Malo Kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Chipululu cha Yuda—Chosabala Koma Chosangalatsa
KODI mumalingalira chipululu cha Yuda m’Dziko Lolonjezedwa kukhala chotani? Ena amaganiza za nkhalango yaikulu, ya mitengo yambiri. Ena amalingalira chipululu chofanana ndi Sahara chokhala ndi malo aakulu a mchenga.
Palibe nchimodzi cha zithunzi ziŵirizi chimene chimafanana ndi chipululu chimenechi, monga mmene mungawonere pa chithunzithunzi chapamwambacho. M’kawonedweka, inu mukuyang’ana pa mbali ya chipululucho yogwirizanitsidwa ndi Yesu. Mwambo umanena kuti Satana anasonyeza Yesu “maiko onse a dziko lapansi” kuchokera pa malo apamwamba ameneŵa, omwe ali pothera pa chipululu ndipo moyang’ana pansi pali mzinda wa Yeriko wokometsedwa ndi mitengo ya kanjedza m’Chigwa cha Yordano cha kum’mawa.—Mateyu 3:1; 4:1-11.
Kuchokera ku mbali imeneyi ya kumpoto koma chakum’mawa, chipululu cha Yuda chimafutukuka kulinga ku mbali ya kumadzulo kwa Dead Sea. Ngati muyang’ana pa mapu ya pa chikuto cha 1989 Kalenda ya Mboni za Yehova, mudzathandizidwa kukhala ndi chithunzi cha malo amenewa. (Kalendayo irinso ndi chithunzi chachikulu cha chithunzithunzi chapamwambachi.) Chipululucho (chotakata makilomita 16 kufika ku 24) chiri pa malo otsetsereka a kum’mawa kwa mapiri a Yudeya, kutsika kufika ku gombe la Dead Sea.
Mapiri amenewo amatsekereza mphepo ya chinyontho yochokera ku Mediterranean Sea. Chotero zitunda zopanda kanthu za mwala wofeŵa wa chalk, mbali ya kum’mawa zimalandira mvula yochepera kusiyapo kokha m’miyezi ya nyengo yachisanu ya November ndi December. Pa nthaŵiyo udzu umamera, kukhozetsa nkhosa kubudula kumeneko. Chotero, “makola a nkhosa” otchulidwa pa 1 Samueli 24:3 molondola amayenerera chigawo chimenechi.
Udzu womakula pamenepa sumakhala kwa nthaŵi yaitali. Mphepo ya kum’mawa kuchokera ku chipululucho mwamsanga imapsyereza malo obiriŵirawo. Zimenezi zimachitira fanizo bwino lomwe chotani nanga ndemanga ya ulosi yakuti: “Udzu unyala, duŵa lifota, koma mawu a Mulungu wathu adzakhala nthaŵi zachikhalire.”—Yesaya 40:8; 1 Petro 1:24, 25.
Mwinamwake Yesu anakumbukira lemba limeneli pamene ankapupulika m’chipululuchi kwa usana 40 ndi usiku 40. Tangolingalirani mmene Yesu ayenera kukhala anadzimverera m’dzuŵa lotentha lomaŵala pa matanthwe amenewo opanda mitengo ndi m’mipata. (Yesaya 32:2) Nzomveka chotani nanga kuti pambuyo pake “angelo anadza, namtumikira iye”!—Mateyu 4:1-11.
Chifukwa cha kusabala kwake ndi kusakhalidwa ndi anthu, chipululu cha Yuda kaŵirikaŵiri chinagwiritsiridwa ntchito monga malo othaŵirako. Pamene ankathaŵa kwa Mfumu yokwiya Sauli, Davide anapeza chitetezo kumeneko, akuchilongosola kukhala “m’dziko lowuma ndi lotopetsa, lopanda madzi.” (Salmo 63:1 ndi mawu apamwamba; 1 Samueli 23:29) Kwa kanthaŵi iye anabisala m’phanga, mwinamwake lofanana ndi Phanga la Umm Qatafa mu Wadi Khareitun (chigwa chofutukuka kuchokera kum’mawa kwa Betelehemu kulinga ku Dead Sea). (Ahebri 11:32, 38) Kawonedwe kameneka kuchokera pa phangalo, mungawone m’munsi kulamanja nkhosa zakuda zikufunafuna udzu.
Davide anali kuphanga m’chigawo cha Engedi pamene Sauli analoŵa kuti adzithandize. Ngakhale kuti Davide anadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli, iye sakanavulaza “wodzozedwa wa Yehova.” Pambuyo pake Davide anaitana Sauli, mwinamwake pamene mfumuyo inali pansi pakati pa zitsamba zambiri. (1 Samueli 24:1-22) ‘Zitsamba zambiri pano?’ inu mungadabwe.
Inde, ngati pali madzi okwanira, chipululu chimenechi chimamera. Chitsanzo ndicho Engedi. Madzi omakwera kupyolera m’thanthwe lofeŵa amatumphuka monga akasupe ndi mathinthi m’chigwa chimenechi chomwe chimayambira pa gombe la kumadzulo la Dead Sea. Zimenezi zimapangitsa Engedi kukhala nkhalango yeniyeni, yodzaza ndi zomera. Mutapitako, mungapeze mitundu yambiri ya maluŵa ndi zipatso. Mungawonenso nyama zakutchire, kuyamba ndi achiwuli a m’matanthwe kufika ku agwape; malowo alinso ndi akambuku!—1 Samueli 24:2; Nyimbo ya Solomo 1:14.
Kudziŵa kuti chipululu cha Yuda chosabala chimenechi chingakhale chobiriŵira motero ndi zomera kumamveketsa bwinopo kwa ife masomphenya a Ezekieli a madzi oyenda kuchokera ku kachisi m’Yerusalemu. Madzi oyendawo anaŵirikiza kufikira anakhala m’kokomo wa madzi othamanga mwamphamvu otsikira kum’mawa kupyolera m’chipululu cha Yuda. Ndi chotulukapo chotani? Ezekieli adalemba kuti: “Tawonani, pa gombe la mtsinjewo mitengo yambirimbiri . . . Zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake la kuchiritsa.” Madziwo anathirira mu Dead Sea, nachiritsadi madzi ake opanda zamoyo.—Ezekieli 47:1-12; Yesaya 35:1, 6, 7.
Chotero, ngakhale kuti chipululu cha Yuda nchowumirako ndi chosakhalidwa, chirinso mbali yosangalatsa ya malo osiyanasiyana opezeka m’zolembera zambiri za Baibulo.—Luka 10:29-37.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 17]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.