Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/15 tsamba 7-9
  • Yunike ndi Loisi—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo Chabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yunike ndi Loisi—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo Chabwino
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maphunziro “Kuyambira Ukhanda”
  • Kuchoka kwa Timoteo
  • Maphunziro Ofunika
  • Zimene Azimayi Angaphunzire kwa Yunike
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • “Mwana Wanga Wokondedwa Ndi Wokhulupirika Mwa Ambuye”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Timoteyo Ankafuna Kuthandiza Anthu
    Phunzitsani Ana Anu
  • Achinyamata—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/15 tsamba 7-9

Yunike ndi Loisi​—Aphunzitsi Opereka Chitsanzo Chabwino

Monga atumiki a Yehova, timadziŵa kuti kupereka maphunziro auzimu othandiza kwa ana athu uli udindo wofunika kwambiri. Ngakhale m’mikhalidwe yabwino kwambiri, udindo umenewu ungakhale ndi zopinga ndi mavuto ambiri. Zimenezi zimakhala zovutanso kwambiri pamene kholo lachikristulo likuchita udindowo m’banja limene anthu ake amapita kuzipembedzo zosiyana. Zimenezi sizachilendo. Malemba amatiuza za kholo lina limene linali mumkhalidwe wofananawo m’zaka za zana loyamba C.E.

Banja la mkazi wina wotchedwa Yunike linali kukhala ku Lustra, mzinda umene unali m’chigawo cha Lukaoniya kummwera chapakati pa Asia Minor. Lustra unali mzinda waung’ono wosatchuka kwenikweni wa m’chigawocho. Unali m’chitaganya cha Aroma chotchedwa Julia Felix Gemina Lustra, chimene chinakhazikitsidwa ndi Kaisara Augusto pofuna kutsekereza achifwamba ochokera kumalo oyandikana nawo. Yunike anali Mkristu wachiyuda pamodzi ndi mwana wake Timoteo, ndi amayi ake Loisi amene anali kukhala m’banja losiyana chipembedzo ndi mwamuna wake wachigiriki.​—Machitidwe 16:1-3.

Mwinamwake kunali Ayuda ochepa ku Lustra, popeza kuti Baibulo silitchulapo zoti kumeneko kunali sunagoge, ngakhale kuti Ayuda ena anali kukhala ku Ikoniyo, mtunda wa makilomita pafupifupi 30. (Machitidwe 14:19) Choncho, kuyenera kuti sikunali kwapafupi kwa Yunike kutsatira chikhulupiriro chake. Akatswiri ena amaphunziro amalingalira kuti mwamuna wa Yunike analetsa kuti Timoteo asadulidwe, ndipo nchifukwa chake mwana wakeyo anali wosadulidwa.

Komabe, Yunike sanali yekha amene anali ndi zikhulupirirozo. Zimaonetsa kuti Timoteo anaphunzitsidwa “malembo opatulika” ndi onse aŵiri amayi ake ndi agogo ake aakazi otchedwa Loisi, amene anabala amake.a Mtumwi Paulo analangiza Timoteo kuti: “Ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziŵa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziŵa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.”​—2 Timoteo 3:14, 15.

Maphunziro “Kuyambira Ukhanda”

Pamene Paulo ananena kuti Timoteo anaphunzitsidwa “malembo opatulika” “kuyambira ukhanda,” mwachionekere zimenezi zimasonyeza kuti anayamba kuphunzitsidwa akali wamng’ono kwambiri. Zimenezi nzogwirizana ndi mawu achigiriki (breʹphos) amene amatanthauza mwana wobadwa kumene. (Yerekezerani ndi Luka 2:12, 16.) Choncho, Yunike anachita udindo wake wopatsidwa ndi Mulungu umenewo mosamalitsa, ndipo anayamba kuphunzitsa Timoteo akali wochepa zimene zinamthandiza kuti akhale mtumiki wodzipereka wa Mulungu pamene anakula.​—Deuteronomo 6:6-9; Miyambo 1:8.

Timoteo ‘anatsimikizika mtima’ ndi choonadi cha m’Malemba. Malinga nkunena kwa dikishonale ina yachigiriki, mawu amene Paulo anagwiritsira ntchito panopo amatanthauza “kukopeka kwambiri ndi; kukhutiritsidwa ndi” chinachake. Mosakayika konse, panafunikira nthaŵi yaitali ndi khama kuti akhomereze chikhulupiriro chimenecho mumtima mwa Timoteo, zimene zinamthandiza kuti azisinkhasinkha za Mawu a Mulungu ndi kuwakhulupirira. Choncho, mwachionekere, onse aŵiri Yunike ndi Loisi anachita khama pophunzitsa Timoteo za m’Malemba. Ndipo ndi phindu lotani nanga limene akazi aumulungu amenewo anapeza! Ponena za Timoteo, Paulo analemba kuti: “Pokumbukira chikhulupiriro chosanyenga chili mwa iwe, chimene chinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mayi wako Yunike, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.”​—2 Timoteo 1:5.

Yunike ndi Loisi anagwira ntchito yofunika chotani nanga pamoyo wa Timoteo! Ponena za zimenezi, wolemba David Read anati: “Ngati mtumwiyo anakhulupirira kuti chimene chinali chofunika kwambiri chinali kutembenuka kwa Timoteo iyemwini, iye sadakazengereza kumkumbutsa zimenezo. Koma chinthu choyamba chimene ananena chokhudza chikhulupiriro cha Timoteo nchakuti chikhulupirirocho chinali ‘chitakhala kale mwa Loisi . . . ndi Yunike.’” Mawu a Paulo onena za chikhulupiriro cha Loisi, Yunike, ndi Timoteo amasonyeza kuti kaŵirikaŵiri maphunziro oyambirira auzimu operekedwa pabanja ndi makolo ndiponso ngakhale agogo ngofunika kwambiri kuti mwana akhale ndi chiyembekezo chabwino cha zinthu zauzimu mtsogolo. Kodi zimenezo siziyenera kusonkhezera makolo kuti azilingalira mosamalitsa za zimene akuchita pokwaniritsa udindo umenewu kwa Mulungu ndi ana awo omwe?

Mwinamwake Paulo anali kulingaliranso za mkhalidwe wa banja la Loisi ndi Yunike. Mwina mtumwiyo anakacheza kunyumba kwawo paulendo wake woyamba kukhala ku Lustra, cha m’ma 47/48 C.E. Mwina akazi aŵiriwo anatembenukira ku Chikristu nthaŵi imeneyo. (Machitidwe 14:8-20) Mwinamwake chikondi ndi chimwemwe chimene chinali m’banjamo ndicho chimene chinasonkhezera Paulo kuti alembe mawu oyenerera onena za Loisi monga “mbuye” wa Timoteo. Malinga nkunena kwa katswiri wamaphunziro Ceslas Spicq, mawu achigiriki amene iye anagwiritsira ntchito (mamʹme, powasiyanitsa ndi mawu ozoloŵereka ndiponso aulemu akuti teʹthe) ndi “mawu achikondi a mwana” kwa agogo ake aakazi, amene panopo “akusonyeza kumdziŵa bwino ndiponso kumkonda.”

Kuchoka kwa Timoteo

Sizidziŵika bwino kuti kaya Yunike anali ndi mwamuna kapena ayi pamene Paulo anakacheza ku Lustra kachiŵiri (cha m’ma 50 C.E.). Akatswiri ambiri amaphunziro amalingalira kuti iye anali mkazi wamasiye. Mulimonse mmene zinalili, motsogozedwa ndi amayi ake ndi agogo ake, Timoteo anakula kukhala mnyamata wabwino, amene mwina panthaŵiyo anali ndi zaka zakubadwa za m’ma 20. Iye “anamchitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.” (Machitidwe 16:2) Mwachionekere, chilakolako cha kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu chinali chitakhomerezedwa mumtima mwa Timoteo, popeza kuti iye analola pamene Paulo anampempha kuti ayende naye ndi Sila paulendo wawo waumishonale.

Tangolingalirani mmene Yunike ndi Loisi anakhudzidwira pamene Timoteo anali pafupi kunyamuka! Iwo anadziŵa kuti paulendo wake woyamba wochezera mzinda wawo, mtumwi Paulo anaponyedwa miyala nasiyidwa pomyesa kuti wafa. (Machitidwe 14:19) Choncho, kuyenera kuti sikunali kwapafupi kuti iwo alole Timoteo wachinyamatayo kuti apite. Mosakayika konse, iwo anafuna kudziŵa kuti akakhala kumeneko kwa nthaŵi yaitali motani ndiponso kuti kaya adzabwerako bwino. Mosasamala kanthu zakuti mwina anali ndi nkhaŵa zimenezo, amayi ake ndi agogo ake mosakayika konse anamlimbikitsa kuti alole mwayi wapadera umenewu umene unamtheketsa kutumikira Yehova mokwanira.

Maphunziro Ofunika

Tingaphunzire zambiri ngati tisinkhasinkha mosamalitsa za nkhani ya Yunike ndi Loisi. Chikhulupiriro chawo chinawasonkhezera kuti alere bwino Timoteo mwauzimu. Chitsanzo chabwino kwambiri cha kudzipereka kwaumulungu kumene agogo amasonyeza kwa adzukulu awo ndi ena chingakhaledi chopindulitsa mumpingo wonse wachikristu. (Tito 2:3-5) Chitsanzo cha Yunike chimakumbutsanso amayi amene ali ndi amuna osakhulupirira za udindo wawo ndiponso mapindu amene angapeze pamene apereka maphunziro auzimu kwa ana awo. Nthaŵi zina pamafunikira kulimba mtima kwambiri kuti achite zimenezi, makamaka ngati atate sagwirizana ndi zikhulupiriro za chipembedzo cha mkazi wake. Pamafunikiranso luso, popeza kuti mkazi wachikristu amayenera kulemekeza umutu wa mwamuna wake.

Chikhulupiriro, khama, ndi kudzimana kwa Loisi ndi Yunike zinadziŵika kuti zinali zopindulitsa pamene anaona Timoteo akupita patsogolo mwauzimu mpaka kukhala mmishonale ndi woyang’anira wabwino kwambiri. (Afilipi 2:19-22) Mofananamo lerolino, kuphunzitsa ana athu zikhulupiriro zauzimu kumafuna nthaŵi, kuleza mtima, ndiponso kukhala wofunitsitsa kuchita zimenezo, koma zotsatirapo zake zabwino zidzasonyeza kuti khama lonselo linali lopindulitsa. Achinyamata ambiri opereka chitsanzo chabwino amene aphunzitsidwa ‘malembo opatulika kuyambira ukhanda wawo’ m’mabanja amene anthu ake amapita kuzipembedzo zosiyanasiyana amadzetsa chimwemwe chachikulu kwa kholo lawo loopa Mulungu. Ndipo mwambi uwu umanenadi molondola kuti: “Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye”!​—Miyambo 23:23-25.

Ponena za ana ake auzimu, mtumwi Yohane anati: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.” (3 Yohane 4) Zoonadi, malingaliro amene afotokozedwa m’mawu amenewo amapezekanso mwa anthu ambiri amene akhala ngati Yunike ndi Loisi, aphunzitsi aŵiri opereka chitsanzo chabwino.

[Mawu a M’munsi]

a Zonena kuti Loisi sanali agogo aakazi a Timoteo amene anabala atate ake zinasonyezedwa ndi matembenuzidwe a Syriac akuti “amayi awo a amako” pa 2 Timoteo 1:5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena