Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/15 tsamba 4-6
  • Kodi Chuma Chingakupatseni Chimwemwe?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chuma Chingakupatseni Chimwemwe?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukonda Ndalama Sikudzetsa Chimwemwe
  • Kukhutira ndi Zimene Tili Nazo
  • Mmene Tingapezere Chimwemwe
  • Kukhala Wokhutira Komanso Wopatsa
    Galamukani!—2018
  • Tiziona Ndalama Moyenera
    Galamukani!—2007
  • Mfumu Yachuma ndi Nzeru
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Chuma Chenicheni Chidzakhala M’dziko Latsopano la Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/15 tsamba 4-6

Kodi Chuma Chingakupatseni Chimwemwe?

Mfumu Solomo anadziŵa kufunika kwa ndalama. Iye analemba kuti: “Amaphikira zakudya kuti asekere, vinyo nakondweretsa moyo; ndipo ndalama zivomera zonse.” (Mlaliki 10:19) Kudya ndi mabwenzi kungakhale kosangalatsa kwambiri, koma kuti mupeze chakudya kapena vinyo, pamafunikira ndalama. Popeza kuti timagula zinthu ndi ndalama, izo “zivomera zonse.”

NGAKHALE kuti Solomo anali wolemera kwambiri, iye anadziŵa kuti chuma chili ndi malire ake. Anadziŵa kuti moyo wofunafuna chuma sindiwo njira yopezera chimwemwe. Iye analemba kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.”​—Mlaliki 5:10.

Tiyeni tinene kuti munthu wolemera kale wapezanso chuma china chambiri. Solomo anati: “Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso.” (Mlaliki 5:11) Pamene “katundu” wa munthu, kapena kuti chuma, chichuluka, pamafunikira anthu ambiri osamalira katunduyo. Anthu okonza zowonongeka, osamalira, atumiki, alonda, ndi enanso ambiri​—onsewo amafunikira kulipidwa chifukwa cha ntchito zawozo. Ndipotu zimenezi zimafuna ndalama zinanso zambiri.

Zimenezi zimakhudza kwambiri chimwemwe cha munthu. Wolemba mbiri wachigiriki Xenophon, amene anakhalapo m’zaka za zana lachinayi B.C.E., analemba nkhani ya munthu wosauka amene kenaka anakhala wolemera, ndipo iye anati:

“Aha, kodi ukuganiza . . . kuti pamene ndikhala ndi zambiri, mpamenenso ndimakhala ndi chimwemwe kwambiri? Sukudziŵa,” iye anapitiriza kuti, “sindipeza chimwemwe mpang’ono pomwe pamene ndidya, kumwa, ndipo sindipezanso tulo tokwanira tsopano kusiyana ndi nthaŵi imene ndinali wosauka. Phindu lokha limene ndimapeza pokhala ndi zinthu zambiri ndilo lakuti ndimakakamizika kusamalira zambiri, kupereka zambiri kwa ena, ndiponso ndimayang’anira zinthu zambiri kusiyana ndi zimene ndinkayang’anira kale. Tsopano anansi ambiri amayembekeza ine kuti ndiwapatse chakudya, ena ambiri amafuna zakumwa, ndipo ena ambiri amafuna zovala, pamene ena amafuna kupita kuchipatala; ndipo wina amabwera ndi kundiuza kuti nkhosa zagwidwa ndi mimbulu, kapena kuti ng’ombe zamagoli zagwera m’phompho ndipo zafa, kapenanso kuti ng’ombe zanga zagwidwa ndi matenda ena. Ndiye ndimaona . . . kuti ndili ndi mavuto ambiri tsopano chifukwa chokhala ndi katundu wambiri kusiyana ndi nthaŵi imene ndinali ndi katundu wochepa.”

Chifukwa china chimene anthu amafunira chuma chochuluka ndicho chakuti amapusitsidwa ndi zimene Yesu anazitcha kuti “mphamvu yonyenga ya chuma.” (Mateyu 13:22, NW) Iwo amapusitsidwa chifukwa chakuti m’chuma chimene amachifunitsitsa mwakhamacho, sapezamo chikhutiro kapena chimwemwe chimene anali kuyembekezera. Iwo amalingalira kuti zinthu zimene chuma chochepa chalephera kudzetsa, chuma chochuluka ndicho chidzazidzetsa. Choncho, amafunafunabe mosalekeza chuma china chambiri.

Kukonda Ndalama Sikudzetsa Chimwemwe

Nkhaŵa ya chuma chake ingalepheretse munthu wolemera kukhala ndi tulo tabwino. Solomo analemba kuti: “Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.”​—Mlaliki 5:12.

Pamene munthu akhala ndi nkhaŵa yaikulu yakuti mwina chuma chake chingamthere, amapeza mavuto ambiri osati kusoŵa tulo kokha ayi. Ponena za munthu waumbombo, Solomo analemba kuti: “Masiku ake onse amadya mumdima, nizimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.” (Mlaliki 5:17) M’malo mopeza chimwemwe m’chuma chake, iye amadya ‘mwachisoni,’ kungokhalanso ngati wawononga ndalama chifukwa chogula chakudyacho. Malingaliro oipa amenewo angafooketse thanzi la munthu. Kenaka, munthu waumbomboyo amakhalanso ndi nkhaŵa chifukwa cha thanzi lofookalo, popeza kuti limamlepheretsa kukundika chuma chambiri.

Mwinamwake zimenezi zakukumbutsani zimene mtumwi Paulo analemba kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, . . . adzipyoza ndi zoŵaŵa zambiri.” (1 Timoteo 6:9, 10) Pamene afunafuna ndalama, anthu amachita mwachinyengo, kunama, kuba, kuchita upsuta, ndipo ngakhale kupha anzawo. Chotsatirapo chake munthuyo amadzipyoza ndi zoŵaŵa za maganizo, zakuthupi, ndiponso zauzimu chifukwa cha kuyesa kupeza ndi kukundika chuma. Kodi zimenezi zikuoneka kuti ndizo njira yopezera chimwemwe? Kutalitali!

Kukhutira ndi Zimene Tili Nazo

Solomo ananena zambiri ponena za kaonedwe koyenera ka chuma. Iye analemba kuti: “Monga anatuluka m’mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m’dzanja lake. Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.”​—Mlaliki 5:15, 18.

Mawu ameneŵa akusonyeza kuti chimwemwe sichidalira pa kukundika chuma chifukwa chakuti mwina tingafe ndi kuchisiya chumacho. Kuli bwino kwambiri kukhala wokhutira ndi kusangalala ndi mapindu a kugwira ntchito kwathu mwakhama. Mtumwi Paulo anafotokoza za malingaliro ofananawo m’kalata yake youziridwa yolembera Timoteo, nati: “Sitinatenga kanthu poloŵa m’dziko lapansi, ndiponso sitikhoza kupita nako kanthu pochoka pano; koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”​—1 Timoteo 6:7, 8; yerekezerani ndi Luka 12:16-21.

Mmene Tingapezere Chimwemwe

Solomo anali ndi chuma chambiri ndiponso nzeru zambiri zaumulungu. Koma iye ananena kuti chimwemwe chimadza chifukwa chokhala ndi nzeru, osati ndalama. Iye anati: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala.”​—Miyambo 3:13-18.

Kodi nchifukwa ninji nzeru nzopambana kuposa chuma? Solomo analemba kuti: “Pakuti nzeru ichinjiriza monga ndalama zichinjiriza; koma kudziŵa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.” (Mlaliki 7:12) Pamene kuli kwakuti ndalama zingachinjirize, popeza kuti mwiniwake angagule chilichonse chimene afuna, nzeru zingachinjirize munthu mwa kumthandiza kupeŵa kuchita zinthu zimene zingaike pangozi moyo wake. Nzeru zenizeni zingapulumutse munthu kuti asafe akali wochepa, ndiponso, popeza kuti nzeruzo zimadza chifukwa cha kuopa Mulungu moyenerera, nzeru zotero zidzapangitsa munthuyo kuti apeze moyo wosatha.

Kodi nchifukwa ninji nzeru zaumulungu zimapatsa chimwemwe? Nchifukwa chakuti chimwemwe chenicheni chimachokera kwa Yehova Mulungu yekha basi. Umboni umasonyeza kuti chimwemwe chenicheni tingachipeze kokha mwa kumvera Wam’mwambamwamba. Chimwemwe chokhalitsa chimadalira pa kukhala ndi makhalidwe ovomerezeka ndi Mulungu. (Mateyu 5:3-10) Mwa kutsatira zimene timaphunzira paphunziro la Baibulo, tidzakulitsa “nzeru yochokera kumwamba.” (Yakobo 3:17) Idzatipatsa chimwemwe chimene sichingadze ndi chuma.

[Zithunzi pamasamba 4, 5]

Mfumu Solomo anadziŵa chimene chimapatsa munthu chimwemwe. Kodi inu mumachidziŵa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena