Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 11/8 tsamba 26-31
  • Kusuta—Maupanduwo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusuta—Maupanduwo
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malipiro Apamwamba Ofunika Kuperekedwa!
  • Kupenda Chodzikhululukira Choipa
  • Kukhala M’malo Anu Abwino Koposa Mwauzimu
  • Kodi Kusuta Kulidi Koipa Motero?
    Galamukani!—1991
  • N’kusiyiranji Kusuta?
    Galamukani!—2000
  • Ochirikiza Fodya Aponya Zibaluni Zawo za Mpweya Wotentha wa Zinyengo
    Galamukani!—1995
  • Ogulitsa Imfa—Kodi Ndinu Wogula?
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 11/8 tsamba 26-31

Lingaliro la Baibulo

Kusuta—Maupanduwo

M’MA 1950, kampani ina yopanga ndudu inasatsa fodya wake kukhala “weniweni amene dokotala analangiza.” Mopereka chidaliro, masilogani oterowo nthaŵi ina anachirikiza ndudu kukhala thandizo ndi nyonga ku umoyo—koma sizirinso tero! Ano ali masiku pamene maboma akufuna kuti pa mapaketi a ndudu palembedwe machenjezo a maupandu aakulu ku umoyo.

Mosasamala kanthu za izo, osuta ena akumamatira ku lingaliro lakuti ‘ndudu imandithandiza kuganiza ndi kugwira bwino ntchito.’ Iwo angasulize chiwopsyezo cha umoyocho mwakuchilinganiza ndi kudya masiwiti kuti apeze nyonga ya mwamsanga kapena kumwa kofi kuti achotse tulo m’mawa. Kapena iwo angawone upandu wa kusuta kukhala kokha wakuthupi. Kodi angakhale olondola? Kodi palidi nkhani yofunikira kukangana kuti ndudu—pa maupandu ake onse—ingawathandize iwo kuchita bwinopo?

Malipiro Apamwamba Ofunika Kuperekedwa!

Kaya ndudu imapindulitsadi wosutayo kukhala wamaso mokulira ndi wochita bwino kapena imangopanga chinyengo cha kutero, palibe chikaikiro kuti mphothoyo imadza pa malipiro owopsya. Pambali pa upandu wa kansa ya pambuyo pake ndi nthenda ya mtima, lingalirani zotulukapo za mwamsanga: Mkati mwa timphindi tisanu ndi tiŵiri kufika ku khumi ta kukoka kulikonse, wosutayo amamva kukankha kwa mankhwala, chikonga: “Icho chimadzilamulira chokha,” akutero katswiri wa chiyambukiro cha makhwala pa maganizo a munthu Nina Schneider, wa pa Yunivesite ya California, “ndipo chimalamulira mkhalidwe wa maganizo ndi kugwira kwake ntchito. Ndizo zomwe zimachipangitsa kukhala chomwerekeretsa mwamphamvu chotero.”

Kodi nchamphamvu yogodomalitsa mofanana ndi heroin ndi cocaine? Inde, anatero sing’anga wotumbula wamkulu wa ku United States m’chenjezo loperekedwa pa May 16, 1988. Iye analongosola kuti mphamvu yomwerekeretsa imeneyi, ndiyo chifukwa chimene osuta ena “adzapitirizabe mosasamala kanthu za zotulukapo zoipa zovulaza thupi, maganizo kapena makhalidwe.”

Ndipo nzotulukapo zoipa chotani nanga! Podzafika 1985 kusuta kunachititsa imfa 100,000 pachaka mu Britain, 350,000 pachaka mu United States, ndipo mbali imodzi mwa zitatu ya imfa zonse mu Greece. Chochitika chimenechi monga vuto la zaumoyo wa anthu sichingakhululukidwe. Vutolo, utsi wa fodya, suli kokha chakudya kapena chakumwa chopanda ntchito ku thupi komanso ngwovulaza mwachibadwa.

Chotero, kodi chikonga mu utsi wa fodya nchoipitsitsa kuposa caffeine mu kofi, tii, kapena chocolate? Mogwirizana ndi kawonedwe ka zamankhwala, palibe kuyerekeza. Dr. Peter Dews, wofufuza caffeine wa pa Yunivesite ya Harvard akutero kuti: “M’zonse, caffeine siri chowononga chachikulu cha mkhalidwe wabwino wa dzikolo m’njira imene kusuta fodya kuliri.” Koma upandu wopezedwa umenewu wa kusuta uli kokha chiyambi chake.

