Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 3/15 tsamba 4-7
  • Akazi Achikristu—Kusunga Umphumphu Mmalo Antchito

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Akazi Achikristu—Kusunga Umphumphu Mmalo Antchito
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Olemba Ntchito “Ovuta Kusangalatsa”
  • Kukhala Oyera Mmakhalidwe
  • Njira Zochinjirizira
  • Kuletsa Kuvutitsidwa
  • Kuvuta Akazi—Mmene Mungadzitetezerere
    Galamukani!—1996
  • Akazi M’malo Antchito—Ziyeso ndi Zitokoso
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Ndingachitenji Ndikamavutitsidwa ndi Amuna Kapena Akazi?
    Galamukani!—2000
  • Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 3/15 tsamba 4-7

Akazi Achikristu​—Kusunga Umphumphu Mmalo Antchito

NTHAWl ZINA kukwinjika pa [ntchito] kumakhala kokakala kotero kuti ungathe kukudula ndi mpeni.” Anatero mkazi wogwira ntchito mmodzi.aChitsenderezo ku kutulutsa, mpikisano wodzilasa iwe mwini, kulamulira kwa oyang’anira a ntchito, kubwerezabwereza zinthu—izi ziri zochepa za zinthu zimene zimapanga ntchito zambiri kukhala zovuta. Ntchito zochepera zimapereka kuthuzitsa mtima koteroko ndi chisangalalo cholonjezedwa ndi obukitsa malingaliro pa nyuzipepala. Koma ngati inu muli mkazi wogwira ntchito, muyenera kukalamira kupanga chipambano cha ntchito yanu.

Ndi ichi, komabe, sitikutanthauza phindu la ndalama. Malo a ntchito liri bwalo lanu la chiwonetsero mu limene Umphumphu Wanu Wachikristu umaikidwa pa chiyeso! Njira mu imene mugwirira ntchito yanu, kukana mzimu wampikisano wa upandu, ndi kupewa maukonde a mikhalidwe kumavumbulutsa ndi ku mlingo wotani ku umene inu mumadzipereka ku maprinsipulo aumulungu. Kuti apeze chiyanjo cha Yehova Mulungu, mkazi wogwira ntchito ayenera kukhala wokhoza kunena monga momwe ananenera wa masalmo: “Pakuti ndayenda m’ungwiro wanga.”​—Masalmo 26:1.

Baibulo limakuthandizani inu kuchita chimenecho. Mwachitsanzo, pamene mukakamizidwa kutenga kachitidwe kazinthu ka galu-amadya-galu-mnzake kapena pamene muyesedwa kulola ntchito kuphimba mathayo a banja, phunziro la Baibulo, misonkhano ya Chikristu, ndi utumiki, mungachite bwino kukumbukira mawu a Mfumu Solomo: “Ndipo ndinapenyera mabvuto onse ndi ntchito zonse zompindulira bwino, kuti chifukwa cha zimenezi anansi ache achitira munthu nsanje. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Kuyang’ana ntchito yolembedwa mwa njira imeneyi kumaletsa kapena kuziziritsa chikhumbo choyaka moto. Kumakuthandizani inu kukhala ndi kayang’anidwe kabwino ka ntchito, kumaiwona iyo kukhala yachiwiri ku zinthu zauzimu.​—Mateyu 6:33.

Koma kodi ichi chimatanthauza kukhala wosiyana kulinga ku ntchito yolembedwa? Kutalitali, chifukwa Baibulo limaletsa ulesi. (Miyambo 19:15) Ilo limalankhula ponena za ‘kuwona zabwino chifukwa cha ntchito yako.’ (Mlaliki 2:24) Kuwonjezerapo, kupereka zosowa za banja la iye yekha liri thayo lopatsidwa ndi Mulungu. (1 Timoteo 5:8) Chotero ngati kukwaniritsa thayo limenelo kumatanthauza kugwira ntchito yolembedwa imene siyiri yabwino, lingalirani pa mawu a Baibulo opezeka pa Akolose 3:23: “Chiri chonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.” Kumadziona inu mwini monga mukugwirira ntchito “Yehova” chiri chifulumizo champhamvu cha kukhala ophula kanthu, champhamvu koposa kuwonjezeredwa kwa ndalama kapena kunyengereredwa kwa kukwezedwa pa ntchito.

Olemba Ntchito “Ovuta Kusangalatsa”

Mkazi wina wotchedwa Sally anati: “Ndimamva ngati kuti [mlangizi wanga ali] kuyang’ana pa mapewa panga nthawi zonse. Iye alibe nkomwe liwu labwino loti anene kwa aliyense.” Kugwira ntchito pansi pa woyang’anira amene ali “wovuta kusangalatsa” kapena wopsa mti ma msanga kungakhale kopsetsa mtima, makamaka pamene wina ali watsopano pa malo a ntchito.​—1 Petro 2:18.

Kusiya, ngakhale kuli tero, kungakhale mwachuma kopanda phindu. Chingakhale cholondola kwambiri chotero kutsatira langizo la Baibulo lakuti ogwira ntchito​—amuna ndi akazi—​“akhale ogonjera.” (1 Petro 2:18) Mmalo mokulitsa mkangano, ndi kunyodola kapena kupanda ulemu, yesani “kusangalatsa [olemba ntchito] bwino, osakana mawu awo.” (Tito 2:9) Kudziletsa koteroko kungakuthandizeni inu kusataya ntchito yanu. Anatero Solomo: “Ngati mzimu wa [woyang’anira wina wake wokhala ndi thayo] ukukwiyira, usasiye malo ako, chifukwa chifatso icho chokha [chichepetsa, NW] machimo aakulu.”​—Mlaliki 10:4.

Wogawira ntchito wokakala angachititsidwe manyazi pamene kusapirira kwakekukumanizana ndi chifatso, kulamulira kwake kosalingalira ndi chisomo. (Miyambo 15:1; Akolose 4:6) Ndipo pamene mutsimikizira kuthekera kwanu ndi kudzidalira, khalidwe lanu kulinga kwa inu pang’ono pang’ono lingawongokere. Ngati ayi, mungakhale ndi chosankha chochepa, “kusonyeza kupirira,” mukudziwa kuti Mulungu-ali wokondweretsedwa ndi khalidwe lanu la Chikristu.​—Yakobo 5: 7, 8.

Kukhala Oyera Mmakhalidwe

Umphumphu umaphatikizamo makhalidwe a Chikristu. Nkhani ina mu Ladies’ Home Journal inachenjeza: “Ofesi​—kumene aliyense amayembekezeredwa kuvala bwino, kukhala ndi khalidwe labwino, kuwononga nthawi pamodzi ndi kulondola zonulirapo zofanana​—iri ndi mkhalidwe umene mosavuta ungakhale woloza ku khalidwe la chisembwere.” Kuchita mu ofesi kuli kofala. Chotero chiri chanzeru kukhala wochenjera. Sungani mayanjano ndi amuna pa ntchito pa maziko a ntchito; Pewani makambitsirano amene angadzutse chilakolako. “Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, . . . kuti mudzipatule kudama.”​—1 Atesalonika 4: 3, 4.

Panthawi zina, ngakhale kuli tero, akazi ali minkhole ya vuto la ukalamba: kuipsidwa kwa kugonedwa. Baibulo limatiuza ife kuti mwamuna wotchedwa Boazi analamulira anyamata owalemba ntchito “kusakhudza” Rute, mkazi amene anali kugwira ntchito mmunda wake. Wophunzira Baibulo John P. Lange amalankhula ponena za “kuseketsa kokakala kumene ogwira ntchito oterowo mwina mwake chinali chizolowezi chovutitsira akazi.” (Rute 2:9) Ndipo ngakhale kuti olemba ntchito amakono akuyesa kutetezera olembedwa ntchito awo a akazi, ena amayerekezera kuti 40 mpaka 85 peresenti ya akazi ogwira ntchito (mu United States) akhala ataperekedwa ku mkhalidwe wina wake wakuvutitsidwa kwa kugonedwa.

