“Osafooka”
PAMENE anabadwa, Wilma Rudolph anali wamng’ono ndi wodwaladwala. Iye anayamba kuyenda ali ndi zaka zinayi. Ndiyeno anadwala kwakayakaya matenda a scarlet fever ndi chibayo. Ngakhale kuti anapulumuka, mwendo wake wakumanzere unafa. Potsimikiza mtima kuti Wilma adzayenda, amayi ake anasisita mwendo wake wopuwalawo ndipo anaphunzitsa ana awo achikulire atatu kuchita zofananazo. Choncho panali kusinthanasintha kunayi patsiku kwa “kusisita Wilma.”
Pamene Wilma anali ndi zaka zisanu ndi zitatu, anali wokhoza kuyenda ndi ndodo. Posakhalitsa anayamba kuthamanga ndi kuseŵera. Anatsimikiza mtima kulaka kupunduka kwake. Maseŵera anamthandiza, ndiponso uphungu wa amayi ake wakuti: “Osafooka.”
Wilma sanafooke. Ndipo mu 1960, pamaseŵera a Olympics m’Roma, Italiya, analandira mamedulo atatu a golidi. Iye anapambana mipikisano yothamanga ya mamita 100 ndi 200 ndipo anakhala woyamba m’mpikisano womalizira wa kuthamanga kopatsirana timitengo wa mamita 400.
M’nthaŵi ya nkhondo yoyamba yadziko, pamene anali mnyamata wa zaka zisanu ndi ziŵiri, miyendo ya Glenn Cunningham inapsa kwadzaoneni. Iye anabindikiritsidwa kwa miyezi yambiri m’kama ndipo anauzidwa kuti mwina sakayendanso. Amayi ake anakanya tsiku ndi tsiku minofu yake yovulazidwayo ndipo anamlimbikitsa kumayenda ndi kuthamanga. Glenn sanafooke. Kwenikwenidi, potsirizira pake anapambana mipikisano 21 ya liŵiro la m’nyumba la mamita 1,600 ku Madison Square Garden. Ndipo, mu 1934, anapanga mbiri padziko lonse paliŵiro la mtunda wa mailo imodzi.
Nthaŵi zina tonsefe timakumana ndi zokhumudwitsa zosiyanasiyana m’moyo. Kaŵirikaŵiri limakhala vuto laumoyo. M’malo mokhala wogonjetsedwa, kukakhala kwabwino chotani nanga kutsimikiza mtima ndi kusafooka! Paulo analemba motere m’chigwirizano ndi zoyesayesa zauzimu: ‘Sitifooka; koma ungakhale umunthu [thupi lathu] wathu wakunja uvunda, wa mkati mwathu ukonzedwa kwatsopano [kapena kupatsidwa nyonga yatsopano] tsiku ndi tsiku.’—2 Akorinto 4:16.
[Mawu a Chithunzi patsamba 27]
UPI/Bettmann Newsphotos