“Mulungu Akonda Wopereka Mokondwera”
YEHOVA ndiye mwini kupatsa. Kwenikweni, Baibulo limatero kuti iye ndiye Mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Mwachitsanzo, talingalirani za zinthu zimene Mulungu analenga. Anapanga chakudya chokoma, osati chozizira; maluŵa okongola, osati ongoti bii; kuloŵa kwa dzuŵa kochititsa kaso, osati kongoti mbuu. Inde, zonse zokhudza chilengedwe cha Yehova zimapereka umboni wakuti ndi wachikondi ndiponso wooloŵa manja. (Salmo 19:1, 2; 139:14) Ndiponso, Yehova ndi wopereka wokondwera. Amakondwera kuchitira atumiki ake zabwino.—Salmo 84:11; 149:4.
Aisrayeli analamulidwa kuti akhale opatsa kwa wina ndi mnzake monga momwe Mulungu alili. “Musakakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphaŵi,” anawauza motero Mose. “Muzimpatsa ndithu, osaŵaŵa mtima wanu pompatsa.” (Deuteronomo 15:7, 10) Popeza kuti kupatsa kunayenera kumachokera mumtima, Aisrayeli anayenera kusangalala ndi kuoloŵa manja.
Akristu anapatsidwanso malangizo ofananawo. Ndithudi, Yesu anati “kupatsa kutidalitsa.” (Machitidwe 20:35) Ophunzira a Yesu anapereka chitsanzo chabwino cha kupatsa mokondwera. Mwachitsanzo, Baibulo limasimba kuti ku Yerusalemu aja amene anakhala okhulupirira “[anagulitsa] zimene anali nazo, ndi chuma chawo, . . . nazigaŵira kwa onse, monga momwe yense anasoŵera.”—Machitidwe 2:44, 45.
Koma Ayuda ooloŵa manja amenewa pambuyo pake anakhala aumphaŵi. Baibulo silitchula chimene chinachititsa mkhalidwewo. Akatswiri ena amaphunziro amatero kuti njala yotchulidwa pa Machitidwe 11:28, 29 iyenera kuti ndiyo inachititsa zimenezi. Mulimonse mmene zinalili, Akristu a ku Yudeya anali pavuto lalikulu, ndipo Paulo anafuna kuonetsetsa kuti iwo akupeza zosoŵa zawo. Kodi anachita motani?
Zopereka za Osoŵa
Paulo anapempha thandizo kumipingo yakutali monga ku Makedoniya, ndipo analinganiza kuti pakhale zopereka zokathandizira Akristu okanthidwa ndi njala ku Yudeya. Kwa Akorinto, Paulo analemba kuti: “Monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula.”a—1 Akorinto 16:1, 2.
Paulo anali ncholinga choti ndalama zimenezi ziperekedwe msangamsanga kwa abale a ku Yerusalemu, koma Akorinto sanachitepo kanthu msanga pamalangizo a Paulo. Chifukwa chiyani? Kodi iwo anali kunyalanyaza vuto la abale awo a ku Yudeya? Ayi, popeza Paulo anadziŵa kuti Akorinto anali ‘kuchulukira m’zonse, m’chikhulupiriro, ndi m’mawu, ndi m’chidziŵitso, ndi m’khama lonse.’ (2 Akorinto 8:7) Ayenera kuti anali otanganidwa ndi nkhani zina zazikulu zimene Paulo anawalembera m’kalata yake yoyamba. Koma tsopano zinthu ku Yerusalemu zinali kufunika chisamaliro chamwamsanga. Choncho Paulo anafotokoza nkhaniyi m’kalata yake yachiŵiri kwa Akorinto.
Kuwapempha Kuti Asonyeze Kuoloŵa Manja
Choyamba, Paulo anauza Akorinto za Amakedoniya, amene anapereka chitsanzo chabwino popereka thangato. “M’chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chawo, ndi kusauka kwawo kwenikweni zidachulukira kucholemera cha kuoloŵa mtima kwawo.” Amakedoniya sanachite kulimbikitsidwa. M’malo mwake, Paulo anati “eni ake, [a]natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho.” Kupatsa mokondwera kwa Amakedoniya nkwapadera kwambiri makamaka pamene tikumbukira kuti iwo anali ‘osauka kwenikweni.’—2 Akorinto 8:2-4.
Pothokoza Amakedoniya, kodi Paulo anali kuyesa kudzutsa mzimu wampikisano pakati pa Akorinto? Kutalitali, popeza anali kudziŵa kuti imeneyi sindiyo njira yabwino yoperekera chisonkhezero. (Agalatiya 6:4) Ndiponso, anali kudziŵa kuti Akorinto sanafunikire kuchititsidwa manyazi kuti achite chinthu choyenera. M’malo mwake, anali ndi chidaliro chakuti Akorinto anali kukondadi abale awo a ku Yudeya ndipo anali ndi chikhumbo chopereka thangato kwa iwo. Iye anawauza kuti: “Munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira.” (2 Akorinto 8:10) Ndithudi, pambali zina zopereka thangato, Akorintowo anali kupereka chitsanzo chabwino. “Ndidziŵa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi [kwa, NW] Amakedoniya,” anawauza motero Paulo, nawonjezera kuti: ‘Changu chanu chinautsa ochulukawo.’ (2 Akorinto 9:2) Komano tsopano, Akorinto anafunikira kusonyeza ntchito za changu ndi chivomerezo chawo.
Chotero Paulo anawauza kuti: “Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwachisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.” (2 Akorinto 9:7) Chotero, cholinga cha Paulo sichinali kukakamiza Akorinto, chifukwa chakuti munthu sangapereke mokondwera ngati wakakamizidwa. Mwachionekere, Paulo anadziŵa kuti iwo anali kale ndi cholinga chabwino, kuti aliyense anali atatsimikiza mtima kale kuti adzapereka. Ndiponso, Paulo anawauza kuti: “Ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsoŵa.” (2 Akorinto 8:12) Inde, ngati pali kufunitsitsa—ngati munthu wasonkhezeredwa ndi chikondi—zimene akupereka zidzakhala zovomerezedwa kwa Mulungu, ngakhale zitaoneka kukhala zochepa motani.—Yerekezerani ndi Luka 21:1-4.
Opereka Mokondwera Lerolino
Thangato loperekedwa kwa Akristu a ku Yudeya likutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri m’tsiku lathuli. Mboni za Yehova zili pantchito yapadziko lonse yolalikira, kupereka chakudya kwa anthu mamiliyoni amene ali ndi njala yauzimu. (Yesaya 65:13, 14) Zimachita zimenezi potsatira lamulo la Yesu lakuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo . . . ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.”—Mateyu 28:19, 20.
Kuchita ntchito imeneyi nkovuta. Kumafuna kusamalira nyumba za amishonale ndi nthambi zoposa zana limodzi padziko lonse lapansi. Kumaloŵetsaponso kumanga Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Misonkhano kuti olambira Yehova akhale ndi malo abwino osonkhaniramo ndi kulimbikitsana. (Ahebri 10:24, 25) Nthaŵi zina, Mboni za Yehova zimaperekanso thangato kumadera kumene kwagwa tsoka lachilengedwe.
Talingaliraninso za ndalama zambiri zofunika posindikiza. Mlungu uliwonse, pa avareji, makope a Nsanja ya Olonda oposa 22,000,000 kapena makope ngati 20,000,000 a Galamukani! amasindikizidwa. Kuwonjezera pa chakudya chauzimu chanthaŵi zonse chimenechi, mamiliyoni a mabuku, mabolosha, makaseti omvetsera, ndi mavidiyo kaseti amapangidwa chaka chilichonse.
Kodi ntchito yonseyi imachirikizidwa bwanji? Mwa zopereka zaufulu. Zimenezi sizimaperekedwa kuti munthu atchuke kapena pachifukwa china chadyera, koma pofuna kupititsa patsogolo kulambira koona. Chotero, kupereka koteroko kumadzetsa chimwemwe kwa woperekayo, ndipo amadalitsidwa ndi Mulungu. (Malaki 3:10; Mateyu 6:1-4) Ngakhale ana pakati pa Mboni za Yehova amasonyeza kuti ngooloŵa manja, opereka mokondwera. Mwachitsanzo, Allison wa zaka zinayi atamva za mkuntho umene unawononga zinthu zambiri kuchigawo china cha United States, iye anapereka $2. “Ndalama zonse zimene ndinali nditasunga ndi zomwezo,” analemba motero. “Ndikudziŵa kuti zidole zonse ndi mabuku onse a ana zinawonongeka. Mwina mungagwiritsire ntchito ndalamayi kugulira mtsikana wa msinkhu wanga buku.” Maclean, wazaka zisanu ndi zitatu, analemba kuti anakondwera kuti palibe mbale amene anamwalira mumkunthowo. Anawonjezera kuti: “Ndinapeza $17 pogulitsa zitsulo za kumawilo a galimoto ndi bambo anga. Ndimafuna kugula zinazake ndi ndalamayi, komano ndinaganiza za abale.”—Onaninso bokosi pamwambapo.
Ndithudi, mtima wa Yehova umakondwera kuona ana ndi akuluakulu akuika za Ufumu wake patsogolo mwa ‘kumlemekeza ndi chuma chawo.’ (Miyambo 3:9, 10) Inde, palibe amene angalemeretse Yehova, popeza kuti zinthu zonse nzake. (1 Mbiri 29:14-17) Koma kuchirikiza ntchitoyi ndiko mwayi umene umapatsa wolambira mpata wosonyezera chikondi chake kwa Yehova. Tikuthokoza aliyense amene mtima wake wamsonkhezera kuchita zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti Paulo ‘analangiza,’ sizikutanthauza kuti anaika malamulo ake oti aliyense adziwatsatira. M’malo mwake, Paulo anali kungoyang’anira zoperekazo, zochokera kumipingo ingapo. Ndiponso, Paulo ananena kuti aliyense ‘payekha’ anafunikira kupereka “monga momwe anapindula.” M’mawu ena, chopereka chilichonse chinayenera kuperekedwa ndi munthu kwayekha ndiponso modzifunira. Palibe amene anakakamizidwa.
[Bokosi pamasamba 26, 27]
Njira Zimene Ena Amasankha Popereka Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse
Ambiri amapatula, kapena kulinganiza, ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku likulu la dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yakwawo.
Ndalama zoperekedwa mwaufulu zingatumizidwenso mwachindunji ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu. Majuwelo kapena zinthu zina za mtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso yeniyeni iyenera kutsagana ndi zoperekazo.
Makonzedwe a Chopereka cha Conditional-Donation
ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society pamakonzedwe apadera akuti, ngati woperekayo wakhala ndi kusoŵa kwinakwake, zoperekazo zidzabwezeredwa kwa iye. Kuti mudziŵe zambiri, chonde lemberani ku Treasurer’s Office paadiresi yosonyezedwa pamwambayo.
Kupatsa Kolinganiza
Kuwonjezera pa mphatso zenizeni za ndalama ndi ndalama zoperekedwa za conditional, palinso njira zina zoperekera kuti tithandize utumiki wa Ufumu wapadziko lonse. Zimenezi zikuphatikizapo:
Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni.
Maakaunti a ku Banki: Maakaunti a ku banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angaikiziridwe kapena kulipiridwa ku Watch Tower Society mwini wake atamwalira, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akwanuko.
Stock ndi Bond: Stock ndi bond ingaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kakonzedwe kamene woperekayo angapitirize kulandira ndalama za chiwongoladzanja.
Malo: Malo okhoza kugulitsidwa angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo mwini wake, amene angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Munthuyo ayenera kulankhula ndi Sosaite asanailoŵetse m’pangano la malo alionse.
Chuma cha Masiye ndi Choikizira: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma cha masiye lochitidwa mwalamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzalandira mapindu a pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma chopindulitsa gulu lachipembedzo lingakhale ndi mapindu ena a kuchepetsa msonkho.
Monga mwa tanthauzo la mawuwo “kupatsa kolinganiza,” zopereka zotere zimafunadi kuti woperekayo alinganize bwino. Kuti ithandize anthu ofuna kupindulitsa Sosaite kudzera mwa mtundu wina wa kupatsa kolinganiza, Sosaite yalemba bolosha lachingelezi lakuti Planned Giving to Benefit Kingdom Service Worldwide [Kupatsa Kolinganiza Kopindulitsa Utumiki wa Ufumu Padziko Lonse]. Boloshali linalembedwa chifukwa cha mafunso ambiri amene Sosaite inafunsidwa ponena za mphatso, chuma cha masiye, ndi chuma choikizira. Lilinso ndi chidziŵitso china chothandiza chonena za malo, kulinganiza ndalama ndi misonkho. Ndiponso lakonzedwa kuti lithandize anthu ku United States ofuna kupereka mphatso ku Sosaite panopo kapena kuisiyira chuma atamwalira kuti asankhe njira zopindulitsa ndiponso zabwino kwambiri malinga ndi mikhalidwe ya banja lawo ndi mikhalidwe yawo yaumwini.
Ataŵerenga bolosha limeneli ndi kukambirana ndi amene amagwira ntchito pa Planned Giving Desk, ambiri athandiza Sosaite ndiponso panthaŵi imodzimodziyo kupeza mapindu aakulu kwambiri a msonkho pochita zimenezo. Planned Giving Desk iyenera kudziŵitsidwa ndi kulandira makope a zikalata zilizonse zofunika za makonzedwe alionse amenewa. Awo amene akulifuna boloshali kapena amene akufuna kudziŵa za alionse mwa makonzedwe a kupereka kolinganiza kumeneku ayenera kulankhula ndi Planned Giving Desk, kaya mwa kuwalembera kalata kapena pafoni, paadiresi yosonyezedwa pansipa kapena ku ofesi ya Sosaite imene ikutumikira dziko lanu.
Planned Giving Desk
Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
100 Watchtower Drive, Patterson, New York 12563-9204
Telefoni (914) 878-7000
[Bokosi patsamba 28]
Ananso Amapereka Mokondwera!
Ndikukupatsani ndalamayi kuti mutipangire mabuku ambiri. Ndinaipeza pothandiza atate anga. Zikomo kwambiri pantchito yaikulu imene mumaichita.—Pamela, zaka zisanu ndi ziŵiri.
Ndikukutumizirani $6.85 kuti ithandizire kumanga Nyumba za Ufumu zowonjezereka. Ndaipeza chilimwe chino pamene ndinali kugulitsa lemonedi.—Selena, zaka zisanu ndi chimodzi.
Ndinali kusunga nkhuku imene inaswa tambala ndi msoti. Ndinapereka msotiyu kwa Yehova. Pomalizira pake inadzaswa misoti itatu, imene ndinagulitsa. Ndaikamo ndalama zake za ntchito ya Yehova.—Thierry, zaka zisanu ndi zitatu.
Ndalama zonse zomwe ndili nazo ndi zomwezo! Zigwiritsireni ntchito bwino. Zinali zovuta kupeza. Nayi $21.—Sarah, zaka khumi.
Ndinalandira mphotho yoyamba pantchito ina imene anatipatsa kusukulu, choncho ndinapita kukapikisana ndi a m’chigawo chathu. Ndinapatanso mphotho yoyamba kumeneko kenako mphotho yachiŵiri pampikisano womaliza wa m’chigawo. Pazonsezi, mphotho zake zinali ndalama. Ndikufuna kugaŵirako Sosaite ndalamazo. Ndikuona kuti ndinatha kupata mphotho zimenezi chifukwa cha maphunziro amene ndalandira pa Sukulu ya Utumiki Wateokratiki. Sindinatekeseke popereka lipoti langa pamaso pa oweruza.—Amber, wagiledi yachisanu ndi chimodzi.
Ndati ndikupatseni izi kaamba ka Yehova. Mfunseni chochita nazo. Akudziŵa zonse.—Karen, zaka zisanu ndi chimodzi.
[Zithunzi patsamba 25]
Ntchito ya Mboni za Yehova imachirikizidwa ndi zopereka zaufulu