Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 6/8 tsamba 14-16
  • Kodi Mulungu Adzakhalabe Bwenzi Langa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Adzakhalabe Bwenzi Langa?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Munga m’Thupi”
  • Chithandizo Popirira Zovuta
  • Mmene Tingapezere Chithandizo cha Mulungu
  • Kugwira Ntchito ndi Mulungu
  • “Talaŵani, Ndipo Onani Kuti Yehova Ndiye Wabwino”
  • Kulimbana ndi “Munga M’thupi”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kufooka kwa Anthu Kusonyeza Mphamvu ya Yehova
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Tingakhale Amphamvu Ngakhale Tili Ndi Zofooka
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Muli ndi “Munga m’Thupi”?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 6/8 tsamba 14-16

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Mulungu Adzakhalabe Bwenzi Langa?

MFUMU DAVIDE ndi munthu amene anali bwenzi la Mulungu. Koma panthaŵi ina anati: “Masautso a mtima wanga akula.” Davide anali kuvutika osati chifukwa chabe chosautsidwa ndi ena, komanso chifukwa cha zolakwa zake. Anayamba kumva ngati kuti Mulungu anamukana, ndipo anapemphera: “cheukirani ine ndipo ndichitireni chifundo; pakuti ndili wounguruma ndi wozunzika.”—Salmo 25:11, 16-19.

Mwina inunso mukusautsidwa. Mwina ndi kunyumba kwanu kapena kusukulu komwe zinthu sizikukuyenderani bwino ndipo mwathedwa nzeru. Ndiye mwinanso, muli ndi matenda aakulu kapena mwina muli ndi mphwayi chifukwa cha zofooka zomwe muli nazo. Mulimonse momwe zilili, simuyenera kuvutika panokha; Mulungu amadzipereka mofunitsitsa kukhala bwenzi ndi kuthandiza.a Ngati mwayamba kale kukulitsa ubwenzi ndi iye, mudzasangalala kuzindikira kuti iye sasiya mabwenzi ake pamene akuvutika. Ngakhale nditero, pamene muli m’mavuto, mungaone ngati kuti Mulungu ali patali. Mukhoza kuona ngati kuti sakuthandiza nkomwe. Koma kodi zili chonchodi?

“Munga m’Thupi”

Choyamba, ŵerengani 2 Akorinto 12:7-10. Pamenepo mtumwi Paulo akunena za mmene anavutikira ndi chinachake chotchedwa “munga m’thupi.” “Munga” umenewo ungakhale unali chilema, mwinamwake linali vuto la maso. Kaya chinali chiyani, koma chinali ‘kumutundudza’ m’maganizo. Ngakhale kuti anachonderera katatu kwa Mulungu kuti auchotse, “munga” sunachoke.

Kodi Yehova anali kunyalanyaza mapemphero a Paulo? Ayi! Mulungu anati kwa iye: “Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.” Ngakhale kuti Yehova anasankha kusachotsa ‘mungawo,’ iye sanamusiye Paulo. Mwa chisomo cha Mulungu, Paulo anasangalala ndi ubwenzi wathithithi ndi iye. Izi zinali ‘zokwana’ kuthandiza Paulo kupirira chilemacho m’thupi. Pamene Paulo anayesayesa kutero, anafikanso pozindikira njira yatsopano imene mphamvu ya Mulungu inamthandizira.

Chithandizo Popirira Zovuta

Monga Paulo, mungakhale ndi “munga,” kapena vuto, lomwe limakubayani, kukutayitsani mtima ndi kukulefulani. Monga momwe zinalili ndi Paulo, Mulungu angalole kuti vutolo lipitirize. Izi sizitanthauza kuti iye sali Bwenzi lanunso. Mulungu anauza mtumwi Paulo kuti: ‘Mphamvu yanga ithedwa m’ufoko.’ Ngati mumadalira mphamvu ya Mulungu osati yanu, mungathe kupirira. Mungapezenso kuti ndi chithandizo cha mzimu wa Mulungu, mukutha kuchita zomwe munkaganiza kuti nzosatheka. Paulo anati: “Chifukwa chake ndisangalala m’maufoko . . . Pakuti pamene ndifoka, pamenepo ndili wamphamvu.”

Mayi wachitsikana wina wotchedwa Robinb anaona kuti zimenezi nzoona. Pausinkhu wa zaka 14 anafa maso ndi matenda a maso otchedwa glaucoma. Chaka chomwecho amayi ake anamwalira mwadzidzidzi. “Ndinatsala ndi Yehova yekha,” akutero Robin ponena za kuyamba kulimbana ndi ‘minga’ zoŵaŵazi. “Ndinazindikira kuti ngati ndinati ndithane nazo, ndinayenera kumamatira kwambiri kwa iye.” Robin anaterodi, pambuyo pake akumatumikira monga mlaliki wanthaŵi zonse. Iye akuti: “Ndinapempha Yehova kuti andithandize pa chilichonse. Ndipo iye anaterodi.”

Achinyamata ambiri apeza kuti kukumana ndi ziyeso kumawathandiza kuyandikira kwa Mulungu. Lingalirani za mnyamata wina Jeff. Atate ake analileka banjalo, akumasiyira amayi ake a Jeff kusamalira ana asanu ndi aŵiri. “Ndinawalakalaka kwambiri atate,” akuvomereza tero Jeff, amene anali ndi zaka 12 zokha panthaŵiyo. “Ndinalakalaka kuti bwenzi panali wina wonditonthoza masiku onse.” Kodi Jeff anachita chiyani? “Ndinapemphera kwa Yehova kuti akwaniritse, zomwe ndinali kufuna.” Jeff anachita mogwirizana ndi pemphero lake ndipo anamwerekera m’zinthu zauzimu. M’kupita kwa nthaŵi, anatha kuzindikira kuti Yehova anali kumthandiza—akumatero kupyolera mwa chilimbikitso cha mzimu wake woyera ndiponso mwa mpingo wachikristu. (Yerekezerani ndi Salmo 27:10.) Tsopano pausinkhu wa zaka 27 Jeff akukumbukira: “Ndinalibe aliyense woti nkudalira, choncho ndinayandikira kwa Yehova.” Iye amatcha ubwenzi wathithithi umenewo “dalitso lamtengo wapatali lomwe linabwera pa kuyesayesa kumeneku.”

Mmene Tingapezere Chithandizo cha Mulungu

Bwenzi lanu lakumwamba lidzakuthandizani mofananamo pa mavuto anu. Koma kodi muyenera kuchitanji? Chabwino, kuti ubwenzi uliwonse ukonde, pamafunika kulankhulana. Pemphero ndiyo njira yathu yolankhulirana ndi Mulungu. Kupyolera mwa ilo timamdziŵitsa Mulungu kuti tikufuna thandizo lake. Komabe, pemphero nlopanda phindu kwenikweni ngati silili lochokera pansi pamtima kapena longonena chinenenene. Monga achinyamata omwe tanenapo kale, inu muyenera ‘kutsanulira mtima wanu’ kwa Mulungu! (Salmo 62:8) Mungafunikire mwina mpaka kupembedzera. (Afilipi 4:6) Mapembedzero ndi mapemphero omwe mumapereka mochonderera kwambiri ndiponso mwaphamphu.

Mwinamwake muli ndi vuto kulamulira maganizo anu kapena mukulephera kuthetsa chizoloŵezi china choipa. Pembedzani Yehova! Pemphani chithandizo chake pomwe muli pa chiyeso. Izi sikuti zingakhale zapafupi nthaŵi zonse. “Pamene ndikakamizika kwambiri kuchita chinachake chomwe chili choipa, ndimadzikakamiza kupemphera,” anatero Gary. “Nthaŵi zina ndimaganiza kuti, ‘Kodi ndingamfikire motani Yehova?’ Koma, ndimachondererabe thandizo lake. Amandipatsa mphamvu zomwe ndimafuna kuti ndipirire.” Ngakhale ngati zili zovuta poyamba, pitirizanibe kutsanulira mtima wanu kwa Mulungu.

Komabe bwanji ngati kukuoneka kuti mapemphero anu sakuyankhidwa? Mwachitsanzo, Lora, anali kuyesayesa kugonjetsa chizoloŵezi cha psotopsoto. “Ndimanena kwa Yehova za vutolo moona mtima,” iye akulongosola, “koma zimachitika ngati sindidzasiya.” Nthaŵi zina Mulungu angatilole kuti tisonyeze kufunitsitsa kwathu zimene tikupemphazo. (Yerekezerani ndi Salmo 88:13, 14.) Choncho tiyenera kulimbikira kupemphera! (Mateyu 7:7; Aroma 12:12) Lora anachitadi zimenezo. Ndiponso, anayamba kugwiritsira ntchito mfundo zopezeka m’zofalitsa za Watch Tower Society zonena za vutolo.c M’kupita kwa nthaŵi, anayamba kuona zotsatira zake. Iye akukumbukira: “Nthaŵi iliyonse pamene ndigonjetsa chiyesocho, ndimathokoza Yehova chifukwa ndimadziŵa kuti akundithandiza.” Zoona, nthaŵi zina mungafokere pamene muli mkati molimbana ndi vuto lanulo kuti muligonjetse. Komabe ngati mukuyesetsa kulimbana nalo ndipo simukugonjera dala pa chofooka chanucho, Mulungu adzakondwera ndi “changu [chanu] chonse” ndipo adzakhalabe Bwenzi lanu.—2 Petro 1:5.

Kugwira Ntchito ndi Mulungu

Njira ina yopezera chithandizo cha Mulungu ndiyo kuvomera pempho lake lakuti tikhale “antchito anzake.” (1 Akorinto 3:9) Izi zimaphatikizapo kuthandiza ena kuphunzira za Mulungu. (Mateyu 28:19, 20) Ngati mwapsinjika maganizo kapena mwataya mtima, ganizo loyamba ntchito ya mtundu uliwonse simungakondwere nalo. Komabe, kukhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye” kukhoza kukuthandizani kwambiri. (1 Akorinto 15:58) Mudzaiŵala za mavuto anu. (Yerekezerani ndi Miyambo 18:1.) Robin wotchulidwa poyamba uja, anati ponena za nthaŵi yake ya mavuto: “Chomwe chinandithandiza kupirira chinali kugwira ntchito ya Yehova!”

Kugwira ntchito ndi Mulungu kudzakuthandizaninso kutaya malingaliro alionse akuti Mulungu wakusiyani. Pamene anthu aŵiri akugwirira ntchito limodzi ncholinga chimodzi, kodi sizoona kuti kaŵirikaŵiri amagwirizana? Ndipo pamene muli pa ntchito yaulaliki, kaŵirikaŵiri mumakumana ndi zothetsa nzeru. Mudzapeza kuti mukutembenukira kwa Mulungu kupempha chithandizo. Ndipo pamene Mulungu akudalitsa ntchito yanu, mpamene ubwenzi wake umaonekera kwambiri. Mumayamba kuzindikira chikhulupiriro chomwe Mulungu ali nacho pa inu monga wantchito mnzake. Izi zingakulitse chidaliro chanu.

Mwachitsanzo, Carol anali wopanda chitetezo. Amayi ake anali atadzipha, ndipo atate ake anali kumunyoza kosalekeza. Koma pausinkhu wa zaka 17 anakhala Mboni ya Yehova ndipo anayamba ntchito yolalikira. Tsopano pambuyo pa zaka khumi ali mlaliki wanthaŵi zonse, iye akuti: “Ntchito iyi yandithandiza kwambiri chifukwa ndaona madalitso a Yehova pa ine. Ndimadziuza kuti, ‘Ngati Mulungu amandikonda, sindine wachabechabe.’ Kugwiritsiridwa ntchito ndi Yehova kulengeza dzina lake kwandipangitsa kukhala wotetezereka kwambiri.”

“Talaŵani, Ndipo Onani Kuti Yehova Ndiye Wabwino”

“[Mulungu a]nandilanditsa m’mantha anga onse,” inalemba tero Mfumu Davide itapulumuka mkamwa mwa mkango. (Salmo 34:4, 6, timawu tapamwamba; 1 Samuel 21:10-12) Davide malinga ndi zomwe zinamchitikira anatha kunena kuti: “Talaŵani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino, wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.”—Salmo 34:8.

Ngakhale kuti moyo wanu sungakhale pangozi monga momwe wa Davide unalili, nkosakayikitsa kuti nthaŵi zina mudzapsinjika maganizo ndiponso kuvutika. Ngati ‘masautso a mtima wanu akula,’ pembedzani Mulungu. (Salmo 25:17) Musaope kuti Mulungu adzathetsa ubwenzi wake. Pamene mupirira moleza mtima ndi kulandira thandizo ndi chisamaliro chochokera kwa Yehova, ‘mudzalaŵa ndi kuona’ nokha “kuti Yehova ndiye wabwino.” Ndipo adzakhalabe Bwenzi lanu kosatha.—Yakobo 4:8.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Achichepere akufunsa kuti . . . Kodi Ndingakhale Bwenzi la Mulungu?” m’kope lathu la August 8, 1995.

b Maina ena asinthidwa.

c Onani mitu 25 ndi 26 m’buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 15]

Kodi Mulungu amasiya mabwenzi ake panthaŵi ya mavuto?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena