Mukhoza Kugonjetsa Zopinga Zimenezi!
NDEGE yaikulu inganyamule anthu mazana ambiri ndi katundu wochuluka. Kodi ndege yolemera motero ingathe bwanji kuuluka? Mwa kungogwiritsira ntchito mphamvu youlutsa yotchedwa lift.
Pamene ndege ikuthamanga pansi, mphepo imawomba pamwamba ndi pansi pa mapiko ake opindika. Zimenezi zimatulutsa mphamvu yonyamula m’mwamba yotchedwa lift. Pamene mphamvu ya lift yokwanira yapangika, ndegeyo imanyamuka pansi niiuluka. Zoona, ndege yolemera mopambanitsa singathe kupanga mphamvu ya lift yokhoza kuiulutsa.
Nafenso tingakhale olemera kwambiri. Zaka mazana ambiri zapitazo, Mfumu Davide ananena kuti ‘mphulupulu zake zinali monga katundu wolemera’ kwa iye. (Salmo 38:4) Nayenso Yesu Kristu anachenjeza za kulemetsedwa ndi zosamalira za moyo. (Luka 21:34) Malingaliro oipa ndi kupsinjika mtima zikhoza kutilemetsa kwakuti kungaoneke kukhala kovuta “kuuluka.” Kodi ndinu wolemetsedwa mwa njira imeneyo? Kapena kodi mwakumana ndi chopinga china pa kupita patsogolo kwanu kwauzimu? Ngati ndi mmene zilili, kodi chingathandize nchiyani?
Kodi Ndinu Wonyong’onyeka?
Kunyong’onyeka—dandaulo lofala lerolino—kungakhale chopinga cha m’maganizo, ngakhale kwa anthu ena a Yehova. Makamaka achichepere ali ndi chizoloŵezi cha kuona zochita zina kukhala zogwetsa ulesi. Kodi nthaŵi zina mumaiona motero misonkhano Yachikristu? Ngati mumatero, kodi mungachitenji kuti muzisangalala nayo misonkhano?
Chinsinsi chake ndicho kutengamo mbali. Paulo analembera mnyamatayo Timoteo kuti: “Udzizoloŵeretse kuchita chipembedzo; pakuti chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.” (1 Timoteo 4:7, 8) Buku lophunzitsa za kulimbitsa thupi lingakhale logwetsa ulesi ndi losapindula kwenikweni ngati sitichita maseŵero olimbitsa thupi osonyezedwamo. Misonkhano Yachikristu yakonzedwa kuti ilimbitse maganizo athu ndipo idzatero ngati timakonzekera ndi kutengamo mbali. Kutengamo mbali kumeneku kudzachititsa misonkhano kukhala yofupa ndi yosangalatsa kwambiri.
Ponena za zimenezi, mtsikana wina Wachikristu wotchedwa Mara anati: “Ngati sindinakonzekere misonkhano, siimandisangalatsa. Komabe, ngati ndakonzekera pasadakhale, zinthu zimaloŵa kwambiri m’maganizo anga ndi mumtima mwanga. Misonkhano imakhala yopindulitsa kwambiri, ndipo ndimayembekeza kukayankhapo.”
Kuphunzira kumvetsera kungathandizenso. Kumvetsera nyimbo yokoma nkosavuta ndipo kumasangalatsa mosavuta. Koma si nthaŵi zonse pamene chikhutiro chimapezeka mosavuta. Timapeza chikhutiro m’programu ya misonkhano kokha ngati titchera khutu ku zimene zikunenedwa. Mkristu wina wotchedwa Rachel anati: “Ngati mlankhuli saali wotentha, ndiyenera kutchera khutu kwambiri. Chizoloŵezi changa nchakuti, ‘Ngati nkhani siili yochititsa chidwi kwambiri, ndiyeneranso kutchera khutu kwambiri.’ . . . Ndimasamalira kwambiri malemba, pofuna kupindula nawo kwambiri.” Tifunikira kudziletsa, monga Rachel, kuti timvetsere. Buku la Miyambo limati: “Mwananga, mvera nzeru yanga; tchera makutu ku luntha langa.”—Miyambo 5:1.
Chidziŵitso china choperekedwa pamisonkhano chingakhale chobwereza mwa njira ina. Zimenezi nzofunika! Atumiki onse a Mulungu afunikira zikumbutso. Thupi lopanda ungwiro, limodzi ndi zikhoterero zake zoipa ndi kuiŵalaiŵala, lifunikira chithandizo chilichonse chimene chilipo. Mtumwi Petro ‘sanaleka kukumbutsa okhulupirira anzake za zinthu zina, ngakhale anazidziŵa ndipo anali okhazikika m’choonadi.’ (2 Petro 1:12) Yesu nayenso anafotokoza kuti “mlembi aliyense, wophunzitsidwa . . . ali wofanana ndi munthu mwini banja, amene atulutsa m’chuma chake zinthu zakale ndi zatsopano.” (Mateyu 13:52) Chotero, pamene kuli kwakuti misonkhano yathu imapereka malingaliro a Malemba odziŵika, kapena ‘chuma chakale,’ nthaŵi zonse pamakhala ‘chuma chatsopano’ chotikondweretsa.
Kukhala wotsimikiza mtima kugwiritsira ntchito bwino misonkhano kungakulimbikitseni kwambiri mwauzimu. “Achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu [opemphapempha mzimu],” Yesu anatero. (Mateyu 5:3, NW, mawu amtsinde) Mkhalidwe wotero kulinga ku chakudya chauzimu choyenera choperekedwa pamisonkhano udzathetsa kunyong’onyeka.—Mateyu 24:45-47.
Kodi Mwalefulidwa ndi Chitsanzo Choipa?
Kodi munakhumudwapo ndi khalidwe la wina mumpingo mwanu? Mwinamwake mwadabwa kuti, ‘Kodi mbale angachite bwanji zimenezi nakhalabe ndi kaimidwe kabwino?’ Malingaliro otero angakhale chopinga cha m’maganizo, akumatiphimba kumaso kuti tisaone phindu la unansi wabwino umene tingakhale nawo ndi anthu a Mulungu.—Salmo 133:1.
Mwinamwake ena mumpingo wa ku Kolose anali ndi vuto longa limeneli. Paulo anawalangiza kuti: “[Pitirizanibe, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake.” (Akolose 3:13) Paulo anazindikira kuti Akristu ena a ku Kolose angakhale anachita zoipa napatsa ena chifukwa chomveka chodandaulira. Chotero sitiyenera kudabwa kwambiri ngati mmodzi wa abale athu kapena mlongo nthaŵi zina amaphonya pa mkhalidwe Wachikristu. Yesu anapereka uphungu wabwino wothetsera mavuto aakulu. (Mateyu 5:23, 24; 18:15-17) Koma nthaŵi zambiri, tingangopirira zophophonya za okhulupirira anzathu ndi kuwakhululukira. (1 Petro 4:8) Kwenikweni, njira imeneyo ingatithandize kwambiri ifeyo ndi ena. Kodi nchifukwa ninji zili choncho?
“Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa,” imatero Miyambo 19:11. Nkwabwino chotani nanga kukhululukira kuposa kulola mkwiyo ndi kuipidwa kukula! Salvador, mkulu wodziŵika chifukwa cha mzimu wake wachikondi, anati: “Pamene mbale wandichitira choipa kapena kunena mawu oipa, ndimadzifunsa kuti: ‘Kodi ndingamthandize motani mbale wanga? Kodi ndingapeŵe motani kutaya unansi wamtengo wapatali ndi iye?’ Nthaŵi zonse ndimakumbukira kuti nkwapafupi kunena chinthu cholakwa. Ngati wina walankhula mosalingalira, njira yabwino ingakhale ya kufafaniza mawu amene wanena ndi kuyambanso. Koma zimenezo nzosatheka, chotero ndimatenga njira yotsatira yabwino koposa ndi kunyalanyaza mawuwo. Ndimangoti watero chifukwa cha kupanda ungwiro kwa thupi lake osati chifukwa chakuti ndi mmene mbale wanga alili.”
Mungaganize kuti kunena zimenezi nkwapafupi kuposa kuzichita. Koma zochuluka zimadalira pa njira imene timalamulirira kalingaliridwe kathu. “Zilizonse zokongola, . . . zilingirireni izi,” analangiza motero Paulo. (Afilipi 4:8) “Zokongola” kwenikweni zimatanthauza “zosonkhezera chikondi.” Yehova amafuna kuti tizilingalira zimene zili zabwino mwa anthu, kusumika maganizo pa zimene zimasonkhezera chikondi m’malo mwa kuipidwa. Iye yekha amatipatsa chitsanzo chopambana pankhaniyi. Wamasalmo anatikumbutsa za zimenezi, akumati: “Mukanasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chiriri ndani, Ambuye?”—Salmo 103:12; 130:3.
Zoona, nthaŵi zina khalidwe la mbale lingakhale logwiritsa mwala, koma unyinji waukulu wa alambiri anzathu ali zitsanzo zabwino kwambiri za makhalidwe Achikristu. Ngati tikumbukira zimenezi, tidzakhala okondwa monga Davide ‘kuyamika Yehova kwakukulu ndi kumlemekeza pakati pa anthu aunyinji.’—Salmo 109:30.
Kodi Kukhala Mboni Kumaoneka Kovuta Kwambiri?
Nzachisoni kuti, chifukwa cha chopinga china cha m’maganizo, ena sanayambebe kulemekeza Yehova. Amuna ambiri amene saali Mboni za Yehova amasamalira bwino mabanja awo ngakhale kuchirikiza akazi awo mu utumiki Wachikristu. Iwo ngaubwenzi ndipo angakonde mpingo, koma amapeŵa kukhala atumiki a Mulungu odzipatulira. Kodi chikuwaletsa nchiyani?
Vuto lina lingakhale lakuti amuna ameneŵa amaona zochita zotangwanitsa zateokrase za akazi awo naganiza kuti kukhala Mboni kumafuna zambiri. Mwinamwake amawopa kuti sangapite m’ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba. Malinga ndi kuona kwawo, mathayowo amachita ngati akuphimba madalitso. Chifukwa ninji ali ndi chopingacho m’maganizo? Ophunzira Baibulo ambiri amaphunzira choonadi ndi kuchigwiritsira ntchito pang’onopang’ono. Koma amuna osakhulupirira kaŵirikaŵiri amadziŵa bwino kwambiri mathayo onse Achikristu asanakhale ndi chikhumbo cha kuwalandira.
Manuel, amene anali mumkhalidwe umenewu, akufotokoza kuti: “Kwa zaka pafupifupi khumi, ndinali kupita ndi mkazi wanga kumisonkhano yaikulu ndi yampingo. Kunena zoona, ndinakonda kuyanjana ndi Mboni kuposa anthu akudziko, ndipo ndinali wokonzekera kuwathandiza pamene ndinali wokhoza. Ndinachita chidwi ndi chikondi chimene chinali pakati pawo. Koma lingaliro la kupita kunyumba ndi nyumba linali chopinga chachikulu kwa ine, ndipo ndinali kuchita mantha kuti anzanga akuntchito adzandiseka.
“Mkazi wanga anali woleza mtima nane ndipo sanayesepo kundikakamiza kuphunzira Baibulo. Iye ndi ana omwe ‘analalikira’ makamaka mwa chitsanzo chawo chabwino. José, mkulu mumpingo, anandikonda kwambiri. Ndikhulupirira chilimbikitso chake nchimene chinandiyambitsa kuphunzira mwamphamvu. Nditabatizidwa, ndinazindikira kuti zopingazo zinali m’maganizo mwanga chabe. Nditangosankha kutumikira Yehova, ndinalandira thandizo lake la kugonjetsa mantha anga.”
Kodi akazi ndi akulu Achikristu angathandize motani amuna onga Manuel kugonjetsa chopinga chawo cha m’maganizo? Phunziro la Baibulo lingakulitse chiyamikiro ndi chikhumbo cha kuchita chifuniro cha Mulungu. Inde, chidziŵitso chokwana cha Malemba ndicho maziko osonyezera chikhulupiriro ndi okhalira ndi chidaliro cha chiyembekezo cha mtsogolo.—Aroma 15:13.
Kodi nchiyani chimene chingalimbikitse amuna otero kulandira phunziro la Baibulo? Kaŵirikaŵiri, zimene zingathandize ndi unansi ndi mbale wina wachifundo mumpingo. Mwinamwake mkulu kapena mbale wina wachidziŵitso angadziŵane ndi mwamunayo. Unansi wabwinowo utangokhazikitsidwa, zokha zimene angafunikire ndi kuti wina adzipereke kuphunzira naye. (1 Akorinto 9:19-23) Apo nkuti mkazi wanzeru Wachikristu akugaŵira mwamuna wake wosakhulupirira chakudya chauzimu pang’ono ndi pang’ono, pozindikira kuti iye sangafune kukakamizidwa.—Miyambo 19:14.
Monga momwe Manuel anaphunzirira ndi zimene zinamchitikira, munthu atangopeza nyonga yauzimu, zopinga zonga mapiri zimakhala ngati matutu a mfuko. Yehova amapatsa mphamvu aja amene afuna kumtumikira. (Yesaya 40:29-31) Mwa mphamvu ya Mulungu ndi chichirikizo cha Mboni zokhwima, zopinga zingachotsedwe. Motero ntchito ya kunyumba ndi nyumba simakhalanso yovuta ndi mabwenzi akuntchito samakhalanso owopsa, pamene kuli kwakuti utumiki wa mtima wonse umakhala wokondeka kwambiri.—Yesaya 51:12; Aroma 10:10.
Kusungabe Mphamvu
Kuli kotheka kugonjetsa zopinga monga zitatu zimene takambitsirana. Pamene ndege ikunyamuka, pamafunikira mphamvu yaikulu ya injini yake limodzinso ndi chisamaliro chosasunthika cha oiyendetsa. Pamene ikunyamuka, mainjini amadya mafuta kwambiri kuposa nthaŵi ina iliyonse ya ulendowo. Momwemonso, kumasuka ku malingaliro oipa ndi kupsinjika mtima kumafuna kuyesayesa kwamphamvu ndi chisamaliro chachikulu. Kuyamba ndiko kungakhale mbali yovuta koposa, pamene kuli kwakuti kupita patsogolo kumakhala kwapafupi mphamvu itangopezeka.—Yerekezerani ndi 2 Petro 1:10.
Mphamvu yopita patsogolo imasungidwa mwa kulabadira msanga chilimbikitso cha Malemba. (Salmo 119:60) Tikutsimikizira kuti mpingo udzathandiza. (Agalatiya 6:2) Komabe, chichirikizo cha Yehova Mulungu chiposa zonse. Monga momwe Davide ananenera, “wolemekezeka [Yehova, NW], tsiku ndi tsiku atisenzera katundu.” (Salmo 68:19) Pamene titula mtolo mwa pemphero, katundu wathu amapepuka.
Nthaŵi zina, ndege imasiya kumbuyo mvula ndi mitambo, kupyola mitamboyo, ndi kuuluka m’mwamba mmene dzuŵa likuŵala. Nafenso tingasiye kumbuyo malingaliro oipa. Ndi chithandizo cha Mulungu, tikhoza kupyola mitambo, titero kunena kwake, ndi kukhala mumkhalidwe woŵala ndi wachimwemwe wa banja la Yehova la padziko lonse la alambiri ake.
[Zithunzi patsamba 23]
Ndi chithandizo cha Yehova, tikhoza kugonjetsa zopinga za maganizo