Mkazi wachichepere wotchedwa Valerie, mwachitsanzo, anagwira ntchito monga mlembi. Kwa nthawi ndi nthawi, mkulu wake wa pa ntchito​—wokhala ndi zaka zowirikiza katatu kuposa zake—angapange ndemanga zolingalira ponena za kavalidwe kake. Kamodzi anayesa kumnyenga iye mkuwona zithunzithunzi za anthu amaliseche. Potsirizira, anamuitana iye mu ofesi yake ndi kumuuza kuti, “Kuti usunge ntchito yako, uyenera kuchita mchitidwe wina wake wa chiyanjo chogonana kwa ine.” Komabe, iye anakana kuchita tero.

Mkhalidwe wochititsa manyazi umenewu umatenga njira zambiri. Ikutero magazini ya Chibritish New Statesman: “Iko kumayambiraku kuyang’anira cha m’mbali, kutsinana, kukhudzana kwa kuthupi kosayenerera ndi kunyazitsidwa kwa mawu.” Kawirikawiri chitsenderezo cha kulowa mu mkhalidwe woipa wa kugonana kuli konyenga mofanana ndi kutchulidwa maina osangalatsa (Honey, Sweetheart) kapena mwapoyera monga chifunsiro chapoyera. Akazi ena amapirira kuipsidwako kaamba ka mantha akutaya ntchito zawo. Ndipo mafufuzidwe asonyeza kuti akazi ochepera amawoneka kukhala osangalatsidwa ndi chidwicho!

Koma pamene chisamaliro kuchokera kwa chiwalo chosiyana chingakhale chosangalatsa, chiyanjo chopambanitsa kawirikawiri chimakhala njira yotseguka ya kusewero la kucheta. Icho motero chiri cholakwika ku umphumphu wanu ndipo chochititsa manyazi ku ulemu wanu wa Chikristu.​—1 Akorinto 6:18.

Njira Zochinjirizira

“Pamene nzeru ilowa mu mtima mwako . . ., kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza.” (Miyambo 2:10, 11) Chotero kodi ndimotani mmene mungagwiritsire ntchito nzeru ndi kulingalira kudzichinjiriza inu mwini? Mkazi wogwira ntchito wotchedwa Diana akuti: “Ndimachilola icho kudziwika pa ntchitopo kuti ine ndiri m’modzi wa Mboni za Yehova.” (Yerekezani ndi Mateyu 5:16. ) Pamene amuna adziwa kuti uli ndi makhalidwe abwino apamwamba kwambiri, kaŵirikaŵiri mochepera amakhala wosayedzamiraku kukufikira.

Mkazi wolingalira wotchedwa Betty amatenga chinjirizo lina lake. Iye akuti: “Ndimakhala wochenjera ponena za kuyanjana ndi anzanga ogwira nawo ntchito chifukwa makhalidwe awo siali ofanana ndi anga.” (1 Akorinto 15:33) Ichi sichikutanthauza kuti muyenera kudzipatula kapena kukhala waukali kwa ogwira nawo ntchito. Koma pamene iwo akakamira pa kukambitsirana nkhani zomwe ziri zonyansa kwa Mkristu, musachedwe kudzichotsapo inu eni. (Aefeso 5:3, 4) Kumvetsera kwanu ku nkhani yoipa imeneyo kungapereke kwa amuna apantchito chikhutiritso chakuti mungakhale wovomereza ku kukufikirani kwawo.

Kusunga mawonekedwe apantchito kungabwevutse chisamaliro chosafunidwa. Kachiwirinso, Baibulo limalangiza akazi “kudzibvekaokha ndi chovala choyenera, ndi manyazi ndichidziletso.” (1 Timoteo 2:9; siyanitsani ndi Miyambo 7:10. ) Limatero bukhu la Sexual Harassment on the Job: “Zovala zodzutsa chilakolako—zimenezo ziri, malaya okhala ndi nkhosi lotsika kwambiri; zovala za nthawi yotentha; kabudula, masiketi aafupi; ndi unyinji wa zodzoladzola zowala kwambiri​—siziri zakumalo antchito. . . . Mwawi wanu wa kupanga chithunzi cha ntchito umawonjezedwa ngati musankha kuvala mosawonekera kwambiri.”

Pomalizira, mkazi wolingalira amapewa mkhalidwe yogonjera. Kuitanidwa kumwa chakumwa choledzeretsa kapena kutsalira kuntchito pambuyo pa nthaŵi ya ntchito popanda chifukwa chenicheni kungakhale msampha. (Yerekezani ndi 2 Samueli 13:1-14. ) “Wochenjera awona zoipa nabisala,” umatero mwambo wanzeru.​—Miyambo 22:3.

Kuletsa Kuvutitsidwa

Komabe, sichiri chenicheni kulingalira kuti mungakonzenso kulingalira kwa amuna onse pa ntchito kapena kusintha njira ya mikhalidwe yakale. (Yerekezani ndi Yeremiya 13:23. ) Ndipo sichirinso chabwino kumaliza kuti amuna onse amene amawoneka aubwenzi kwambiri ali ndi “maso odzala ndi chigololo.” (2 Petro 2:14) Chotero nthaŵi zina chiri choyenerera kufutukula phindu la chikaikiro.

Koma pamene chizolowezi chokulira chowonekera chaphatikizidwamo, imani nji. Pamene Solomo anapanga maimbidwe osafunidwa opitirira kwa mtsikana wachichepere, iye sanagonjere. Iye anavomereza kuchisangalatso chake ndi chisonyezero cha chikondi chosagwedezeka kaamba ka mbusa wodekha wa chinyamata. Popeza iye anakana kugonjera ku zifunsiro za Solomo, iye akanati: “Ndine khomo​.”—Nyimbo ya Solomo 8:10:

Sonyezani kulimba nji kofananako. Kaŵirikaŵiri mafikiridwe angatsekerezedwe mumphukira mwa kunena kuti: “Osandikhudza, chonde,” “Ndiitaneni ndi dzina langa,” kapena “Sindiyamikira chisangalatso cha mtundu umenewo.” Mkazi Wachikristu wina koposa kamodzi anangonena mwachidule, “Chiduleni icho!” Mwanjira iriyonse, chipangeni icho kukhala chowonekera kuti ayi wanu amatanthauza ayi! (Yerekezani ndi Mateyu 5:37. ) Yankho lofooka kapena losamveka kwenikweni lingalimbikitse wovutitsayo kuyesetsa molimbikira.

Ngati muli wokwatiwa, chingakhale bwino kugawana malingaliro anu ndi mwamuna wanu. Iye mwina mwake angakhale ndi malingaliro ena oyenerera ponena za mmene mungasamalire mkhalidwewu. Ngati chiwoneka kukhala chabwino koposa kusintha ntchito, kumbukirani lonjezo la Mulungu: “Sindidzakusiya konse angakhale kukutaya sindidzakutaya ndithu.”​—Ahebri 13:5.

Ntchito Yanu ndi Umphumphu Wanu

Chotero pamene ntchito yolembedwa iri kaŵirikaŵiri yoyenerera, iyo munjira zina ingapereke chiwopsyezo ku umphumphu wanu Wachikristu. Chotero mawu a Yesu pa Mateyu 10:16 ali oyenerera: “Khalani ochenjera monga njoka, ndi owona mtima monga nkhunda.”

Kusunga umphumphu Wachikristu m’malo antchito sikuli kokhweka, koma kungachitidwe. Zikwi za akazi pakati pa Mboni za Yehova akuchita choncho mwakutsatira uphungu wa Baibulo. Iwo amadzisunga iwo eni olimba mwauzimu mwanjira ya phunziro la Baibulo, pemphero, misonkhano Yachikristu, ntchito yolalikira Ufumu, ndi zochita zina za umulungu. Monga chotulukapo chake, iwo amasangalala ndi china chake chomwe ndalama sizingapereke. Chiri chidziwitso chakuti iwo ali ndi chiyanjo cha Yehova, Amene Mawu ake amalonjeza: “Iye amene akuyenda mu umphumphu adzayenda mu chisungiko.”​—Miyambo10:9.

[Mawu a M’munsi]

a Pano akusonyeza mkazi wogwira ntchito yolembedwa. Komabe, akazi apanyumba, amayi, ndi akazi ena nawonso amagwira ntchito.

[Chithunzi patsamba 7]

Kaamba ka Kusunga Umphumphu M’malo Antchito​

Lolani kuti chidziwike kuti muli ndi Makhalidwe apamwamba abwino

Khalani osamal ponena za kuyanjana ndi ogwira nawo ntchito

Dzivekeni inu eni ndi zovala zoyenerera

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena