Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nchifukwa ninji Chilamulo cha Mulungu chimanena kuti mwamuna Wachiisrayeli amene anagonana ndi namwali wosatomeredwa anayenera kumkwatira ndipo sakamsudzula?
Pa Eksodo 22:16, 17 ndi Deuteronomo 22:28, 29, timapezapo chilamulochi, chimene ena akunena kuti chikuwoneka kukhala chopanda chifundo kwa akazi. Kwenikwenidi, chinalimbikitsa muyezo wapamwamba wa makhalidwe abwino kaamba ka ponse paŵiri amuna ndi akazi.
Deuteronomo chaputala 22 chinapereka malamulo a pabanja ambiri osiyanasiyana. Mwachitsanzo, linachita ndi mkhalidwe wa mwamuna amene sanali kukondanso mkazi wake ndipo ananena kuti sanali namwali. Chinaperekanso malamulo a Mulungu onena za chigololo ndi kugwirira chigololo. Pamenepo timaŵerenga kuti:
“Munthu akapeza namwali wosadziŵa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, nakamgwira nagona naye, napezedwa iwo, pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wake wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wake; popeza anachepetsa; sakhoza kumchotsa masiku ake onse.”—Deuteronomo 22:28, 29.
Iyi inali nkhani ya kunyengerera kokakamiza ndipo/kapena dama. Ngati mwamuna wosadzilamulira anadzimva kukhala waufulu kugonana ndi namwali, mkaziyo ndiye amene akaluza. Pambali pa kuthekera kwa kukhala ndi mwana wachigololo, phindu lake monga mkwatibwi likazimiririka, popeza kuti Aisrayeli ambiri sakafuna kukwatira mkaziyo ngati adziŵa kuti sanalinso namwali. Komabe, kodi nchiyani chimene chikaletsa mwamuna kukhala waufulu kwa namwali? Chilamulo “cholungama ndi chabwino” cha Mulungu.—Aroma 7:12.
Lamulo la Mose linali ndi makonzedwe a kulola mwamuna kusudzula mkazi wake pa zifukwa zinazake. (Deuteronomo 22:13-19; 24:1; Mateyu 19:7, 8) Komatu zimene tikuŵerenga pa Eksodo 22:16, 17 ndi Deuteronomo 22:28, 29 zikusonyeza kuti chosankha cha kusudzula chinatha pambuyo pa dama la ukwati usanakhale. Chotero, zimenezi zikapangitsa mwamuna (kapena namwali wamkazi) kupeŵa chiyeso cha kuchita dama. Mwamuna sakadzimva kuti, ‘Mkaziyu ngwokongola ndi wosangalatsa, chotero ndidzasangalala naye ngakhale kuti siamene ndingakonde kukwatira.’ M’malo mwake, lamulo limeneli likakhoza kuletsa chisembwere mwakupangitsa aliyense yemwe akanakhala wolakwayo kupenda zotulukapo zosatha za dama—kuyenera kukhala ndi munthuyo kwa moyo wake wonse.
Chilamulocho chinachepetsanso vuto la ana achigololo. Mulungu analamula kuti: “Mwana wachigololo asaloŵe m’msonkhano wa Yehova.” (Deuteronomo 23:2) Chotero ngati mwamuna yemwe ananyengerera namwali anayenera kumukwatira, dama lawo silikatulukapo mwana wachigololo pakati pa Aisrayeli.
Polingalira chimenechi, Akristu akukhala m’mikhalidwe ya mayanjano imene iri yosiyana ndi ija ya Aisrayeli akale. Sitiri pansi pa malamulo a Chilamulo cha Mose, kuphatikizapo lamulo limeneli lofunikira ukwati wa anthu aŵiri amene anachita dama loterolo. Mosasamala kanthu za izo, sitingalingalire kuti kugonana ukwati usanakhale sikuli chinthu chofunika. Akristu ayenera kulingalira mosamalitsa zotulukapo za nthaŵi yaitali, mongadi mmene lamuloli linafulumizira Aisrayeli kuchita tero.
Kunyenga munthu wosakwatira kumaipitsa kuyenera kwa munthuyo kuloŵa ukwati Wachikristu monga namwali woyera (mwamuna kapena mkazi). Dama la ukwati usanakhale limayambukiranso kuyenera kwa munthu aliyense yemwe angakhale mnzake wa mu ukwati wa munthuyo, uku ndiko kuti, kuyenera kwa munthuyo kwa kukwatira Mkristu woyera. Chofunika koposa, dama liyenera kupeŵedwa chifukwa chakuti Mulungu amanena kuti nkulakwa; ndi chimo. Mtumwi molondola ananena kuti: “Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama.”—1 Atesalonika 4:3-6; Ahebri 13:4.