Yesu—Wolamulira Yemwe “Matulukiro Ake Ndiwo Akale Lomwe”
MTIMA umangoti gu-gu-gu podikira kulandira wachibale yemwe munalekana naye kale kwambiri. Kenaka, mukumana nkumpatsa moni mwachimwemwe. Mumvetsera mwatcheru pokuuzani chifukwa chimene atate wake amtumira kudzakuchezerani. Ndiyeno msangamsanga ifika nthaŵi yoti azibwerera kwawo. Mukutsazikana naye mosakondwa. Chisoni chimene munamva ponyamuka iye chikutha pamene mwamva kuti wafika kwawo bwinobwino.
Kenaka, pofufuzafufuza mapepala ena akale, mupeza makalata ena amene akutchula zimene mbale wanuyo anachita kale asanayambe ulendo wake wodzakuonani. Zimene makalatawo akukuuzani zikukuthandizani kudziŵa za moyo wake wakale ndipo zikukuthandizani kuzindikira chifukwa chimene anadzakuchezerani ndiponso ntchito imene akuchita tsopano.
‘Wakale Lomwe’
Mwa mapepala akale omwe Ayuda a m’zaka za zana loyamba anali nawo, panalinso ena amene analembedwa ndi mneneri wa Mulungu Mika. Panali patapita zaka mazana asanu ndi aŵiri chilembere. Mapepala amenewo anatchula malo obadwira Mesiya. “Koma iwe, Betelehemu Efrata, ndiwe wamng’ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza m’Israyeli; matulukiro ake ndiwo akale lomwe, kuyambira nthaŵi yosayamba.” (Mika 5:2) Mawuwo analidi oona, Yesu anadzabadwa m’mudzi wa Betelehemu ku Yudeya, m’chaka chimene tsopano chikutchedwa kuti 2 B.C.E. Komano chiyambi chake ‘nchakale lomwe’ bwanji?
Yesu anakhalako kale asanakhale munthu. Mtumwi Paulo, m’kalata yake kwa Akristu a ku Kolose, anati Yesu ali ‘fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.’—Akolose 1:15.
Kuti tinene monga mwa mawu ouziridwa omwe Mfumu Solomo analemba m’buku la Miyambo, Yehova, Mwini nzeruyo, analenga Mwana wake woyamba ‘asanalenge zake zakale.’ Atakhala padziko lapansi kwa kanthaŵi nkubwereranso kumwamba, Yesu anachitira umboni kuti iyeyo ndiyedi “woyamba wa chilengo cha Mulungu.” Monga nzeru imene inalankhula ngati munthu, Yesu asanadze padziko lapansi ananena kuti: “Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo.”—Miyambo 8:22, 23, 27; Chivumbulutso 3:14.
Kungoyambira pachiyambi, Mwana wa Mulungu anapatsidwa ntchito yapadera, anali “mmisiri” pambali pa Atate wake. Zimenezotu ndiye zinamsangalatsa Yehova! Miyambo 8:30 ikutinso: “Ndinali munthu amene iye [Yehova] anali kukonda ndithu masiku onse, ndi kukondwera pamaso pake nthaŵi zonse.”—NW.
Patapita nthaŵi Yehova anapempha Mwana wake woyamba kubadwayo kuti agwire naye ntchito yolenga anthu. Anatero kuti, “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.” (Genesis 1:26) Zitatero, chikondi chinanso chinayambika. Yesuyo akali mzimu anafotokoza kuti: ‘Ndinkasekerera ndi ana a anthu.’ (Miyambo 8:31) Kuchiyambi kwa Uthenga wake Wabwino, mtumwi Yohane anachitira umboni kuti Yesu asanakhale munthu ntchito yake inali yakulenga: “Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.”—Yohane 1:3.
Wolankhulira Yehova
Mawu a Yohane akusonyezanso mwayi wina umene Mwana wa Mulungu anali nawo, anali womlankhulira. Kuyambira pachiyambi, anatumikira monga Mawu. Choncho, pamene Yehova ankalankhula ndi Adamu, ndipo kenaka pamene analankhula ndi Adamu limodzi ndi Hava, mwina analankhula nawo kudzera mwa Mawuyo. Ndipo ndani winanso amene akanapereka kwa mtundu wa anthu malangizo a Mulungu kuti apindule nawo kuposa uyo amene anawakonda anthuwo?—Yohane 1:1, 2.
Ndipotu Mawuyo ayenera kukhala ataŵaŵidwa mtima poona Hava ndiyeno Adamu atalephera kumvera Mlengi wawo! Ndipo ayenera kukhala atakhumba kuchotsera ana a anthuwo mavuto amene kusamvera kwa makolowo kunayambitsa. (Genesis 2:15-17; 3:6, 8; Aroma 5:12) Polankhula ndi Satana, yemwe analimbikitsa Hava kupanduka, Yehova anati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake.” (Genesis 3:15) Poti anaona zimene zinachitika m’Edene, Mawuyo anadziŵa kuti poti iye ndiye anali woyamba wa “mbewu” ya mkazi, adzadedwa zedi. Anadziŵa kuti Satana anali wambanda.—Yohane 8:44.
Pamene Satana anakayikira kukhulupirika kwa Yobu, Mawuyo ziyenera kukhala zitampsetsa mtima kumva Satana akuneneza Atate wake mwanjiru. (Yobu 1:6-10; 2:1-4) Ndithudi, pantchito yake monga mngelo wamkulu, Mawuyo amatchedwa Mikaeli, ndipo dzina lake limatanthauza kuti “Ali Ngati Mulungu Ndani?” ndipo likusonyeza mmene adzamenyera nkhondo Yehova polimbana ndi onse amene amayesayesa kulanda uchifumu wa Mulungu.—Danieli 12:1; Chivumbulutso 12:7-10.
Mmene mbiri ya Israyeli inali kukula, Mawuyo ankaona kuti Satana ankayesa kupatutsa anthu pa kulambira koyera. Aisrayeli atangotuluka m’Igupto, Mulungu anawauza kudzera mwa Mose kuti: “Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamalo pomwe ndakonzeratu. Musamalire iye, ndi kumvera mawu ake; musamwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m’mtima mwake.” (Eksodo 23:20, 21) Kodi mngelo ameneyo anali yani? Mwina anali Yesu asanakhale munthu.
Kugonjera Mokhulupirika
Mose anafa mu 1473 B.C.E., ndipo mtembo wake unaikidwa “m’chigwa m’dziko la Moabu popenyana ndi Beti-peori.” (Deuteronomo 34:5, 6) Mwinamwake, nkutheka kuti Satana ankafuna kugwiritsira ntchito mtembowo kuchirikiza kulambira mafano. Mikaeli anatsutsa zimenezo komabe, mogonjera, anadikira kuti Atate wake Yehova achitepo kanthu mwaulamuliro wawo. ‘Posalimbika mtima kumtchulira Satana chifukwa chomchitira mwano,’ Mikaeli anachenjeza Satana kuti: “Ambuye akudzudzule.”—Yuda 9.
Kenaka Israyeli anayamba kulanda Dziko Lolonjezedwa la Kanani. Pafupi ndi mzinda wa Yeriko, Yoswa analonjezedwa kuti Mawuyo adzapitiriza kutsogolera mtunduwo. Kumeneko anakumana ndi mwamuna atagwiriza lupanga lake losolola. Yoswa anamuyandikira munthu wachilendoyo nkumfunsa kuti: “Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?” Tangoganizani mmene Yoswa anadabwira pamene wachilendoyo anadzidziŵikitsa kuti: “Iyayi, koma ndadza ine, kazembe wa ankhondo a Yehova.” Nzosadabwitsa kuti Yoswa anagwetsa nkhope pansi pamaso pa woimira Yehova wamphamvu ameneyo, mosakayikira yemwe anali Yesu asanakhale munthu, amene anali kudzakhala “Mesiya Mtsogoleri.”—Yoswa 5:13-15; Danieli 9:25, NW.
Mkangano winanso ndi Satana unachitika m’masiku a mneneri wa Mulungu Danieli. Pachochitika chimenecho Mikaeli anachirikiza mngelo mnzake pamene kalonga wa ziŵanda wa Peresiya ‘anamtsekerezera njira’ milungu itatu. Mngeloyo anafotokoza kuti: “Taonani, Mikaeli, wina wa akalonga omveka, anadza kundithandiza; ndipo ndinakhala komweko ndi mafumu a Perisiya.”—Danieli 10:13, 21.
Ulemerero Wake Asanakhale Munthu Ndiponso Atakhala Munthu
Mu 778 B.C.E., chaka chimene Mfumu ya Yudeya Uziya anafa, mneneri wa Mulungu Yesaya anaona masomphenya a Yehova ali pampando wake wachifumu wokwezeka. Yehova anafunsa kuti: ‘Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?’ Yesaya anadzipereka, koma Yehova anamchenjeza kuti Aisrayeli anzake sakamvera zonena zake. Mtumwi Yohane anayerekezera Ayuda osakhulupirirawo a m’zaka za zana loyamba ndi anthu a m’tsiku la Yesaya, ndipo anati: “Izi anati Yesaya, chifukwa anaona ulemerero wake.” Ulemerero wandani? Wa Yehova ndi wa Yesu pambali pake kumwamba asanakhale munthu.—Yesaya 6:1, 8-10; Yohane 12:37-41.
Patatha mazana a zaka, Yesu anapatsidwano ntchito yaikulu zedi kuposa zonse panthaŵiyo. Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake wokondedwa kuchokera kumwamba nkuuika m’mimba mwa Mariya. Patatha miyezi isanu ndi inayi anabala mwana wamwamuna, Yesu. (Luka 2:1-7, 21) Malinga ndi kunena kwa mtumwi Paulo: “Pokwaniridwa nthaŵi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi.” (Agalatiya 4:4) Mtumwi Yohane nayenso anavomereza kuti: “Mawu anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.”—Yohane 1:14.
Mesiya Aonekera
Ngakhale pamene anali wazaka 12 zokha, mnyamatayo Yesu anali atadziŵa kuti ayenera kutanganidwa pantchito ya Atate wake wakumwamba. (Luka 2:48, 49) Patatha zaka 18, Yesu anabwera kwa Yohane Mbatizi kumtsinje wa Yordano ndipo anabatizidwa. Pamene Yesu anali kupemphera, kumwamba kunatseguka, ndipo mzimu woyera unatsikira pa iye. Tangolingalirani zinthu zambiri zimene zinabwera m’maganizo mwake pokumbukira zaka zikwizikwi zimene anagwira ntchito pambali pa Atate wake monga mmisiri, mlankhuli, kazembe wa ankhondo a Mulungu, ndiponso monga mngelo wamkulu, Mikaeli. Kenako anadzasangalala atamva mawu a Atate wake pouza Yohane Mbatizi kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.”—Mateyu 3:16, 17; Luka 3:21, 22.
Ndithu Yohane Mbatizi sanakayikire zoti Yesu analipo kale asanakhale munthu. Pamene Yesu anapita kwa iye, Yohane anati: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!” Ndiyeno anadzatinso: ‘Ndiye amene ndinati za Iye, Pambuyo panga palinkudza munthu amene analipo ndisanabadwe ine; pakuti anali woyamba wa ine.’ (Yohane 1:15, 29, 30) Mtumwi Yohane nayenso anadziŵa zoti Yesu anakhalako kale. Analemba kuti: “Iye wochokera kumwamba ali woposa onse.” Ndipo anabwerezanso kuti: ‘Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse. Chimene anachiona nachimva, achita umboni wa ichi chomwe.’—Yohane 3:31, 32.
Pomafika chaka cha 61 C.E., mtumwi Paulo anasonkhezera Akristu achihebri kuzindikira kuti kufika kwa Mesiya padziko lapansi kunali kofunika ndi kutinso adziŵe ntchito yake monga Mkulu wa Ansembe. Powauza za ntchito ya Yesu kuti anali Mlankhuli, Paulo anati: “Mulungu . . . pakutha pake pa masiku ano analankhula ndi ife ndi Mwana . . . mwa iyenso analenga maiko ndi a m’mwamba omwe.” Kaya zimenezo zikutanthauza ntchito ya Yesu monga “mmisiri” polenga zinthu kapena zoti ali ndi mbali m’makonzedwe a Mulungu a kuyanjanitsanso anthu, panopa Paulo akuchitira umboni kuti Yesu anakhalako kale asanakhale munthu.—Ahebri 1:1-6; 2:9.
Wokhulupirika Kuyambira “Kale Lomwe”
Akristu a m’zaka za zana loyamba ku Filipi anapatsidwa uphungu ndi Paulo wakuti: “Mukhale nawo mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu, ameneyo, pokhala nawo maonekedwe a Mulungu, sanachiyesa cholanda kukhala wofana ndi Mulungu, koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu; ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu, anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.” (Afilipi 2:5-8) Mwachikondi Yehova anayamikira kukhulupirika kwa Yesu mwa kumuukitsa ndi kumlandiranso kumwamba. Chimenechotu ndiye chinali chitsanzo chabwino zedi chimene Yesu anatisiira cha kukhulupirika kwa zaka zosaŵerengeka!—1 Petro 2:21.
Tikuyamikiratu kuti Baibulo limatisonyeza zimene Yesu anachita kale asanakhale munthu! Zimatilimbikitsadi kutsimikiza kutsanzira chitsanzo chake chakutumikira mokhulupirika, makamaka tsopano poona kuti ali Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Waumesiya ndipo akulamulira. Tiyeni titame ‘Kalonga Wamtendere,’ Kristu Yesu, Wolamulira wathu, yemwe “matulukiro ake ndiwo akale lomwe”!—Yesaya 9:6; Mika 5:2.
[Bokosi patsamba 24]
Umboni Wakuti Anakhalako Kale Asanakhale Munthu
Mawu a Yesu mwiniyo, omwe atchulidwa pansipa, akuchitira umboni wokwanira wakuti iye anakhalako kale asanakhale munthu:
◻ ‘Kulibe munthu anakwera Kumwamba, koma Iye wotsikayo kuchokera Kumwamba, ndiye Mwana wa munthu.’—Yohane 3:13.
◻ ‘Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba. Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi. . . . Ndinatsika Kumwamba, si kuti ndichite chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye amene anandituma Ine.’—Yohane 6:32, 33, 38.
◻ ‘Mkate wotsika Kumwamba ndi uwu, kuti munthu akadyeko ndi kusamwalira. Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha.’—Yohane 6:50, 51.
◻ ‘Nanga bwanji ngati mukaona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?’—Yohane 6:62.
◻ ‘Umboni wanga uli woona; chifukwa ndidziŵa kumene ndinachokera ndi kumene ndimukako. . . . Ine ndine wochokera Kumwamba. Inu ndinu a dziko lino lapansi; sindili Ine wa dziko lino lapansi.’—Yohane 8:14, 23.
◻ ‘Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine.’—Yohane 8:42.
◻ ‘Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.’—Yohane 8:58.
◻ ‘Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nawo ndi Inu lisanakhale dziko lapansi. Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang’anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.’—Yohane 17:5, 24.
[Chithunzi patsamba 23]
Yoswa akumana ndi kalonga wa ankhondo a Yehova