Kupenda Chodzikhululukira Choipa

Kuti muwone chifukwa chimene kusuta kuli m’gulu losiyana kotheratu ndi zakudya ndi zakumwa, lingalirani kapangidwe ka thupi lanu. Mlaliki 7:29 amati “Mulungu analenga anthu owongoka mtima, koma iwowo afunafuna malongosoledwe amitundumitundu.” Pamene kuli kwakuti kudya kuli kachitidwe ka thupi lanu koperekedwa ndi Mulungu, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala osachiritsa kuli koyambitsidwa ndi munthu. Sipangakhale kagwiritsidwe kachibadwa, kapena kachikatikati ka zinthu zomwerekeretsa zimenezi. Kaya zisutidwa, kutengedwa monga mibulu, kapena mwa kulasidwa singano, izo zimadzutsa ndi kusokoneza kagwiridwe ka thupi m’njira zosemphana ndi zachibadwa.

Mosemphana, chifupifupi chakudya ndi chakumwa chirichonse chidzapereka zofunikira zachibadwa ku thupi lanu za mafuta, kukula, ndi kukonzanso zowonongeka za m’thupi. Kunenadi zowona, anthu okhala ndi mavuto aumoyo afunikira kupeŵa zakudya zamchere, mafuta, kapena caffeine. (Kwa odwala diabetes, suga wamba njangozi.) Koma kwa anthu ambiri, zakudya zimenezi ziridi ndi mapindu ena akuthupi ndipo, mwachikatikati, sizimapereka chivulazo. Koma ponena za kusuta iko kuli nkhani yosiyana kotheratu.

Ngakhale ndudu imodzi kapena ziŵiri, mofanana ndi kugwiritsira ntchito kamodzi kokha cocaine kaamba ka chisangalalo, kuli kogodomalitsa mwangozi. Phunziro la boma la Britain linapeza kuti pamene achichepere anasuta ndudu zochepera monga ziŵiri, iwo anali ndi 15 peresenti yokha ya mwaŵi wa kusakhala osuta kwa nthaŵi yonse.

Kukhala M’malo Anu Abwino Koposa Mwauzimu

Ndithudi inu simungakhale m’malo abwino koposa pokhala wosoŵa chochita wodalira pa mankhwala ogodomalitsa—“zisonkhezero zosakanika” za chikonga monga mmene sing’anga wamkulu wa ku U.S. anachilongosolera icho. M’malo molola thupi lanu kukutsogozani monga kapolo wake, Baibulo limalangiza kukhala wodziletsa, mphamvu ya ‘kutsogolera thupi lanu monga kapolo wanu.’—1 Akorinto 9:24-27.

Fodya samangowukira thupi la wosutayo—kuchititsa upandu wa kansa, emphysema, ndi nthenda ya mtima ndi mitsempha yake—koma amawukiranso mphamvu yake ya chifuno. Chotero, mwa kuipitsa kwake kwamachenjera, chizoloŵezicho chimaika umunthu wa wosutayo, kapena mkhalidwe wake wa maganizo mu ukapolo. “Kwa zaka 26,” anavomereza tero wolemba m’magazine ya Time, “ndakhala kapolo wa ndudu. Kwa chifupifupi zaka khumi, ndakhala ndikuyesera kudzimasula ndekha. Ali omwerekera ndi chikonga okha omwe ayesera mobwerezabwereza kuleka chizoloŵezicho ndipo alephera amene angamvetsetsedi mmene kuleka kuliri kovuta.”

Baibulo limatilangiza, pokhala okondedwa ndi Mulungu, “kudziyeretsera ife eni chidetso chirichonse [kuipitsidwa] cha thupi ndi mzimu.”—2 Akorinto 7:1; Kingdom Interlinear.

Kodi nchifukwa ninji Mulungu ayenera kusamala kaya timagwiritsira ntchito molakwa matupi athuathu ndi mphamvu za maganizo? Nchifukwa chakuti iye ali Mlengi wathu wachikondi, yemwe amatifuna kukhala bwino mokwanira molingana ndi chilengedwe chake. Mokomera malingaliro athu, iye akunena kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula [osati kudzivulaza].”—Yesaya 48:17.

Pamenepa, chitokoso chenicheni ndicho kukhala owona mtima kwa ife eni kaamba ka ubwino wathu. Kuli kopanda ntchito kuchirikiza kusuta chifukwa cha ziyambukiro zake zotonthoza kapena “maubwino” ena omwe samachita n’zochepera zomwe koma kokha kulephera kuchinjiriza mavuto okhalapo pofuna kuleka chikonga. M’kawonedwe ka zamankhwala, kusuta kwakhala ngozi ku umoyo wa anthu; koma mwachipembedzo, choyambitsidwa ndi anthu chimenechi cha kuloŵetsa chikonga m’njira za mwazi kupyola m’mapapo chanyalanyaza miyezo ya udongo ya Mlengi wathu nichiipitsa ndi kuwononga thupi la munthu. Chotero kodi nkuitaniranji vuto? Nkwabwinopo chotani nanga kulabadira mwambi wakuti: “Wochenjera awona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3.

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Vincent van Gogh, Skull With Cigarette, 1885. Courtesy of the National Museum, Amsterdam, Holland

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena