Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/1 tsamba 29
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani Yofanana
  • Atumiki Othandiza Amagwira Ntchito Yofunika Kwambiri
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Kodi Mukuyesetsa Kuti Mukhale Mtumiki Wothandiza?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Kodi Muli Woyeneretsedwa Kutumikira?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kusunga Mgwirizano—Pakati pa Akulu ndi Atumiki Otumikira
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/1 tsamba 29

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Kodi pali msinkhu wochepera wolekezera kaamba ka mwamuna Wachikristu kuyamikiridwa monga mtumiki wotumikira mu mpingo?

Ayi, Baibulo silimaika msinkhu wochepera wolekezera uliwonse.

Mu Israyeli wakale, Mulungu ananena mwachindunji misinkhu m’nkhani zina. Amuna olembetsedwa kaamba ka utumiki wa nkhondo anayenera kukhala a zaka 20 zakubadwa; anyamata ochepera sanali kutumizidwa ku nkhondo, monga mmene zimawonekera m’malo ena lerolino. Msinkhu unalinso chigamulo kaamba ka Alevi. Akohati otumikira pa chihema anayenera kukhala ochokera pa msinkhu wa zaka 30 kufika ku 50 zakubadwa. Chifukwa ninji? Polekezera pamenepa panatchulidwa m’chigwirizano ndi “ntchito ya utumikiwo, ndiyo ntchito ya akatundu m’chihema chokomanako.” (Numeri 4:3, 47) Chikuwoneka kuti Alevi akanayamba kuchita ntchito zopepuka pa msinkhu wa zaka 25, koma iwo anayenera kukhala pa msinkhu wa 30 asanayambe kugawanamo mu ntchito zolemera ndi mwaŵi wa mathayo owonjezereka a kupasula, kunyamula, ndi kumanganso chihemacho. (Numeri 8:24-26) Ntchito yolemetsa yoteroyo sikafunikira pambuyo pake pa kachisi, chotero Alevi kenaka anayamba kutumikira pa msinkhu wa 20.​—1 Mbiri 23:24.

Koma pamene Yehova analeka kugwiritsira ntchito Israyeli wakuthupi ndi kuyamba kugwiritsira ntchito Israyeli wauzimu, kodi iye anaika msinkhu wochepera wolekezera kaamba ka atumiki otumikira (adikoni) mu mpingo Wachikristu?

Wina angalingalire tero, mozikidwa pa cholembedwa cha mazana a kumapeto. Mu Tchalitchi cha Roma Katolika, dikoni ali “mtumiki woikidwa, pansi pa thayo la wansembe, m’madongosolo oikidwa mwaumulungu a ulamuliro wa atsogoleri a chipembedzo m’Tchalitchi.” Antiquities of the Christian Church ya Bingham inawona kuti: “Mabishopu ndi apresbyter [akulu] . . . sangaikidwe mwa wamba asanafike zaka makumi atatu; koma adikoni analoledwa kuikidwa pa msinkhu wa zaka makumi aŵiri mphambu zisanu, ndipo osati asanafike pamenepo. Uwu ndi mlingo wokhazikitsidwa ponse paŵiri ndi boma ndi lamulo la zolembedwa za chipembedzo . . . Ife sitimakumana kaŵirikaŵiri ndi nthaŵi pamene winawake anaikidwa asanafike msinkhu wa makumi aŵiri mphambu zisanu, mu mbiri yonse ya Tchalitchi.”

Ndi ziti, ngakhale ndi tero, zimene ziri ziyeneretso zopezeka m’Baibulo? Zomwe zaperekedwa zokha ziri zija zotchulidwa pa 1 Timoteo 3:8-10, 12, 13 (NW): “Momwemonso atumiki otumikira ayenera kukhala olingalira, osanena paŵiri, osakonda vinyo wambiri, osati a umbombo wa phindu losawona mtima, okhala ndi chinsinsi chopatulika cha chikhulupiriro limodzi ndi chikumbumtima choyera. Ndiponso, aloleni amenewa ayesedwe ponena za kuyenera choyamba, pamenepo aloleni atumikire monga atumiki, popeza ali opanda chinenezo. Atumiki otumikira akhale amuna okwatira a mkazi mmodzi, wotsogoza mu mkhalidwe wabwino ana ndi mabanja a iwo okha. Pakuti amuna amene amatumikira mu mkhalidwe wabwino akudzipezera mbiri yabwino ndi ufulu waukulu wa kulankhula chikhulupiriro mogwirizana ndi Kristu Yesu.”

Tingawone pano kuti palibe msinkhu waung’ono wolekezera kaamba ka kuikidwa monga mtumiki wotumikira womwe wasonyezedwa. Chotero pamene akulu akumana kukambitsirana ziyeneretso za amuna mu mpingo, iwo angasunge m’maganizo kuti palibe maziko a m’Baibulo ofunira kuti mwamuna Wachikristu akhale wa zaka 20, 25, kapena 30 zakubadwa asanayamikiridwe ndi kutumikira. Baibulo limalozera kwa awo omwe amakhala ndi thayo limeneli kukhala “amuna otumikira,” chotero sitiyenera konse kuwayembekezera iwo kukhala a m’zaka zawo za kumayambiriro kapena za pakati pa zaka 13 ndi 19. Likumasonyeza ichi, Baibulo likunena kuti atumiki otumikira oterowo angakhale okwatira ndi kukhala ndi ana a iwo eni.

M’kuwonjezerapo, amuna oyamikiridwa monga atumiki otumikira ayenera kukhala “[atayesedwa] ponena za kuyenera,” kupereka umboni wa kukhala ndi lingaliro la thayo. Kumeneko sindiko kunena kuti iwo ayenera kutumikira pa maziko a kuyesedwa. M’malomwake, iwo ayenera kukhala atasonyeza uchikulire Wachikristu mkati mwa nyengo yolingalirika ya nthaŵi (kukhala atabatizidwa chifupifupi kwa chaka chimodzi), kukhala amuna omwe ali ofunitsitsa ndi okhoza kusamalira nkhani zogawiridwa kwa iwo. Ngati mwamuna wachichepere “wolingalira” asonyeza mikhalidwe imeneyi, ndipo ali wodzichepetsa ndipo akuzifikira ziyeneretso zina, akulu angamuyamikire iye kaamba ka kuikidwa ngakhale ngati iye sanakwanitse zaka 20 zakubadwa. Amuna ena angakhale okulirapo pamene asonyeza mowonekera kuti iwo akuzifikiritsa ziyeneretso kaamba ka ‘kutumikira mu mkhalidwe wabwino, akudzipezera mbiri yabwino ndi ufulu wa kulankhula.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena