Kodi Tikukhaladi ‘M’masiku Otsiriza’?
ZOCHITIKA za mitundu iwiri zimatithandiza kudziwa nthawi imene Baibulo limati masiku otsiriza. Malemba ananeneratu za zinthu zomwe zidzachitike pa “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3) Baibulo limafotokozanso za kusintha kwa makhalidwe ndi zochita za anthu a ‘m’masiku otsiriza.’—2 Timoteo 3:1.
Zochitika padzikoli komanso makhalidwe a anthu, zikutsimikizira kuti tikukhala m’masiku otsiriza ndiponso kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu ubweretsa madalitso osatha kwa amene amakonda Mulungu. Tiyeni tiyambe n’kuona zochitika zitatu zimene Yesu ananena kuti zidzapereka umboni wa masiku otsiriza.
“Zowawa Zoyamba”
Yesu anati: “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu ndi ufumu wina; ndipo kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo akutiakuti.” Ndipo anawonjezera kuti: “Koma ndizo zonsezi zowawa zoyamba.” (Mateyu 24:7, 8) Tiyeni tione “zonsezi” pachokhapachokha.
Anthu ambiri anaphedwa mu nkhondo ndi m’mikangano ya mafuko m’zaka 100 zapitazi. Lipoti lina la akatswiri a zofufuzafufuza a bungwe la Worldwatch Institute linati: “Chiwerengero cha anthu omwe anafa pankhondo za m’zaka za m’ma [1900] chinawirikiza katatu poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu omwe anafa mu nkhondo zonse zomwe zinachitika kuyambira m’zaka 100 zoyambirira kufika mpaka 1899.” Jonathan Glover m’buku lake lakuti Humanity—A Moral History of the Twentieth Century anati: “Anthu akuganiza kuti kuchokera mu 1900 mpaka 1989 anthu pafupifupi 86 miliyoni anafa pankhondo. . . . Anthu amene anafa pankhondo m’zaka zimenezi anali ochuluka zedi moti n’zovuta kumvetsa. Kuti titchule chiwerengero cha anthu amene anafa, pa avereji sizigwirizana kwenikweni ndi zimene zinachitikadi, popeza kuti, mwa anthu omwe anafawo, pafupifupi awiri pa anthu atatu alionse (omwe ndi 58 miliyoni) anafa pankhondo ziwiri za padziko lonse. Koma, ngati anthu amenewa atagawidwa mofanana m’nyengo imeneyi, ndiye kuti anthu pafupifupi 2,500 anali kufa pankhondo tsiku lililonse. Kutanthauza kuti anthu oposa 100 anali kufa paola lililonse mosalekeza kwa zaka 90.” Tangoganizirani chisoni ndi kupwetekedwa mtima kumene mamiliyoni a achibale ndiponso mabwenzi a anthu amene anafawo anakhala nako!
Ngakhale kuti dziko limakhala ndi chakudya chochuluka, zochitika za masiku otsiriza zikuphatikizaponso kusowa kwa chakudya. Ochita kafukufuku amanena kuti pa zaka 30 zapitazi, chakudya chimene chapezeka chaposa kuchuluka kwa anthu amene awonjezeka. Komabe, m’madera ambiri padziko lonse mukukhala njala chifukwa chakuti anthu sakhala ndi malo olimapo okwanira kapena sakhala ndi ndalama zokwanira zogulira chakudya. M’mayiko osauka, anthu pafupifupi 1.2 biliyoni sakhala ndi ndalama zokwanira zogulira chakudya patsiku. Ndipo mwa anthu amenewa, anthu pafupifupi 780 miliyoni amakhala ndi njala yosatha. Bungwe loona za umoyo pa dziko lonse, la World Health Organization linati, ana oposa mamiliyoni asanu amafa chaka chilichonse chifukwa cha kuperewera kwa zakudya m’thupi.
Kodi tingati chiyani ponena za zivomezi zomwe zinanenedweratu? Malinga n’kunena kwa bungwe lofufuza za nthaka ndi miyala la ku United States lotchedwa Geological Survey, tingati kungoyambira m’chaka cha 1990, chaka chilichonse pakhala pakuchitika zivomezi 17 zamphamvu kwambiri moti n’kuwononga nyumba. Ndipo chaka chilichonse pakhala pakuchitika chivomezi champhamvu kwambiri moti n’kufafaniziratu chilichonse. Nkhani ina inati: “Zivomezi zapha anthu masauzande ambiri m’zaka 100 zapitazi.” Chimodzi cha zinthu zimene zachititsa zimenezi n’chakuti kuyambira m’chaka cha 1914, madera ambiri omwe mukumka muchuluka anthu ali m’malo amene mumachitika zivomezi.
Zochitika Zina Zikuluzikulu
Yesu anati: “Kudzakhala . . . miliri m’malo akutiakuti.” (Luka 21:11) Sayansi ya zamankhwala yapita patsogolo kwambiri masiku ano kuposa kale lonse. Komabe, matenda akale ndi atsopano omwe akupitirizabe kuwononga anthu. Lipoti lina lochokera ku bungwe la National Intelligence Council la ku United States linati: “Matenda osiyanasiyana 20 odziwika bwino, kuphatikizapo TB, malungo, ndi kolera, ayambiranso ndipo afalikira m’madera ambiri kuyambira mu 1973, ndipo kawirikawiri amabwera mwamphamvu ndiponso mosamva mankhwala. Ndipotu, kuyambira m’chaka chomwecho cha 1973, atulukira tizilombo tatsopano toyambitsa matenda tosachepera 30, kuphatikizapo ta HIV, Ebola, toyambitsa matenda a chiwindi, ndi tizilombo tina totupitsa ubongo, timene tilibe mankhwala.” Mogwirizana ndi lipoti la bungwe la Red Cross la pa June 28, 2000, chiwerengero cha anthu amene anafa ndi matenda opatsirana chinawirikiza nthawi 160 kuposa cha anthu amene anafa ndi masoka achilengedwe m’chaka cha 1999.
“Kuchuluka kwa kusayeruzika” ndicho chochitika china chodziwika bwino cha masiku otsiriza. (Mateyu 24:12) Masiku ano, m’madera ambiri padziko lonse lapansi, anthu sasiya nyumba zawo zosakhoma, ndipo amachita mantha kuyenda mumsewu usiku. Nanga bwanji ponena za kuipitsa mpweya, madzi ndi malo kumene kukuchitika makamaka chifukwa cha kuswa malamulo? Zimenezinso zikukwaniritsa zimene Baibulo linaneneratu. Buku la Chivumbulutso limanena za nthawi yoikika ya Mulungu imene ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.
Makhalidwe a Anthu M’masiku Otsiriza
Tsegulani Baibulo lanu, ndipo muwerenge 2 Timoteo 3:1-5. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.” Ndipo kenako anapitiriza ndi kundandalika makhalidwe 20 amene adzasonyezedwa ndi anthu osaopa Mulungu. Kodi mwaonapo ena mwa makhalidwe amenewa kwa anthu amene akukhala m’dera lanu? Taonani zimene zanenedwa posachedwapa ponena za anthu a masiku ano.
“Odzikonda okha.” (2 Timoteo 3:2) “[Anthu] akuumirira kuchita zofuna zawo kusiyana n’kale lonse. [Iwo] akusanduka milungu, ndipo akufuna kuti anthu ena aziwalambira.”—Inatero nyuzipepala ya ku England yotchedwa Financial Times.
“Okonda ndalama.” (2 Timoteo 3:2) “Mzimu wokonda chuma masiku ano waposa mzimu wokhutira ndi zomwe munthu ali nazo. Munthu umasangalala ndi moyo ngati m’dera lomwe ukukhalalo ukuoneka kuti ndiwe wolemera.”—Inatero nyuzipepala ya ku Indonesia yotchedwa Jakarta Post.
“Osamvera akuwabala.” (2 Timoteo 3:2) “Makolo amadabwa kuona mwana wawo wa zaka zinayi akuwalamulira ngati kuti ndi Louis 14, [Mfumu yotchuka ya ku France], kapena mwana wawo wa zaka eyiti akulankhula mofuula kuti, ‘Sindikukondani!’”—Inatero magazini ya ku United States yotchedwa American Educator.
“Osayera mtima.” (2 Timoteo 3:3) “Amuna ndi akazi ali ndi chikhumbo chachikulu chofuna kusiya akazi awo kapenanso amuna awo ndiponso ana awo, ndipo uku mwina ndi kusintha kwakukulu kwambiri kwa makhalidwe a anthu kumene kwachitika pa [zaka 40 zapitazi].”—Inatero magazini ya ku United States yotchedwa Wilson Quarterly.
“Opanda chikondi chachibadwidwe.” (2 Timoteo 3:3) “Kuchitirana nkhanza m’banja ndi moyo umene wafala pa moyo watsiku ndi tsiku wa anthu padziko lonse lapansi.”—Inatero magazini ya ku United States yotchedwa Journal of the American Medical Association.
“Osakhoza kudziletsa.” (2 Timoteo 3:3) “Mitu yambiri ya nkhani zimene zimalembedwa pa tsamba loyambirira la manyuzipepala m’mawa uliwonse zimasonyeza maganizo osadziletsa, kupanda khalidwe ndiponso kupanda chifundo kwa anthu anzawo ngakhalenso kwa iwo eni. . . . Ngati anthu apitirizebe kukhala a chiwawa monga mmene zililimu, dziko lathuli posachedwapa lidzakhala lopanda khalidwe m’pang’ono pomwe.”—Inatero nyuzipepala ya ku Thailand yotchedwa Bangkok Post.
“Aukali.” (2 Timoteo 3:3) “Kukwiya pa zilizonse ndi kukalipa kwambiri zimaoneka pakati pa madalaivala, m’mabanja, . . . ndiponso [mu] ziwawa zosadziwika bwino ndi zosafunikira zimene kawirikawiri zimathera mu umbanda. Anthu amakhala ngati ali okhaokha ndipo sangathandizidwe ndiponso akhoza kuchitidwa chipongwe nthawi ina iliyonse.”—Inatero nyuzipepala yotchedwa Business Day, ya ku South Africa.
“Okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:4) “Anthu ambiri akufuna kukhala ndi ufulu wakugonana mosemphana ndi khalidwe lachikristu.”—Inatero magazini ina ya pa Intaneti yotchedwa Boundless.
“Akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.” (2 Timoteo 3:5) “[Mkazi wina wa ku Netherlands yemwe kale anali hule] anati, magulu azipembedzo ndi amene amatsutsa kwambiri lamulo lovomereza [uhule]. Anapuma pang’ono, kenako akumwetulira anati pamene iye anali hule, abusa angapo [azipembedzo] ndiwo anali makasitomala ake a nthawi zonse. Anaseka, n’kunena kuti ‘Nthawi zonse, mahule amati makasitomala abwino kwambiri ndi anthu opembedza.’”—Inatero nyuzipepala ya ku United States yotchedwa National Catholic Reporter.
Kodi M’tsogolo Muli Zotani?
Masiku ano, dziko ladzala ndi mavuto, monga mmene Baibulo linanenera. Komabe, ulosi wonena za “chizindikiro cha kufika kwa [Kristu], ndiponso cha mathedwe a nthawi ya pansi pano” uli ndi chochitika china chabwino. Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:3, 14) Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa m’mayiko oposa 230. Anthu oposa sikisi miliyoni ochokera “mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe” akuchita nawo mwakhama ntchito imeneyi yofalitsa Ufumu. (Chivumbulutso 7:9) Kodi kugwira ntchito mwachangu kumeneku kwakwaniritsa chiyani? Kwakwaniritsa izi: Uthenga wonena kuti Ufumu n’chiyani, zimene udzachite, ndiponso mmene anthu angalandirire madalitso ake ukufika pafupifupi kwa aliyense padziko lapansi. Zoonadi, ‘chidziwitso choona chachuluka mu nthawi ya mapeto ino.’—Danieli 12:4.
Muyenera kudziwa zimenezi. Taonani zimene zidzachitike uthenga wabwino ukadzalalikidwa monga mmene Yehova akufunira. Yesu anati: “Pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Idzakhala nthawi ya Mulungu yothetsa kuipa konse padziko lapansi. Lemba la Miyambo 2:22 limati: “Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” Bwanji ponena za Satana ndi ziwanda zake? Adzaponyedwa m’phompho, ndipo sadzanyenganso anthu. (Chivumbulutso 20:1-3) Kenako ‘owongoka mtima . . . ndi angwiro adzatsala’ m’dziko. Ndipo adzasangalala ndi madalitso aakulu a Ufumu.—Miyambo 2:21; Chivumbulutso 21:3-5.
Kodi Mungachite Chiyani?
Sitikukayikira kuti mapeto a dongosolo la Satana, afika posachedwapa. Mapeto adzafika modzidzimutsa kwa anthu amene akunyalanyaza umboni woti tikukhala m’masiku otsiriza. (Mateyu 24:37-39; 1 Atesalonika 5:2) Choncho Yesu ananena kwa omvetsera ake kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.”—Luka 21:34-36.
Anthu okha amene adzakhale ovomerezeka pamaso pa Mwana wa munthu, Yesu, adzakhala ndi mwayi wopulumuka mapeto a dongosolo la zinthu ili. Ndiyetu, m’pofunika kuti tigwiritse ntchito nthawi imene yatsalayi kufunafuna kuyanjidwa ndi Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. Popemphera kwa Mulungu, Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Choncho mungachite bwino kuphunzira zambiri za Yehova Mulungu ndi zofuna zake. Mboni za Yehova za m’dera lanu zidzasangalala kukuthandizani kuti mudziwe zimene Baibulo limaphunzitsa. Tikukupemphani kuti muonane nawo kapena mulembe kalata kwa ofalitsa magaziniyi.
[Bokosi/Zithunzi patsamba 7]
ZOCHITIKA ZA M’MASIKU OTSIRIZA
ZOCHITIKA ZIKULUZIKULU:
▪ Nkhondo.—Mateyu 24:6, 7.
▪ Njala.—Mateyu 24:7.
▪ Zivomezi.—Mateyu 24:7.
▪ Miliri.—Luka 21:11.
▪ Kuchuluka kwa kusayeruzika.—Mateyu 24:12.
▪ Kuwononga dziko.—Chivumbulutso 11:18.
ANTHU:
▪ Odzikonda okha.—2 Timoteo 3:2.
▪ Okonda ndalama.—2 Timoteo 3:2.
▪ Odzitamandira.—2 Timoteo 3:2
▪ Osamvera akuwabala.—2 Timoteo 3:2.
▪ Osayamika.—2 Timoteo 3:2.
▪ Osayera mtima.—2 Timoteo 3:3.
▪ Opanda chikondi chachibadwidwe.—2 Timoteo 3:3.
▪ Osakhoza kudziletsa.—2 Timoteo 3:3.
▪ Aukali.—2 Timoteo 3:3.
▪ Okonda zokondweretsa munthu.—2 Timoteo 3:4.
▪ Opembedza mwachiphamaso.—2 Timoteo 3:5.
OLAMBIRA OONA:
▪ Ali ndi chidziwitso chochuluka.—Danieli 12:4.
▪ Amalalikira uthenga wabwino padziko lonse.—Mateyu 24:14.
[Mawu a Chithunzi]
UNITED NATIONS/Photo by F. GRIFFING