Pezani Mapindu a Chiphunzitso Chaumulungu
“Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula.”—YESAYA 48:17.
1. Kodi nchiyani chidzatichitikira ngati tigwiritsira ntchito chiphunzitso chaumulungu m’miyoyo yathu?
YEHOVA MULUNGU adziŵa zinthu bwino koposa. Palibe aliyense amene amposa m’kuganiza, mawu kapena m’zochita. Monga Mlengi wathu, amadziŵa zosoŵa zathu ndipo amazipereka mochuluka. Ndithudi iye amadziŵa mmene angatilangizire. Ndipo ngati tigwiritsira ntchito chiphunzitso chaumulungu, timadzipindulitsa ndi kupeza chimwemwe chenicheni.
2, 3. (a) Kodi ndimotani mmene anthu akale a Mulungu akanapindulira ngati akanamvera malamulo ake? (b) Kodi nchiyani chidzachitika ngati tigwiritsira ntchito chiphunzitso chaumulungu m’miyoyo yathu lerolino?
2 Chiphunzitso chaumulungu chimavumbula chikhumbo chachikulu cha Mulungu chakuti atumiki ake apeŵe tsoka ndi kusangalala ndi moyo mwa kutsatira malamulo ndi miyezo yake. Ngati anthu akale a Yehova akanamumvera, akanapeza madalitso ochuluka, pakuti anawauza kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.
3 Anthu akale a Mulungu akanapindula ngati akanamvera malamulo ndi malangizo ake. Mmalo mwa kugwera m’tsoka kwa Ababulo, iwo akanapeza mtendere ndi chuma chochuluka, chodzala ndi chanthaŵi zonse ngati mtsinje. Ndiponso, ntchito zawo zolungama zikanakhala zosaŵerengeka monga mafunde a nyanja. Mofananamo, ngati tigwiritsira ntchito chiphunzitso chaumulungu m’miyoyo yathu, tingapeze mapindu ake ochuluka. Kodi ena a mapindu ameneŵa ndiati?
Chimasintha Miyoyo
4. Kodi chiphunzitso chaumulungu chakhala chikuyambukira motani miyoyo ya anthu ambiri?
4 Chiphunzitso chaumulungu chakhala chikupindulitsa anthu ambiri mwa kusintha miyoyo yawo kukhala yabwino. Awo amene amagwiritsira ntchito malangizo a Yehova amasiya “ntchito zathupi,” zonga uchiwerewere, kupembedza mafano, kukhulupirira mizimu, ndewu, ndi nsanje. Mmalomwake, amasonyeza zipatso za mzimu za chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso. (Agalatiya 5:19-23) Iwo amalabadiranso uphungu wa pa Aefeso 4:17-24 (NW), pamene Paulo amafulumiza okhulupirira anzake kusayenda mmene ayendera amitundu, muuchitsiru wa malingaliro awo ndi mumdima wa maganizo awo, ndi opatutsidwa pa moyo wa kwa Mulungu. Pokhala osatsogozedwa ndi mitima yokakala, anthu onga Kristu ‘amavula umunthu wakale umene umagwirizana ndi makhalidwe awo akale ndipo akhalitsidwa atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo awo.’ Iwo ‘amavala umunthu watsopano wolengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.’
