomwe mmenemo. Mwachitsanzo, timachiona m’mawu amene Yobu analankhula pa kuvutika kwake: “Ha! mukadandibisa kumanda, . . . mukadandiikira nthaŵi, ndi kundikumbukira.” (Yobu 14:13) Mofananamo, pa Hoseya 13:14, timaŵerenga kuti: “Ndidzawaombola ku mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola ku imfa; imfa, miliri yako ili kuti? Manda, chiwonongeko chako chili kuti?” Pa 1 Akorinto 15:55, mtumwi Paulo anagwira mawu ameneŵa nasonyeza kuti chilakiko choloseredwacho pa imfa chimachitika mwa chiukiriro. (Zoonadi, m’lemba limenelo Paulo anali kulankhula za chiukiriro chakumwamba.)

Okhulupirira ‘Ayesedwa Olungama’

8, 9. (a) Kodi anthu opanda ungwiro angapezeke bwanji m’kuuka kwa olungama? (b) Kodi maziko a chiyembekezo chathu cha moyo umene sudzathetsedwa ndi imfa ndi ati?

8 M’mawu ake kwa Felike, ogwidwa m’ndime 5, Paulo ananena kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama. Kodi olungama amene adzaukitsidwa ndani? Aha, palibe munthu amene ali wolungama mwachibadwa. Ife tonse ndife ochimwa kuyambira pa kubadwa, ndipo timalakwa m’moyo wathu wonse​—zimene zimatichititsa kuyenerera imfa pa zifukwa ziŵiri. (Aroma 5:12; 6:23) Komabe, m’Baibulo timapezamo mawu akuti ‘kuyesedwa olungama.’ (Aroma 3:28) Ameneŵa amanena za anthu amene, ngakhale kuti ali opanda ungwiro, akhululukidwa machimo awo ndi Yehova.

9 Mawuwo amagwiritsiridwa ntchito kwambiri kwa Akristu odzozedwa, amene ali ndi chiyembekezo chakumwamba. Pa Aroma 5:1, mtumwi Paulo akunena kuti: “Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.” Akristu onse odzozedwa amayesedwa olungama chifukwa cha chikhulupiriro. Chikhulupiriro m’chiyani? Monga momwe Paulo akufotokozera mwatsatanetsatane m’buku la Aroma, ndicho chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. (Aroma 10:4, 9, 10) Yesu anafa monga munthu wangwiro ndiyeno anaukitsidwa kwa akufa nakwera kumwamba kukapereka mtengo wa moyo wake waumunthu kaamba ka ife. (Ahebri 7:26, 27; 9:11, 12) Pamene Yehova analandira nsembe imeneyo, Yesu, kwenikweni, anaombola fuko la anthu ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Awo amene amasonyeza chikhulupiriro m’kakonzedwe kameneka amapindula nako kwambiri. (1 Akorinto 15:45) Pamaziko ake, amuna ndi akazi okhulupirika ali ndi chiyembekezo cha kulandira moyo umene sudzathetsedwa ndi mdani wankhanzayo, imfa.​—Yohane 3:16.

10, 11. (a) Kodi ndi chiukiriro chiti chimene chikuyembekezera Akristu odzozedwa? (b) Kodi alambiri okhalako Chikristu chisanakhale anayembekezera chiukiriro chotani?

10 Chifukwa cha nsembe ya dipo ya Yesu, odzozedwa okhulupirika, oyesedwa olungama, ali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kuukitsidwa monga zolengedwa zauzimu zosafa mofanana ndi Yesu. (Chivumbulutso 2:10) Chiukiriro chawo chimatchulidwa pa Chivumbulutso 20:6, pamene pamati: “Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiŵiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.” Chimenechi ndi chiukiriro chakumwamba. Komabe, onani kuti Baibulo limachitcha “kuuka koyamba,” zimene zikutanthauza kuti pali kwinanso kumene kulinkudza.

11 Mu Ahebri chaputala 11, Paulo anatchula mzera wautali wa atumiki a Mulungu okhalako Chikristu chisanakhale amene anasonyeza chikhulupiriro cholimba mwa Yehova Mulungu. Awanso anali ndi chikhulupiriro m’chiukiriro. M’mavesi 35 ndi 36 a chaputalacho, Paulo amalankhula za ziukiriro zozizwitsa zimene zinachitika m’mbiri ya Israyeli, kuti: “Akazi analandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa; ndipo ena anakwapulidwa, osalola kuomboledwa, kuti akalandire kuuka koposa.” Mboni zokhulupirika zakale zimenezo zinatha kuyembekezera chiukiriro chabwino kuposa chimene chinachitidwa, mwachitsanzo, ndi Eliya ndi Elisa. (1 Mafumu 17:17-22; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21) Chiyembekezo chawo chinali kuukitsidwira m’dziko limene atumiki a Mulungu sakazunzidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, dziko limene akazi sakatayikidwa okondedwa awo mu imfa. Inde, anayembekezera kuuka kwa akufa m’dziko latsopano limodzimodzilo limene tikuyembekezera. (Yesaya 65:17-25) Yehova sanawavumbulire zambiri ponena za dziko latsopano limeneli monga wachitira kwa ife. Komabe, anadziŵa kuti linali kudza, ndipo anafuna kudzakhalamo.

Chiukiriro cha pa Dziko Lapansi

12. Kodi anthu okhulupirika okhalako Chikristu chisanakhale anayesedwa olungama? Fotokozani.

12 Kodi tiyenera kuganiza za kuuka kwa amuna ndi akazi okhulupirika amenewo okhalako Chikristu chisanakhale m’dziko latsopano limenelo kukhala mbali ya kuuka kwa olungama? Malinga ndi umboni umene tili nawo, inde, chifukwa chakuti Baibulo limawatcha kukhala olungama. Mwachitsanzo, wophunzira Yakobo amatchulapo za mwamuna ndi mkazi wina wakale amene anayesedwa olungama. Mwamunayo anali Abrahamu, kholo la fuko la Ahebri. Ponena za iye timaŵerenga kuti: “Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudaŵerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.” Mkaziyo anali Rahabi, wosakhala Mwisrayeli amene anasonyeza chikhulupiriro mwa Yehova. ‘Anayesedwa wolungama’ nakhala mbali ya mtundu wa Ahebri. (Yakobo 2:23-25) Chotero, amuna ndi akazi akale amene anasonyeza chikhulupiriro cholimba mwa Yehova ndi m’malonjezo ake ndi kukhalabe okhulupirika kufikira imfa anayesedwa olungama ndi Yehova chifukwa cha chikhulupiriro chawo, ndipo iwo mosakayikira adzapezeka pa “kuuka kwa olungama.”

13, 14. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti Akristu amene ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi angayesedwe olungama? (b) Kodi zimenezi zimatanthauzanji kwa iwo?

13 Komabe, bwanji za anthu onga nkhosa lerolino, awo amene ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi amene amadzipatulira kwa Yehova ndi amene amafa ali okhulupirika m’nthaŵi ya mapeto ino? Kodi adzapezeka m’kuuka kwa olungama? Zilidi choncho mwachionekere. Khamu lalikulu la okhulupirika amenewo linaonedwa ndi mtumwi Yohane m’masomphenya. Taonani mmene akulifotokozera: “Ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo; ndipo afuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.”​—Chivumbulutso 7:9, 10.

14 Onani kuti ofatsa ameneŵa ali otsimikiza kwambiri za chipulumutso chawo, ndipo akuti chikuchokera kwa Yehova ndi Yesu, “Mwanawankhosa.” Ndiponso, iwo akuimirira pamaso pa Yehova ndi pa Mwanawankhosa, onsewo atavala zoyera. Kodi nchifukwa ninji avala zoyera? Cholengedwa chakumwamba chikuuza Yohane kuti: “Anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:14) M’Baibulo, kuyera kumaphiphiritsira chiyero, chilungamo. (Salmo 51:7; Danieli 12:10; Chivumbulutso 19:8) Kuonedwa kwa khamu lalikulu litavala zovala zoyera kumatanthauza kuti Yehova amaliona kukhala lolungama. Kodi zimenezo zikutheka bwanji? Chifukwa chakuti, m’lingaliro lophiphiritsira, atsuka zovala zawo m’mwazi wa Mwanawankhosa. Amasonyeza chikhulupiriro m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu Kristu ndipo chotero ayesedwa olungama monga mabwenzi a Mulungu okhala ndi chiyembekezo cha kupulumuka chisautso chachikulu. Chifukwa chake, Mkristu wodzipatulira ndi wokhulupirika aliyense amene tsopano ali wa “khamu lalikulu” amene amwalira chisautso chachikulu chisanadze angatsimikizire kuti adzapezeka m’chiukiriro cha pa dziko lapansi cha olungama.

15. Popeza olungama ndi osalungama omwe adzaukitsidwa, kodi ubwino wake wa kuuka kwa olungama ngwotani?

15 Chiukiriro chimenecho chikufotokozedwa pa Chivumbulutso chaputala 20, vesi 13, m’mawu aŵa: “Nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali mmenemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.” Motero, mkati mwa Tsiku Lachiweruzo lalikulu la zaka chikwi la Yehova, awo onse okhala m’chikumbukiro cha Mulungu adzaukitsidwa​—olungama ndi osalungama omwe. (Machitidwe 17:31) Komabe, kudzakhala kwabwino kwambiri chotani nanga kwa olungama! Iwo ali kale ndi miyoyo ya chikhulupiriro. Ali kale ndi unansi wolimba ndi Yehova ndipo ali ndi chidaliro m’kukwaniritsidwa kwa zifuno zake. Mboni zolungama kuyambira Nyengo Yachikristu isanadze zidzauka kwa akufa zili zofunitsitsa kudziŵa mmene malonjezo a Yehova onena za Mbewu anakwaniritsidwira. (1 Petro 1:10-12) Awo a nkhosa zina amene Yehova wawayesa olungama m’tsiku lathu adzauka kumanda ali ofunitsitsa kuona dziko la Paradaiso limene anauza ena pamene analengeza mbiri yabwino m’dongosolo lino la zinthu. Imeneyo idzakhala nthaŵi yosangalatsa chotani nanga!

16. Kodi tinganenenji za kuuka kwa m’Tsiku Lachiweruzo kwa awo amene akumwalira m’nthaŵi yathu?

16 Mkati mwa Tsiku Lachiweruzo la zaka chikwi limenelo, kodi ndi liti kwenikweni pamene awo amene anafa ali okhulupirika m’zaka zino zomalizira za dongosolo la zinthu la Satana adzaukitsidwa? Baibulo silimanena. Komabe, kodi si kwanzeru kunena kuti awo oyesedwa olungama amene akufa m’tsiku lathu adzaukitsidwa poyamba kotero kuti adzagwirizane ndi khamu lalikulu la opulumuka Armagedo m’ntchito ya kulandira anthu a mibadwo yoyambirira kuchokera kwa akufa? Inde, ndithudi!

Chiyembekezo Chimene Chimapatsa Chitonthozo

17, 18. (a) Kodi chiyembekezo cha chiukiriro chimapereka chitonthozo chotani? (b) Kodi timasonkhezeredwa kulengeza chiyani ponena za Yehova?

17 Chiyembekezo cha chiukiriro chimapatsa nyonga ndi chitonthozo kwa Akristu onse lerolino. Ngati tikhalabe okhulupirika, palibe zochitika zosayembekezera kapena mdani aliyense amene angatilande mfupo yathu! Mwachitsanzo, mu 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, patsamba 177, pali zithunzithunzi za Akristu olimba mtima ku Ethiopia amene anafa m’malo mwakuti alolere molakwa chikhulupiriro chawo. Mawu ake ofotokoza zithunzizo amati: “Nkhope zimene tikuyembekezera kudzaona pa chiukiriro.” Ha, udzakhala mwaŵi wotani nanga kudziŵana ndi ameneŵa ndi ena osaŵerengeka amene anasonyeza kukhulupirika kofananako poyang’anizana ndi imfa!

18 Bwanji nanga ponena za okondedwa athu ndi mabwenzi amene chifukwa cha ukalamba kapena matenda sangakhoze kupyola chisautso chachikulu? Chifukwa cha chiyembekezo cha chiukiriro, iwo ali ndi mtsogolo mwabwino kwambiri ngati akhalabe okhulupirika. Ndipo ngati nafenso molimba mtima tisonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Yesu, tili ndi mtsogolo mwabwino kwambiri. Chifukwa ninji? Chifukwa, monga Paulo, timayembekezera “kuuka kwa olungama ndi osalungama.” Tikuthokoza Yehova ndi mitima yathu yonse kaamba ka chiyembekezo chimenechi. Ndithudi, chimatisonkhezera kubwereza mawu a wamasalmo akuti: “Fotokozerani ulemerero wake [Mulungu] mwa amitundu; zodabwiza zake mwa mitundu yonse ya anthu. Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu.”​—Salmo 96:3, 4.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi ndi malemba ati amene amathandiza kutsimikizira chiyembekezo chathu cha chiukiriro cha pa dziko lapansi?

◻ Kodi Akristu tsopano akuyesedwa olungama pamaziko ati?

◻ Kodi chiyembekezo cha chiukiriro chimatipatsa motani kulimba mtima ndi kutsimikiza mtima?

[Chithunzi patsamba 9]

Monga Paulo, Akristu odzozedwa akuyembekezera chiukiriro chakumwamba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena