Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 11/15 tsamba 26-29
  • Akulu—Bwezani Ena Mumzimu Wachifatso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akulu—Bwezani Ena Mumzimu Wachifatso
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu wa Mtumwi
  • Njira Zina Zothandiza
  • Magwero Achisangalalo
  • Mverani Atsogoleri
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Akulu—Samalirani Gulu la Mulungu Mokoma Mtima!
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Pitirizani Kusunga Amuna Oterowo Okondedwa”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Ŵetani Gulu la Nkhosa la Mulungu Mofunitsitsa
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 11/15 tsamba 26-29

Akulu​—Bwezani Ena Mumzimu Wachifatso

MTIMA wa Mkristu wowona ungayerekezeredwe ndi dimba lauzimu lobala zipatso zabwino kwambiri. Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi kudziletsa zimene kaŵirikaŵiri zikafunga kumeneko. Ndipo kulekeranji? Ndiiko komwe, zimenezi ziri zipatso za mzimu woyera umene Yehova Mulungu amapatsa atumiki ake odzipatulira. (Agalatiya 5:22, 23) Chikhalirechobe, Mkristu aliyense wofuna kusunga dimba la mtima wake kukhala malo okondweretsa kwa Atate wake wakumwamba ayenera kumenya nkhondo yamphamvu, yosalekeza motsutsana ndi kaufiti wauchimo wacholoŵa.​—Aroma 5:5, 12.

Panthaŵi zina, kanthu kena kosakondweretsa kamayamba kukula mumtima wopanda ungwiro wamunthu wopembedza. Iye angakhale anali ndi mbiri yabwino kwambiri yauzimu. Ndiyeno pangabuke vuto lina, mwinamwake lochokera m’mayanjano oipa kapena chosankha chosakhala chanzeru. Kodi akulu mumpingo angathandize motani munthu wotero mwauzimu?

Uphungu wa Mtumwi

Pothandiza Mkristu amene walakwa, akulu afunikira kutsatira uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Abale, ngakhale kuli kwakuti munthu atenga njira ina yoipa iye asanaizindikire, inu amene muli ndi ziyeneretso zauzimu yesani kubweza munthu woteroyo mumzimu wachifatso, pamene inu aliyense payekha mukudzipenyerera, kuwopera kuti nanunso mungayesedwe.” (Agalatiya 6:1, NW) Pamene wokhulupirira mnzathu watenga “njira ina yoipa iye asanaizindikire,” akulu ali ndi thayo lakupereka chithandizo mwamsanga monga momwe kungathekere.

Paulo akusonya kwa ‘mwamuna’ kukhala akutenga njira ina yoipa. Komabe, liwu Lachigiriki (anʹthro·pos) logwiritsidwa ntchito pano lingagwiritsiridwe ntchito kwa mwamuna kapena kwa mkazi. Ndipo kodi “kubweza” munthu kumatanthauzanji? Liwu Lachigiriki (ka·tar·tiʹzo) limeneli limatanthauza “kubwezera mmalo oyenera.” Liwu lofananalo limagwiritsidwa ntchito posoka makoka. (Mateyu 4:21) Limagwiranso ntchito pokonza chiŵalo chothyoka cha munthu. Dokotala amachita zimenezi mosamalitsa kuti apewe kumvetsa ululu mopambanitsa mtenda wake. Mofananamo, kuthandiza mbale kapena mlongo kumbwezeretsa mumkhalidwe woyenerera wauzimu kumafunikira kusamala, luso, ndi chifundo.

Akulu amapereka umboni wa mkhalidwe wauzimu wa iwo eni mwakusonyeza mzimu wachifatso pamene ayesa kubweza munthuyo. Ndithudi, Yesu wamtima wofatsayo anali wokhoza kusamalira zochitika zotero mwachifatso. (Mateyu 11:29) Akulu akayenera kusonyeza mkhalidwe umenewu kwa mtumiki wa Yehova amene wotenga njira yoipa chifukwa chakuti akulu eniwo sali osakhoza kugonjetsedwa ndi uchimo, motsutsana ndi zikhumbo za mtima wawo. Zimenezi zingachitike mtsogolo ngati sizinachitike kale nthaŵi yapita.

Amuna oyeneretsedwa mwauzimu amenewa ayenera mwachikondi ‘kusenza zothodwetsa’ za olambira anzawo. Ndithudi, akulu ali ndi chikhumbo m’mitima yawo chakuthandiza mbale kapena mlongo kulimbana ndi Satana, mayesero, zofooka zathupi, ndi nsautso za uchimo. Zimenezi ziridi njira imodzi imene oyang’anira Achikristu ‘angakwaniritsire lamulo la Kristu.’​—Agalatiya 6:2.

Amuna okhala ndi ziyeneretso zauzimu zowona ngodzichepetsa, akumazindikira kuti “ngati aliyense aganiza kuti ali kanthu pamene iye sali kanthu, akunyenga maganizo ake a iyemwini.” (Agalatiya 6:3, NW) Mosasamala kanthu mmene akulu angayeseyesere mwamphamvu kuchita cholungama ndi kukhala othandiza, iwo adzapereŵerabe kufikira ungwiro ndi kukoma mtima kwachikondi za Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu. Koma chimenecho sichiri chifukwa chakusachitira zothekera koposa.

Akulu amazindikira kuti kukakhala kulakwa kutsutsa wokhulupirira mnzawo mwanjira yodzitamandira, monga ngati kuti iwo ali angwiro! Ndithudi Yesu sakachita zimenezo. Eya, iye anapereka moyo wake osati kaamba ka mabwenzi ake okha, komanso kaamba ka adani ake! Akulu amayesayesa kusonyeza chikondi chofananacho poyesa kuthandiza abale ndi alongo kutuluka m’vuto ndi kuwabweretsa pafupi kwambiri ndi Atate wawo wakumwamba ndi miyezo yake yolungama. Kodi nziti zimene ziri njira zina zomwe zidzathandiza akulu kubweza okhulupirira anzawo?

Njira Zina Zothandiza

Dalirani Yehova mwapemphero pamene mukulankhula ndi kuchita mwanjira yachifatso. Yesu anali wofatsa, anapemphera mwakhama kwa Atate wake wakumwamba kaamba ka chitsogozo, ndipo nthaŵi zonse anachita zinthu zokondweretsa Atateyo. (Mateyu 21:5; Yohane 8:29) Akulu ayenera kuchita zofananazo pamene akuyesa kubweza munthu amene watenga njira yoipa. Monga mbusa wamng’ono wodekha, mkulu adzakhala wolimbikitsa ndi womangirira m’kulankhula, osati wowopseza. Mkati mwakukambitsirana, iye adzayesa kupanga mkhalidwe mu umene Mkristu wofunikira chithandizoyo adzadziwona kukhala wopeza bwino kwambiri monga momwe kungathekere kuti alankhule zakukhosi kwake. Chifukwa chake, pemphero lochokera pansi pamtima lakutsegula lidzakhala lothandiza kwambiri. Wolandira uphungu woperekedwa m’chifatso adzatsegula mtima wake koposerapo kuulandira ngati azindikira kuti, mofanana ndi Yesu, wopereka uphunguyo akufuna kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Mwachiwonekere pemphero lomaliza lidzakhomereza pa munthuyo kufunika kwa kugwiritsira ntchito uphungu wopatsidwa kwa iye mwanjira yachikondi, ndi yokoma mtima imeneyo.

Pambuyo pa pemphero, perekani chiyamikiro chowona mtima. Kungaphatikizepo mikhalidwe yabwino kwambiri ya munthuyo, monga ngati chifundo, kudalirika kapena changu. Mungatchule mbiri yake yautumiki wokhulupirika kwa Yehova, mwinamwake mkati mwa zaka zambiri. Mwanjirayi, timasonyeza kuti timadera nkhaŵa ndipo tiri ndi nkhaŵa yonga ya Kristu pa munthuyo. Yesu anayamba uthenga wake kumpingo wa Tiyatira ndi chiyamikiro, akumati: “Ndidziŵa ntchito zako, ndi chikondi, ndi chikhulupiriro, ndi utumiki, ndi chipiriro chako, ndi kuti ntchito zako zotsiriza zichuluka koposa zoyambazo.” (Chivumbulutso 2:19) Mawu amenewo anapereka chitsimikiziro ku ziŵalo za mpingowo chakuti Yesu anali kuzindikira ntchito yabwino imene iwo anali kuchita. Ngakhale kuti mpingowo unali ndi zolakwa zake​—chisonkhezero cha “Yezebeli” chinali kulekereredwa​—unali kuchita bwino m’mbali zina, ndipo Yesu anafuna kuti abale ndi alongo amenewo adziŵe kuti ntchito yawo yachangu inali itawonedwa. (Chivumbulutso 2:20) Mofananamo, akulu ayenera kupereka chiyamikiro pamene chiri choyenerera.

Osachitira otenga njira yoipayo mwamphamvu kwambiri kuposa zimene mikhalidwe ifunikiritsa. Akulu ayenera kutetezera gulu lankhosa la Mulungu ndi kusunga gulu lake liri loyera. Koma kuphophonya kwauzimu kwina kumene kumafunikira uphungu wamphamvu kungaikidwe m’chisamaliro cha mkulu mmodzi kapena aŵiri popanda bwalo loweruza. M’zochitika zambiri, kuli kufooka kwaumunthu ndipo osati kuipa kwadala kumene kumachititsa Mkristu kutenga njira yoipa. Akulu ayenera kuchitira gulu lankhosa mwachifundo nakumbukira mfundo yakuti: “Chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.” (Yakobo 2:13; Machitidwe 20:28-30) Pamenepa, mmalo mwakukulitsa mbuto ya kalulu ndidzawoneni, akulu ayenera kusamalira okhulupirira anzawo osweka mtima modekha, mofanana ndi Mulungu wathu wachifundo ndi wokoma mtima, Yehova.​—Aefeso 4:32.

Sonyezani kumvetsetsa mikhalidwe imene ingakhale itatsogolera kunjira yolakwayo. Akulu afunikira kumvetsera mosamalitsa pamene wokhulupirira mnzawo alankhula zakukhosi kwake. Popeza kuti ‘Mulungu samapeputsa mtima wosweka ndi wolapa,’ iwonso sayenera kutero. (Salmo 51:17) Mwinamwake kupanda chichirikizo cha maganizo kwa mnzawo wa muukwati ndiko nakatande wavutolo. Kuchita tondovi kwadzawoneni ndi kwanthaŵi yaitali kungafooketse nyonga ya maganizo ya munthuyo imene mwachibadwa ingakhale yamphamvu kapena ingakhale itakupangitsa kukhala kovuta kwambiri kupanga zosankha zanzeru. Akulu achikondi adzalingalira mikhalidwe imeneyi, chifukwa chakuti ngakhale kuti Paulo analimbikitsa abale ake kuti ‘dandaulirani amphwayi,’ iye anachichizanso kuti: “limbikitsani amantha, chirikizani ofoka, mukhale oleza mtima pa onse.” (1 Atesalonika 5:14) Ngakhale kuti akulu sayenera kufoketsa mphamvu ya miyezo yolungama ya Mulungu, iwo ayenera kupenda mikhalidwe yozungulira chochitikacho, monga momwe Mulungu amachitira.​—Salmo 103:10-14; 130:3.

Peŵani kululuza ulemu wa Mkristu mnzanu. Sitimafuna konse kulanda mbale aliyense kapena mlongo ulemu wake kapena kupereka lingaliro lakuti iye ngwosanunkha kanthu. Mmalo mwake, zitsimikiziro zakuti tiri ndi chidaliro m’mikhalidwe Yachikristu ya munthuyo ndi kukonda kwake Mulungu zidzatumikira monga chilimbikitso chakuwongolera cholakwacho. Mwachiwonekere, Akorinto analimbikitsidwa kukhala owolowa manja pamene Paulo anawauza kuti iye anadzitamandira kwa ena ponena za ‘kukonzekeratu kwa maganizo’ ndi ‘changu’ chawo pamfundoyi.​—2 Akorinto 9:1-3.

Sonyezani kuti vutolo lingagonjetsedwe mwakudalira Yehova. Inde, mwachangu yesayesani kuthandiza munthuyo kuwona kuti kudalira Mulungu ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa Mawu Ake kudzathandiza kudzetsa kukonzedwa kofunikako. Chifukwa chake, mawu athu ayenera kukhala ochokera m’Malemba ndi m’mabukhu ofotokoza Baibulo. Chonulirapo chathu chiri cha mfundo ziŵiri: (1) kuthandiza wofunikira chithandizoyo kuti awone ndi kumvetsetsa lingaliro la Yehova ndi (2) kusonyeza munthuyo mmene kumlingo wakutiwakuti wanyalanyazira kapena kulephera kulondola malangizo aumulungu amenewa.

Sanganizani uphungu Wamalemba ndi mafunso osonyeza chifundo koma olunjika. Zimenezi zingakhale zothandiza kwambiri kufika mtima. Kupyolera mwa mneneri wake Malaki, Yehova anagwiritsira ntchito funso kupangitsa anthu Ake kuzindikira mmene analiri atasochera. “Kodi munthu adzalanda za Mulungu?” Iye anafunsa, nawonjezera kuti: “Ndipo inu mundilanda ine.” (Malaki 3:8) Kulephera kwa Israyeli kupereka mbali yakhumi ya zinthu zawo monga momwe Chilamulo cha Mose chinanenera kunali kofanana ndi kulanda Yehova. Kuwongolera mkhalidwe umenewu, Aisrayeli anafunikira kukwaniritsa mathayo awo kulinga kukulambira koyera ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu akawadalitsa molemerera. Kupyolera mwa mafunso odzutsa maganizo ndi achifundo, akulu angagogomezerenso kuti kuchita chinthu chabwino lerolino kumaphatikizapo kudalira Atate wathu wakumwamba ndi kumvera iye. (Malaki 3:10) Kufikitsa lingaliro limenelo mumtima kudzathandizira kwambiri m’kuthandiza mbale wathu ‘kulambulira mapazi ake njira yowongoka.’​—Ahebri 12:13.

Gogomezerani mapindu akuvomereza uphungu. Uphungu wogwira mtima umaphatikizapo ponse paŵiri kuchenjeza za zotulukapo za kulondola njira yolakwa ndiponso zikumbutso za mapindu opezedwa m’kuwongolera mikhalidweyo. Pambuyo pa chenjezo la panthaŵi yake, Yesu anapereka chitsimikiziro kwa ochita mphwayi mwauzimu mumpingo wa ku Laodikaya kuti ngati analapa panjira yawo yoyamba nafikira kukhala ophunzira achangu, akasangalala ndi mwaŵi wapadera, kuphatikizapo chiyembekezo chakulamulira limodzi naye kumwamba.​—Chivumbulutso 3:14-21.

Sonyezani chikondwerero kuti muwone ngati uphunguwo ukulabadiridwa. Monga momwe dokotala wabwino amapendera panthaŵi ndi nthaŵi kuwona ngati fupa limene anaika mmalo likali chikhalirebe pamalo ake, choteronso akulu ayenera kuyesayesa kutsimikizira kuti kaya uphungu Wamalemba ukugwiritsiridwa ntchito. Iwo angadzifunse kuti: Kodi chithandizo chowonjezereka chikufunika? Kodi uphunguwo uyenera kubwerezedwanso, mwinamwake mwanjira ina? Yesu anafunikira kupereka uphungu mobwerezabwereza kwa ophunzira ake pakufunika kwa kudzichepetsa. Mkati mwa nthaŵi yaitali, iye anafunafuna moleza mtima kubweza maganizo awo kupyolera mwauphungu, mafanizo, ndi zinthu zowoneka. (Mateyu 20:20-28; Marko 9:33-37; Luka 22:24-27; Yohane 13:5-17) Mofananamo, akulu angathandize kutsimikizira kukonzedwanso kotheratu kwa mbaleyo kapena mlongo mwakulinganiza makambitsirano otsatira ochokera m’Malemba olinganizidwira kulimbikitsa kupita patsogolo kwa munthuyo kuthanzi lauzimu lokwanira.

Perekani chiyamikiro pakuwongokera kulikonse kopangidwa. Ngati munthu amene anatenga njira yoipa akuyesayesa mowona mtima kugwiritsira ntchito uphungu Wamalemba, myamikireni mwaubwenzi. Kutero kudzalimbikitsa uphungu woyambawo ndipo mwachiwonekere kukalimbikitsa kupita patsogolo kowonjezereka. M’kalata yoyamba ya Paulo kwa Akorinto, anali wokakamizika kuwapatsa uphungu wamphamvu pankhani zingapo. Mwamsanga Tito atauza mtumwiyo za kulabadira kwabwino kwambiri uphungu wa m’kalata yakeyo, Paulo analemba kuwayamikira. “Tsopano ndikondwera,” iye anatero, “sikuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ndi kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu.”​—2 Akorinto 7:9.

Magwero Achisangalalo

Inde, Paulo anasangalala pamene anamva kuti uphungu wake udathandiza Akorinto. Mofananamo, akulu amakono amakhala ndi chisangalalo chachikulu pamene wolambira mnzawo achira kunjira yolakwa chifukwa chakulabadira mwachiyanjo chithandizo chawo chachikondi. Iwo angakondweredi kuthandiza Mkristu wosweka mtima kuchotsa mumtima mwake akaufiti auchimo aminga kotero kuti zipatso zaumulungu zambirimbiri zikhoze kufunga m’menemo.

Ngati akulu apeza chipambano m’kubweza munthu amene watenga njira yoipa, iye angabwezedwe kuchokera kunjira imene ikakhala yowononga kotheratu mwauzimu. (Yerekezerani ndi Yakobo 5:19, 20.) Wolandira chithandizoyo ayenera kusonyeza kuyamikira Yehova Mulungu, kaamba ka chithandizo chotero. Mawu osonyeza chiyamikiro chowona kaamba ka chithandizo chachikondi, chifundo, ndi kukoma mtima kwa akulu akakhalanso oyenerera. Ndipo pamene kuchira kwauzimu kwachitika konse, ophatikizidwa onse angasangalale kuti kubwezedwako kwachititsidwa mumzimu wachifatso.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena