Kuika Maseŵera m’Malo Ake Oyenera
PAMENE anthu aseŵera maseŵera awo apamtima, amasangalatsidwa pamene matupi awo azoloŵera ndi kuchita machitachita olira luso kapena chipiriro. Mulungu anatilenga kuti tizisangalala ndi maseŵera olimbitsa thupi. Ngakhale anthu ambiri mwina amasanguluka ndi kuwonerera ena akuseŵera. Chotero maseŵera ali ofanana kwenikweni ndi zinthu zambiri zomwe ziri zabwino pamene zaikidwa m’malo ake oyenera.
Naku kufotokoza mwafanizo: Pamene anthu apita ku gombe kukasangalala ndi kuwothera dzuŵa, kodi nchiyani chimene chimachitika pamene iwo akhala padzuŵa kwanthaŵi yaitali? Amapsa ndi chitungu cha dzuŵa chimene chimawononga kusangulukako ndipo ngakhale kuika moyo pachiswe. Kuli kofanana ndi maseŵera. Maseŵera achikatikati ngabwino, koma opambanitsa angakhale aupandu.
Maseŵera akhoza kukhala otsitsimula kwenikweni ndi osangulutsa, komabe sayenera kukhala chonulirapo chachikulu. Iwo samadzetsa chikhutiro chenicheni kapena chimwemwe chokhalitsa. Mwachisoni, nthaŵi zina kumalira tsoka lenileni kuti munthu azindikire zimenezi. “Zikho zanga zonse ndi medulo, sizofunika kwenikweni,” anafotokoza motero Mary Wazeter, woseŵera maseŵera olira nyonga wamkazi yemwe analumpha kuchokera pa ulalo nafa ziŵalo.
Iye akusimba kuti: “Ndaphunzira zowona zochuluka ponena za moyo. Chimodzi cha izo nchakuti chikhutiro sichimapezedwa mwa njira zimene anthu ambiri amafunira ukatswiri wachikwanekwane ndi chipambano. Chikhutiro kwa ine sichinadze mwakukhala wophunzira wolandira giredi yapamwamba ya A, ungwazi wa maseŵera othamanga wadziko lino kapena wopata mfupo yokhumbirika.”
Akumaika nkhani zimenezi m’kapenyedwe kabwino mofulumira, John Whitworth, katswiri wazamayanjano anati: “Chomwe mumakhala nacho pamapeto a maseŵerawo ndicho ndandanda ya ziŵerengero za opambana ndi olephera. Iyo iri mphotho yopanda chiyambukiro chenicheni. Komabe, ndikhulupirira kuti iri ndi mpangidwe wosakwanira mofanana ndi chitaganya chathu.” Chigogomezero chopambanitsa choikidwa pa maseŵera chimachotsa lingaliro lenileni la chimene chiri chofunika kwenikweni.
Pambuyo pa chipambano chake m’liŵiro lothamanga mamita 200 m’maseŵera a Olympic mu 1964, Henry Carr anafotokoza kuti: “Pamene ndinkabwerera ku Midzi ya Olympic, ndinayang’anitsitsa kwanthaŵi yoyamba medulo yagolidi. . . . Ndinadzifunsadi kuti: ‘Kalanga ine! Kodi zaka zonsezi zomwe ndakhala ndikugwira ntchito zolimba, ndikudzalandira ichi eti?’ Ndinakwiya ndithu mmalo mwakukhala wachimwemwe. Kunalidi kugwiritsidwa mwala.” Marlon Starling anamva mofananamo pambuyo popambana ungwazi wa nkhonya wa welterweight wa World Boxing Association mu 1987. Iye anati: “Dzina laukatswiri limenelo liposedwa ndi mawu a mwana wanga akuti, ‘Atate, ndimakukondani.’”
Chotero phunziro lalikulu lingaphunziridwe lakuti: Ntchito yopindulitsa, banja, ndipo makamaka kulambira Mulungu kuyenera kukhala koyambirira. Baibulo nlolondola pamene limati: ‘Chizoloŵezi cha thupi [chimene maseŵera amapereka] chipindula pang’ono.’ (1 Timoteo 4:8) Zimenezi zimasonyeza malo oyenera kaamba ka maseŵera m’miyoyo yathu. Iwo ayenera kukhala achiŵiri. Popeza kuti maseŵera angakhale osangulutsa, munthu afunikira kukhala watcheru nthaŵi zonse kotero kuti zinthu zofunika koposa zisanyalanyazidwe.
Chifukwa chake, khalani osamala mwanzeru ngati ziŵalo zabanja zidandaula kuti mumathera nthaŵi yochuluka mukumalankhula za maseŵera, kumawawonerera, kapena kumawaseŵera. Mkazi wina, amene mwamuna wake anapanga masinthidwe m’chidwi chake cha maseŵera, anati moyamikira: “Iye tsopano amathera nthaŵi yochuluka pamodzi ndi ana ndi ine. Nthaŵi zina banja lathu limawonerera maseŵera pa wailesi yakanema, koma madzulo ambiri timapita kokayenda pamodzi ndi kumalankhula za zochitika za tsikulo. Zimenezi nzosangalatsa ndipo zimatithandiza kukhalabe achimwemwe.”
Pozindikira mavuto aakulu, bwanji osalingalira funso lotsatirali mowona mtima: Kodi ndimathera nthaŵi yowonjezereka ndi chisamaliro ku maseŵera yoposa imene ndiyenera kuitha? Komabe, palinso mfundo zina m’nkhani imeneyi ya kuika maseŵera m’malo oyenera.
Bwanji Ponena za Mpikisano?
Kuti maseŵera akhale opindulitsa mmalo mokhala ovulaza, kaimidwe kamaganizo koyenera kulinga kumpikisano nkofunika. “Alangizi, aphunzitsi amaseŵera olimbitsa thupi, makolo, ndi ana omwe akhala oyedzamira kwambiri pa kupambana kwakuti amaiŵala chimene chifuno cha maseŵera chiri [kwa anthu achichepere],” anadandaula motero sing’anga wa timu ya maseŵera a hockey yaukatswiri. Iye anati, chifuno cha maseŵera chiyenera kukhala “kukulitsa mzimu wakugwirira pamodzi monga gulu ndi kudziletsa, kulimbitsa thupi, ndipo, chofunika koposa, kusanguluka.”
Komabe, mwachisoni, chigogomezero cha kupambana chawononga kusanguluka kwa anthu ambiri. Bruce Ogilvie, katswiri wazamaganizo m’maseŵera anati: “Nthaŵi zina ndinafunsa oseŵera oyamba kumene a m’magulu aakulu 10 a baseball okhala m’misasa yoyesezera maseŵera mwakanthaŵi ndipo 87 peresenti anati sanafune kuseŵera ndi timu ya baseball ya Little League chifukwa chakuti kunachotsa kusanguluka m’maseŵera.” Vuto lalikulu ndilo lakuti mzimu wakupikisana mopambanitsa umawonjezera ziŵerengero zazikulu za kuvulala.
Baibulo limapereka zitsogozo, likumati: ‘Tisakhale odzikuza, [outsirana mpikisano, “NW”], akuchitirana njiru.’ (Agalatiya 5:26) Malinga ndi mabuku omasulira mawu kuchotsa m’Chigiriki kupereka m’Chingelezi, liwu Lachigiriki lomasuliridwa “outsirana mpikisano” limatanthauza “kuitanira,” “kutokosera ku kulimbana kapena kuchita makani ndi wina.” Chifukwa chake An American Translation iri ndi mamasulidwe aŵa: “Tisakhale otokosana m’kupanda pake kwathu.” Ndipo mawu amtsinde a New World Translation amapereka lingaliro lina iri: “Kukankhizirana m’kulimbana.”
Mowonekera bwino ndithu, kuutsa mpikisano sikuli kwanzeru. Sikumapanga maunansi abwino. Ngati mwapambanidwa ndi kugonjetsedwa, ndipo wolakikayo adzitama ndi chipambanocho, chokumana nachocho chingakhale chochititsa manyazi. Kaimidwe kamaganizo kofuna kupikisana mopambanitsa kali kopanda chikondi. (Mateyu 22:39) Kumbali ina, ngati mpikisanowo wazikidwa pa mkhalidwe waubwenzi, wosamaliridwa bwino, ukhoza kuwonjezera chikondwerero ndi chisangalalo cha maseŵerawo.
Ena angafune njira zoseŵerera kotero kuti achepetseko mbali yakupikisana. “Ndinali wokhulupirira maseŵera weniweni wosafuna phindu lapadera kufikira msinkhu wazaka 13 kapena 14,” anatero Mngelezi wina wophunzitsa mpira wachitanyu. Anapereka lingaliro la kusasunga zolembedwa za zotulukapo kapena za kaimidwe ka matimu—“sipayenera kukhala masitepe ofunikira kuwafikira akupita patsogolo, sipayenera kukhala mpikisano womalizira.” Inde, chigogomezero cha kupambana chiyenera kuchepetsedwa moyenerera kapena kuchotsedwa kotheratu.
Kaimidwe Kamaganizo Kulinga kwa Oseŵera Maseŵera Olira Nyonga
Kuikabe maseŵera m’malo ake oyenera kudzaphatikizapo kaimidwe kathu kamaganizo kulinga kwa oseŵera maseŵera olira nyonga aluso, otchuka. Zowonadi, tingakhumbire kukhoza kwawo m’maseŵera olira nyonga ndi maluso awo odabwitsa. Koma kodi iwo ayenera kupangidwa kukhala fano? Achichepere amawonedwa kaŵirikaŵiri akuika zithunzithunzi za oseŵera maseŵera olira nyonga oterowo m’zipinda zawo. Kodi zipambano za anthu oterowo zimaŵapangadi kukhala oyenerera ulemu? Mwinamwake chosiyana ndicho chimachitika.
Woseŵera watsopano m’timu yolimbira ungwazi wa National Football League poyamba anakhumbira mabwenzi ake ambiri a m’timu. Koma iye anati mayendedwe awo ndi kaimidwe kamaganizo, “zinangothetsa malingaliro onse ndi ulemu umene ndinali nawo kwa iwo.” Iye anafotokoza kuti: “Mwachitsanzo, iwo akanena kuti: ‘Tamverani, ndinagonana ndi asungwana asanu mlungu wathawu, osaphatikizapo mkazi wanga.’ Ndipo ndinayang’ana munthuyu ndikulingalira kuti: ‘Choncho uyu ndiye munthu yemwe ndinapanga kukhala fano ati.’”
Ndithudi, kuli kosayenera kupanga munthu aliyense kukhala fano, ndipo izi zikakhala zowona makamaka kwa amene amapambana m’machitachita omwe Baibulo limati ali ndiphindu laling’ono kapena losakhalitsa. Atumiki a Mulungu amafulumizidwa ‘kuthaŵa kupembedza mafano.’—1 Akorinto 10:14.
Mmene Maseŵera Aliri Opindulitsa
Monga momwe tawonera, Baibulo limanena kuti chizoloŵezi cha thupi, monga chochitidwa m’maseŵera, ‘chimapindula pang’ono.’ (1 Timoteo 4:8) Kodi zimenezi ziri choncho motani? Kodi ndimotani mmene mungapindulire ndi maseŵera?
Galen, sing’anga Wachigiriki wa m’zaka za zana lachiŵiri yemwe anali sing’anga wa Marcus Aurelius wolamulira wa Roma, anagogomezera kufunika kwa maseŵera olimbitsa thupi kaamba ka thanzi wamba. Ndipo anayamikira maseŵera ampira, popeza kuti ameneŵa amalimbitsa thupi lonse mwachibadwa. Maseŵera ampira kaŵirikaŵiri alinso osangulutsa kuwaseŵera, choncho munthu adzafunitsitsa kuseŵera maseŵera amene amasangalala nawo koposa kukhala ndi phande m’maseŵera ena olimbitsa thupi.
Ambiri amapeza kuti kulimbitsa thupi kumene amapeza m’maseŵera kumaŵapatsa lingaliro lakudzimva bwino. Pambuyo pa nyengo yakuyeseza kotsitsimula kapena maseŵera, iwo amadzimva kukhalanso ndi nyonga ndi mpumulo. Komabe zimenezi siziyenera kutidabwitsa, popeza kuti, monga momwe Dr. Dorothy Harris ananenera, “maseŵera olimbitsa thupi ndiwo mankhwala achibadwa abwino koposa odzetsa mpumulo.”
Kulimbitsa thupi, monga kuja kochitidwa m’maseŵera a calisthenics (maseŵera ochitidwa ncholinga chakukhala ndi thupi lolimba, lokongola ndi lathanzi), kuthamanga pang’onopang’ono, ndi maseŵera ena, kumazindikiridwa ndi ambiri lerolino kukhala kofunika ku thanzi labwino. “Anthu olimba mwakuthupi amagwira ntchito zawo zanthaŵi zonse mosavuta popanda kutopa ndipo amakhalabe ndi nyonga kaamba ka zofuna zina,” ikutero The World Book Encyclopedia. “Iwo angakhalenso okhoza kulimbana bwino ndi ziyambukiro za ukalamba koposa ndi omwe sali olimba mwakuthupi.”
Komabe, mosasamala kanthu za mmene maseŵera angathandizire munthu kukhala ndi thupi lolimba, mapindu ngosakhalitsa. Ukalamba ndi imfa sizingathetsedwe ndi zoyesayesa za anthu. Chikhalirechobe, pambuyo ponena kuti “kuphunzitsa thupi nkopindulitsa pang’ono,” Baibulo limati: “Kudzipereka kwaumulungu nkopindulitsa zinthu zonse, popeza kumakhala ndi lonjezo la moyo tsopano ndi uja umene ulinkudza.”—1 Timoteo 4:8, NW.
Kokha Yehova Mulungu, Mlengi wathu, akhoza kutipatsa moyo. Choncho, palibe chirichonse chimene chiri chofunika kuposa “kudzipereka kwaumulungu,” ndiko kuti, ulemu, kulambira, ndi utumiki kwa Mulungu. Chotero amene amalondola kudzipereka kwaumulungu adzachita chifuniro cha Mulungu monga chinthu chofunika koposa kwa iwo. Adzadziloŵetsa muutumiki wa Mulungu, akumagwiritsira ntchito uchichepere wawo mofanana ndi mmene Yesu Kristu anachitira, kuuza ena zinthu zabwino ponena za Mulungu ndi Ufumu wake.
Inde, mwakuika zabwino za Mulungu patsogolo, anthu angapeze chiyanjo chake ndi moyo wosatha m’dziko lake latsopano lolungama. M’menemo, Yehova, Mulungu wachimwemwe, adzaŵapatsa chimwemwe chenicheni chokhalitsa ndi chikhutiro.