Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mbali Zonse za Baibulo N’zothandiza Masiku Ano?
“Malangizo a m’Baibulo si othandiza kwenikweni masiku ano. Amangothandiza pazinthu zosafunika.”
“Zimene Baibulo limanena zokhudza mibadwo ya anthu, kusagona ndi mwamuna kapena mkazi usanakwatirane naye ndiponso kuopa Mulungu zinali zothandiza kalelo, koma n’zosathandiza kwenikweni masiku ano.”
“Zimene Baibulo limanena zokhudza mibadwo ya anthu, unamwali ndiponso kuopa Mulungu zinali zofunika kalelo, koma masiku ano si zofunika kwenikweni.”
“Pamene Baibulo limasindikizidwa koyamba, linali litatha kale ntchito.”
MAWU amenewa anatengedwa pamalo ena a pa Intaneti pomwe anthu amanena maganizo awo pankhani yakuti “Kodi Baibulo ndi lothandiza masiku ano?” Kodi inuyo mukugwirizana ndi maganizo amenewa?
Mwina inuyo simukugwirizana ndi maganizo akuti Baibulo lonse linatha ntchito. Komabe, mwina mumakaikira ngati mbali zina za Baibulo ndi zothandizadi masiku ano. Ndipotu Mabaibulo ambiri amene amagwiritsidwa ntchito m’matchalitchi ambiri amagawidwa mbali ziwiri, Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano. Zimenezi zimachititsa anthu kuganiza kuti mbali yaikulu ya Baibulo ndi yakale ndipo inatha ntchito.
Mwachitsanzo, masiku ano palibe munthu amene amapereka nsembe za nyama zomwe zinafotokozedwa m’Chilamulo cha Mose. Choncho, ena amaona kuti n’kutaya nthawi kumawerenga za nsembe za nyama zomwe zinafotokozedwa m’buku la Levitiko. (Levitiko 1:1–7:38) Enanso amaona kuti nkhani yonena za mibadwo ya anthu yomwe ili m’machaputala oyambirira a m’buku la 1 Mbiri, ndi yopanda phindu. (1 Mbiri 1:1–9:44) Iwo amaganiza kuti ngati palibe aliyense amene anganene kuti anachokera ku mibadwo imeneyi, ndiye kuti machaputala amenewa alibe phindu.
Koma taganizirani chitsanzo ichi: Ngati mutathyola chipatso mumtengo, kodi mtengowo mungauone kuti ndi wosafunika? Ayi, chifukwa tsiku lina mudzapitanso pamtengo womwewo kukathyola chipatso china. Baibulo tingaliyerekezere ndi mtengo wa zipatso umenewu. Mwina inuyo mumakonda mbali zina za Baibulo monga Masalmo ndi ulaliki wapaphiri, zomwe zili ngati zipatsozo. Koma kodi zimenezi ziyenera kutichititsa kuganiza kuti mbali zina za Baibulo n’zosafunika? Kodi Baibulolo limati chiyani pankhani imeneyi?
Cha mu 65 C.E., mtumwi Paulo analemba kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo, kumukumbutsa kuti: “Kuyambira pamene unali wakhanda, wadziwa malemba opatulika amene angathe kukupatsa nzeru za mmene ungapezere chipulumutso kudzera m’chikhulupiriro chokhudza Khristu Yesu.” Kenako Paulo anati: “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo.” (2 Timoteyo 3:15, 16) Kodi pamene Paulo ankalemba kuti “Malemba onse anawauzira ndi Mulungu,” ankangonena za Chipangano Chatsopano chokha?
Onani kuti Paulo ananena kuti Timoteyo anadziwa “malemba opatulika” kuyambira ali “wakhanda.” Anthu ena amakhulupirira kuti Timoteyo anali ndi zaka 30 panthawi imene Paulo anamulembera kalatayi. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti panthawi imene Yesu ankafa n’kuti Timoteyo ali wakhanda. Ndipo panthawiyi n’kuti malemba a Chigiriki kapena kuti “Chipangano Chatsopano” asanalembedwe. Popeza kuti mayi a Timoteyo anali Myuda, malemba opatulika amene akanagwiritsa ntchito pophunzitsa mwana wawo ndi Malemba Achiheberi kapena kuti Chipangano Chakale. (Machitidwe 16:1) Choncho, n’zosakayikitsa kuti Paulo ponena kuti “Malemba onse” ankaphatikizapo Chipangano Chakale, chomwe chili ndi malamulo onena za kupereka nsembe komanso mibadwo ya anthu.
Panopa papita zaka zoposa 1,900 kuchokera panthawi imeneyo, ndipo mbali za Baibulo zimenezi zingatithandize m’njira zosiyanasiyana. Choyamba, dziwani kuti tili ndi Baibulo chifukwa chakuti Mulungu anasankha anthu ena kuti alembe ndiponso kusunga Baibulo mosamala. (Aroma 3:1, 2) M’nthawi ya Aisiraeli Chilamulo cha Mose chinali chofunika kwambiri. Chilamulochi chinkasungidwa mosamala kuti mibadwo ya mtsogolo idzagwiritse ntchito komanso eni akewo ankachitsatira kwambiri. Mfundo zosiyanasiyana za m’Chilamulo zomwe panopa zingaoneke ngati zopanda phindu, zinali zofunika kwambiri kwa Aisiraeli. Zinkathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino ndiponso kuti mtunduwu upitirizebe kukhalapo. Komanso nkhani za mibadwo ya anthu zinali zofunika kwambiri kuti anthu athe kuzindikira Mesiya, yemwe analoseredwa kuti adzabadwira m’banja la Mfumu Davide.—2 Samueli 7:12, 13; Luka 1:32; 3:23-31.
Ngakhale kuti Akhristu masiku ano satsatira Chilamulo cha Mose, iwo ayenera kusonyeza kuti amakhulupirira Mesiya wolonjezedwa, Yesu Khristu. Nkhani ya mibadwo ya anthu yolembedwa m’Baibulo imasonyeza kuti Yesu ndiye “mwana wa Davide” wolonjezedwa. Ndipo nkhani zokhudza nsembe zimatithandiza kuti tiziyamikira nsembe yofunikira kwambiri yomwe Yesu anapereka, komanso zimalimbitsa chikhulupiriro chathu.—Aheberi 9:11, 12.
Polembera Akhristu a ku Roma, mtumwi Paulo anati: “Zonse zimene zinalembedweratu zinalembedwa kuti zitilangize ife, kuti mwa chipiriro chathu ndi mwa chitonthozo cha m’Malemba tikhale ndi chiyembekezo.” (Aroma 15:4) Lemba limeneli limatikumbutsa kuti Baibulo linalembedwa kuti litithandize. Koma si kuti limathandiza ife tokha. Kwa zaka zoposa 3,500, mawu ake ouziridwa akhala akutsogolera, kulangiza ndiponso kuphunzitsa anthu a Mulungu, kungoyambira m’chipululu cha Sinai, m’dziko Lolonjezedwa, ku ukapolo ku Babulo, mu Ufumu wa Roma ndiponso kulikonse masiku ano. Palibe buku lililonse limene lingafanane ndi Baibulo. Mofanana ndi mizu ya mtengo, nthawi zina phindu la mbali zina za Baibulo zingakhale zovuta kuziona. Kuti muone phindu lake pangafunike khama ndithu, komabe khama limenelo lingakhale ndi zotsatirapo zabwino.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● Kodi Timoteyo anadziwa “malemba opatulika”kuyambira liti?—2 Timoteyo 3:15.
● Kodi ndi mbali ziti za Baibulo zimenenso ndi zouziridwa ndiponso zopindulitsa?—2 Timoteyo 3:16.
● Kodi zinthu “zonse zimene zinalembedweratu” zingatithandize bwanji?—Aroma 15:4.
[Chithunzi patsamba 29]
Nkhani ya m’Baibulo yonena za nsembe imatithandiza kuyamikira nsembe yofunika kwambiri imene Yesu anapereka