Pitirizani ‘Kuchita Zabwino’
1 Munachita bwino kwambiri kukhala mtumiki wa Yehova Mulungu. Komano, m’nthaŵi zoŵaŵitsa zino ntchito yagona pa kupitiriza ‘kuchita zabwino.’ (Agal. 6:9) Ngakhale kuti m’pofunika kulimba, mungakwanitse. Kodi mungakwanitse motani?
2 Khalani ndi Mtima wa Yesu: Mofanana ndi Yesu, mukhoza kupirira ziyeso ngati muika maganizo anu pa zimene Ufumu udzachita. (Aheb. 12:2, 3) Dziŵani kuti Yehova amakukondani ndipo amafuna kuti mupambane. (2 Pet. 3:9) M’dalireni kwambiri ndipo m’khulupirireni kuti adzakuthandizani. (1 Akor. 10:13) Limbikirani kupemphera, kum’pempha Yehova kuti akuthandizeni kupirira. (Aroma 12:12) Sangalalani pokhulupirira kuti mudzakhala ovomerezeka kwa Mulungu chifukwa cha kupirira kwanu. (Aroma 5:3-5) Kupitiriza kukulitsa ‘mtima wa Kristu Yesu’ kudzakupatsani chimwemwe ndiponso kudzakondweretsa mtima wa Yehova.—Aroma 15:5; Miy. 27:11.
3 Pitirizani Kuchita Ntchito Zabwino: Gwiritsani ntchito zinthu zimene Yehova wapatsa anthu ake kuti ziwathandize kupitiriza kuchita zabwino. Pitirizanibe chizoloŵezi chabwino choŵerenga Mawu a Mulungu ndiponso kuphunzira mabuku ofotokoza Baibulo, a gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Konzekerani zenizeni misonkhano, pezekanipo ndiponso tengani mbali m’misonkhano yonse ya mpingo. Chezani bwino ndi abale ndi alongo anu auzimu, misonkhano yachikristu isanayambe ndiponso ikatha. Ikani zolinga zimene mungakwanitse mu utumiki wanu kuti muchite zaphindu mu utumiki wakumunda ndiponso kuti muwongolere maluso anu a mmene mungauzire ena uthenga wabwino.
4 Umu ndi mmene mungapitirizire kuchita zabwino ndi kukhalanso wosangalala kwambiri. Mwa kuchita zimenezi, mbale wina ku Italy anati: “Ndimabwerera kunyumba kukada, pambuyo poti ndakhala muutumiki wa Yehova tsiku lonse, sindingakane, ndimatopadi. Koma ndimasangalala ndipo ndikuthokoza Yehova pondipatsa chimwemwe chimene wina sangandilande.” Chotero pitirizani kuchita zabwino, inunso mudzasangalala kwambiri.