5. Kodi chiphunzitso chaumulungu chimayambukira motani mmene anthu amayendera?
5 Phindu la kugwiritsira ntchito chiphunzitso chaumulungu nlakuti chimatisonyeza mmene tingayendere ndi Mulungu. Ngati tiyenda ndi Yehova, monga momwe anachitira Nowa, timatsatira njira ya moyo yolinganizidwa ndi Mlangizi wathu Wamkulu. (Genesis 6:9; Yesaya 30:20, 21) Anthu a mitundu ‘amayenda muuchitsiru wa malingaliro awo,’ monga momwe mtumwi Paulo ananenera. Ndipo zolemba zina za anthu amaganizo otero ziyenera kukhala zopanda pake chotani nanga! Pamene anaona zolembedwa za ena pachipupa mu Pompeii, munthu wina analemba kuti: “Chipupa iwe, nzodabwitsa kuti sunagwe ndi kulemera kwa zolembedwa pa iwe zopanda pake zochuluka motero.” Koma mulibe zopanda pake mu “chiphunzitso cha [Yehova, NW]” ndi ntchito yolalikira Ufumu imene chimatheketsa. (Machitidwe 13:12) Mwa ntchito imeneyo, anthu okonda chowonadi amathandizidwa kuchitapo kanthu mwanzeru. Iwo amaphunzitsidwa mmene angalekere kuyenda m’njira yawo yauchimo, m’kusadziŵa zifuno za Mulungu. Iwo salinso mumdima wa maganizo, ndipo samasonkhezeredwa ndi mitima yokakala yofunafuna zonulirapo zopanda pake.
6. Kodi pali unansi wotani pakati pa kulabadira kwathu chiphunzitso cha Yehova ndi chimwemwe chathu?
6 Chiphunzitso chaumulungu chimatipindulitsanso pakuti chimatidziŵitsa za Yehova ndi zochita zake. Chidziŵitso chotero chimatiyandikitsa pafupi ndi Mulungu, chimawonjezera chikondi chathu pa iye, ndipo chimakulitsa chikhumbo chathu cha kumvera iye. Lemba la 1 Yohane 5:3 limati: “Pakuti ichi ndichikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” Timamveranso malamulo a Yesu chifukwa timadziŵa kuti chiphunzitso chake chimachokera kwa Mulungu. (Yohane 7:16-18) Kumvera kotero kumatitetezera ku chivulazo chauzimu ndipo kumawonjezera chimwemwe.
Chifuno Chenicheni m’Moyo
7, 8. (a) Kodi ndimotani mmene tiyenera kumvetsetsera Salmo 90:12? (b) Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi mtima wanzeru?
7 Chiphunzitso cha Yehova chipindulitsa potisonyeza mmene tingagwiritsire ntchito moyo wathu mwanjira yatanthauzo. Kwenikweni, chiphunzitso chaumulungu chimatisonyeza mmene tingaŵerengere masiku athu mwanjira yapadera. Utali wa moyo wa zaka 70 umakhala ndi masiku pafupifupi 25,550. Munthu wazaka 50 zakubadwa watha kale 18,250 a masiku amenewo, ndipo masiku ake 7,300 oyembekezeredwa otsalawo amaoneka kukhala ochepa kwambiri. Makamaka panthaŵiyo mpamene munthu akhoza kumvetsetsa bwino chifukwa chake mneneri Mose anapemphera kwa Mulungu pa Salmo 90:12 kuti: “Mutidziŵitse kuŵerenga masiku athu motero, kuti tikhale nawo mtima wanzeru.” Koma kodi Mose anatanthauzanji ndi mawu amenewo?
8 Mose sanatanthauze kuti Mulungu akaulula chiŵerengero chenicheni cha masiku a moyo wa Mwisrayeli aliyense. Malinga ndi Salmo 90, mavesi 9 ndi 10, mneneri Wachihebri ameneyo anazindikira kuti utali wa moyo ungakhale zaka 70 kapena 80—waufupi ndithu. Chotero mawu a Salmo 90:12, mwachionekere anasonyeza chikhumbo cha m’pemphero cha Mose chakuti Yehova asonyeze, kapena aphunzitse, iye limodzi ndi anthu Ake kugwiritsira ntchito nzeru poona ‘masiku a zaka zawo’ ndi kuwagwiritsira ntchito mwanjira yovomerezedwa ndi Mulungu. Eya, komano bwanji ponena za ife? Kodi timaona tsiku lililonse kukhala lofunika kwambiri? Kodi timakhala ndi mtima wanzeru mwa kuyesayesa kuthera tsiku lililonse mwanjira yopindulitsa kuulemerero wa Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova Mulungu? Chiphunzitso chaumulungu chimatithandiza kuchita zimenezo kumene.
9. Kodi nchiyani chimene tingayembekezere ngati tiphunzira kuŵerenga masiku athu kuulemerero wa Yehova?
9 Ngati tiphunzira kuŵerenga masiku athu kuulemerero wa Yehova, tingakhoze kupitirizabe kuŵerenga masiku athu, pakuti chiphunzitso chaumulungu chimapereka chidziŵitso chopatsa moyo wamuyaya. “Koma moyo wosatha ndi uwu,” Yesu anatero, “kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Ndithudi, ngakhale ngati tingapeze nzeru zonse zadziko zimene zilipo, sizingatipatse moyo wamuyaya. Koma moyo wosatha ukhoza kukhala wathu ngati tipeza ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka cha anthu aŵiri ofunika koposa m’chilengedwe chonse ndi kusonyezadi chikhulupiriro.
10. Kodi nchiyani chimene insaikulopediya ina imanena ponena za maphunziro, ndipo kodi zimenezo zifanana motani ndi mapindu a chiphunzitso chaumulungu?
10 Mosasamala kanthu za utali wa moyo umene takhala nawo kale, tiyeni tikumbukire phindu lalikulu la chiphunzitso chaumulungu ili: Chimapatsa awo ochigwiritsira ntchito chifuno chenicheni m’moyo. The World Book Encyclopedia imati: “Maphunziro ayenera kuthandiza anthu kukhala ziŵalo zothandiza za chitaganya. Ayeneranso kuwathandiza kukulitsa chiyamikiro cha mwambo wawo ndi kukhala ndi moyo wokhutiritsa kwambiri.” Chiphunzitso chaumulungu chimatithandizadi kukhala ndi miyoyo yokhutiritsa. Chimakulitsa mwa ife chiyamikiro chachikulu cha mwambo wathu wauzimu monga anthu a Mulungu. Ndipo chimatipangadi kukhala ziŵalo zothandiza za chitaganya, popeza kuti chimatikhozetsa kuchita mbali yofunika kwambiri ya kukwaniritsa zosoŵa za anthu padziko lonse lapansi. Kodi tikuneneranji zimenezo?
Programu Yophunzitsa ya Padziko Lonse
11. Kodi ndimotani mmene Thomas Jefferson anasonyezera kufunika kwa maphunziro abwino?
11 Mosiyana ndi programu iliyonse ya maphunziro, chiphunzitso chaumulungu chimakwaniritsa zosoŵa za maphunziro za anthu. Kufunika kwa kuphunzitsa anthu kunaonedwa ndi Thomas Jefferson, yemwe anakhala prezidenti wachitatu wa United States. M’kalata ya pa August 13, 1786, yomwe analembera George Wythe, bwenzi ndi wosaina mnzake wa Declaration of Independence, Jefferson anati: “Ndiganiza kuti lamulo lofunika koposa pamalamulo athu onse ndilo la kuwanditsa chidziŵitso mwa anthu. Palibe maziko ena otsimikizirika amene angalinganizidwe, osungitsira ufulu ndi chimwemwe. . . . Bwanawe, chirikiza mkupiti wolimbana ndi umbuli; khazikitsa ndi kuwongolera lamulo la kuphunzitsa anthu wamba. Nzika zathu zidziŵetu . . . kuti msonkho umene udzalipiridwa pachifuno [cha maphunziro] suposa gawo limodzi mwa chikwi la umene udzalipiridwa kwa mafumu, ansembe, ndi akalonga amene adzabuka pakati pathu ngati tisiya anthu muumbuli.”
12. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chiphunzitso chaumulungu ndicho programu yachipambano ndi yopindulitsa koposa ya maphunziro apadziko lonse?
12 Mmalo mwa kulekerera anthu a mitima yolungama muumbuli, chiphunzitso cha Yehova chimapereka programu yabwino koposa ya maphunziro apadziko lonse kuti iwo apindule. Pamene Nkhondo Yadziko II inali mkati zaka 50 zapitazo, bungwe la Committee on Educational Reconstruction la United States linaona kufunika kofulumira kwa “maphunziro apadziko lonse.” Kufunika kumeneko kudakalipo, koma chiphunzitso chaumulungu ndicho programu yokha yachipambano ya maphunziro apadziko lonse. Ilinso yopindulitsa koposa chifukwa imawonjola anthu kukutaya mtima, imawalimbikitsa mwamakhalidwe ndi mwauzimu, imawapulumutsa ku malingaliro a dziko onyada ndi atsankho, ndipo imapereka chidziŵitso cha moyo wamuyaya. Koposa zonse, programu imeneyi ikupindulitsa anthu kulikonse mwa kuwaphunzitsa kutumikira Yehova Mulungu.
13. Kodi lemba la Yesaya 2:2-4 likukwaniritsidwa motani lerolino?
13 Mapindu a chiphunzitso chaumulungu akupezedwa ndi miyandamiyanda ya anthu tsopano amene akukhala atumiki a Mulungu. Iwo amazindikira kusoŵa kwawo kwauzimu ndipo akudziŵa bwino lomwe kuti tsiku la Yehova layandikira. (Mateyu 5:3; 1 Atesalonika 5:1-6) Tsopano lino, mu “masiku otsiriza,” anthu a mitundu yonse ameneŵa akukwera kuphiri la Yehova, kulambiridwa kwake koyera. Iko kuli kokhazikitsidwa zolimba ndipo kwakwezedwa pamwamba pa kulambira konse kotsutsana ndi chifuniro cha Mulungu. (Yesaya 2:2-4) Ngati ndinu mmodzi wa Mboni yodzipatulira ya Yehova, kodi simuli wosangalala kukhala m’gulu lomawonjezereka nthaŵi zonse lomlambira ndi kupindula ndi chiphunzitso chaumulungu? Nkwabwino chotani nanga kukhala pakati pa awo amene akufuula kuti: “Tamandani Ya, anthu inu!”—Salmo 150:6, NW.
Chiyambukiro Chopindulitsa pa Mzimu Wathu
14. Kodi kutsatira uphungu wa Paulo wa pa 1 Akorinto 14:20 kuli ndi phindu lotani?
14 Pakati pa mapindu ambiri a chiphunzitso chaumulungu pali chiyambukiro chake chabwino pa kalingaliridwe ndi mzimu wathu. Chimatifulumiza kulingalira zinthu zolungama, zoyera, zokoma, ndi zotamandika. (Afilipi 4:8) Chiphunzitso cha Yehova chimatithandiza kutsatira uphungu wa Paulo wakuti: “M’choipa khalani makanda, koma m’chidziŵitso akulu misinkhu.” (1 Akorinto 14:20) Ngati tigwiritsira ntchito chilangizo chimenechi, sitidzafuna kukhala ndi chidziŵitso m’zoipa. Paulo analembanso kuti: “Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.” (Aefeso 4:31) Kulabadira uphungu wotero kudzatithandiza kupeŵa chisembwere ndi machimo ena aakulu. Pamene kuli kwakuti kuchita motero kungatipindulitse mwakuthupi ndi mwamaganizo, iko makamaka kudzatidzetsera chimwemwe podziŵa kuti tikukondweretsa Mulungu.
15. Kodi nchiyani chingatithandize kukhala aukoma m’malingaliro?
15 Ngati titi tikhalebe aukoma m’malingaliro, chimodzi cha zithandizo ndicho kupeŵa ‘mayanjano oipa amene amaipsa makhalidwe okoma.’ (1 Akorinto 15:33) Monga Akristu, sitingayanjane ndi adama, achigololo, ndi ochita zoipa ena. Moyenerera pamenepa, sitiyenera kuyanjana ndi anthu otero mwa kuŵerenga za iwo kuti tisangalale kapena kuwapenyerera pawailesi yakanema kapena m’mafilimu. Mtima uli wonyenga, ungakulitse mosavuta chikhumbo cha zinthu zoipa, ndipo ungayesedwe kuzichita. (Yeremiya 17:9) Chotero tiyeni tipeŵe ziyeso zotero mwa kumamatira ku chiphunzitso chaumulungu. Chingayambukire kwambiri kalingaliridwe ka “okonda Yehova” kwakuti phindu lake lingawachititse kufikira pa ‘kudana nacho choipa.’—Salmo 97:10.
16. Kodi ndimotani mmene chiphunzitso cha Mulungu chingayambukirire mzimu umene tisonyeza?
16 Paulo anauza wantchito mnzake Timoteo kuti: “Ambuye akhale ndi mzimu wako. Chisomo chikhale nanu.” (2 Timoteo 4:22) Mtumwiyo anakhumba kuti Mulungu, kupyolera mwa Ambuye Yesu Kristu, avomereze mphamvu yosonkhezera Timoteo ndi Akristu ena. Chiphunzitso cha Mulungu chimatithandiza kusonyeza mzimu wa chikondi, kukoma mtima, ndi kufatsa. (Akolose 3:9-14) Ndipo umenewo umasiyana chotani nanga ndi uja wa ambiri m’masiku otsiriza ano! Iwo ngodzikweza, osayamika, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, aliuma, okonda zokondweretsa, ndi opanda kudzipereka kwaumulungu. (2 Timoteo 3:1-5) Komabe, pamene tipitiriza kugwiritsira ntchito mapindu a chiphunzitso chaumulungu m’miyoyo yathu, timasonyeza mzimu umene umatichititsa kukhala okondedwa ndi Mulungu ndi anthu anzathu.
Chipindulitsa m’Maunansi Aumunthu
17. Kodi nchifukwa ninji kugwirizanika modzichepetsa kuli kofunika kwambiri?
17 Chiphunzitso cha Yehova chimatithandiza kupeza mapindu a kugwirizana modzichepetsa ndi olambira anzathu. (Salmo 138:6) Mosiyana ndi anthu ambiri lerolino, sitimaswa malamulo olungama koma ndife oyanjanitsika. Mwachitsanzo, pamakhala ubwino wochuluka chifukwa chakuti akulu oikidwa amakhala oyanjanitsika pamisonkhano ya akulu. Amuna ameneŵa amalankhula mofatsa kuchirikiza chowonadi, pamene kuli kwakuti samalola malingaliro amphamvu kuphimba kulingalira kwabwino kapena kuchititsa magaŵano. Ziŵalo zonse za mpingo zidzapindula ndi mzimu wa umodzi umene timapeza ngati tonsefe tipitirizabe kugwiritsira ntchito chiphunzitso chaumulungu.—Salmo 133:1-3.
18. Kodi chiphunzitso chaumulungu chimatithandiza kukhala ndi lingaliro lotani pa okhulupirira anzathu?
18 Chiphunzitso chaumulungu chimapindulitsanso potithandiza kukhala ndi lingaliro loyenera la okhulupirira anzathu. Yesu anati: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Makamaka chiyambire 1919, Yehova wachititsa atumiki ake kulengeza ziweruzo zake, ndipo dongosolo la dziko la Satana lagwedezedwa ndi chenjezo lapadziko lonse limeneli. Panthaŵi imodzimodzi, anthu owopa Mulungu—“zinthu zofunika”—akokedwa ndi Mulungu kudzilekanitsa iwo eni ku mitundu ndi kugwirizana ndi Akristu odzozedwa kudzaza nyumba ya Yehova yolambirira ndi ulemerero. (Hagai 2:7, NW) Ndithudi, tiyenera kuona ofunika otero okokedwa ndi Mulungu kukhala atsamwali okondedwa.
19. Kodi chiphunzitso cha Mulungu chimavumbula chiyani ponena za kuthetsa mavuto aumwini ndi Akristu anzathu?
19 Ndithudi, chifukwa chakuti tonsefe tili opanda ungwiro, sinthaŵi zonse pamene zinthu zidzayenda bwinobwino. Pamene Paulo anali pafupi kuyamba ulendo wake wachiŵiri waumishonale, Barnaba anafuna kwambiri kupitira limodzi ndi Marko. Paulo sanavomereze chifukwa Marko “anawasiya nabwerera pa Pamfuliya paja osamuka nawo kuntchito.” Pamenepo, panabuka “kupsetsana mtima.” Barnaba anatenga Marko napita naye ku Kupro, pamene Paulo anatenga Sila kutsagana naye kupyola mu Suriya ndi Kilikiya. (Machitidwe 15:36-41) Pambuyo pake, kugaŵanikana kumeneku mwachionekere kunathetsedwa, pakuti Marko anali ndi Paulo ku Roma, ndipo mtumwiyo anasimba zabwino ponena za iye. (Akolose 4:10) Limodzi la mapindu a chiphunzitso chaumulungu nlakuti chimatisonyeza mmene tingathetsere mavuto aumwini pakati pa Akristu mwa kutsatira uphungu wonga wa Yesu pa Mateyu 5:23, 24 ndi Mateyu 18:15-17.
Chipindulitsa ndi Kulakika Nthaŵi Zonse
20, 21. Kodi kupenda kwathu chiphunzitso chaumulungu kuyenera kutisonkhezera kuchitanji?
20 Ngakhale kuchokera m’kupenda kwathu kwachidule kwa ena a mapindu ndi zilakiko za chiphunzitso chaumulungu, mosakayikira tonsefe tingathe kuona kufunika kwa kulimbikira kuchigwiritsira ntchito m’miyoyo yathu. Pamenepa, ndi mzimu wa pemphero, tiyeni tipitirizebe kuphunzira kwa Mlangizi wathu Wamkulu. Posachedwa, chiphunzitso chaumulungu chidzalakika kuposa ndi kalelonse. Icho chidzalakika pamene anzeru adziko lino afafanizidwa. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 1:19.) Ndiponso, pamene ena mamiliyoni ambiri akuphunzira ndi kuchita chifuniro cha Mulungu, chidziŵitso cha Yehova chidzafunga padziko lonse lapansi monga madzi adzaza nyanja yeniyeniyo. (Yesaya 11:9) Zimenezo zidzapindulitsa chotani nanga anthu omvera ndi kulemekeza Yehova monga Mfumu ya Chilengedwe chonse!
21 Chiphunzitso cha Yehova chidzakhala chopindulitsa ndi cholakika nthaŵi zonse. Kod inu mudzapitiriza kupindula nacho monga wophunzira wakhama wa Buku Lophunziridwa lalikulu la Mulungu? Kodi mukukhala ndi moyo mogwirizana ndi Baibulo ndi kuuza ena chowonadi chake? Ngati zili choncho, mungayang’ane kutsogolo mwachidwi ku chilakiko chotheratu cha chiphunzitso chaumulungu, kuulemerero wa Mlangizi wathu Wamkulu, Ambuye Mfumu Yehova.
Kodi Mwaphunziranji?
◻ Kodi nchiyambukiro chotani chimene chiphunzitso chaumulungu chingakhale nacho pamiyoyo yathu?
◻ Kodi ndimotani mmene chiphunzitso cha Yehova chikukwaniritsira zosoŵa za maphunziro?
◻ Kodi nchiyambukiro chopindulitsa chotani chimene chiphunzitso chaumulungu chingakhale nacho pa kalingaliridwe ndi mkhalidwe wathu wa maganizo?
◻ Kodi ndimotani mmene chiphunzitso cha Mulungu chimakhalira chopindulitsa m’maunansi aumunthu?
[Chithunzi patsamba 15]
Chiphunzitso chaumulungu chimatisonyeza mmene tingayendere ndi Mulungu, monga momwe anachitira Nowa
[Chithunzi patsamba 17]
Anthu a mitundu yonse akukwera kuphiri la Yehova